Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 5/10 tsamba 32
  • Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?
  • Galamukani!—2010
Galamukani!—2010
g 5/10 tsamba 32

Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?

Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobe 4:8) Kodi mumaona kuti n’zotheka kuti anthu akhale paubwenzi ndi Mlengi? Komabe musanayankhe funso limeneli, mwina mungafune kudziwa mayankho a mafunso enanso ofunikira kwambiri monga awa:

Kodi Mulungu alipo?

Ngati alipo, kodi iye amalankhula ndi anthu? Ngati amatero, kodi amalankhula nawo bwanji?

Kodi Mulungu amagwiritsa ntchito Baibulo polankhula nafe? Ngati amatero, kodi pali umboni?

Mwina amenewa ndi mafunso ena ofunikira kwambiri amene anthufe timakhala nawo. Mafunso amenewa ndi enanso ambiri adzayankhidwa mu nkhani yakuti, “Kodi Mungatani Kuti Muyandikire Mulungu?” Nkhaniyi idzakambidwa pa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova yomwe idzachitike kuyambira mwezi wa May ku United States ndipo kenako idzachitika m’madera osiyanasiyana padziko lonse.

Tikukupemphani kuti mudzafike kumsonkhano womwe udzachitikire kufupi ndi kwanu. Ngati mukufuna kudziwa zambiri, funsani Mboni za Yehova za kwanuko kapena lemberani kalata ofalitsa a magazini ino. Mukhoza kupeza malo amene kudzachitikire msonkhanowu mu magazini ya Nsanja ya Olonda ya March 1, 2010 kapena pa adiresi ya pa Intaneti iyi: www.pr418.com.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena