Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 21 tsamba 24
  • Yesu Anaukitsidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Anaukitsidwa
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Atumwi Ankalalikira Mopanda Mantha
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Mulungu Anakumbukira Mwana Wake
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Yesu Anaukitsidwa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yesu Analosera Zinthu za M’tsogolo Zimene Zidzakhudze Dziko Lonse
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 21 tsamba 24
Yesu akupita kumwamba

GAWO 21

Yesu Anaukitsidwa

Yesu anaonekera kwa otsatira ake ndipo anawaphunzitsa ndi kuwalimbikitsa

TSIKU lachitatu Yesu atamwalira, azimayi ena amene anali ophunzira ake anapeza mwala umene anatsekera manda ake utagubuduzidwa ndipo m’mandamo munalibe kanthu.

Ndiyeno panaonekera angelo awiri ndipo mmodzi wa iwo ananena kuti: “Ndikudziwa kuti mukufuna Yesu Mnazareti, . . . Iyetu wauka kwa akufa.” (Maliko 16:6) Nthawi yomweyo, azimayiwo anathamanga kukauza atumwi. Ali m’njira anakumana ndi Yesu ndipo anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga, kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.”—Mateyu 28:10.

Nthawi ina tsiku lomwelo, ophunzira ena awiri anali paulendo wopita ku Emau kuchokera ku Yerusalemu. Munthu wina amene sanamudziwe anayamba kuyenda nawo limodzi ndipo anawafunsa zimene ankakambirana. Munthuyo anali Yesu amene anali ataukitsidwa ndipo anaonekera kwa iwo m’njira yoti asamuzindikire. Iwo anayankha mwachisoni kuti akukambirana za Yesu. Munthu wachilendoyo anayamba kuwafotokozera zinthu za m’Malemba onse zokhudza Mesiya. Indedi Yesu anakwaniritsa maulosi onse okhudza Mesiya.a Ophunzirawo atazindikira kuti munthu wachilendoyo ndi Yesu, amene anali ataukitsidwa ndi thupi lauzimu, Yesu sanaonekenso.

Nthawi yomweyo ophunzira awiriwo anabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anapeza atumwi atasonkhana m’nyumba ndipo chitseko chinali chokhoma. Pamene ophunzira awiriwo ankafotokoza zimene anaona, Yesu anaonekera, moti otsatira akewo anali odabwa kwambiri ndipo sanakhulupirire. Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mukukayikakayika m’mitima yanu?” Kenako ananena kuti: “Ndi mmene zinalembedwera kuti Khristu adzazunzika ndi kuuka kwa akufa tsiku lachitatu.”—Luka 24:38, 46.

Kwa masiku 40 kuchokera pamene anaukitsidwa, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake nthawi zosiyanasiyana. Pa nthawi ina iye anaonekera kwa anthu oposa 500. Zikuoneka kuti pa nthawiyi m’pamene anawapatsa ntchito yofunika kwambiri pamene anawauza kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. . . . Ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mateyu 28:19, 20.

Atakumana komaliza ndi ophunzira 11 okhulupirikawo, Yesu anawalonjeza kuti: “Mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Machitidwe 1:8) Kenako Yesu anayamba kukwera kumwamba, ndipo mitambo inamuphimba moti sanaonekenso.

​—Nkhaniyi yachokera pa Mateyu chaputala 28, Maliko chaputala 16, Luka chaputala 24, Yohane chaputala 20 ndi 21; komanso pa 1 Akorinto 15:5, 6.

a Kuti muone zitsanzo za maulosi okhudza Mesiya amene Yesu anakwaniritsa, onani masamba 17 mpaka 19 a kabuku kano, komanso onani buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa, tsamba 209.

  • Kodi ophunzira a Yesu anadziwa bwanji kuti Yesu waukitsidwa?

  • Kodi Yesu anawafotokozera chiyani ophunzira ake awiri amene anakumana nawo pamsewu wopita ku Emau?

  • Kodi Yesu anapereka malangizo otani kwa ophunzira ake iye atatsala pang’ono kupita kumwamba?

MZIMU WOYERA

Mzimu woyera wa Mulungu ndi wamphamvu kwambiri kuposa china chilichonse m’chilengedwe chonse. Yehova Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu wake, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito, polenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso potsogolera ntchito yolemba Baibulo. Zozizwitsa zonse zimene takambirana m’kabuku kano zinachitika chifukwa cha mzimu umenewu. Zimenezi zikuphatikizapo chozizwitsa chachikulu kwambiri pa zonse, chomwe ndi kuukitsidwa kwa Yesu Khristu kuti akhale cholengedwa chauzimu champhamvu kwambiri.—Genesis 1:2; 2 Samueli 23:2; Machitidwe 10:38; 1 Petulo 3:18.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena