Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/09 tsamba 32
  • Ana Amalikonda Bukuli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana Amalikonda Bukuli
  • Galamukani!—2009
Galamukani!—2009
g 4/09 tsamba 32

Ana Amalikonda Bukuli

◼ Ana a zaka zosiyanasiyana amakonda kwambiri buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mtsikana wina analemba kuti: “Bukuli lili ndi zinthu zambiri zimene ndimazikonda. Mwachitsanzo, lili ndi zithunzi zokongola kwambiri. Powerenga bukuli, ndinkatenga nthawi yaitali kuganizira mafanizo ake ndi mmene akugwirizanira ndi nkhaniyo.

“Chinthu chinanso chomwe ndimakondera bukuli n’chakuti mawu ake ndi osavuta kumva, ndipo zimenezi zimachititsa kuti munthu uzingofunabe kuliwerenga.

“Nditawerenga bukuli ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene limafotokozera mavuto amene timakumana nawo masiku ano ndi mmene tingawapewere. Mitu yomwe ndinasangalala nayo kwambiri ndi yakuti, ‘Tifunika Kukana Ziyeso,’ ‘Phunziro la Kukhala Wokoma Mtima,’ ndiponso ‘Kodi Nthawi Zonse Umafuna Kukhala Woyamba?’”

Mukhoza kuitanitsa buku la zithunzi zokongola la masamba 256 limeneli. Masamba a bukuli ndi aakulu mofanana ndi a magazini ino. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena