Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 14 tsamba 30-31
  • Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Ndinu Wokhulupirika kwa Yehova?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Ndinu Wokhulupirika kwa Yehova?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chigawo 14
    Mverani Mulungu
  • Kodi Ndidzipereke kwa Yehova Ndiponso Kubatizidwa?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Chimene Muyenera Kuchita Kuchita kuti Mukhale ndi Moyo Kosatha
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Chikondi Cha Mulungu Sichimatha
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 14 tsamba 30-31

CHIGAWO 14

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Ndinu Wokhulupirika kwa Yehova?

Khalani kumbali ya Mulungu. 1 Petulo 5:6-9

Mkhristu akukana kupembedza konyenga komanso akukana kulowerera zochitika zandale

Muzipewa kuchita nawo miyambo yosagwirizana ndi Baibulo. Munthu amafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi.

Musamachite nawo ndale zadzikoli chifukwa sizigwirizana ndi zofuna za Yehova ndi Ufumu wake.

  • Yehova amateteza anthu okhulupirika kwa iye.​—Salimo 97:10.

Sankhani mwanzeru, mverani Mulungu. Mateyu 7:24, 25

Bambo wina wafika ku misonkhano ku Nyumba ya Ufumu komanso Wayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova

Muzipita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo iwo adzakuthandizani kuti muyandikire Mulungu.

Pitirizani kuphunzira za Mulungu ndipo muziyesetsa kumvera malamulo ake.

Akupereka pemphero losonyeza kuti wadzipereka kwa Yehova kenako akubatizidwa

Chikhulupiriro chanu chikalimba, muyenera kupereka moyo wanu kwa Yehova ndi kubatizidwa.​—Mateyu 28:19.

Muzimvera Mulungu. Muziwerenga Baibulo, ndipo pemphani aliyense wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kulimvetsa. Kenako, muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo. Mukamachita zimenezi mudzapeza moyo wosatha.​—Salimo 37:29.

  • Lapani kuti machimo anu akhululukidwe.​—Machitidwe 3:19.

  • Yendani pa msewu wopita ku moyo wosatha.​—Mateyu 7:13, 14.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena