Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 18 tsamba 21
  • Yesu Ankachita Zozizwitsa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Ankachita Zozizwitsa
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi pa Zozizwitsa za Yesu Mungaphunzirepo Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2004
  • “Khristu Ndi Mphamvu ya Mulungu”
    Yandikirani Yehova
  • Kodi Tingaphunzire Chiyani pa Zozizwitsa za Yesu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kodi Zozizwitsa Zimachitikadi Kapena Ayi?
    Nsanja ya Olonda—2005
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 18 tsamba 21
Yesu wagwira maso a munthu wakhungu ndipo akumuchiritsa

GAWO 18

Yesu Ankachita Zozizwitsa

Zozizwitsa zimene Yesu ankachita zinasonyeza mmene adzagwiritsire ntchito mphamvu zake monga Mfumu

MULUNGU anapatsa Yesu mphamvu kuti azichita zinthu zimene anthu ena sangachite. Yesu anachita zozizwitsa zambirimbiri, ndipo kawirikawiri ankazichita anthu ambiri akuonerera. Zozizwitsa zimenezo zinasonyeza kuti Yesu ali ndi mphamvu zogonjetsera adani ndiponso kuthetsa mavuto onse amene anthu opanda ungwiro amalephera kuwathetsa. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Yesu anadyetsa anthu. Pa chozizwitsa chake choyamba, Yesu anasandutsa madzi kukhala vinyo wabwino. Pa nthawi zinanso ziwiri iye anadyetsa anthu ambirimbiri ndi mitanda yochepa ya mkate komanso nsomba zochepa. Pa nthawi zonsezi aliyense anadya ndipo anakhuta.

Yesu anachiritsa anthu odwala. Yesu anachiritsa anthu amene anali ndi “matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.” (Mateyu 4:23) Iye anachiritsa anthu akhungu, ogontha, akhate, akhunyu komanso olumala. Panalibe matenda aliwonse amene analephera kuwachiritsa.

Yesu analetsa mphepo yamkuntho. Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankawoloka nyanja ya Galileya pangalawa, panyanjapo panayamba mphepo yamkuntho ndipo ophunzirawo anachita mantha kwambiri. Koma Yesu anangoyang’ana mphepo yamkunthoyo n’kunena kuti: “Leka! Khala bata!” Atatero mphepoyo inaleka ndipo panachita bata lalikulu. (Maliko 4:37-39) Pa nthawi inanso, Yesu anayenda pamadzi amene ankachita mafunde akuluakulu chifukwa cha mphepo yamphamvu.—Mateyu 14:24-33.

Yesu anatulutsa mizimu yoipa. Mizimu yoipa ndi yamphamvu kwambiri kuposa anthu. Anthu ambiri alephera kumasuka ku mizimu yoipayi yomwe ndi adani a Mulungu. Koma nthawi zingapo, Yesu anailamula kuti ituluke mwa anthu, ndipo inatulukadi. Iye sankaopa mizimu imeneyo. Koma mizimuyo inkadziwa mphamvu zimene iye ali nazo ndipo inkamuopa.

Yesu anaukitsa akufa. Moyenerera, imfa imatchedwa “mdani womalizira” ndipo palibe munthu amene angaigonjetse. (1 Akorinto 15:26) Koma Yesu anaukitsa anthu akufa. Mwachitsanzo, anaukitsa mnyamata wina ndi kumupereka kwa mayi ake amene anali amasiye, komanso anaukitsa mtsikana wamng’ono ndi kumupereka kwa makolo ake amene anali ndi chisoni kwambiri. Pa nthawi ina, Yesu anachita zinthu zosaiwalika. Iye anaukitsa mnzake wapamtima Lazaro pamaso pa khamu la anthu amene ankalira maliro a Lazaroyo. Iye anachita zimenezi ngakhale kuti panapita masiku anayi kuchokera pamene anamwalira. Ngakhale adani enieni a Yesu, anavomereza kuti iye anachitadi chozizwitsa chimenechi.—Yohane 11:38-48; 12:9-11.

N’chifukwa chiyani Yesu anachita zozizwitsa zonsezi? N’zoona kuti anthu onse amene anawathandizawo anafabe patapita nthawi, koma zozizwitsa zimene Yesu ankachita n’zothandiza kwambiri. Zinasonyeza kuti maulosi onse osangalatsa okhudza Ufumu wa Mesiya adzakwaniritsidwadi. Sitingakayikire n’komwe kuti Mfumu yoikidwa ndi Mulungu imeneyi idzathetsa njala, matenda, masoka achilengedwe komanso kugonjetsa mizimu yoipa ngakhalenso imfa. Yesu anasonyeza kale kuti Mulungu anam’patsa mphamvu zochitira zinthu zimenezi.

​—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane.

  • Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ali ndi mphamvu pa zinthu zotsatirazi: Njala, matenda, mphepo yamkuntho, mizimu yoipa ndiponso imfa?

  • Kodi zozizwitsa za Yesu zinasonyeza kuti adzachita chiyani m’tsogolo pamene azidzalamulira dziko lapansi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena