Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bm gawo 24 tsamba 27-28
  • Paulo Analemba Makalata Opita Kumipingo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Paulo Analemba Makalata Opita Kumipingo
  • Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Nkhani Yofanana
  • Malangizo Okhudza Kukhala ndi Chikhulupiriro, Makhalidwe Abwino Ndiponso Chikondi
    Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
  • Timoteo—‘Mwana Weniweni m’Chikhulupiriro’
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Paulo m’Roma
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Kugwirizana kwa Baibulo Lonse
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Kodi Baibulo Lili Ndi Uthenga Wotani?
bm gawo 24 tsamba 27-28
Under house arrest, Paul dictates a letter

GAWO 24

Paulo Analemba Makalata Opita Kumipingo

Makalata amene Paulo analemba analimbikitsa mipingo yachikhristu

MPINGO wachikhristu umene unali utangokhazikitsidwa kumene, unali ndi udindo waukulu kwambiri wokwaniritsa cholinga cha Yehova. Koma pasanapite nthawi, Akhristu a m’nthawi ya atumwi anayamba kuzunzidwa. Kodi iwo akanapitirizabe kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika ngakhale kuti ankazunzidwa ndi adani awo komanso ankakumana ndi mavuto ena mumpingo momwemo? M’Malemba Achigiriki muli makalata 21 omwe ali ndi malangizo othandiza komanso mfundo zolimbikitsa.

Mtumwi Paulo ndi amene analemba makalata 14 mwa makalata onse 21, kuyambira pa Aroma mpaka pa Aheberi. Makalata amenewa ali ndi mayina a anthu kapena mipingo imene ankailembera. Tiyeni tione nkhani zina zimene zili m’makalata a Paulo amenewa.

Malangizo othandiza kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino. Anthu amene amachita dama, chigololo ndiponso machimo ena akuluakulu “sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.” (Agalatiya 5:19-21; 1 Akorinto 6:9-11) Anthu amene amalambira Mulungu ayenera kukhala ogwirizana ngakhale atakhala osiyana dziko limene akuchokera. (Aroma 2:11; Aefeso 4:1-6) Akhristu ayenera kudzipereka pothandiza Akhristu anzawo amene akufunikira thandizo. (2 Akorinto 9:7) Paulo anati: “Muzipemphera mosalekeza.” N’zoonadi, anthu amene amalambira Mulungu akulimbikitsidwa kuti azipemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima. (1 Atesalonika 5:17; 2 Atesalonika 3:1; Afilipi 4:6, 7) Kuti Mulungu azimva mapemphero athu, tiyenera kukhala ndi chikhulupiriro.—Aheberi 11:6.

Kodi n’chiyani chingathandize kuti mabanja aziyenda bwino? Amuna ayenera kukonda akazi awo ngati mmene amakondera thupi lawo. Akazinso ayenera kulemekeza kwambiri amuna awo. Ana nawonso ayenera kumvera makolo awo, chifukwa zimenezi zimasangalatsa Mulungu. Makolo ayenera kulangiza ndi kuphunzitsa ana awo mwachikondi, pogwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu.—Aefeso 5:22–6:4; Akolose 3:18-21.

Mapu a malo amene Paulo anali pamene ankalemba makalata ake

Akhristu anathandizidwa kuti amvetse cholinga cha Mulungu. Mbali zambiri za Chilamulo cha Mose zinkateteza Aisiraeli ndiponso kuwapatsa malangizo kufikira nthawi imene Khristu anabwera. (Agalatiya 3:24) Komabe, Akhristu sachita kufunikira kuti azitsatira Chilamulo polambira Mulungu. M’kalata imene analembera Aheberi kapena kuti Akhristu achiyuda, Paulo anawathandiza kumvetsa cholinga cha Chilamulo ndiponso mmene Khristu anakwaniritsira cholinga cha Mulungu. Paulo anafotokoza kuti zinthu zosiyanasiyana zimene zinkachitika potsatira Chilamulo zinali zaulosi. Mwachitsanzo, nyama zimene ankapereka nsembe zinkaimira Yesu amene anapereka moyo wake monga nsembe, imene inathandiza kuti machimo athu azikhululukidwa. (Aheberi 10:1-4) Pogwiritsa ntchito imfa ya Yesu, Mulungu anafafaniza pangano la Chilamulo chifukwa silinalinso lofunika.—Akolose 2:13-17; Aheberi 8:13.

Malangizo othandiza kuti mpingo uziyenda bwino. Amuna amene amafuna kukhala ndi udindo mumpingo ayenera kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kukwaniritsa zowayenereza za m’Malemba. (1 Timoteyo 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Anthu amene amalambira Yehova Mulungu amafunika kusonkhana pamodzi ndi Akhristu anzawo nthawi zonse kuti azilimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Misonkhano yolambira Mulungu iyenera kukhala yolimbikitsa ndiponso yophunzitsa.—1 Akorinto 14:26, 31.

Pa nthawi imene Paulo analembera Timoteyo kalata yachiwiri, mtumwiyu anali atabwerera ku Roma. Pa nthawiyi iye anali m’ndende, kudikirira kuti aweruzidwe. Anthu ochepa chabe ndi amene analimba mtima kukamuona. Paulo anadziwa kuti watsala pang’ono kufa. Iye anati: “Ndamenya nkhondo yabwino. Ndathamanga panjirayo mpaka pa mapeto pake. Ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteyo 4:7) Zikuoneka kuti patangopita nthawi yochepa atalemba kalatayi, Paulo anaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chake. Koma makalata amene mtumwiyu analemba, amathandizabe anthu amene amalambira Mulungu m’njira yoyenera mpaka pano.

​—Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Aroma; 1 Akorinto; 2 Akorinto; Agalatiya; Aefeso; Afilipi; Akolose; 1 Atesalonika; 2 Atesalonika; 1 Timoteyo; 2 Timoteyo; Tito; Filimoni; Aheberi.

  • Kodi m’makalata a Paulo muli malangizo otani othandiza munthu kuti akhale ndi makhalidwe abwino?

  • Kodi Paulo anathandiza bwanji anthu kumvetsa mmene Mulungu adzakwaniritsire cholinga chake kudzera mwa Yesu?

  • Kodi Paulo anapereka malangizo ati othandiza kuti mpingo uziyenda bwino?

KODI MBEWU YOLONJEZEDWA NDANI?

Adamu ndi Hava atachimwa, Mulungu anagwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa pamene anauza njoka kuti: “Ndidzaika chidani pakati pa iwe ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake. Mbewu ya mkaziyo idzaphwanya mutu wako, ndipo iwe udzaivulaza chidendene.” (Genesis 3:15) Malemba amasonyeza kuti Mdyerekezi ndi “njoka yakale.” (Chivumbulutso 12:9) Mbewu yolonjezedwa, kapena kuti Mpulumutsi amene Mulungu analonjeza, sinkadziwika chifukwa chinali chinsinsi, ndipo chinsinsi chimenechi chinaululidwa pang’onopang’ono m’Baibulo kwa zaka zambiri.

Patapita zaka pafupifupi 2,000 Adamu ndi Hava atachimwa, Yehova anasonyeza kuti Mbewu yolonjezedwayo idzabadwira m’banja la Abulahamu. (Genesis 22:17, 18) Patapita zaka zambirimbiri, mtumwi Paulo ananena kuti mbali yoyamba ya Mbewuyo ndi Mesiya, yemwe ndi Yesu Khristu. (Agalatiya 3:16) Mogwirizana ndi lemba la Genesis 3:15, mophiphiritsa Yesu anavulazidwa “chidendene” pamene anaphedwa. Komabe, Mulungu anaukitsa Yesu “monga mzimu.”—1 Petulo 3:18.

Mulungu anakonza zoti anthu 144,000 akhale mbali yachiwiri ya mbewuyo. (Agalatiya 3:29; Chivumbulutso 14:1) Anthu amenewa akamwalira, amaukitsidwa ndi moyo wauzimu kuti akalamulire limodzi ndi Khristu mu Ufumu wakumwamba.—Aroma 8:16, 17.

Monga Mfumu yamphamvu kumwamba, Yesu posachedwapa adzawononga Mdyerekezi ndi mbewu yake, yomwe ndi ziwanda ndiponso anthu onse oipa amene amamutsatira. (Yohane 8:44; Aefeso 6:12) Ulamuliro wa Yesu udzabweretsa mtendere ndiponso moyo wosangalatsa kwa anthu onse omvera Mulungu. Kenako Yesu adzaphwanya “mutu” wa njoka, kutanthauza kuti adzawonongeratu Mdyerekezi.—Aheberi 2:14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena