Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g05 1/8 tsamba 19
  • Kunyanyira Kufuna Kukongola

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kunyanyira Kufuna Kukongola
  • Galamukani!—2005
  • Nkhani Yofanana
  • Ndinapeza Cholinga cha Moyo
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • “Ndinkamenya Nkhondo Ngati Mkango”
    Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Kuipa Kofunitsitsa Kukhala Wokongola
    Galamukani!—2005
  • Tikapirira Mavuto Tidzadalitsidwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—2005
g05 1/8 tsamba 19

Kunyanyira Kufuna Kukongola

MARIAa ndi mtsikana amene zinthu zikumuyendera bwino pamoyo wake ndipo amachokera ku banja labwino kwambiri. Komabe, iye si wosangalala. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti sasangalala ndi maonekedwe ake. Ngakhale kuti anthu a m’banja lake amayesetsa kumulimbikitsa, Maria amadziona kuti si wokongola, ndipo zimenezi zimamuvutitsa maganizo.

José amachokera ku banja lolemekezeka ndipo anayenera kukhala wosangalala. Koma iye amaganiza kuti sadzapeza munthu wokwatirana naye. Chifukwa chiyani? José amaganiza kuti si wooneka bwino, ndiponso kuti ndi wonyansa kumene. Amakhulupirira kuti palibe mkazi wabwinobwino amene angakopeke naye.

Luis, amene ali ndi zaka eyiti, amakonda kupita ku sukulu ndiponso ndi wochezeka. Amakonda kusewera ndi anzake a kusukulu, koma nthawi zambiri amalira chifukwa anzakewo amamuseka chifukwa cha maonekedwe ake. Amamunena kuti ndi wonenepa kwambiri.

Zimenezi sikuti zikungochitikira anthu okhawa ayi. Sitinganene kuti vuto la Maria, José, ndi Luis n’kudzikayikira basi. Zoona zake n’zakuti palibe amene amafuna kuti anthu ena azimusala chifukwa cha maonekedwe ake.

Komabe, anthu masiku ano amakokomeza kwambiri kufunika kwa maonekedwe abwino. Ndipo kuti zinthu zikuyendereni bwino, nthawi zambiri zimadalira maonekedwe anu. Mwachitsanzo, anthu okongola nthawi zambiri savutika kupeza ntchito. Pilar Muriedas, mmodzi wa atsogoleri a bungwe lotchedwa Latin-American and Caribbean Women’s Health Network, anati “kukhala ndi maonekedwe abwino ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri [kwa akazi] kuti zinthu ziwayendere bwino.” Ndipo malinga ndi Dr. Laura Martínez, akazi amadziwa bwino kuti kuposa china chilichonse, “maonekedwe ndi amene amachititsa kwambiri kuti munthu alembedwe ntchito kapena asalembedwe.”

Ndipo amuna ambiri nawonso ayamba kuda nkhawa kwambiri pofuna kukhala ndi thupi labwino kwambiri. Zoonadi, amuna ndi akazi ambiri amachita zinthu zosiyanasiyana pofuna kukhala okongola. Ena amalolera kupirira ndi njala kapena kuchitidwa maopaleshoni opweteka pofuna kukhala ndi nkhope kapena thupi labwino kwambiri. Kodi kufunafuna kukongola koteroko n’kwaphindudi? Kodi kuli ndi kuipa kwake?

[Mawu a M’munsi]

a Mayina asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 19]

Maonekedwe angachititse kuti munthu alembedwe ntchito inayake kapena asalembedwe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena