Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/12 tsamba 10-12
  • Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?—Gawo 1

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?—Gawo 1
  • Galamukani!—2012
  • Nkhani Yofanana
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
  • Kodi Mungatani Kuti Banja Lanu Liziyenda Bwino?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Kodi Chofunika Ndi Chiyani Kuti Ukwati Ukhale Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Ukwati Ndi Mphatso Yochokera Kwa Mulungu Wachikondi
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
Onani Zambiri
Galamukani!—2012
g 9/12 tsamba 10-12

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndiziyembekezera Chiyani M’banja?​—Gawo 1

“Ndikamacheza naye, kumtimaku kumangoti myaa. Ndikungoona ngati tsiku la ukwati wathu likuchedwa.”

“Palibiretu chimene timagwirizana. Palibenso za banja moti timangokhala ngati anthu ongokhala nyumba imodzi basi.”

MWINA mutawerenga ziganizo zili pamwambapa, mungaganize kuti zinanenedwa ndi anthu awiri osiyana. Koma choti mudziwe n’chakuti mawu onse amene ali muziganizo ziwirizi ananenedwa ndi munthu mmodzi. Mawu a muchiganizo choyamba anawanena ali pachibwenzi ndipo mawu amuchiganizo chachiwiri anawanena atalowa m’banja.

Koma kodi chinalakwika ndi chiyani? Ngati mukukonzekera kuti tsiku lina mudzalowa m’banja, kodi mungatani kuti mudzakhale osangalala m’banja ngati mmene munkafunira muli pa chibwenzi?

Dziwani izi: Kuti munthu akhale wosangalala m’banja zimangodalira zimene amayembekezera m’banjamo.

Nkhani ino komanso nkhani ya “Zimene Achinyamata Amadzifunsa,” yomwe idzatuluke mu Galamukani! ya mwezi wamawa, idzakuthandizani kuti musamayembekezere zinthu zomwe sizingachitike m’banja.

Kodi ndi zinthu ziti zimene munthu angayembekezere kuti zizidzachitika akadzalowa m’banja? Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:

  1. Zinthu zabwino

  2. Mavuto

  3. Zinthu zosayembekezereka

Tiyeni tikambirane zinthu zimenezi chimodzi ndi chimodzi.

ZINTHU ZABWINO

Baibulo limasonyeza kuti banja ndi chinthu chabwino. (Miyambo 18:22) Taonani zina mwa zinthu zabwino zimene mungayembekezere m’banja.

Mumapeza mnzanu weniweni. Baibulo limanena kuti patapita kanthawi Adamu atalengedwa, Mulungu ananena kuti: “Si bwino kuti munthu akhale yekha.” Kenako analenga Hava kuti akhale mnzake womuyenerera. (Genesis 2:18) Mulungu analenga Adamu ndi Hava monga anthu awiri osiyana koma anali oyenererana. N’chifukwa chake mwamuna ndi mkazi okwatirana amakhala ogwirizana kwambiri.—Miyambo 5:18.

Mumapeza wothandizana naye. Baibulo limanena kuti: “Awiri amaposa mmodzi, . . . ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kum’dzutsa mnzakeyo.” (Mlaliki 4:9, 10) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwambiri m’banja. Mwachitsanzo, mtsikana wina yemwe wangokwatiwa kumene, dzina lake Brenda,a anati: “Ndikuona kuti banja limayenda bwino ngati mumachitira zinthu limodzi. Nthawi zina umafunika kudzichepetsa komanso kungololera zinthu zina.”

Kugonana. Baibulo limati: “Mwamuna azipereka kwa mkazi wake mangawa ake, mkazinso achite chimodzimodzi kwa mwamuna wake.” (1 Akorinto 7:3) Anthu amene ali m’banja amakhala omasuka kugonana popanda kudziimba mlandu kapena kudera nkhawa za mavuto amene anthu omwe amagonana asanalowe m’banja amakumana nawo.—Miyambo 7:22, 23; 1 Akorinto 7:8, 9.

Mfundo yoti muziikumbukira: Ukwati ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. (Yakobo 1:17) Mukamadzatsatira malangizo ake, ndiye kuti muzidzakhala osangalala m’banja mwanu.

Zoti muganizire: Kodi inuyo mumaona kuti banja silabwino chifukwa cha zimene mwaonapo zikuchitika m’mabanja ena, kapenanso m’banja lanu? Ngati ndi choncho, kodi ndi zitsanzo zabwino ziti zimene mungatengere?

MAVUTO

Baibulo silibisa kuti nthawi zina m’banja mumakhala mavuto. (1 Akorinto 7:28) Mavuto ena amene mungayembekezere ndi awa:

Kusemphana maganizo. N’zosatheka kuti mwamuna ndi mkazi azigwirizana pa chilichonse chifukwa tonse ndife opanda ungwiro. (Aroma 3:23) N’chifukwa chake nthawi zina mwamuna ndi mkazi wake akhoza kusiyana maganizo ngakhale kuti amakondana kwambiri. Nthawi zinanso angathe kulankhulirana mawu opweteka ndipo pambuyo pake akhoza kudandaula nazo. Baibulo limanena kuti: “Munthu amene sananenerepo mnzake mawu oipa . . . ndiye kuti ndi munthu wangwiro.” (Yakobo 3:2, Holy Bible—Easy-to-Read Version) N’zoona kuti anthu amene ali pabanja ayenera kuyesetsa kupewa mikangano, koma kuti banja lawo likhale losangalala, ayenera kumakambirana akasemphana maganizo.

Zimene mumayembekezera sizikuchitika. Mtsikana wina, dzina lake Karen, ananena kuti: “Timapusitsika ndi mafilimu komanso mapulogalamu a pa TV omwe amasonyeza mkazi atapeza mwamuna wopanda vuto lililonse, akukhala mosangalala kwa moyo wawo wonse.” Anthu amene ali m’banja akaona kuti zimene amaonera m’mafilimu sizikuchitika, amakhala okhumudwa. N’zoona kuti anthu akakwatirana amadzazindikira kuti mwamuna kapena mkaziyo ali ndi mavuto ena omwe samawadziwa poyamba. Ngati zimenezi zitachitika, mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti chikondi chenicheni “chimapirira zinthu zonse.” Zimenezi zikuphatikizapo kukhumudwa chifukwa chakuti zimene mumayembekezera sizikuchitika.—1 Akorinto 13:4, 7.

Nkhawa. Baibulo limanenanso kuti anthu amene ali pa banja “amadera nkhawa zinthu za dziko.” (1 Akorinto 7:33, 34) Nthawi zina nkhawa imeneyi ndi yabwino. Mwachitsanzo, m’banja mungakhale vuto la ndalama. Mwina mwamuna ndi mkazi angafunike kumagwira ntchito kuti apeze chakudya, zovala ndi malo okhala. Komabe akamachita zinthu mogwirizana posamalira banja lawo, angamakhale osangalala.—1 Timoteyo 5:8.

Mfundo yoti muziikumbukira: Munthu akakhala pa chibwenzi amakhala ngati akuyendetsa galimoto ya mawaya. Koma akalowa m’banja amakhala ngati akuyendetsa galimoto yeniyeni. Choncho, kuti banja lanu lidzakhale losangalala mudzafunika kuchita zinthu mwaluso komanso mwakhama polimbana ndi mavuto amene mungakumane nawo.

Zoti muganizire: Kodi panopo mumatani mukakhala kuti simukugwirizana ndi makolo kapena abale anu? Kodi mumatha kuganiza bwinobwino mukakhumudwa? Kodi mumatani mukakhala ndi nkhawa?

NKHANI YOTSATIRA YA “ZIMENE ACHINYAMATA AMADZIFUNSA” IDZAFOTOKOZA . . . Mfundo za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuthana ndi zinthu zimene simumaziyembekezera.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.

a Tasintha mayina ena m’nkhani ino.

ZIMENE ACHINYAMATA ANZANU AMANENA

Brittany—Ndimaona kuti si nzeru kukwatiwa chifukwa chongoti ena akumakonda kukufunsa kuti, “Kodi mukwatiwa liti?” Ndimadziwa kuti ngati nditakwatiwa n’kumakumana ndi mavuto, ndi ineyo amene ndizidzalimbana ndi mavutowo osati iwowo.

Ciara​—Nthawi zina munthu akagwa m’chikondi saganiza bwino. N’chifukwa chake ndimaona kuti ndi bwino kuti makolo azithandizabe ana awo kusankha munthu womanga naye banja. Chifukwa choti makolowo amamudziwa bwino mwana wawoyo, akhoza kumuthandiza kusankha bwino munthu wodzakwatirana naye.

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

Josh ndi Melanie atha chaka ali pa chibwenzi. Nthawi ina chibwenzi chawo chinatsala pang’ono kutha kawiri konse. Nthawi yoyamba, Josh ankafuna kuthetsa chibwenzicho chifukwa ankaganiza kuti Melanie ankakopana ndi anyamata ena. Kachiwiri, Melanie ankafuna kuthetsa chibwenzicho chifukwa chakuti Josh ankangomunena kuti amakopana ndi anyamata ena. Koma maulendo onsewa, Josh ndi Melanie anakambirana n’kuthetsa nkhaniyo.

Kodi inuyo mukuganiza bwanji pankhani imeneyi? Kodi mukuona kuti pangadzakhale vuto lanji ngati anthuwa atadzakwatirana? Kodi mfundo yakuti chibwenzi cha Josh ndi Melanie chinafuna kutha kawiri konse ikusonyeza chiyani? Nanga zimene anachita pothana ndi vutolo zikusonyezani chiyani? Kodi mukuganiza kuti Josh ndi Melanie atakwatirana, banja lawo lidzakhala lotani?

FUNSANI MAKOLO ANU

Kambiranani ndi makolo anu bokosi lakuti, “Kodi Inuyo Mukuganiza Bwanji?” Onani ngati zimene makolo anu akuganiza pa nkhani ya Josh ndi Melanie, zikusiyana ndi zimene inuyo mukuganiza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena