Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 4/11 tsamba 32
  • Yesu “Akuchotsa Uchimo wa Dziko”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu “Akuchotsa Uchimo wa Dziko”
  • Galamukani!—2011
Galamukani!—2011
g 4/11 tsamba 32

Yesu “Akuchotsa Uchimo wa Dziko”

● Yohane M’batizi ananena kuti Yesu “akuchotsa uchimo wa dziko.” (Yohane 1:29) Mawu amenewa anachititsa anthu kufuna kudziwa udindo umene Yesu anali nawo populumutsa anthu ofunitsitsa kumvera malamulo ake.

Komano n’chifukwa chiyani Yesu anafunikira kufa kuti apulumutse anthu ochimwa? Kodi iye anakwaniritsa chiyani chifukwa cha imfa yakeyi? Kodi ndani amene akupindula ndi imfa ya Yesu? Kodi imfa yake ingakuthandizeni bwanji?

Chaka ndi chaka, a Mboni za Yehova amasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Chaka chino mwambo umenewu udzachitika Lamlungu, April 17, dzuwa litalowa.

A Mboni za Yehova akukuitanani kuti mudzakhale nawo pa mwambowu n’cholinga choti mudzadziwe bwino za kufunika kwa imfa ya Yesu. Pa mwambowu padzakambidwa nkhani imene idzapereke mayankho a m’Baibulo a mafunso amene ali pamwambawa.

Dzapiteni kumalo amene kudzachitikire mwambowu akufupi ndi kumene mumakhala. Tikukulimbikitsani kuti mufunse a Mboni za Yehova a m’dera lanu kuti akuuzeni nthawi ndi malo amene kudzachitikire mwambowu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena