Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g02 5/8 tsamba 32
  • Buku Limene Lingathandize Kumanga Mabanja

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Buku Limene Lingathandize Kumanga Mabanja
  • Galamukani!—2002
Galamukani!—2002
g02 5/8 tsamba 32

Buku Limene Lingathandize Kumanga Mabanja

MKAZI WINA DZINA LAKE LESLIE, wa ku America mumzinda wina wotchedwa Louisiana, analandira telefoni chaka chatha yochokera kwa nthumwi ina ya payunivesite ya Tulane. Nthumwiyo inanena kuti anthu a payunivesite ya Tulane komanso payunivesite ina ankafufuza zinazake zokhudza anthu amene anangokwatirana kumene mumzinda wa Louisiana.

Mkazi winanso atavomereza kuti amufunse mafunso enaake a nkhaniyi, analandira chikalata choti alembepo mayankho ake ndipo anayankha mafunso onsewo, kenaka n’kuchitumiza pamodzi ndi buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Mkaziyo anafotokoza kuti iye pamodzi ndi mwamuna wake ndi Mboni za Yehova ndiponso kuti bukulo analiŵerenga ali limodzi pokonzekera ukwati wawo.

Patangotha masabata ochepa chabe, mkulu amene ankayang’anira za kufufuzako analandira kalatayo, ndipo analemba kuti: “Tikukhulupirira kuti mabanja ofanana ndi banja lanu akhoza kutiphunzitsa chinsinsi chomangira banja lolimba ndiponso losangalatsa. Nthaŵi zambiri okwatirana amangokhalira kukangana chifukwa saganizira mfundo yofunika yakuti anakula mosiyana. Koma mmene inuyo munakonzekerera banja lanu, makamaka pogwiritsa ntchito mabuku ngati buku limene munatumiza kuno, zidzakuthandizani kuti muzikambirana bwinobwino mukasiyana maganizo pankhani iliyonse. Ndiponsotu, kulimbikira kupembedza ndi chinthu chofunika kwambiri m’banja. Muli ndi mwayi nonsenu pokhala ndi chikhulupiriro cholimba ndiponso podalira Mulungu kuti akuthandizeni.

“Buku limene munanditumizira ndaliika padesiki yanga kuti anthu onse aziliona, ndipo tsopano anthu amene ndimawaphunzitsa akandifunsa malangizo okhudza za kuloŵa m’banja ndimawaonetsa bukuli. M’mbuyo monsemu ndinali ndisanalioneko, ndipo osanamizana, bukuli ndi labwino kwambiri.”

Tikukhulupirira kuti inunso mungaone kuti bukuli ndi lofunika kwambiri. Kuti mulandire buku lanu lotere, chonde lembani zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kukatumiza ku adiresi imene ili pomwepo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino. Mudzapezamo mfundo zenizeni zimene zingathandize pothetsa mavuto ndiponso kupangitsa moyo wabanja kukhala wosangalatsa monga mmene Mlengi wathu ankafunira.

□ Nditumizireni buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja.

□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena