Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 6/12 tsamba 32
  • Linandithandiza Kuthana ndi Khalidwe Loipa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Linandithandiza Kuthana ndi Khalidwe Loipa
  • Galamukani!—2012
Galamukani!—2012
g 6/12 tsamba 32

Linandithandiza Kuthana ndi Khalidwe Loipa

● Chaka chathachi kunatuluka buku lachingelezi lonena za achinyamata. (Questions Young People Ask—Answers That Work, Volume I) Patsamba 180 la bukuli anafotokozapo bwino kwambiri lemba la Miyambo 24:16 lomwe limati wolungama angagwe nthawi 7 koma n’kudzuka. Bukuli linathandiza kwambiri mtsikana wina yemwe ananena kuti: “Chithunzi chomwe chili patsamba limeneli chinandithandiza kudziwa kuti Mulungu amasangalala akaona kuti ndikuyesetsa kulimbana ndi khalidwe loipa. . . . Linandithandizanso kudziwa kuti ndikamapemphera kwa Mulungu ndizitchula zinthuzo mwachindunji komanso ndizimupempha kuti andithandize kulimbana ndi maganizo odziona kuti ndine wosafunika. Zimenezi zindithandizanso kuti ndizipemphera kwa Mulungu ndikamayesedwa kuti ndichite khalidwe loipa.

“Panopa ndili ndi chikhulupiriro chakuti ndidzasiya khalidwe langa loipali ngakhale kuti ndakhala ndikulichita kwa nthawi yaitali. Komanso ndinasiya kudziona kuti ndine munthu wochimwa kwambiri padziko lonse.”

Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba adiresi yanu m’mizere ili m’munsiyi, n’kutumiza ku adiresi yoyenera yomwe ili patsamba 5 m’magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire bukuli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena