Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 11/08 tsamba 10
  • Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita
  • Galamukani!—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Luso la Agulugufe a Monarch Loyenda Ulendo Wautali
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Wamkulu Kwambiri Ndiponso Wamng’ono Kwambiri
    Galamukani!—1999
  • Luso la Gulugufe Woyera Lotha Kuimitsa Mapiko Ake Ngati V
    Kodi Zinangochitika Zokha?
  • Mapiko a Gulugufe
    Galamukani!—2012
Onani Zambiri
Galamukani!—2008
g 11/08 tsamba 10

Panagona Luso

Mmene Gulugufe Amadziwira Komwe Akupita

◼ Mtundu winawake wa agulugufe umauluka makilomita 3,000 kuchoka ku Canada kupita ku nkhalango ina yaing’ono ya ku Mexico. Komatu agulugufe amenewa ali ndi ubongo waung’ono ngati kanjere kampiru. Kodi amadziwa bwanji komwe akupita?

Taganizirani Izi: Agulugufe amenewa amadziwa komwe akupita poona pomwe pali dzuwa. Koma palinso zina zimene zimawathandiza. Agulugufe amenewa mwachibadwa amadziwa nthawi ndi zomwe angachite malinga ndi kayendedwe ka dzuwa. Dokotala wa mitsempha, Steven Reppert, ananena kuti mtundu umenewu wa agulugufe “uli ndi luso lapadera kwambiri lochita zinthu potsatira nthawi kuposa tizilombo ndiponso nyama zina zomwe zafufuzidwapo.”

Kuphunzira zambiri za mmene agulugufe amenewa amadziwira nthawi kungathandize asayansi kudziwa zochuluka za mmene anthu ndi nyama amadziwira nthawi mwachibadwa. Zingathandizenso kupeza mankhwala atsopano a matenda a mitsempha. Reppert anapitiriza kuti: “Ndikufuna kudziwa mmene ubongo umadziwira nthawi ndi koyenera kupita ndipo agulugufe amenewa ndi chitsanzo chabwino kwambiri pankhani imeneyi.”

Kodi Mukuganiza bwanji? Kodi luso limene agulugufe amenewa ali nalo lotha kudziwa kumene akupita anangokhala nalo mwangozi kapena ndi umboni wakuti analengedwa ndi Mlengi waluso?

[Chithunzi/Mapu patsamba 10]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Agulugufe awa amauluka makilomita 3,000 kuchoka ku Canada kupita ku nkhalango yaing’ono ya ku Mexico

[Mapu]

CANADA

UNITED STATES OF AMERICA

MEXICO

MEXICO CITY

[Mawu a Chithunzi patsamba 10]

Background: © Fritz Poelking/age fotostock

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena