Mutu 120
Kukanidwa m’Bwalo Lamilandu
PAMBUYO pakusiya Yesu m’munda wa Getsemane ndi kuthaŵa mwamantha limodzi ndi atumwi ena, Petro ndi Yohane akuima kaye m’kuthaŵa kwawoko. Mwinamwake iwo akupezana ndi Yesu pamene akutengeredwa kunyumba ya Anasi. Pamene Anasi akumtumiza kwa Mkulu wa Ansembe Kayafa, Petro ndi Yohane akutsatira chapatalipo, mwachiwonekere athedwa nzeru ndi mantha kuwopera miyoyo ya iwo eni ndi nkhaŵa yawo yaikulu ponena za zimene zidzachitikira Mbuye wawo.
Atafika panyumba yaikulu ya Kayafa, Yohane wakhoza kuloŵa m’bwalolo popeza kuti ngwodziŵika ndi mkulu wa ansembeyo. Komabe, Petro, wasiyidwa ataimirira chiriri kunja pachipata. Koma mwamsanga Yohane akubwerera nalankhula kwa wosunga pakhomo, mdzakazi, ndipo Petro akuloledwa kuloŵa.
Pofika tsopano kwazizira, ndipo akalinde a panyumbapo ndi adindo a mkulu wa ansembe akoleza moto wamakala. Petro akugwirizana nawo kuti adzifunditse pamene akuyembekezera zotulukapo za mlandu wa Yesu. Pamenepo, m’kuunika kwa moto woyaka, wosunga pakhomo amene analola Petro kuloŵa akumyang’anitsitsa. “Iwenso, unali ndi Yesu wa ku Galileya!” Iye akutero.
Atakwiya kuti wadziŵika, Petro akukana pamaso pa onse kuti sanadziŵe Yesu nkale lomwe. “Sindidziŵa kapena kumvetsetsa chimene uchinena,” iye akutero.
Pamenepo Petro akutuluka kumka pafupi ndi chipata. Kumeneko, msungwana wina akumuwona ndipo nayenso akuuza oimirirapo: “Uyonso anali ndi Yesu Mnazarayo.” Kachiŵirinso Petro akulandula, akumalumbira kuti: “Sindidziŵa munthuyo.”
Petro akukhalabe m’bwalo la nyumbayo, akumayesayesa kudzibisa monga momwe angathere. Mwinamwake panthaŵi ino akuchita kakasi ndi kulira kwa tambala mumdima wambandakucha. Pakali pano, kuzengedwa mlandu kwa Yesu kuli mkati, mwachiwonekere ukuzengedwera m’chipinda cha nyumbayo chapamwamba pa bwalo limenelo. Mosakayikira, Petro ndi ena oyembekezera pansipo akuwona mboni zoloŵa ndi zotuluka zosiyanasiyana zimene zaloŵetsedwa kudzachitira umboni.
Pafupifupi ola limodzi lapita kuyambira panthaŵi yotsiriza pamene Petro anadziŵika monga bwenzi la Yesu. Tsopano angapo a oimirira pamenepo akudza kwa iye nanena: “Zowonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.” Mmodzi wa a m’kaguluko ndiwachibale wa Malko, amene Petro anadula khutu. “Ine sindinakuwona iwe kodi m’munda pamodzi ndi iye?” Iye akutero.
“Sindidziŵa munthuyo.” Petro akunenetsa mokalipa. Kunena zowona, iye akuyesa kuwakhutiritsa kuti iwo onse alakwa mwa kutemberera ndi kulumbira pankhaniyo, m’chenicheni, akumadziitanira themberero iye mwiniyo ngati salankhula chowonadi.
Mwamsanga Petro atakana nthaŵi yachitatuyi, tambala akulira. Ndipo pamphindi imeneyo, Yesu, amene mwachiwonekere watulukira palikole lapamwamba la nyumbayo, akutembenuka namuyang’anitsitsa. Mwamsanga, Petro akukumbukira zimene Yesu ananena maola ochepekera okha apitawo m’chipinda chapamwamba kuti: “Tambala asanalire kaŵiri, udzandikana katatu.” Atapsinjidwa maganizo ndi kulemera kwa tchimo lake, Petro akutuluka ndipo akulira kwambiri.
Kodi izi zikanachitika motani? Kodi ndimotani mmene, pambuyo pakukhala wotsimikizira kwambiri za nyonga yake yauzimu, kuti Petro akanakana Mbuye wake nthaŵi zitatu zotsatizana mofulumira? Mosakayikira mikhalidweyo inapezerera Petro modzidzimutsa. Chowonadi chikupotozedwa, ndipo Yesu akusonyezedwa kukhala mpandu woipitsitsa. Chimene chiri cholungama chikuchititsidwa kuwonekera kukhala cholakwa, wopanda liwongo monga waliwongo. Chotero chifukwa cha chitsenderezo cha panthaŵiyo Petro akukhumudwa. Mwadzidzidzi maganizo ake olama a kukhulupirika adodometsedwa; mwachisoni kwa iye wagonjetsedwa ndi kuwopa munthu. Zimenezo zisachitiketu kwa ife! Mateyu 26:57, 58, 69-75; Marko 14:30, 53, 54, 66-72; Luka 22:54-62; Yohane 18:15-18, 25-27.
▪ Kodi ndimotani mmene Petro ndi Yohane aloŵera kubwalo la nyumba ya mkulu wa ansembe?
▪ Pamene Petro ndi Yohane ali m’bwalo la nyumbayo, kodi chikuchitika nchiyani m’nyumbamo?
▪ Kodi ndinthaŵi zingati zimene tambala akulira, ndipo ndinthaŵi zingati zimene Petro akukana kudziŵa Kristu?
▪ Kodi kukutanthauzanji kuti Petro akutemberera ndi kulumbira?
▪ Kodi chikuchititsa Petro kulandula kuti akudziŵa Yesu nchiyani?