Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 12/08 tsamba 28
  • Kuchokera kwa Owerenga

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchokera kwa Owerenga
  • Galamukani!—2008
  • Nkhani Yofanana
  • Mmene Mungathandizire Ana Anu pa Nkhani ya Mowa
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Mmene Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso Kumakhudzira Thanzi la Munthu
    Galamukani!—2005
  • Kupulumuka ku Msampha wa Kumwa Mowa Mopitirira Muyeso
    Galamukani!—2005
  • Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Kumwa Mowa
    Nsanja ya Olonda—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—2008
g 12/08 tsamba 28

Kuchokera kwa Owerenga

Sindinenso Kapolo wa Mowa (May 2007) Mboni zikandibweretsera magazini, nthawi zina ndimawawerenga. Ndimaona kuti nkhani zake zimakhala zabwino poyerekezera ndi nkhani zoipa zimene timaona pa TV ndiponso zimene timawerenga m’nyuzipepala. Ine sindinakhalepo ndi vuto lomwa mowa mwauchidakwa, koma ndili ndi achibale ndi anzanga amene ali ndi vuto limeneli. Munthu amene anafotokozedwa m’nkhaniyi ananena kuti anathetsa vuto lomwa mowa mwauchidakwa m’miyezi itatu yokha. Zimenezi zinachitika munthuyu atakhala ndi vutoli kwa zaka zambiri. Ngakhale ndikumuthokoza pa zimene anachitazi, ndikukayikira ngati zimenezi ndi zenizeni komanso ndikuganiza kuti sangalimbikitse ena amene akulimbana ndi vuto limeneli. Munthu yemwe alidi ndi vutoli nthawi zambiri samalithetsa kamodzinkamodzi.

G. A., United States

Yankho la “Galamukani!”: Sitinatanthauze kuti n’kosavuta kuthetsa vuto la kumwa mowa mwauchidakwa. Tikudziwa kuti anthu amene akufuna kuthetsa vutoli samalithetsa kamodzinkamodzi ndipo pamakhala zinthu zina zowalepheretsa. Ngakhale anthu amene angathetse vutoli kamodzinkamodzi, amafunika kusamala kuti asayambirenso. N’chifukwa chake nkhaniyi inanena kuti, “kapolo wa mowa” atatha zaka 10 osamwa anati: “Ambiri sadziwa nkhondo yaikulu imene ndili nayo kuti ndikangomwa botolo limodzi lokha, nditha kuyambiranso moyo wanga wakale. Chilakolako cha mowa ndikadali nachobe. Kuti ndikane mowa, ndimafunika kupemphera kwambiri ndiponso kulimba mtima.” Anthu ambiri athetsa vutoli mwa kudalira Mulungu.—Salmo 55:22.

Kodi Tiyenera Kukhulupirira Baibulo? (November 2007) Ndili ndi zaka 12, ndipo ndikufuna ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha nkhani yosangalatsa komanso mfundo zabwino za m’magazini yapadera ya Galamukani! Ndinasangalala kwambiri ndi mfundo za patsamba 7 zosonyeza kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo. Mfundo zina zimene zinafotokozedwa m’nkhaniyi zinali zachilendo kwambiri kwa ine. Ndipo ndikuyembekezera mwachidwi magazini ina yapadera.

D. F., United States

Zoti Muganizire Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha kalembedwe katsopano ka Galamukani! Mafunso amene akumakhala ku mapeto kwa nkhani zina andithandiza kwambiri. Andithandiza kuti ndizitha kukumbukira ndi kusinkhasinkha zimene ndawerenga. Masiku ano, timakhala ndi zochita zambiri moti powerenga tingaphonye mfundo zofunika ndi zolimbikitsa.

M.A.S., Brazil

Kodi Imfa ndi Mapeto a Zonse? (December 2007) Miyezi 6 yapitayi mayi anga anamwalira pangozi. Nkhaniyi inandilimbikitsa kwambiri chifukwa inawonjezera chikhulupiriro changa kuti ndidzawaonanso akadzaukitsidwa. Ndikukuthokozani kwambiri.

L.L.R., Brazil

Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . Ndizitsatira Mfundo za M’Baibulo Chifukwa Chiyani? (November 2007) Ndinkaganiza kuti sikulakwa kukhala ndi chibwenzi malinga ngati sitikugonana. Koma sindimakhutira kumangocheza ndi bwenzi langalo. Ndinayamba kukhala ndi zilakolako zoipa. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cholemba nkhani za m’Baibulo zimenezi mwa njira imene achinyamata amene sadziwa zinthu zambiri angamve mosavuta.

E.F., Japan

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena