Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 9/15 tsamba 8-9
  • Kodi Mungatani Ngati Kupepesa Kumakuvutani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungatani Ngati Kupepesa Kumakuvutani?
  • Galamukani!—2015
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • VUTO LIMENE LIMAKHALAPO
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupepesa?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Mufunikiradi Kupepesa?
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Kupepesa—Njira Yothandiza Yopezera Mtendere
    Nsanja ya Olonda—2002
  • N’chifukwa Chiyani Kupepesa Kumavuta?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 9/15 tsamba 8-9
Mwamuna akulankhula ndi mkazi wake yemwe akuyang’ana kumbali atakwiya

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

Kodi Mungatani Ngati Kupepesa Kumakuvutani?

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Tiyerekeze kuti inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu mwasemphana maganizo pa nkhani inayake. Ndiyeno inuyo mukunena kuti: ‘Sindingapepese. Nanga vuto ndi ineyo?’

Kenako mukuganiza zongonyalanyaza nkhaniyo, komabe inuyo komanso mnzanuyo mudakali chikwiyire. Mukuona kuti mutati mupepese, nkhaniyo ikhoza kutha koma kungoti zikukuvutani kupepesa.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kunyada. Mwamuna wina dzina lake Charlesa ananena kuti: “Nthawi zina zimakhala zovuta kuti upepese chifukwa umaona kuti ukapepesa uoneka ngati wopusa.” Choncho, kunyada kungachititse kuti munthu asavomereze kuti walakwa.

Mmene mumaganizira. Anthu ena amaganiza kuti m’pomveka kupepesa akazindikira kuti alakwitsadi zinthu. Mkazi wina dzina lake Jill anati: “Sizindivuta kupepesa ndikazindikira kuti ineyo ndi amene ndili wolakwa. Koma ndikazindikira kuti amene ndalakwitsa si ine ndekha, zimandivuta kupepesa. Ndimaona kuti sindingathe kupepesa ndikaona kuti tonse ndi amene tachititsa kuti zinthu zisokonekere.”

Anthu ambiri safuna kupepesa zikakhala kuti mnzawoyo ndi amene wawalakwira. Mwamuna wina dzina lake Joseph, ananena kuti: “Ukaona kuti iweyo sunalakwe, supepesa pofuna kumusonyeza mnzakoyo kuti ndiwe wosalakwa.”

Mmene munaleredwera. Ngati munakulira m’banja limene anthu ake sankapepesana, zimakhalanso zovuta kuti muvomereze zimene mwalakwitsa. Choncho ngati simunkachita zimenezi muli mwana, zingakhaledi zovuta kuti muzipepesa.

ZIMENE MUNGACHITE

Mwamuna ndi mkazi akuzimitsa moto ndi madzi

Kupepesa n’kofanana ndi kuzimitsa moto woopsa

Muziganizira mnzanuyo. Mungachite bwino kumakumbukira nthawi imene munthu wina anakupepesani komanso mmene munamvera. Muyenera kuti munamva bwino mumtima. Choncho mkazi kapena mwamuna wanu angamve bwino ngati mutam’pepesa. Ngakhale zitakhala kuti inuyo mukuona kuti simunalakwitse, mungachitebe bwino kupepesa chifukwa mnzanuyo wakhumudwa. Kuchita zimenezi kungathandize kuti mtima wake ukhale m’malo.​​—⁠Lemba lothandiza: Luka 6:⁠31.

Muziganizira banja lanu. Musamaone kuti kupepesa n’kupusa, koma muziona kuti kungathandize banja lanu kuti liziyenda bwino. Lemba la Miyambo 18:19 limanena kuti munthu amene wakwiya chifukwa choti munthu wina wamukhumudwitsa, safuna kumvanso maganizo a mnzake moti “amaposa mzinda wolimba.” Ngati aliyense akuona kuti sanalakwitse, zimakhala zovuta kuti mukambirane n’kuthetsa nkhaniyo. Mukapepesa zimathandiza kuti nkhaniyo isakule. Mukamachita zimenezi, mumasonyeza kuti mumaona kuti banja lanu ndi lofunika kwambiri.​​—⁠Lemba lothandiza: Afilipi 2:⁠3.

Muzipepesa mwamsanga. Anthu ambiri zimawavuta kuti apepese akazindikira kuti onse analakwitsa. Ngati mkazi kapena mwamuna wanu walakwitsa, si bwino kusiya kumuchitira zinthu zabwino. Choncho ndi bwino kuti muyambe ndinu kupepesa m’malo moganiza kuti pakapita nthawi, nkhaniyo izizira. Ngati mutayamba ndinu kuchita zimenezi, mnzanuyo sangavutike kuti akupepeseni. Ngati nthawi zonse mutamapepesa mukhoza kuzolowera ndipo simungamaonenso kuti kupepesa n’kovuta.​​—⁠Lemba lothandiza: Mateyu 5:⁠25.

Muzipepesa kuchokera pansi pa mtima. Kuyesetsa kufotokoza zimene zakuchititsani kuti muchite zinazake si kupepesa. Komanso sikungakhale kupepesa ngati mutalankhula monyoza kuti, “Pepanitu sindimadziwa kuti zimene ndachitazi zikukhudwitsani.” Ndi bwino kuvomereza kuti mwalakwitsa komanso kuti mwakhumudwitsa mnzanuyo m’malo modziikira kumbuyo. Muyenerabe kuchita zimenezi kaya mnzanuyo wakhumudwa kapena ayi.

Muzivomereza mukalakwitsa. Ndi bwino kukhala wodzichepetsa n’kumadziwa kuti nthawi zina mukhoza kulakwitsa. Ndipo palibe munthu yemwe amachita zabwino zokhazokha osalakwitsa. Ngakhale mutaona kuti simunalakwitse chilichonse, muzikumbukira kuti nthawi zina timaona zinthu molakwika. Baibulo limanena kuti: “Woyamba kufotokoza mbali yake pa mlandu amaoneka ngati wolondola, koma mnzake amabwera n’kumufufuzafufuza.” (Miyambo 18:17) Sizingakuvuteni kupepesa ngati mumadziwa kuti simungachite zinthu zonse molondola.

a Tasintha mayina m’nkhaniyi.

MALEMBA OMWE MUNGAGWIRITSE NTCHITO

  • “Zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inuyo muwachitire zomwezo.”—Luka 6:31

  • ‘Muzikhala odzichepetsa, n’kumaona ena kukhala okuposani.”​—Afilipi 2:3.

  • ‘Muzithetsa nkhani mofulumira.’​—Mateyu 5:25.

Jason ndi Alexandra

JASON NDI ALEXANDRA

“Mukamapepesana mumakhala ndi banja labwino ndipo simukhalira kukangana. Kupepesa kumathandiza kuti muzisonyeza mwamuna kapena mkazi wanu kuti mumamukonda.”

Kai ndi Julia

KAI NDI JULIA

“Mumapepesana kuti mukhale pa mtendere. Cholinga chanu chimakhala chofuna kuthetsa nkhaniyo osati kudziwa kuti walakwa ndani. Ngati mwamuna kapena mkazi wanu wakhumudwa chifukwa cha zimene mwachita, mungachite bwino kumupepesa kuti mtima wake ukhale m’malo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena