“Kanafika pa Nthaŵi Yofunika”
ZIMENEZO n’zimene mwamuna wina amene amakhala mumzinda wotchedwa Abakaliki ananena mu kalata imene analembera ku ofesi ya Mboni za Yehova ku Nigeria. Mwamunayu ankatchula za kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, kamene anali atangopatsidwa kumene. Iye anafotokoza kuti:
“Mkazi wanga dzina lake Tochi anatisiya atangobereka kumene pa June 18, 2000. Ngakhale kuti mwezi ndi masiku ena anali atapita, sindinaiwale kwenikweni, maganizo anali balala m’mutu mwanga, nyumba inkangondikulira, ndipo sindinakhulupirire zatsoka lopweteka kwambiri m’moyo wanga wonse lomwe linandigwerali. Kenaka m’mwezi wa July munthu wina wa m’gulu la Mboni za Yehova anandipatsa kabuku kanu kena kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Kabukuka kanali ngati mankhwala kwa ine, ndipo pang’ono ndi pang’ono ndayamba kulimba nkhongono, makamaka chifukwa cha malangizo amene ali m’kabukuka. Kunena zoona kabukuka kapangitsa kuti maganizo anga abwerere mwakale ndipo kandipangitsa kuzindikira kuti ngakhale kuti ineyo ndili m’mavuto aakulu kwambiri, zinthu zidzasintha m’tsogolomu.”
Mwinatu inuyo kapena munthu wina amene mukum’dziŵa nayenso angalimbikitsidwe ataŵerenga kabuku kamasamba 32 kameneka. Mungathe kuitanitsa kabuku kanu polemba zofunika m’kabokosi kali pamunsika ndi kutumiza ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Nditumizireni kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira.
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.