MUNGATANI KUTI MUCHEPETSE NKHAWA?
Zomwe Zimachititsa Kuti Anthu Azikhala ndi Nkhawa
Akatswiri a pachipatala china chotchuka, chotchedwa Mayo, anati: “Nthawi zambiri anthu akuluakulu ndi amene akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Zimenezi zili chonchi chifukwa moyo wa masiku ano umasinthasintha komanso ndi wosadalirika.” Zina mwa zinthu zimene zimachititsa kuti anthu azikhala ndi nkhawa ndi monga:
kutha kwa banja
kumwalira kwa munthu amene timamukonda
matenda aakulu
ngozi yaikulu
kuphwanya malamulo
kukhala wotanganidwa nthawi zonse
ngozi zachilengedwe kapena zochititsidwa ndi anthu
kupanikizika ndi zochitika za kuntchito kapena kusukulu
kusowa kwa ntchito komanso mavuto a zachuma