Chitsanzo Chabwino—Asafu
M’nthawi ya Asafu, anthu ambiri sankamvera malamulo a Mulungu ndipo ankaoneka kuti zinthu zikuwayendera bwino. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri pamoyo wa Asafu, ndipo iye anakayikira ngati kuyesetsa kumvera malamulo a Mulungu kunalidi kopindulitsa. Iye anafika ponena kuti: “Indedi, ndinayeretsa mtima wanga kwachabe, ndipo ndinasamba m’manja mosalakwa.” Komabe, Asafu ataiganizira mofatsa nkhaniyi, anasintha maganizo ake. Iye anazindikira kuti chisangalalo chilichonse chimene anthu oipa amakhala nacho sichikhalitsa. Kodi iye anati chiyani atazindikira zimenezi? Kudzera m’nyimbo, Asafu anauza Yehova kuti: “Padziko lapansi palibe wina wondikonda koma Inu.”—Salmo 73:3, 13, 16, 25, 27.
Mwina nanunso nthawi ina munakayikirapo ngati kutsatira malangizo a m’Baibulo n’kopindulitsa. Tsatirani chitsanzo cha Asafu amene anaona zinthu mwanzeru. Ganizirani za anthu amene amanyalanyaza malamulo a Yehova. Kodi iwo alidi ndi mtendere? Kapena kodi iwo apeza chimwemwe chimene atumiki okhulupirika a Mulungu sakuchipeza? Mukaganizira nkhani imeneyi mwanzeru, mudzagwirizana ndi zimene Asafu ananena kuti: “Ine, kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.”—Salmo 73:28.