Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g03 12/8 tsamba 12-14
  • Kodi Ndingatani Kuti Anthu Asamangofanizira Zochita Zanga ndi za Mbale Wanga?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndingatani Kuti Anthu Asamangofanizira Zochita Zanga ndi za Mbale Wanga?
  • Galamukani!—2003
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Aoneni Moyenera Abale Anu
  • Phunzirani kwa Iwowo!
  • Pezani Zimene Inu Panokha Mungathe Kuchita Bwino
  • Kodi Ndingatani Ngati M’bale Wanga Wadzipha?
    Galamukani!—2008
  • Nchifukwa Ninji Chiri Chovuta Kukhala Limodzi Ndi Mbale Wanga ndi Mlongo?
    Galamukani!—1988
  • Kodi ndingatani kuti ndizigwirizana ndi abale anga?
    Galamukani!—2010
  • Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwirizana Ndi Abale Anga?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—2003
g03 12/8 tsamba 12-14

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndingatani Kuti Anthu Asamangofanizira Zochita Zanga ndi za Mbale Wanga?

“Ndinkafuna kuti ndikhale wodziŵika pandekha, koma nthaŵi zonse ndinkaona kuti ndinkafunika kuchita zinthu zimene akulu anga ankachita. Ndinkaona kuti sindingathe kuchita zinthu zimene akulu anga anakwanitsa kuchita.”—Anatero Clare.

KODI muli ndi mchimwene kapena mchemwali wanu amene zikuoneka kuti pafupifupi chilichonse chimene amachita chimamuyendera bwino? Kodi makolo anu nthaŵi zonse amakulimbikitsani kuti muzitengera mbale wanuyo? Ngati zili choncho, mungayambe kuda nkhaŵa kuti nthaŵi zonse anthu azidzafanizira zochita zanu ndi za mbale wanuyo, zomwe zikutanthauza kuti anthu adzakuonani kuti mukuchita bwino ngati muyesetsa kufika pamene mbale wanuyo wafikapo.

Azikulu ake a Barrya anamaliza Sukulu Yophunzitsa Utumikib imene imalemekezedwa kwambiri ndipo ali ndi mbiri yabwino monga Akristu. Barry anavomereza kuti: “Sindinkadziona kuti ndine wofunika pandekha chifukwa ndinkaona kuti sindingakwanitse kuchita zinthu mogwira mtima ngati azikulu anga pa ntchito yolalikira kapenanso kulankhula bwino pamaso pa anthu. Zinkandivuta kupeza mabwenzi angaanga chifukwa ndinkangoperekeza azikulu anga akaitanidwa kuti akacheze. Ndinkaona kuti anthu ankacheza nane chifukwa chakuti ankadziŵa abale anga basi.”

N’zachibadwa kuchita nsanje ngati muli ndi mbale wanu amene anthu nthaŵi zonse amamulemekeza. M’nthaŵi za m’Baibulo, Yosefe wachinyamata ankakondedwa kwambiri kuposa abale ake. Kodi abale ake anamva bwanji? “Anamuda iye, ndipo sanathe kulankhula ndi iye mwamtendere.” (Genesis 37:1-4) Komabe, Yosefe anali wofatsa. Koma mwina mbale wanu angayambitse mpikisano ndiponso kukukwiyitsani pokukumbutsani nthaŵi zonse zinthu zimene wachita bwino.

Achinyamata ena pofuna kusonyeza kukwiya kwawo amapanduka, mwina kumalephera dala kusukulu, kusachita nawo ntchito zachikristu mokwanira, kapena kuchita khalidwe loipa kwambiri. Angayambe kuganiza kuti ngati sangathe kuchita zinthu ngati mmene mbale wawo amachitira, palibe chifukwa choti aziyesera kuchita zoterozo. Komatu m’kupita kwa nthaŵi, kupanduka kudzangokuvulazani. Kodi mungatani kuti anthu asamangofanizira zochita zanu ndi za mbale wanu mwa njira imene muzidziona kuti ndinu wofunika panokha?

Aoneni Moyenera Abale Anu

Mukamaona mmene anthu amakondera mbale wanu, mukhoza kuyamba kukhulupirira kuti mbale wanuyo salakwitsa zinthu pamene inu simungakwanitse m’pang’ono pomwe kuchita zinthu ngati iyeyo. Koma kodi zimenezo n’zoona? Baibulo limafotokoza mosabisa kuti: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.”—Aroma 3:23.

Inde, kaya abale athu ali ndi luso lotani, ndi ‘anthu a mkhalidwe umodzimodzi’ ngati ife. (Machitidwe 14:15) Palibe chifukwa chowaonera ngati apamwamba kapena kuwakhumbira mopambanitsa. Munthu mmodzi yekha amene anakhazikitsa chitsanzo chochita zinthu mosalakwitsa ndi Yesu Kristu.—1 Petro 2:21.

Phunzirani kwa Iwowo!

Chinthu chotsatira chimene mufunika kuchita ndicho kuona zimene zikukuchitikiranizo kukhala mwayi wanu wophunzirapo kanthu. Mwachitsanzo, taganizirani za abale ndi alongo ake a Yesu Kristu. (Mateyu 13:55, 56) Talingalirani zinthu zimene akanaphunzira kwa mbale wawo wangwiroyo! Komabe, “abale ake sanakhulupirira Iye.” (Yohane 7:5) Mwina kunyada ndi nsanje n’zimene zinawalepheretsa kukhala ndi chikhulupiriro. Abale a Yesu auzimu, ophunzira ake, ndi amene anamvera pempho lake lakuti: “Phunzirani kwa Ine.” (Mateyu 11:29) Ndipo Yesu ataukitsidwa m’pamene abale ake enieni anazindikira kuti akanatha kuphunzira zambiri kwa Yesu. (Machitidwe 1:14) Koma panthaŵiyo anali ataphonya mwayi waukulu wophunzira kuchokera kwa mbale wawo walusoyo.

Kaini analinso ndi vuto lofananalo. Mng’ono wake, Abele, anali mtumiki wokondedwa ndi Mulungu. Baibulo limati “Yehova ndipo anayang’anira Abele [mokondwera, NW] ndi nsembe yake.” (Genesis 4:4) Komabe, pa zifukwa zina, Mulungu “sanayang’anira [mokondwera, NW] Kaini ndi nsembe yake.” Kaini anafunika kusonyeza khalidwe lodzichepetsa ndiponso kuphunzirapo kwa mbale wake. Mosiyana ndi zimenezo, “Kaini . . . anakwiya kwambiri” ndipo pomalizira pake anapha Abele.—Genesis 4:5-8.

Sikuti inu mungakwiyire mbale wanu kufika pamenepo. Komabe, inunso mukhoza kuphonya mwayi waukulu ngati mungalole kuti kunyada ndi nsanje zikulepheretseni. Ngati muli ndi mbale wanu amene amakhoza bwino masamu, ndi katswiri pa phunziro la mbiri yakale, amaseŵera bwino maseŵera amene inu mumakonda, amadziŵa bwino Malemba, kapena amadziŵa kulankhula bwino pamaso pa anthu, muyenera kupeŵa nsanje! Dziŵani kuti “nsanje ivunditsa mafupa” ndipo ikhoza kungokuwonongani. (Miyambo 14:30; 27:4) Mmalo mokwiya, yesetsani kuphunzira kwa mbale wanuyo. Vomerezani mfundo yakuti iyeyo ali ndi luso limene inuyo mulibe. Onetsetsani mmene mbale wanuyo amachitira zinthu kapena kungomufunsa kuti akuthandizeni.

Barry, amene tamutchula koyambirira uja, anapindula ndi zitsanzo zabwino zimene abale ake ankasonyeza. Iye anati: “Ndinkaona mmene abale anga ankasangalalira chifukwa chakuti anali ofunitsitsa kuthandiza anthu mu mpingo ndiponso pa ntchito yolalikira. Choncho, ndinaganiza zotengera chitsanzo cha abale anga, ndipo ndinayamba kugwira nawo ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu ndi Beteli. Zimene ndinadziŵa zinandilimbitsa mtima ndiponso kundithandiza kuti ndikulitse ubwenzi wanga ndi Yehova.”

Pezani Zimene Inu Panokha Mungathe Kuchita Bwino

Mwina mungaope kuti kutengera chitsanzo cha mbale wanu kukuchititsani kuti musakhalenso munthu wodziŵika panokha. Koma musaganize zimenezo. Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino kuti: “Khalani akutsanza ine.” (1 Akorinto 4:16) Kodi zimenezi zinatanthauza kuti Paulo ankafuna kuti Akristuwo asakhale odziŵika paokha? Ayi. Anthu ndi osiyanasiyana. Ngati simukhoza bwino masamu ngati mbale wanuyo, sizikutanthauza kuti ndinu wopereŵera. Zikungotanthauza kuti ndinu wosiyana ndi iyeyo.

Paulo anapereka langizo lothandiza ili: “Yense ayesere ntchito yake ya iye yekha, ndipo pamenepo adzakhala nako kudzitamandira chifukwa cha iye yekha, si chifukwa cha wina.” (Agalatiya 6:4) Bwanji osakulitsa luso lanulanu? Kuphunzira chilankhulo cha dziko lina, kugwiritsa ntchito chida choimbira, kapena kugwiritsa ntchito kompyuta kungakuthandizeni kuti muzidziona kuti ndinu munthu wofunika panokha, ndiponso kungakuthandizeni kuti mukhale ndi luso lofunika kwambiri. Musade nkhaŵa ndi kufuna kuchita zinthu mosalakwitsa! Phunzirani kuchita zinthu mosamala ndi mwaluso. (Miyambo 22:29) Mwina simungakhale ndi luso lachibadwa pa chinthu chinachake, koma ‘dzanja la akhama lidzalamulira,’ limatero lemba la Miyambo 12:24.

Komabe, muyenera kukulitsa makamaka moyo wanu wauzimu. Kukhala ndi luso pa zinthu zauzimu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi luso lina lililonse limene lingachititse chidwi anthu ena. Taganizirani za anthu aŵiri a mapasa, Esau ndi Yakobo. Esau ankakondedwa kwambiri ndi bambo ake chifukwa “anali munthu wakudziŵa zakusaka nyama, munthu wa m’thengo.” Poyamba mwina mungaone kuti mbale wake Yakobo, anali wonyozeka chifukwa chakuti anali “munthu wofatsa, wakukhala m’mahema.” (Genesis 25:27) Esau analephera kukulitsa moyo wake wauzimu ndipo sanalandire madalitso. Yakobo anakonda zinthu zauzimu ndipo anadalitsidwa kwambiri ndi Yehova. (Genesis 27:28, 29; Ahebri 12:16, 17) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kulitsani moyo wanu wauzimu, ‘walitsani kuunika kwanu,’ ndipo ‘[“kupita kwanu patsogolo,” NW] kudzaonekera kwa onse.’—Mateyu 5:16; 1 Timoteo 4:15.

Clare, amene tam’tchula koyambirira uja anati: “Ndinkasangalala anthu akamandifanizira zochita zanga ndi za azikulu anga. Koma kenaka ndinaganiza zotsatira langizo la m’Malemba lakuti ‘ndikule,’ pa zochita zanga. Ndinayamba kupita mu utumiki wakumunda ndi anthu osiyanasiyana mu mpingo, ndipo ndinafunafuna njira zabwino zothandizira anthu ofunika thandizo mu mpingo. Ndinayambanso kuitana abale ndi alongo a misinkhu yosiyanasiyana ku nyumba kwathu ndipo ndinkawaphikira chakudya. Tsopano ndili ndi mabwenzi ambiri, ndipo ndimadziona kuti ndine wofunika.”—2 Akorinto 6:13, NW.

Nthaŵi zina, makolo anu angaphonyetse n’kumakulimbikitsani kuti muzitengera mchimwene kapena mchemwali wanu. Koma kuzindikira kuti makolo anu amakufunirani zabwino kungakuthandizeni kuti musakhumudwe. (Miyambo 19:11) Komabe, zingakhale bwino kuwauza makolo anuwo mwaulemu mmene mumamvera akamakuyerekezerani ndi wina. Mwina angapeze njira zina zofotokozera maganizo awo.

Musaiwale kuti Yehova Mulungu adzakuonani pamene mukum’tumikira. (1 Akorinto 8:3) Barry anamaliza ndi mawu akuti: “Pamene ndikutumikira Yehova kwa nthaŵi yaitali, m’pamenenso ndimakhala wosangalala kwambiri. Anthu tsopano amandiona mmene ndilili ndipo amandikonda monga mmene amachitira ndi abale anga.”

[Mawu a M’munsi]

a Mayina ena tasintha.

b Imakonzedwa ndi Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 12]

Kodi maso a anthu amangokhala pa mbale wanu nthaŵi zambiri?

[Chithunzi patsamba 13]

Phunzirani luso lanulanu

[Chithunzi patsamba 13]

‘Walitsani kuunika kwanu’ mwa kukulitsa luso lanu lauzimu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena