Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • jt tsamba 22-24
  • Phindu Lenileni la Uthenga Wabwino M’dera Lakwanu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phindu Lenileni la Uthenga Wabwino M’dera Lakwanu
  • Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
  • Nkhani Yofanana
  • Yendani Motsatira Mfundo za Makhalidwe Abwino za Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Mboni za Yehova
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!
    Galamukani!—1990
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokwatirana ndi Munthu wa Mtundu Wina
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Mboni za Yehova—Kodi Iwo Ndani? Kodi Amakhulupirira Chiyani?
jt tsamba 22-24

Phindu Lenileni la Uthenga Wabwino M’dera Lakwanu

M’DZIKO lerolino kaŵirikaŵiri timamva maganizo akuti: “Makhalidwe achikristu si othandiza. N’ngosatheka m’dziko lovuta lamasiku ano.” Komabe, m’kukambirana kwina pakati pa mtsogoleri wachihindu Mohandas K. Gandhi ndi kazembe wa Britain ku India, Lord Irwin, panatchulidwa malingaliro osiyana kwambiri ndi zimenezo. Akuti Lord Irwin anafunsa Gandhi za chimene anali kuganiza kuti chingathetse mavuto pakati pa Great Britain ndi India. Gandhi ananyamula Baibulo ndi kutsegula pa chaputala faifi cha Mateyu ndi kunena kuti: “Pamene dziko lako ndi langa angagwirizane pa ziphunzitso zoperekedwa ndi Kristu mu ulaliki uwu wa pa Phiri, tidzathetsa mavuto osati a mayiko athu okha koma a dziko lonse lapansi.”

Ulaliki umenewo umanena za kufunafuna moyo wauzimu ndi kukhala wodekha, wamtendere, wokonda chilungamo. Umatsutsa umbanda komanso kukwiyirana wina ndi mnzake, chigololo limodzinso ndi maganizo a chilakolako chonyansa. Umadzudzula kusudzulana kosayenerera kumene kumathetsa mabanja ndi kuvutitsa ana. Umatiuza kuti: ‘Kondani ngakhale adani anu, patsani osoŵa, musaweruzane mosamverana chifundo, chitirani ena zimene mukafuna kuti iwo akuchitireni.’ Ngati uphungu wonsewu ungagwiritsidwe ntchito, pangakhale mapindu osaneneka. Ngati anthu ochuluka m’dera lakwanu angaugwiritse ntchito, dera lanu lingakhale labata ndi lamtendere!

A Mboni za Yehova amathandiza kwambiri kulimbikitsa mkhalidwe umenewu. Baibulo limawaphunzitsa kulemekeza ukwati. Amaphunzitsa ana awo mfundo za chikhalidwe choyenera. Amalimbikitsa za kufunika kwa banja. Mabanja ogwirizana ali dalitso m’dera lakwanu, ngakhale ku dziko lanu. Mbiri yakale ili ndi zitsanzo zambiri za maboma amphamvu padziko lonse amene anagwa chifukwa chakuti mabanja awo anafooka ndipo zachiwerewere zinachuluka. Pamene Mboni za Yehova zithandiza anthu ambiri ndi mabanja kutsata mfundo za chikhalidwe chachikristu, kupulupudza, zachiwerewere ndi zaupandu zidzachepa m’dera lanu.

Vuto lina lalikulu kwambiri m’madera ndi mayiko ambiri ndilo kusankhana mitundu. Motsutsa zimenezo, mtumwi Petro ananena kuti: “Zoona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” Ndipo Paulo analemba kuti: “Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.” (Machitidwe 10:34, 35; Agalatiya 3:28) Mboni za Yehova zimavomereza zimenezi. Anthu a mafuko onse komanso osiyanasiyana khungu amagwira ntchito pamodzi ku likulu lawo la padziko lonse, m’maofesi a nthambi, ndi m’mipingo yawo.

Mu Africa mitundu ina singathe kukhalira limodzi popanda kumenyana. Komabe, pamisonkhano ya Mboni za Yehova, anthu a mitundu yosiyanasiyana amadyera limodzi, kugonera limodzi, ndi kulambirira limodzi mogwirizana ndi mtima wonse komanso mwa ubwenzi weniweni. Akuluakulu a boma adabwa poona zimenezi. Chitsanzo cha mphamvu yakugwirizanitsa ya Chikristu choona chinatchulidwa ndi maganizi yotchedwa Amsterdam News ya ku New York, ya pa August 2, 1958. Ndemangayo inakhalapo poona zochitika za pa msonkhano wa mayiko umene watchulidwa m’mutu wina wam’mbuyomu kumene Mboni zopitirira kota ya miliyoni zinasonkhana mu mzinda wotchedwa New York City.

“Paliponse Akuda, Oyera ndi Amwenye, osauka ndi olemera ndi ochokera ku mbali zonse za dziko lapansi, anayanjana mosangalala ndi momasuka. .  . . Mboni zimene zinali kulambirazo zochokera kumayiko 120 zinakhalira pamodzi ndi kulambira pamodzi mwamtendere, ndipo zaonetsa nzika za America kuti zimenezo n’zotheka mosavuta. .  . . Msonkhanowu ndi chitsanzo chochititsa chidwi choonetsa mmene anthu angagwirire ntchito pamodzi ndi kukhalira limodzi.”

Ambiri anganene kuti makhalidwe achikristu n’ngosathandiza m’dziko lino lamakono. Komabe, kodi zimene zakhala zothandiza kapena zimene zidzathandiza ndiye ziti? Makhalidwe achikristu akhoza kukhala a phindu lenileni ngati agwiritsidwa ntchito m’dera lanu tsopano, ndipo adzakhala maziko ogwirizanitsira ‘mitundu yonse, mafuko, ndi anthu’ padziko lonse lapansi mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu pa anthu onse.—Chivumbulutso 7:9, 10.

[Mawu otsindika patsamba 23]

Anthu a mafuko onse komanso osiyanasiyana khungu amagwira ntchito pamodzi

[Mawu otsindika patsamba 24]

Moyo wachikristu n’ngwothandiza. Kodi palinso china chimene chakhala chopindulitsa kuposa apa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena