2 Muzilankhulana Momasuka ndi Ana Anu
“Ndaona kuti ndi bwino kumamvetsera ana anga akamalankhula ngakhale nditatopa kwambiri.”—ANATERO MIRANDA WA KU SOUTH AFRICA.
Vuto.
Mayi wina dzina lake Cristina ananena kuti: “Vuto limene ndili nalo ndi loti mwana wanga akamalankhula, maganizo anga amakhala ali kwina chifukwa ndimakhala ndi zambiri zochita komanso ndimakhala nditatopa.”
Zimene mungachite.
Muzichita zinthu zoti ana anu azimasuka kulankhula nanu. Mayi wina yemwe ali ndi ana asanu, dzina lake Elizabeth, ananena kuti: “Ndimayesetsa kulankhula momasuka ndi ana anga zomwe zimachititsa kuti iwonso azimasuka nane. Ndimawaphunzitsanso kuti azilankhulana bwino komanso ngati alakwirana asamakagone ali chikwiyire. Komanso amadziwa kuti sindimalola zoti akalakwirana azisiya kulankhulana.”
Muzimvetsera mwachidwi akamalankhula. Mayi wina, dzina lake Lyanne, ananena kuti: “Mwana wanga ali wamng’ono ankakonda kulankhula kwambiri moti nthawi zambiri sindinkamvetsera akamalankhula. Zimenezi zinachititsa kuti atakula asamakonde kulankhula nane. Ndinazindikira kuti ndinkalakwitsa kwambiri. Nthawi zambiri ndinkachita kumukakamiza kuti azimasuka nane moti nthawi ina ndinachita kupempha mkulu wina wa mu mpingo mwathu kuti andithandize. Iye anandiuza kuti ndisamachite kumukakamiza chifukwa nthawi zambiri zimatenga nthawi kuti mwana ayambenso kulankhula momasuka. Ndinatsatira zimene anandiuzazo ndipo zinthu zinayambadi kusintha.”
Muzikhala oleza mtima. Lemba la Mlaliki 3:7 limanena kuti pali “nthawi yokhala chete ndi nthawi yolankhula.” Mayi wina yemwe ali ndi ana atatu, dzina lake Dulce, ananena kuti: “Ndikaona kuti ana anga akuoneka kuti sakufuna kulankhula nane sindinkawakakamiza, m’malo mwake ndinkawauza kuti akhale omasuka kulankhula nane nthawi iliyonse imene angafune.” Choncho, m’malo mokakamiza ana anu kuti akulankhuleni, ndi bwino kuwauza kuti ndinu okonzeka kucheza nawo nthawi iliyonse imene iwo angafune. Zimenezi n’zimene Baibulo limalimbikitsa chifukwa limati: “Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.”—Miyambo 20:5.
“Munthu aliyense akhale wofulumira kumva, wodekha polankhula.” (Yakobo 1:19) Lizaan, yemwe watchulidwa mu nkhani yapitayi, ananena kuti: “Ndaona kuti ndi bwino kumvetsera kaye ana anga akamandiuza za vuto linalake. Komanso ndaphunzira kuti mwana wanga akamandiuza nkhani imene yamukhumudwitsa, ndisamafulumire kumupatsa malangizo koma ndizilankhula naye modekha.” Mayi wina yemwe ali ndi ana aamuna awiri, dzina lake Leasa, ananena kuti: “Ndili ndi vuto loti munthu akamalankhula sindimvetsera. Nthawi zina, zimene ana anga ankandiuza zinkaoneka zachibwana komabe ndinkayesetsa kumvetsera akamalankhula.”
“Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo.” (Akolose 4:6) Lyanne ananenanso kuti: “Kuti ana anga azimasuka nane, ndimayesetsa kukhalabe wodekha ngakhale patachitika vuto linalake lalikulu.”
Ngati mutalephera kuugwira mtima, mukhoza kukwiya n’kuyamba kulankhula mwaukali ndipo zimenezi zingachititse kuti vutolo likule kwambiri. (Aefeso 4:31) Mwachitsanzo, ngati mungamamulankhule mwana wanu mwaukali, zingachititse kuti asamakuuzeni zakukhosi kwake komanso zingabweretse mavuto ena.
Muziwadziwa bwino ana anu. Mayi wina, dzina lake Yasmin, ananena kuti: “Ndili ndi ana awiri aamuna koma ndi osiyana kwambiri. Wina amakonda kulankhula kwambiri pomwe winayo ndi wofatsa. Ndikafuna kulankhula ndi wofatsayo ndimaona kuti ndibwino kulankhula naye tili awiriwiri, mwina tikamachita masewera enaake kapena tikamacheza. Nthawi imeneyi ndi imene ndimaona kuti ndingamufunse zimene akuganiza pa nkhani inayake.”
Nanga bwanji ngati mwana wamwamuna akuona kuti sangakambirane ndi amayi ake nkhani zinazake? Zimenezi ndi zimene zinachitikira mayi wina, dzina lake Misao, yemwe ali ndi mwana wamwamuna. Mwanayo ankaona kuti mayi ake sankamumvetsa. Choncho Misao anapempha m’bale wina wachikulire wa mumpingo mwawo kuti amuthandize. Misao ananena kuti: “Panopa m’baleyu amathandiza mwana wanga pa zinthu zosiyanasiyana ndipo zamuthandiza kuti azikhala wodekha.”
Muzichita naye zinthu modzilemekeza. Mayi wina yemwe ali ndi ana awiri achinyamata, dzina lake Iwona, ananena kuti: “Poyamba ndinkakonda kuuza mwana wanga chilichonse ngakhale kuti ndinkadziwa kuti zimenezi n’zolakwika. Koma kenako ndinaona kuti ndinafunika kusintha.” Ngakhale kuti mungafune kumacheza momasuka ndi mwana wanu, muzikumbukira kuti ndinu kholo lake. Mukamachita zinthu mwanzeru komanso monga munthu wachikulire zingathandize kuti mwanayo azikulemekezani komanso azitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Ananu, muzimvera makolo anu.”—Aefeso 6:1, 2.
‘Muzikonda ana anu.’ (Tito 2:4) Ana amafuna kukondedwa ngati mmene amafunira zakudya. Choncho nthawi zonse muziwauza komanso kuchita zinthu zosonyeza kuti mumawakonda. Zimenezi zidzathandiza kuti azikudalirani, azimasuka nanu komanso kuti azikumverani.