Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 10 tsamba 78-86
  • Ufumu Umene “Sudzawonongeka”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ufumu Umene “Sudzawonongeka”
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuzonda Kosonkhezera Mtima
  • Zolinga Zake—Mmene Zimapezedwera
  • Zipambano Zikuwoneka Kale
  • Mkhalidwe Wokhalitsa wa Ufumu
  • Ufumu “Woti Sudzawonongeka ku Nthaŵi Zonse”
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Ufumu wa Mulungu—Ulamuliro Watsopano wa Dziko Lapansi
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Ufumu wa Mulungu Umaposa Mafumu Onse
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 10 tsamba 78-86

Mutu 10

Ufumu Umene “Sudzawonongeka”

1, 2. (a) Kodi nchenicheni chotani chimene chimagogomezeredwa tsiku lirilonse ndi zochitika zadziko, ndipo motani? (b) Kodi nchiyani chiri mankhwala okha?

ZOCHITIKA zadziko tsiku lirilonse zimatsimikizira chenicheni chakuti anthu sanapeze chimwemwe mwa kukana ulamuliro wa Yehova koma, mmalo mwake, kuyesayesa kudzilamulira. Palibe dongosolo laboma laumunthu limene labweretsa mapindu popanda tsankhu kwa anthu. Ngakhale kuli kwakuti anthu akulitsa chidziwitso chawo cha sayansi kumlingo waukulu koposa ndi kale lonse, iwo sanakhoze kuchotsa uchimo, kugonjetsa matenda ndi kuthetsa imfa, ngakhale kwa mmodzi wa nzika zawo. M’malo mwake, mitundu yapitirizabe kupanga zida zankhondo zatsopano ndi zowononga kopambana. Chiwawa chaupandu chikufunga. Luso lazopangapanga, umbombo ndi umbuli zagwirizana kuipitsa mtunda, madzi ndi mpweya. Kukwera kwa mitengo kowonjezereka mofulumirako ndi ulova kukuchititsa kukhala kovuta kwambiri kwa ochuluka kupeza zofunika za moyo. Anthu akusowa njira yotulukira.—Mlal. 8:9.

2 Kodi nchiyani chimene chiri yankho? Ufumu wa Mulungu, umene Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuupempherera. (Mat. 6:9, 10) Ha ndi okondwera chotani nanga m’mene tiyenera kukhalira kuti chitonthozo chimene udzabweretsa tsopano chayandikira kwambiri!

3. (a) Mogwirizana ndi Ufumu uwu, kodi nchiyani chinachitika m’mwamba mu 1914 C.E.? (b) Kodi nchifukwa ninji chimenecho chiri chofunika kwa ife?

3 Ufumu wa Mulungu, wayamba kale kugwira ntchito m’manja mwa Yesu Kristu, kuyambira 1914.a M’chaka chimenecho zochitika zimene Danieli anawona m’masomphenya olosera zinachitikadi m’mwamba. “Nkhalamba yakale lomwe,” Yehova Mulungu anapatsa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, ndi anthu onse ndi mitundu yonse ya anthu ndi amanenedwe onse, amtumikire.” Posimba za masomphenyawo, Danieli analemba kuti: “Ulamuliro wake ndi ulamuliro wosatha wosapitirira, ndi ufumu wake sudzawonongeka.” (Dan. 7:13, 14) Kuli kupyolera mwa Ufumu uwu kuti Mulungu adzachititsa okonda chilungamo kudzasangalala ndi zinthu zabwino zosawerengeka zimene analinganiza pamene anaika makolo athu aumunthu oyamba m’Paradaiso.

4. Kodi ndichidziwitso chotani chonena za Ufumu chimene chiri chokondweretsa kwambiri kwa ife, ndipo chifukwa ninji?

4 Nzika zokhulupirika za Ufumu ziri ndi chikondwerero chachikulu m’kaumbidwe ndi kugwira ntchito kwa boma limeneli. Zimafuna kudziwa chimene likuchita tsopano, chimene lidzachita mtsogolo ndi chimene limafuna kwa iwo. Amalipenda mosamalitsa, ndipo pamene akutero, chiyamikiro chawo cha ilo chimakula ndipo amazikonzekeretsa kuuza ena za ilo.—Sal. 48:12, 13.

Kuzonda Kosonkhezera Mtima

5. (a) Kodi ndimotani mmene Malemba amasonyezera mwini ulamuliro umene ukusonyezedwa mwa Ufumu Waumesiya? (b) Chotero kodi ndimotani mmene tikuyambukidwira ndi zimene timaphunzira za Ufumuwo?

5 Chimodzi cha zinthu zoyamba zimene kupenda kotero kumavumbula nchakuti Ufumu Waumesiya uli chitsimikiziro cha ulamuliro wa Yehova iyemwiniyo. Ali Iye amene anapereka “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu” kwa Mwana wake. Chotero, Ufumuwo utayamba kulamulira, moyenerera mawu m’mwamba analengeza kuti: “Ufumu wadziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova Mulungu] ndi wa Kristu wake: ndipo [Yehova] adzachita ufumu kufikira nthawi zanthawi.” (Chiv. 11:15) Chotero chirichonse chonena za Ufumu uwu ndi chimene umakwaniritsa chimatiyandikizitsa pafupi kwambiri kwa Yehova iyemwiniyo. Chimalowetsa mwa ife chikhumbo cha kugonjera ku ulamuliro wake kosatha.

6. Kodi nchifukwa ninji chiri chotikondweretsa mwapadera kuti Yesu Kristu ali wolamulira wachiwiri wa Yehova?

6 Ha ndi kwabwino kwambiri chotani mmene kuliri nanga kuti Yehova waika Yesu Kristu pampando wachifumu monga wolamulira wachiwiri kwa Iye! Monga Mmisiri amene Mulungu anagwiritsira ntchito kulenga dziko lapansi ndi munthu, Yesu amadziwa zochita zathu bwino kwambiri koposa mmene aliyense wa ife amachitira. Ndiponso, kuyambira pachiyambi cha mbiri anasonyeza ‘kusekerera ndi ana a anthu’ kwakeko. (Miy. 8:30, 31; Akol. 1:15-17) Chikondi chimenecho chinali chachikulu kwambiri kotero kuti anadza iyemwiniyo kudziko lapansi ndi kupereka moyo wake monga dipo mmalo mwawo. Mwakutero anachititsa kupezeka kwa ife njira yomasulidwira ku uchimo ndi imfa, ndi mwayi wa moyo wosatha.—Mat. 20:28.

7. (a) Mosiyana ndi ulamuliro wochitidwa ndi anthu, kodi nchifukwa ninji bomali lidzakhala lokhalitsa? (b) Kodi ndiunansi wanji umene “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” alinawo ndi boma lakumwamba?

7 Limeneli liri boma lokhazikika, lokhalitsa. Mkhalidwe wake wokhalitsawo watsimikiziridwa ndi chenicheni chakuti Yehova iyemwiniyo samafa. (Hab. 1:12; Sal. 146:3-5, 10) Mosiyana ndi mafumu aumunthu, Yesu Kristu kupyolera mwa amene Mulungu waikizira ufumu, alinso wosakhoza kufa. (Aroma 6:9; 1 Tim. 6:15, 16) Ogwirizana ndi Kristu m’mipando yachifumu yakumwamba adzakhala ena 144 000, atumiki okhulupirika a Mulungu otengedwa kuchokera ku “mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse.” Amenewanso, amapatsidwa moyo wosakhoza kufa. (Chiv. 5:9, 10; 1 Akor. 15:42-44, 53) Unyinji wa iwo uli kale m’miyamba, ndipo otsalira a iwo amene akali chikhalirebe padziko lapansi apanga kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kamene mokhulupirika kakupititsa patsogolo zinthu za Ufumu umenewo pano.—Mat. 24:45-47.

8, 9. (a) Kodi nziyambukiro zogawanitsa, zoipitsa ziti zimene Ufumuwo udzachotsa? (b) Chotero ngati titi tipewe kukhala adani a Ufumu wa Mulungu, kodi ndimagulu ati ndi machitachita amene tikapewa kukhala okoledwamo?

8 Posachedwapa, panthawi yokwanira ya Mulungu, magulu ake owononga adzachitapo kanthu kuyeretsa dziko lapansi. Adzawononga kosatha anthu onsewo amene modzifunira sadziwa Mulungu, akukana kuvomereza ulamuliro wake, ndi amene amaseka makonzedwe achikondi amene iye amapanga kupyolera mwa Yesu Kristu. (2 Ates. 1:6-9) Iri lidzakhala tsiku la Yehova, nthawi yoyembekezeredwa kwanthawi yaitali ya kulemekezedwa kwake monga Wolamulira wa Chilengedwe chonse.

9 Chipembedzo chonyenga chonse, ndiponso maboma aumunthu onse ndi magulu awo ankhondo, amene akusonkhezeredwa ndi wolamulira woipa wosawoneka wadziko lino, adzawonongedwa kosatha. Onse odzidziwikitsa kukhala mbali yadziko lino mwa kulondola njira ya moyo yodzigangira, yachinyengo, yachisembwere adzadulidwa mu imfa. Satana ndi ziwanda zake adzaleketsedwa kuwonana ndi nzika zadziko lapansi, atabindikiritsidwa zolimba kwa zaka chikwi. Ha umenewu udzakhala mpumulo wotani nanga kwa onse okonda chilungamo!—Chiv. 18:21, 24; 19:11-16, 19-21; 20:1, 2.

Zolinga Zake—Mmene Zimapezedwera

10. (a) Kodi ndimotani mmene Ufumu Waumesiya udzakwaniritsira chifuno cha Yehova kaamba ka dziko lapansi lenilenilo? (b) Kodi ichi chidzatanthauzanji kaamba ka anthu okhala padziko lapansi panthawiyo?

10 Ufumu Waumesiya uwu udzakwaniritsa kotheratu chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi. (Gen. 2:8, 9, 15; 1:28) Kufikira lero, munthu walephera kukwaniritsa chifuno chimenecho. Komabe, “m’dziko lokhalidwa lirinkudza” laikidwa m’manja mwa mwana wa munthu, Yesu Kristu. Onse opulumuka chiwonongeko cha chiweruzo cha Yehova padongosolo lakale lazinthu iri adzagwira ntchito mogwirizana pansi pa Kristu monga Mfumu, mokondwera akumachita chirichonse chimene iye akuwalangiza kotero kuti dziko lapansi lonse likufikira kukhala Paradaiso. (Aheb. 2:5-9) Anthu onse adzasangalala ndi ntchito ya manja awo ndi kupindula mokwanira ndi zipatso zadziko lapansi zambirizo.—Sal. 72:1, 7, 8, 16-17; yerekezerani Yesaya 65:21, 22.

11. (a) Kodi ndimotani mmene ungwiro m’maganizo ndi m’thupi udzachitikira kaamba ka nzika za Ufumu? (b) Kodi ichi chidzaphatikizapo chiyani?

11 Pamene Adamu ndi Hava analengedwa anali angwiro, ndipo chinali chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi kulidzadza ndi mbadwa zawo, iwo onse akumasangalala ndi ungwiro m’maganizo ndi m’thupi. Pansi paulamuliro wa Ufumu, chifuno chimenecho chidzakwaniritsidwa mwaulemerero. Izi zikufunikiritsa kuchotsedwa kwa ziyambukiro zonse zauchimo, ncholinga chimenecho Kristu akutumikira osati kokha monga Mfumu komanso monga Mkulu wa Ansembe. Moleza mtima adzathandiza nzika zake zomvera kupindula ndi mtengo wansembe yotetezera uchimo ya moyo wake waumunthu. Maso akhungu adzatsegulidwa. Makutu ogontha adzamva. Mnofu wokhwinyatitsidwa ndi ukalamba kapena nthenda udzakhala wosalala kuposa wa mwana. Nthenda zosachiritsika zidzalowedwa mmalo ndi thanzi lamphamvu. Tsiku lidzafika pamene sipadzakhala munthu wokhala ndi chifukwa chonenera kuti, “ndikudwala,” chifukwa chakuti anthu owopa Mulungu adzamasulidwa ku chothodwetsa cha uchimo ndi ziyambukiro zake zomvetsa chisoni.—Yerekezerani ndi Yesaya 33:22, 24; 35:5, 6; Yobu 33:25; Luka 13:11-13.

12. (a) Kodi nchiyaninso chimene ungwiro waumunthu umafunikiritsa? (b) Kodi udzapezedwa motani, ndipo kodi nchiyani chidzachokeramo?

12 Komabe, kupeza ungwiro, kumaphatikizapo zambiri koposa kukhala kokha ndi thupi lolama ndi maganizo olama. Kumaphatikizapo kusonyeza moyenerera mikhalidwe ya umunthu wa Yehova, chifukwa chakuti munthu analengedwa ‘m’chifanizo cha Mulungu, mogwirizana ndi chifanefane chake.’ (Gen. 1:26) Ncholinga ichi, maphunziro ambiri adzafunika. Limeneli liri Dongosolo Latsopano mmene “mukhalitsa chilungamo,” kotero kuti, monga momwe mneneri Yesaya ananeneratu, “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (2 Pet. 3:13; Yes. 26:9) Khalidwe iri limatsogolera kumtendere—pakati pa anthu amitundu yonse, pakati pa mabwenzi oyandikana, m’banja lamunthu ndipo, koposa zonse, ndi Mulungu iyemwiniyo. (Yes. 32:17; Sal. 85:10-13) Ophunzira chilungamo amenewo adzaphunzitsidwa mopita patsogolo chimene chiri chifuniro cha Mulungu kwa iwo. Pamene kukonda njira za Yehova kufikira kukhala kozika mizu kwambiri m’mitima yawo, adzatsatira njirazo mbali iriyonse ya miyoyo yawo. Munthu wangwiro Yesu anali wokhoza kunena kuti, ‘Nthawi zonse ndichita zinthu zokondweretsa Atate wanga.’ (Yoh. 8:29) Ha ndi wosangalatsa chotani nanga mmene moyo udzakhalira pamene zimenezo zichitika kwa anthu onse!

Zipambano Zikuwoneka Kale

13. Gwiritsirani ntchito mafunso ali pamwambapowo kugogomezera zipambano za Ufumu ndi zimene chifukwa cha chimenecho tiyenera kukhala tikuchita.

13 Zipambano zochititsa chidwi za Ufumu ziri kale umboni wowoneka bwino kwa anthu amene ali ndi maso achikhulupiriro. Mafunso otsatira ndi Malemba olembedwa adzakukumbutsani zina za zimenezi, kudzanso za zinthu zimene nzika zonse za Ufumu zingakhoze ndipo ziyenera kukhala zikuchita tsopano:

Kodi Mfumuyo inayamba kuchitapo kanthu motsutsana ndi yani, ndipo nzotulukapo zotani? (Chiv. 12:7-10, 12)

Kodi ndikusonkhanitsidwa kwa ziwalo zotsirizira za kagulu kati kumene kunapatsidwa chisamaliro chofulumira Kristu atangokhazikitsidwa pampando wachifumu? (Mat. 24:31; Chiv. 7:1-4)

Pa Mateyu 25:31-33, kodi ndintchito ina iti imene Yesu adaneneratu kuti akaichita atakhala pa mpando wake wachifumu ndipo asanawononge oipa?

Kodi ntchito imeneyi ikuchitidwa motani? Kodi ndani akukhala ndi phande mu iyo? (Mat. 24:14; Sal. 110:3; Chiv. 14:6, 7)

Kodi nchifukwa ninji otsutsa andale zadziko ndi achipembedzo akhala osakhoza kuiyimika? (Mac. 5:38, 39; Zek. 4:6)

Monga chotulukapo cha ntchito yophunzitsa yochitidwayo, kodi ndimasinthidwe otani amene achitika kale m’miyoyo ya anthu amene amagonjera ku ulamuliro wa Ufumu? (Yes. 2:4; 1 Akor. 6:9-11)

Mkhalidwe Wokhalitsa wa Ufumu

14. (a) Kodi Kristu adzalamulira kwa utali wotani? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakwaniritsidwa mkati mwa nthawiyo?

14 Pambuyo pa kuponyedwa m’phompho kwa Satana ndi ziwanda zake, Yesu Kristu limodzi ndi 144 000 olamulira anzakewo adzachita ufumu kwa zaka chikwi. (Chiv. 20:6) Mkati mwa nthawiyo anthu adzafikitsidwa ku ungwiro. Boma liri lonse ndi ulamuliro ndi mphamvu zotsutsana ndi Yehova zidzachotsedwa. Zimenezo zitakwaniritsidwa, Yesu adzabwezeranso Ufumu kwa Atate wake, “kuti Mulungu akhale zonse mu zonse.”—1 Akor. 15:24, 28.

15. Kodi nzowona motani kuti Ufumu umenewo ‘sudzawonongeka’?

15 Chotero malo antchito a Yesu iyemwiniyo ponena za dziko lapansi adzasintha. Komabe, ulamuliro wake udzakhala “ulamuliro wosatha” ndipo Ufumu wake “sudzawonongeka.” (Dan. 7:14) M’lingaliro lotani? M’chakuti mphamvu ya kulamulira sidzapatsidwa m’manja mwa anthu ena amene ali ndi zolinga zosiyana. Zipambano za Ufumu ‘sizidzawonongeka.’ Zimene Ufumu umachita kulemekeza dzina la Yehova ndi chifuno chake ponena za dziko lapansi iri zidzakhala kosatha.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani bukhu la “Let Your Kingdom Come,” tsamba 127-139.

Makambitsirano Openda

● Kodi nchifukwa ninji Ufumu wa Mulungu uli chothetsera chokha cha mavuto a anthu? Kodi ndiliti pamene unayamba kulamulira?

● Kodi nchiyani chimene makamaka chiri chochititsa chidwi kwa inu ponena za Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzakwaniritsa? Chifukwa ninji?

● Kodi nzipambano zotani za Ufumu zimene tingathe kuziwona kale? Kodi ndimbali yotani imene tiri nayo m’zimenezi?

[Chithunzi pamasamba 84, 85]

Anthu adzaphunzira chilungamo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena