Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 280-tsamba 284
  • Misa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Misa
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Akristu Amaiona Bwanji Misa?
    Galamukani!—1999
  • Chikumbutso (Mgonero wa Ambuye)
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Mumachita Mwambo wa Mgonero wa Ambuye Mosiyana ndi Zipembedzo Zina?
    Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 280-tsamba 284

Misa

Tanthauzo: Monga momwe kwafotokozedwera ndi Mpingo Wopatulika wa Madzoma a Tchalitchi cha Roma Katolika, Misa ndiyo “—nsembe mu imene Nsembe Yamtanda imapitirizidwa;—Chikumbukiro cha imfa ndi chiukiriro za Ambuye, amene anati ‘chitani ichi chikhale chikumbukiro changa’ (Luka 22:19);—Phwando lopatulika limene, Thupi ndi Mwazi za Ambuye zimagwirizanitsidwa, Anthu a Mulungu amapeza mapindu a Nsembe ya Paskha, kuyambiranso Pangano Latsopano limene Mulungu wapangana ndi anthu kamodzi kunthaŵi zonse kupyolera mwa Mwazi wa Kristu, ndipo mwachikhulupiriro ndi chiyembekezo limaphiphiritsira ndipo limakhala kalambule bwalo wa phwando la pambuyo kutha kwadziko mu ufumu wa Atate, kulengeza imfa ya Ambuye ‘kufikira kudza Kwake.’” (Eucharisticum Mysterium, May 25, 1967) Ndiyo njira ya Tchalitchi cha Katolika yochitira zimene amazindikira kuti Yesu Kristu anachita pa Mgonero Womaliza.

Kodi mkate ndi vinyo zimasandulizidwadi kukhala thupi ndi mwazi za Kristu?

Mu “Dzoma la Kulengezedwa kwa Chikhulupiriro” pa June 30, 1968, Papa Paul VI anati: “Tikhulupirira kuti monga momwe mkate ndi vinyo zodalitsidwa ndi Ambuye pa Mgonero Womaliza zinasandulizidwira kukhala Thupi Lake ndi Mwazi Wake zimene zinayenera kuperekedwa kaamba ka ife pamtanda, chotero mkate ndi vinyo zodalitsidwa ndi wansembe zimasandulizidwa kukhala Thupi ndi Mwazi za Kristu woikidwa pampando wachifumu waulemerero kumwamba, ndipo Ife timakhulupirira kuti kukhalapo kwachinsinsi kwa Ambuye, mwa mawonekedwe a zinthuzo zimene m’maganizo mwathu zimawonekera kukhala zofanana ndi panthaŵi imene zinali Zisanadalitsidwe ndi pambuyo pake, ndiko kwenikweni ndi kotsimikizirika. . . . Masinthidwe amenewa akutchedwa moyenerera kwambiri ndi Tchalitchi kukhala kusandulika kwenikweni.” (Official Catholic Teachings—Christ Our Lord, Wilmington, N.C.; 1978, Amanda G. Watlington, p. 411) Kodi Malemba Opatulika amavomereza chikhulupiriro chimenecho?

Kodi Yesu anatanthauzanji pamene ananena kuti “Iri ndithupi langa,” “Uwu ndimwazi wanga”?

Mat. 26:26-29: “Ndipo pamene iwo anali nkudya, Yesu anatenga mkate, nadalitsa, naunyema; ndipo mmene anapatsa kwa ophunzira, anati, Tengani, idyani, ichi ndithupi langa. Ndipo pamene anatenga chikho, anayamika, napatsa iwo, nanena, Mwerani ichi inu nonse, pakuti ichi ndimwazi wanga wa pangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri kuchotsa machimo. Ndipo ndinena kwa inu, sindidzamwanso chipatso ichi champesa, kufikira tsiku limene ndidzamwa chatsopano, pamodzi ndi inu, muufumu wa Atate wanga.”

Ponena za mawu akutiwo “iri ndithupi langa” ndi “ichi ndimwazi wanga” zotsatirazi nzoyenera kwambiri; Mo imati, “utanthauza thupi langa” “uwu utanthauza mwazi wanga.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) NW ali ndi mawu ofanana. LEF amamasulira mawuwo kuti, “uwu uimira thupi langa,” “uwu uimira mwazi wanga.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) Mamasulidwe amenewa amavomerezana ndi zimene zafotokozedwa mmawu apatsogolo ndi apambuyo, m’vesi 29, m’matembenuzidwe osiyanasiyana Achikatolika. Kx imati: “Sindidzamwanso za chipatso champesa ichi, kufikira ndidzachimwa limodzi nanu, vinyo watsopano mu ufumu wa Atate wanga.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) CC, NAB, Dy nawonso amasonyeza Yesu kukhala akunena zimene zinali m’chikho kukhala “chipatso cha mpesa,” ndipo zimenezi zinanenedwa Yesu atatha kunena kuti, ‘uwu ndiwo mwazi wanga.’

Talingalirani mawu akutiwo ‘uwu ndithupi langa’ ndi “uwu ndimwazi wanga” mothandizidwa ndi mawu ena otsimikizirika ogwiritsiridwa ntchito m’Malemba. Yesu anatinso, “ndine kuunika kwa dziko,” “ndine khomo la nkhosa,” “ndine mpesa weniweni.” (Yoh. 8:12; 10:7; 15:1) Palibe alionse a mawu amenewa amene anatathauza kusandulizidwa kozizwitsa, kodi sichoncho?

Pa 1 Akorinto 11:25 (JB), mtumwi Paulo analemba za Mgonero Womaliza ndipo anafotokoza malingaliro ofananawo m’mawu osiyanirapo pang’ono. Mmalo mwakugwira mawu Yesu ponena za chikho akuti, “mwerani ichi inu nonse . . . popeza ndicho mwazi wanga, mwazi wa pangano,” iye ananena mawuwo motere, “Chikho ichi ndipangano latsopano mmwazi wanga.” Ndithudi zimenezo sizinatanthauze kuti chikhocho mwanjira inayake chinasandulitsidwa mozizwitsa kukhala pangano latsopano. Kodi sikuli kwanzeru kwambiri kunena kuti zimene zinali m’chikho zinaimira mwazi wa Yesu umene unachititsa pangano latsopano kugwira ntchito?

Kodi Yesu anatanthauzanji mwamawu ake a pa Yohane 6:55-57?

“Yesu anati kwa iwo. Indetu, Indetu, ndinena ndi inu, Ngati simukudya thupi la Mwana wa munthu ndi kumwa mwazi wake, mulibe moyo mwa inu nokha. Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga ali nawo moyo wosatha; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndichakudya ndithu, ndi mwazi wanga ndichakumwa ndithu. Iye wakudya thupi langa, ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa ine, ndi ine mwa iye. Monga Atate wamoyo anandituma ine, ndipo inenso ndiri ndi moyo chifukwa cha Atate; momwemo wondidya ine, iyeyu adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.”—Yohane 6:53-57, JB.

Kodi zimenezi ziyenera kumvedwa kukhala zikutanthauza kuti iwo anayenera kudyadi thupi la Yesu ndi kumwa mwazi wake? Ngati ziri choncho, Yesu akanakhala ali kuchirikiza kuswedwa kwa Chilamulo chimene Mulungu adapereka kwa Israyeli kupyolera mwa Mose. Chilamulo chimenecho chinaletsa kudyedwa kwa mtundu uliwonse wa mwazi. (Lev. 17:10-12) Mosiyana ndi kuchirikiza chinthu choterocho, Yesu anatsutsa mwamphamvu kuswa chirichonse cha zofunika za Chilamulo. (Mat. 5:17-19) Chotero zimene Yesu anali kulingalira ziyenera kukhala zinali kudya ndi kumwa m’lingaliro lophiphiritsira, mwa kusonyeza chikhulupiriro mumtengo wa nsembe yake yaumunthu yangwiro.—Yerekezerani ndi Yohane 3:16; 6:35, 40.

Kodi Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kusakhala ndi chikumbutso chabe cha imfa yake koma dzoma limene kwenikweni likanayambitsanso nsembe yake?

Mogwirizana ndi kunena kwa The Documents of Vatican II: “Pa Mgonero Womaliza, pausikuwo umene Iye anaperekedwa, Mpulumutsi wathu anayambitsa Nsembe ya Ukaristiya ya Thupi Lake ndi Mwazi. Iye anachita izi kupitirizabe nsembe ya Mtanda . . . ”—(New York, 1966), lolembedwa ndi W. M. Abbott, S.J., p. 154; kanyenye wawonjezeredwa.

The Catholic Encyclopedia imati: “Tchalitchi chikulinganiza kuti Misa iwonedwe kukhala ‘nsembe yeniyeni ndi yoyenera’ . . . Komabe, magwero aakulu achiphunzitso chathu, ndiwo mwambo, umene kuyambira nthaŵi zakalekale umalengeza kufunika kwakupempha Nsembe ya Misa.”—(1913), Vol. X, pp. 6, 17.

Yesu mwiniyo anati: “Chitani ichi chikhale chikumbukiro changa.” (Luka 22:19; 1 Akor. 11:24, JB) Pa Luka 22:19, Kx ndi Dy pamati: “Chitani chimenechi kuchitira kundikumbukira.” NAB imati: “Chitani ichi monga chondikumbukira nacho.” Yesu sananena kuti chimene anachita pa Mgonero Womaliza chinali kudzipereka nsembe kwake kapena kuti mwinamwake ophunzira ake akafunikira kuyambiranso nsembe yake.

Aheb. 9:25-28, imati: “Kosati kuti adzipereke yekha kaŵirikaŵiri; monga mkulu wa ansembe [Wachiyuda] aloŵa m’malo opatulika chaka ndi chaka ndi mwazi wosati wake, chikadatero, kukadamuyenera kumva zoŵaŵa kaŵirikaŵiri kuyambira kuzika kwa dziko lapansi; koma tsopano kamodzi . . . kuchotsa uchimo mwa nsembe ya iye yekha. Ndipo popeza kwaikikatu kwa anthu kufa kamodzi, ndipo atafa, chiweruziro; kotero Kristunso ataperekedwa nsembe kamodzi.” (Kanyenye wawonjezeredwa.)

Kodi ndi “chinsinsi chosadziŵika” chabe?

Baibulo limatchula zinsinsi za Mulungu, kapena zinsinsi zopatulika. Koma palibe chirichonse cha zimenezi chimene chimawombana ndi chowonadi chofotokozedwa momvekera bwino cha Malemba. Ponena za awo amene amaika miyambo yawo patsogolo pa Malemba, Yesu anati: “Onyenga! Ndinu amene Yesaya anatanthauza pamene analosera molondola kwambiri kuti: Anthu aŵa amandilemekeza kokha ndi utumiki wachipamaso, pamene mitima yawo iri kutali ndi ine. Kundilambira kwawo nkopanda pake; ziphunzitso zimene amaphunzitsa ziri kokha malamulo a anthu.”—Mateyu 15:7-9, JB.

Kodi Yesu anatanthauza kuti chikumbutso chimenechi mwinamwake chidzasungidwa tsiku lirilonse kapena mlungu uliwonse?

Basic Catechism imati: “Ntchito Zapadera za Akristu Achikatolika” zimaphatikizapo “kuchita Misa Sande lirilonse ndi tsiku loyera la thayo.” (Boston, 1980, p. 21) “Ndithudi okhulupirika akulimbikitsidwa kukhalapo pa Misa kulandira Mgonero kaŵirikaŵiri, ngakhale tsiku lirilonse.” The Teaching of Christ—A Catholic Catechism for Adults, Kope Lachidule (Huntington, Ind.; 1979), p. 281.

Kodi maumboni onse Amalemba a “kunyema mkate” anasonyeza kuti imfa ya Kristu inali kukumbukiridwa? (Mac. 2:42, 46; 20:7, JB) Yesu ‘ananyema mkate pamene chakudya chinali kugaŵiridwa pachakudya ngakhale Mgonero Womaliza usanachitike. (Marko 6:41; 8:6) Mkate wogwiritsiridwa ntchito ndi Ayuda panthaŵi imeneyo suuli wofanana ndi umene anthu ambiri akuwudziŵa lerolino. Powudya, iwo kaŵirikaŵiri anafunikira kunyema kapena kuswa chidutswa.

Yesu sanafotokoze mwachindunji kuti ndimwakaŵirikaŵiri chotani mmene Chikhumbutso cha imfa yake chinayenera kusungidwira. Komabe, iye anachiyambitsa padeti la Paskha Wachiyuda, amene analoŵedwa mmalo ndi Chikhumbutso cha imfa ya Kristu pakati pa ophunzira ake. Paskha anali chochitika cha chaka ndi chaka, chochitidwa pa Nisan 14. Mofananamo, Phwando Lachiyuda la Mikate Yopanda Chotupitsa, Phwando la Masabata (Pentekoste), Phwando la Misasa, kapena la Kusonkhanitsa, ndi Tsiku la Chitetezo zinali kuchitika kamodzi pachaka.

Kodi mapempherero a pa Misa amabweretsa chimasuko kumiyoyo ya m’purigatoriyo?

The Teaching of Christ—A Catholic Catechism for Adults imalongosola kuti: “Liwu lakuti ‘purigatoriyo’ siliri m’Baibulo, ndipo chiphunzitso cha purigatoriyo sichimaphunzitsidwamo mwachindunji . . . Mabukhu a Abambo ali ndi maumboni ambiri osati kokha a kukhalako kwa purigatoriyo, komanso chenicheni chakuti akufa okhulupirika angathandizidwe ndi mapemphero a amoyo, makamaka mwa Nsembe ya Misa.”—Pp. 347, 348.

Ponena za mkhalidwe wa akufa, Malemba Opatulika amati: “Amoyo adziŵadi kuti adzafa, akufa sadziŵa chirichonse.” (Mlal. 9:5, JB) “Moyo [“moyo,” Kx; “munthu,” JB] wochita choipa, ndiwo udzafa.” (Ezek. 18:4, Dy) (Wonaninso tsamba 153, 154, pamutu wakuti “Imfa.”)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena