Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 7/14 tsamba 3
  • Zochitika Padzikoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika Padzikoli
  • Galamukani!—2014
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • United States
  • Spain
  • Pacific Ocean
  • United Arab Emirates
  • Kodi Kuchita Khama Kuti Muchepetse Kunenepa N’kwaphindudi?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Kumwa Moŵa Wambiri Nthaŵi Imodzi Kuli ndi Vuto Lanji?
    Galamukani!—2004
  • Kodi Kumwa Mowa Wambiri Kuli Ndi Vuto Lanji?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
  • Pamene Chachikulu Sichikhalanso Bwino
    Galamukani!—1997
Onani Zambiri
Galamukani!—2014
g 7/14 tsamba 3

ZOCHITIKA PADZIKOLI

United States

Firiji yomwe muli zakudya zochepa kwambiri

Lipoti lina la bungwe loona za chakudya linasonyeza kuti mu 2012, anthu 49 miliyoni a ku United States pa nthawi ina “sankadziwa ngati angakwanitse kupeza chakudya chokwanira banja lonse, mwinanso sankachipeza n’komwe.”

Spain

Mwamuna akupapira mowa

Kafukufuku amene ophunzira a pa yunivesite ina anachita anasonyeza kuti akazi 56 pa 100 alionse komanso amuna 41 pa 100 alionse, anavomera kuti anapapirapo mowa mpaka kuledzera. Izi zikusonyeza kuti amuna anamwa mabotolo a mowa oposa 8 a mamililita 250 nthawi imodzi, ndipo akazi anamwa mabotolo a mowa oposa 6 a mamililita 250 nthawi imodzi.

Pacific Ocean

Nyanja ya Pacific

Akatswiri ena asayansi anatenga zinthu zina pamalo otchedwa Mariana Trench. Malowa ndi akuya mamita 11,000 ndipo ali m’nyanja ya Pacific. Atayeza zinthuzi, anapeza kuti munali mabakiteriya ndiponso tizinthu tina tamoyo tambirimbiri. Iwo sankayembekezera kuti m’malo amenewa mungapezeke zinthu zamoyo chifukwa ndi a mdima, opanikizika komanso ozizira kwambiri.

United Arab Emirates

Ndalama za golide zili pasikelo

Pofuna kuthana ndi vuto la kunenepa kwambiri, chaposachedwapa akuluakulu a mumzinda wa Dubai anayamba kupereka ndalama kwa munthu aliyense amene wachepetsa thupi. Akuluakuluwa ankapereka ndalama zokwana madola 45 a ku America pa kilogalamu iliyonse imene munthu wachotsa. Kuti munthu alandire ndalamazi, ankayenera kulembetsa kenako n’kuchepetsa thupi ndi makilogalamu awiri m’mwezi wa Ramadan.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena