Nyimbo 104
Tiyeni Tonse Titamande Ya
Losindikizidwa
1. Titamande
Ya momveka.
Amatipatsa zonse zabwino.
Titamande
Dzina lake.
Ndi wachikondi, n’ngwamphamvu zonse
Ndipo dzina lake tilengeze.
2. Titamande
Ya chifukwa
Amatimva tikamapemphera.
Dzanja lake
Ndi lamphamvu.
Amalimbikitsa ofooka.
Za mphamvu zake timalengeza.
3. Titamande
Ya mokondwa.
N’ngolungama ndi wodalirika.
Adzakonza
Zolakwika
Ndipo anthu adzadalitsidwa.
Timutamande mosangalala.
(Onaninso Sal. 94:18, 19; 145:21; 147:1; 150:2.)