Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • fy mutu 7 tsamba 76-89
  • Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?
  • Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI WOPANDUKA NDI WOTANI?
  • ZOCHITITSA KUPANDUKA
  • ELI WOLEKERERA NDI REHABIAMU WOUMITSA ZINTHU
  • KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZAZIKULU KUNGALETSE KUPANDUKA
  • PAMENE ANA AGWERA M’VUTO
  • KUCHITA NDI WOPANDUKA WENIWENI
  • Sonyezani chikondi ndi chiyamikiro kwa ana anu
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Makolo Phunzitsani Ana Anu Mwachikondi
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Phunzitsani Ana Anu kukonda Yehova
    Nsanja ya Olonda—2007
Onani Zambiri
Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
fy mutu 7 tsamba 76-89

Mutu 7

Kodi Muli ndi Wopanduka m’Nyumba?

Chithunzi patsamba 76

1, 2. (a) Kodi Yesu anapereka fanizo lotani kuti agogomezere kupanda chikhulupiriro kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda? (b) Kodi ndi mfundo yotani yonena za achinyamata omasinkhuka imene tingaphunzire m’fanizo la Yesu?

MASIKU oŵerengeka imfa yake isanachitike, Yesu anafunsa gulu la atsogoleri achipembedzo achiyuda funso lodzutsa maganizo. Iye anati: “Nanga mutani? Munthu anali nawo ana aŵiri; nadza iye kwa woyamba, nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wampesa. Koma iye anakana, nati, Sindifuna ine; koma pambuyo pake analapa mtima napita. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo iye anavomera, nati, Ndipita mbuye; koma sanapita. Ndani wa aŵiriwo anachita chifuniro cha atate wake?” Atsogoleri achiyudawo anayankha kuti: “Woyambayo.”—Mateyu 21:28-31.

2 Yesu pano anali kugogomezera kusakhulupirika kwa atsogoleri achiyuda. Iwo anali ngati mwana wachiŵiri uja, akumalonjeza kuchita chifuniro cha Mulungu koma nalephera kusunga pangano lawo. Koma makolo ambiri adzazindikira kuti fanizo la Yesu linazikidwa pa kudziŵa bwino kwake za moyo wa banja. Monga momwe anasonyezera bwino lomwe, kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kudziŵa zimene achichepere amalingalira kapena kudziŵiratu zimene adzachita. Wachichepere angachititse mavuto ochuluka m’zaka zake zakusinkhuka komabe nkukula ndi kukhala wachikulire wanzeru ndi wolemekezeka. Izi nzimene tiyenera kukumbukira pamene tikambitsirana vuto la kupanduka kwa achinyamata.

KODI WOPANDUKA NDI WOTANI?

3. Kodi nchifukwa ninji makolo sayenera kufulumira kutcha mwana wawo wopanduka?

3 Nthaŵi ndi nthaŵi, mwina mwamva za achinyamata amene amapandukira makolo awo kotheratu. Mwinamwake mukudziŵa banja limene lili ndi wachinyamata wooneka kukhala wosatheka kulamulira. Komabe, nthaŵi zina nkovuta kudziŵa kaya ngati mwana ali wopanduka weniweni. Ndiponso, kungakhale kovuta kudziŵa chifukwa chake ana ena amapanduka pamene ena—ngakhale m’banja limodzimodzi—samatero. Ngati makolo aona kuti mwina mmodzi wa ana awo akufuna kukhala wopanduka weniweni, kodi ayenera kuchitanji? Kuti tiyankhe, choyamba tiyenera kulongosola amene ali wopanduka.

4-6. (a) Kodi wopanduka ndi wotani? (b) Kodi makolo ayenera kukumbukiranji ngati mwana wawo wachinyamata samamvera nthaŵi ndi nthaŵi?

4 Mwachidule, wopanduka ndi munthu amene amapitiriza kusamvera mwadala kapena amene amatsutsa ndi kunyalanyaza ulamuliro. Ndithudi, ‘utsiru umangika mumtima mwa mwana.’ (Miyambo 22:15) Chotero ana onse panthaŵi ina amatsutsa ulamuliro wa makolo ndi wina uliwonse. Zimenezi zimachitika makamaka m’nthaŵi ya kukula kuthupi ndi m’maganizo kotchedwa zaka zakusinkhuka. Kusintha m’moyo wa munthu aliyense kumachititsa kupsinjika maganizo, ndipo zaka zakusinkhuka zili zamasinthidwe okhaokha. Mtsikana kapena mnyamata wanu womasinkhuka ali panjira yochoka ku ubwana kupita ku uchikulire. Pachifukwa chimenechi, mkati mwa zaka zakusinkhuka, makolo ena ndi ana awo akhala asakumvana. Kaŵirikaŵiri, makolo mwachibadwa amayesa kugwira kusinthako kuti kuyende pang’onopang’ono, pamene achinyamata amafuna kukufulumiza.

5 Wachinyamata amene ali wopanduka amafulatira malango a makolo ake. Komabe, kumbukirani kuti machitidwe oŵerengeka a kusamvera samapanga mwana kukhala wopanduka. Ndipo ponena za nkhani zauzimu, ana ena poyamba angasonyeze chidwi chochepa m’choonadi cha Baibulo ndipo mwina sangachisonyeze konse, koma angakhale osapanduka. Monga kholo, musafulumire kugamula ponena za mwana wanu.

6 Kodi achichepere onse amapandukira ulamuliro wa makolo awo m’zaka zawo zakusinkhuka? Ayi, osati onse. Ndithudi, umboni umasonyeza kuti ndi achinyamata oŵerengeka chabe amene amasonyeza kupanduka kwakukulu m’zaka zawo zakusinkhuka. Komabe, bwanji za mwana amene amapanduka mouma khosi ndi mopitirizabe? Kodi nchiyani chimene chingayambitse kupanduka koteroko?

ZOCHITITSA KUPANDUKA

7. Kodi ndi motani mmene mkhalidwe wausatana ungasonkhezerere mwana kupanduka?

7 Chochititsa kupanduka chachikulu ndicho mkhalidwe wausatana wa dzikoli. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Dziko lokhala m’mphamvu ya Satana lapanga makhalidwe owononga amene Akristu ayenera kulimbana nawo. (Yohane 17:15) Ochuluka a makhalidwewo ali oluluzika, angozi, ndi odzala ndi zisonkhezero zoipa lerolino kuposa kale. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Ngati makolo samaphunzitsa ana awo, kuwachenjeza, ndi kuwatetezera, anawo angatengeke mosavuta ndi “mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera.” (Aefeso 2:2) Chogwirizana ndi zimenezi ndicho chisonkhezero cha mabwenzi. Baibulo limati: “Mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Mofananamo, iye amene ayanjana ndi aja omwerekera ndi mzimu wa dzikoli mwachionekere adzasonkhezeredwa ndi mzimu umenewo. Achichepere amafunikira chithandizo cha nthaŵi zonse kuti azindikire kuti kumvera mapulinsipulo aumulungu ndiko maziko a njira yabwino koposa ya moyo.—Yesaya 48:17, 18.

8. Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse mwana kupanduka?

8 China chochititsa kupanduka chingakhale mkhalidwe wa panyumba. Mwachitsanzo, ngati kholo limodzi ndi chidakwa, ngati limagwiritsira ntchito anamgoneka, kapena ngati ndi lachiwawa kwa kholo linalo, kaonedwe ka moyo ka wachinyamata kangapotoke. Ngakhale m’nyumba zimene ziliko pamtendere, mwana angapanduke pamene aona kuti makolo ake samamsamalira. Komabe, si nthaŵi zonse pamene achinyamata amapanduka chifukwa cha zisonkhezero zakunja. Ana ena amafulatira malango a makolo awo mosasamala kanthu za kukhala ndi makolo amene amagwiritsira ntchito mapulinsipulo aumulungu ndi amene amawatetezera, makamaka ku dziko lowazinga. Chifukwa ninji? Mwinamwake chifukwa cha chinthu chinanso chochititsa mavuto athu—kupanda ungwiro kwa anthu. Paulo anati: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Adamu anali wopanduka wadyera, ndipo anasiyira ana ake onse choloŵa cha tsoka. Achichepere ena amangodzifunira kupanduka, monga momwe linachitira kholo lawo lakalero.

ELI WOLEKERERA NDI REHABIAMU WOUMITSA ZINTHU

9. Kodi ndi kupambanitsa kotani polera mwana kumene kungamsonkhezere kupanduka?

9 Chinthu chinanso chimene chimachititsa achinyamata kupanduka ndicho lingaliro losayenera la makolo la kaleredwe ka ana. (Akolose 3:21) Makolo ena odera nkhaŵa amaumitsira zinthu kwambiri ana awo ndi kuwalanga mopambanitsa. Ena ali olekerera, osapereka zitsogozo zofunikira zimene zingatetezere achinyamata awo anthete. Nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeza malo apakati pa mbali ziŵirizo zopambanitsa. Ndipo ana osiyanasiyana amakhala ndi zosoŵa zosiyanasiyana. Wina angafunikire chiyang’aniro chokulira kuposa wina. Komabe, zitsanzo ziŵiri za m’Baibulo zidzathandiza kusonyeza ngozi zake za kuchita mopambanitsa pakuumitsa zinthu kapena pakulekerera.

10. Ngakhale kuti mwachionekere Eli anali mkulu wa ansembe wokhulupirira, kodi nchifukwa ninji anali kholo losachita bwino?

10 Eli, mkulu wa ansembe wa Israyeli wakale anali tate. Anatumikira kwa zaka 40, mosakayikira anali ndi chidziŵitso chachikulu cha Chilamulo cha Mulungu. Mwachionekere, Eli anachita ntchito zake zaunsembe mokhulupirika ndithu ndipo ayenera kuti anaphunzitsa bwino lomwe Chilamulo cha Mulungu kwa ana ake, Hofeni ndi Pinehasi. Komabe, Eli anali wokondera kwambiri kwa ana ake. Hofeni ndi Pinehasi anali ansembe otumikira pazochitika, koma anali amuna “oipa,” okonda chabe kukhutiritsa zokhumba zawo ndi zilakolako zawo zachisembwere. Komabe, pamene anachita zauchisi m’malo opatulika, Eli analephera kulimbika mtima kuti awachotse paudindo wawo. Anangowadzudzula mofeŵa. Mwa kulekerera kwake, Eli analemekeza ana ake kuposa Mulungu. Chotulukapo, ana ake anapanduka pakulambira Yehova koyera ndipo nyumba yonse ya Eli inagwera m’tsoka.—1 Samueli 2:12-17, 22-25, 29; 3:13, 14; 4:11-22.

11. Kodi makolo angatengepo phunziro lanji pa chitsanzo choipa cha Eli?

11 Ana a Eli anali kale achikulire pamene izi zinachitika, koma mbiri yakale imeneyi imasonyeza ngozi ya kulephera kupereka chilango. (Yerekezerani ndi Miyambo 29:21.) Makolo ena angaone monga kulekerera ndiko chikondi, akumalephera kupereka malamulo omvekera bwino, osasintha, ndi anzeru ndi kuona kuti akutsatiridwa. Amanyalanyaza kupereka chilango chachikondi, ngakhale pamene mapulinsipulo aumulungu aswedwa. Chifukwa cha kulekerera kotero, ana awo angaleke kuwopa ulamuliro wa makolo kapena wina uliwonse.—Yerekezerani ndi Mlaliki 8:11.

12. Kodi ndi cholakwa chotani chimene Rehabiamu anachita posonyeza mphamvu yake?

12 Rehabiamu ali chitsanzo cha njira ina yakuchita mopambanitsa ndi ulamuliro. Iye anali mfumu yomaliza ya ufumu wogwirizana wa Israyeli, koma sanali mfumu yabwino. Rehabiamu analoŵa ufumu m’dziko limene anthu ake anali osakhutira chifukwa cha mtolo woikidwa pa iwo ndi atate wake, Solomo. Kodi Rehabiamu anasonyeza chifundo? Ayi. Pamene nthumwi zinampempha kuchepetsako malamulo ena otsendereza, analephera kulabadira uphungu wanzeru wochokera kwa aphungu ake achikulire nalamula kuti goli la anthu lilemetsedwe koposerapo. Kuuma khosi kwake kunabutsa chipanduko cha mafuko khumi akumpoto, ndipo ufumuwo unagaŵanika paŵiri.—1 Mafumu 12:1-21; 2 Mbiri 10:19.

13. Kodi makolo angapeŵe motani kuchita cholakwa cha Rehabiamu?

13 Makolo angatengepo maphunziro ofunika pa nkhani ya m’Baibulo ya Rehabiamu. Amafunikira ‘kufuna Yehova’ m’pemphero ndi kupenda njira zawo zolerera ana mogwirizana ndi mapulinsipulo a Baibulo. (Salmo 105:4) “Nsautso iyalutsa wanzeru,” amatero Mlaliki 7:7. Malire olingaliridwa bwino amapatsa achinyamata omasinkhuka mpata wakukula pamene akuwatetezera ku ngozi. Koma ana sayenera kukhala mumkhalidwe wokhwimitsa kwambiri ndi wopanikiza kwakuti alephera kukulitsa mlingo woyenera wa kudziimira paokha ndi kudzidalira. Pamene makolo ayesa kukhala achikatikati, osapereka ufulu wopambanitsa kapena ziletso zokhwimitsa, achinyamata ambiri sadzakhala ndi chikhoterero cha kupanduka.

KUKWANIRITSA ZOFUNIKA ZAZIKULU KUNGALETSE KUPANDUKA

Chithunzi patsamba 83

Mwachionekere, ana amakula kukhala okhazikika bwino ngati makolo awathandiza kulimbana ndi mavuto apaunyamata

14, 15. Kodi makolo ayenera kuona motani kakulidwe ka mwana wawo?

14 Ngakhale kuti makolo amakondwera kuona mwana wawo akukula mwakuthupi akumakhala wachikulire, iwo angade nkhaŵa pamene mwana wawo womasinkhukayo ayamba kudziimira payekha akumaleka kuwadalira kwambiri. Mkati mwa nyengo yakusintha imeneyi, musadabwe ngati mwana wanu wachinyamata nthaŵi zina akhala wouma khosi kapena wosagwirizana nanu. Kumbukirani kuti cholinga cha makolo achikristu chiyenera kukhala kulera mwana kuti akule ndi kukhala Mkristu wokhwima, wokhazikika, ndi wanzeru.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 13:11; Aefeso 4:13, 14.

15 Ngakhale kuti zingakhale zovuta, makolo amafunikira kuleka chizoloŵezi cha kuyankha mwaukali ku pempho lililonse la mwana womasinkhuka lofuna ufulu wokulirapo. Mwana afunikira kukula mwa njira yabwino monga munthu payekha. Ndithudi, pausinkhu wocheperapo, achinyamata ena amayamba kukhala ndi maganizo achikulire. Mwachitsanzo, Baibulo limanena za Mfumu yachichepere Yosiya kuti: “Akali mnyamata [pafupifupi zaka 15], anayamba kufuna Mulungu wa Davide.” Mwachionekere, wachinyamata wachitsanzo chabwino ameneyu anali ndi nzeru zauchikulire.—2 Mbiri 34:1-3.

16. Pamene ana apatsidwa thayo lowonjezereka, kodi ayenera kudziŵa chiyani?

16 Komabe, ufulu umadza ndi thayo. Chifukwa chake, lolani mwana wanu yemwe akukhwimayo kuyang’anizana ndi zotulukapo za zosankha zake ndi machitidwe ake. Lamulo lakuti, “chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta,” limagwira ntchito kwa achinyamata ndi achikulire omwe. (Agalatiya 6:7) Ana simungawatetezere kosatha. Koma bwanji ngati mwana wanu afuna kuchita chinthu china chosaloleka konse? Monga kholo losamala, muyenera kunena kuti, “Ayi.” Ndipo, pamene kuli kwakuti mungalongosole zifukwa zake, palibe chimene chiyenera kusintha ayi wanu kukhala inde. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:37.) Komabe, yesani kunena “Ayi” wanu mwanjira yofatsa ndi yoyenerera, pakuti “mayankhidwe ofatsa abweza mkwiyo.”—Miyambo 15:1.

17. Kodi ndi zosoŵa zina ziti za wachinyamata zimene kholo liyenera kukwaniritsa?

17 Achichepere amafunikira chitetezero cha chilango cha nthaŵi zonse ngakhale kuti nthaŵi zina samakonda kwenikweni kutsatira ziletso ndi malamulo. Kumakhala kokwiyitsa ngati malamulo amasinthidwa kaŵirikaŵiri, malinga ndi mmene kholo likulingalirira panthaŵiyo. Ndiponso, ngati achinyamata alandira chilimbikitso ndi chithandizo chofunikira, chakuti alimbane ndi manyazi, kapena kupanda chidaliro chaumwini, mwachionekere adzakula ali okhazikika. Achinyamata amayamikiranso pamene makolo awo awadalira.—Yerekezerani ndi Yesaya 35:3, 4; Luka 16:10; 19:17.

18. Kodi pali mfundo zoona zotani zolimbikitsa ponena za achinyamata?

18 Makolo angatonthozedwe podziŵa kuti pamene mtendere, bata, ndi chikondi zilimo m’banja, nthaŵi zonse ana amakula bwino. (Aefeso 4:31, 32; Yakobo 3:17, 18) Inde, achichepere ambiri akula bwino ngakhale kuti analeredwa m’mikhalidwe yoipa, m’mabanja auchidakwa, achiwawa, kapena a zisonkhezero zina zoipa, ndipo akula kukhala achikulire abwino. Chifukwa chake, ngati muchititsa mkhalidwe wapanyumba kukhala wabwino moti ana anu achinyamata akumva kukhala otetezereka ndipo akudziŵa kuti mumawakonda ndi kuwasamalira—ngakhale ngati chichirikizo chimenecho chingatsagane ndi ziletso zoyenerera ndi chilango chogwirizana ndi mapulinsipulo a Malemba—nkothekera kwambiri kuti adzakula ndi kukhala achikulire amene mudzawanyadira.—Yerekezerani ndi Miyambo 27:11.

PAMENE ANA AGWERA M’VUTO

19. Pamene kuli kwakuti makolo ayenera kuphunzitsa mwana njira imene ayenera kuyendamo, kodi ndi thayo lotani limene limakhala pa mwanayo?

19 Kulera ana kwabwino kumathandiza kwambiri. Miyambo 22:6 imati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.” Komabe, bwanji nanga za ana amene amakhala ndi mavuto aakulu mosasamala kanthu kuti ali ndi makolo abwino? Kodi zimenezi nzotheka? Inde. Mawu a mwambo umenewu ayenera kutengedwa pamodzi ndi mavesi ena amene amagogomezera thayo la mwana la ‘kumvera’ makolo ndi kuwalabadira. (Miyambo 1:8) Makolo onse aŵiri limodzi ndi mwanayo ayenera kugwirizana pakugwiritsira ntchito mapulinsipulo a Malemba kuti pakhale chigwirizano cha banja. Ngati makolo ndi ana samagwirizana, padzakhala zovuta.

20. Pamene ana alakwa chifukwa cha kusalingalira bwino, kodi ndi kachitidwe kotani kamene kangakhale koyenera kwa makolo?

20 Kodi makolo ayenera kuchita motani pamene mwana wawo wachinyamata alakwa ndi kugwera m’vuto? Pamenepo, makamaka wachichepereyo afunikira chithandizo. Ngati makolo akumbukira kuti akuchita ndi wachibwana, kudzakhala kosavuta kwambiri kukaniza chikhoterero cha kuchita mopambanitsa. Paulo anapatsa chilangizo anthu okhwima mumpingo kuti: “Ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso.” (Agalatiya 6:1) Makolo angatsatire njira imodzimodziyo pamene achita ndi wachichepere amene alakwa chifukwa cha kusalingalira bwino. Pamene akufotokoza momveka bwino chifukwa chake kachitidwe kake kanali kolakwa ndi mmene angapeŵere kubwerezanso cholakwacho, makolo ayenera kumveketsa bwino kuti chimene anachita ndicho choipa, osati wachichepereyo.—Yerekezerani ndi Yuda 22, 23.

21. Mwa kutsatira chitsanzo cha mpingo wachikristu, kodi makolo ayenera kuchita motani ngati ana awo achita tchimo lalikulu?

21 Bwanji ngati cholakwa cha wachichepereyo nchachikulu kwambiri? Pamenepo mwanayo amafunikira chithandizo chapadera ndi chilangizo chaluso. Pamene munthu amene ali chiŵalo cha mpingo achita tchimo lalikulu, amalimbikitsidwa kulapa ndi kufikira akulu kaamba ka chithandizo. (Yakobo 5:14-16) Pamene alapa, akulu amathandizana naye kuti abwezeretse mkhalidwe wake wauzimu. M’banja, thayo lakuthandiza wachinyamata wolakwa lili la makolo, ngakhale kuti angafunikire kukambitsirana nkhaniyo ndi akulu. Ndithudi, iwo sayenera kuyesa kubisa bungwe la akulu machimo aakulu alionse ochitidwa ndi mmodzi wa ana awo.

22. Mwa kutsanzira Yehova, kodi makolo adzayesa kukhala ndi maganizo otani ngati mwana wawo achita cholakwa chachikulu?

22 Vuto lalikulu loloŵetsamo ana a munthuwe limakhala lopereka chiyeso kwambiri. Pokhala ovutitsidwa maganizo, makolo angafune kuwopseza mwaukali mwana wawo wopandukayo, koma zimenezi angangoipidwa nazo. Kumbukirani kuti mtsogolo mwa wachichepereyo mungadalire panjira imene mumachitira naye panthaŵi yovuta imeneyi. Kumbukiraninso kuti Yehova anali wokonzekera kukhululukira pamene anthu ake anapambuka pachabwino—ngati akanalapa. Tamverani mawu ake achikondi: “Tiyeni, tsono, tiweruzane, ati Yehova; ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.” (Yesaya 1:18) Nchitsanzo chabwino chotani nanga kwa makolo!

23. Ngati mmodzi wa ana awo wachita tchimo lalikulu, kodi makolo ayenera kuchita motani, ndipo ayenera kupeŵanji?

23 Chotero, yesani kulimbikitsa mwana wopandukayo kusintha njira yake. Funani uphungu wanzeru kwa makolo achidziŵitso ndi akulu a mpingo. (Miyambo 11:14) Yesani kusachita mwasontho ndi kunena kapena kuchita zinthu zimene zidzakuchititsa kukhala kovuta kwa mwana wanu kubwerera kwa inu. Peŵani mkwiyo ndi kuipidwa kosalamulirika. (Akolose 3:8) Musataye mtima ndi kuleka mofulumira. (1 Akorinto 13:4, 7) Pamene kuli kwakuti mumadana nacho choipa, peŵani kukhala wouma mtima ndi kuipidwa ndi mwana wanu. Chofunika koposa, makolo ayenera kuyesayesa kupereka chitsanzo chabwino ndi kusunga chikhulupiriro cholimba mwa Mulungu.

KUCHITA NDI WOPANDUKA WENIWENI

24. Kodi ndi mkhalidwe womvetsa chisoni wotani umene nthaŵi zina umakhalapo m’banja lachikristu, ndipo kholo liyenera kuchita motani?

24 Nthaŵi zina kumakhala koonekeratu kuti wachichepere watsimikiza mtima kupanduka ndi kukaniratu makhalidwe achikristu. Pamenepo muyenera kutembenuzira chisamaliro chanu pa kusunga kapena kumangirira moyo wa banja wa otsalawo. Samalani kuti musapereke maganizo anu onse kwa wopandukayo, ndi kunyalanyaza ana enawo. M’malo mwakuyesa kubisa vutolo kwa ena m’banja, kambitsiranani nawo nkhaniyo pamlingo woyenera ndi mwanjira yolimbikitsa.—Yerekezerani ndi Miyambo 20:18.

25. (a) Mwa kutsatira chitsanzo cha mpingo wachikristu, kodi makolo ayenera kuchitanji ngati mwana akhala wopanduka weniweni? (b) Kodi makolo ayenera kukumbukiranji ngati mmodzi wa ana awo apanduka?

25 Mtumwi Yohane anati ponena za munthu amene akhala wopanduka wosabwezeka mumpingo: “Musamlandire iye kunyumba, ndipo musamlankhule.” (2 Yohane 10) Makolo angakuone kukhala kofunikira kuchita zimenezo kwa mwana wawowawo ngati ali wamkulu ndipo ali wopandukiratu. Ngakhale kuti kachitidweko kangakhale kovuta ndi kosautsa maganizo, nthaŵi zina kali kofunika kuti enawo m’banja atetezereke. Muyenera kutetezera ndi kuyang’anira banja lanu nthaŵi zonse. Chifukwa chake, pitirizani kusunga malire a makhalidwe omvekera bwino ndi otsimikizika, komabe oyenerera. Lankhulanani ndi ana enawo. Khalani ndi chidwi cha kufuna kudziŵa mmene akuchitira kusukulu ndi mumpingo. Ndiponso, achititseni kudziŵa kuti ngakhale kuti simukuvomereza machitidwe a mwana wopandukayo, simukumuda iye. Danani ndi mchitidwe woipa osati mwanayo. Pamene ana aŵiri a Yakobo anadzetsa temberero pabanja chifukwa cha mchitidwe wawo wankhalwe, Yakobo anatemberera mkwiyo wawo wachiwawa, osati ana enieniwo.—Genesis 34:1-31; 49:5-7.

26. Kodi makolo oona mtima angapeze kuti chitonthozo ngati mmodzi wa ana awo apanduka?

26 Mungamve kukhala wamlandu pa zimene zachitika pabanja. Koma ngati mwapemphero mwachita zonse zomwe mukanakhoza, mwa kutsatira uphungu wa Yehova bwino lomwe, simufunikira kudziimba mlandu mopambanitsa. Pezani chitonthozo mwa kudziŵa kuti palibe aliyense amene angakhale kholo langwiro, koma inuyo munayesetsa moona mtima kukhala kholo labwino. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:26.) Kukhala ndi wopanduka weniweni m’banja nkopweteka mtima kwambiri, koma ngati zichitika kwa inu, khalani wotsimikiza kuti Mulungu amamvetsetsa ndipo sadzasiya konse atumiki ake okhulupirika. (Salmo 27:10) Chotero yesetsani kuchititsa nyumba yanu kukhala malo achitetezo chauzimu kwa ana alionse otsalawo.

27. Pokumbukira fanizo la mwana woloŵerera, kodi makolo a mwana wopanduka ayenera kukhala ndi chiyembekezo cha chiyani nthaŵi zonse?

27 Ndiponso, simuyenera konse kutaya chiyembekezo. Zoyesayesa zanu zoyambirira zakuphunzitsa koyenera m’kupita kwa nthaŵi zingakhudze mtima wa mwana woloŵererayo ndi kumchititsa kulingaliranso bwino. (Mlaliki 11:6) Mabanja achikristu ambiri akhala ndi chokumana nacho monga chanu, ndipo ena aona ana awo opanduka akubwerera, mofanana kwambiri ndi tate uja wa m’fanizo la Yesu la mwana woloŵerera. (Luka 15:11-32) Zimenezi zingachitikenso kwa inu.

KODI MAPULINSIPULO A BAIBULO AŴA ANGATHANDIZE MOTANI . . . KHOLO KULETSA CHIPANDUKO CHACHIKULU M’BANJA?

Popanda chithandizo, mwana angawonongedwe ndi mzimu wa dziko.—Miyambo 13:20; Aefeso 2:2.

Makolo amafunikira kukhala osapambanitsa pakuika ziletso kapena pakulekerera.—Mlaliki 7:7; 8:11.

Mchitidwe wolakwa uyenera kusamaliridwa, koma mwa mzimu wa chifatso.—Agalatiya 6:1.

Awo amene amachita machimo aakulu ‘angachiritsidwe’ ngati alapa ndi kulandira chithandizo.—Yakobo 5:14-16.

ULULANI ZAKUKHOSI

Achinyamata omasinkhuka amakhala ndi zikayikiro ndi nkhaŵa zimene zimadza ndi ufulu wowonjezereka. Angakayikire za kukhoza kwawo kuima paokha m’dziko lino. Zili monga kuti anali kuyesa kuyenda pamsewu woterera. Inu achichepere, ululirani makolo anu zimene mumaopa ndi nkhaŵa zanu zimene muli nazo. (Miyambo 23:22) Kapena ngati mulingalira kuti makolo anu akukupanikizani kwambiri, lankhulani nawo za kufunika kwanu kupatsidwa ufulu wokulirapo. Linganizani kulankhula nawo panthaŵi imene muli womasuka bwino ndipo iwo sali otanganitsidwa. (Miyambo 15:23) Tcherani khutu bwinobwino kwa wina ndi mnzake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena