N’zotheka Kulera Nokha Ana
“Nthawi zambiri ndimasangalala ndikaona ana anga awiri akundithamangira, kundikumbatira kenako n’kundiuza kuti, ‘Timakukondani kwambiri amayi.’”—ANATERO ANNA, MAYI WA KU POLAND YEMWE AKULERA YEKHA ANA.
“Nthawi zambiri ndimasangalala ana anga akachita zinthu zosonyeza kuti amandiyamikira. Nthawi zina amatha kundipatsa mphatso monga zithunzi zimene ajambula. Zimenezi zimandilimbikitsa kwambiri.”—ANATERO MASSIMO, BAMBO WA KU ITALY YEMWE AKULERA YEKHA ANA.
“Nthawi zina ndikakhala kuti ndili ndi nkhawa kwambiri, mwana wanga mmodzi wamwamuna amabwera n’kundikumbatira n’kundiuza kuti amandikonda kwambiri.”—ANATERO YASMIN, MAYI WA KU SOUTH AFRICA YEMWE AKULERA YEKHA ANA.
MAWU amene ali m’mabokosiwa ndi ena mwa mawu amene makolo ena omwe akulera okha ana anauza mtolankhani wa Galamukani! pa kafukufuku amene anachitika pa dziko lonse. Ambiri mwa makolo amenewa anali azimayi ndipo ananena kuti zikanakhala bwino akanakhala ndi amuna awo kuti aziwathandiza.a Komabe zimene azimayiwo ananena zikusonyeza kuti akukwanitsa kulera bwino ana awo.
Kodi n’chiyani chathandiza makolo amenewa kukwanitsa udindo wovuta umenewu? Mu nkhani zotsatirazi tikambirana zina mwa zimene makolowa ananena moona mtima komanso zimene zawathandiza kulera ana awo. Ngati mukulera nokha ana, nkhani zimenezi zikuthandizani kuti mukwanitse udindo wovuta umenewu. Kunena zoona masiku ano kulera ana n’kovuta kwambiri chifukwa zinthu padzikoli sizikuchedwa kusintha.b
Mu nkhanizi tikambirana mfundo 6 za zimene makolo olera okha ana angachite kuti:
Apeze anthu oti aziwathandiza
Azilankhulana momasuka ndi ana awo
Azichita zinthu zofunika choyamba
Azikhazikitsa malamulo amene ana awo ayenera kutsatira
Azithandiza ana awo kutsatira mfundo za m’Baibulo
Azidalira Mulungu
a Nkhani 7 zoyambirira za m’magazini ino zikusonyeza kuti padziko lonse, makolo ambiri amene akulera okha ana ndi azimayi.
b Malangizo ambiri omwe ali m’nkhani zino angathandizenso mabanja omwe ali ndi makolo onse awiri.