Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 5 tsamba 12-13
  • Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Chingalawa cha Nowa
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Chigawo 5
    Mverani Mulungu
  • Nowa Akhoma Chingalawa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • “Anayenda Ndi Mulungu Woona”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 5 tsamba 12-13

CHIGAWO 5

Chigumula Chisanachitike, Kodi Ndani Anamvera Mulungu Ndipo Ndani Amene Sanamumvere?

Anthu ambiri m’nthawi ya Nowa ankachita zinthu zoipa. Genesis 6:5

Angelo oipa avala matupi a anthu n’kumakwatira akazi

Adamu ndi Hava anabereka ana, ndipo anthu anachuluka padziko lapansi. Patapita nthawi, angelo ena anagwirizana ndi Satana n’kugalukira Mulungu.

Angelowo anabwera padziko lapansi n’kuvala matupi a anthu n’cholinga choti akwatire akazi. Akaziwo anabereka ana achilendo amene anali oopsa ndiponso amphamvu.

Mayi wanyamula mwana koma mnyamata wina akuwamenya. Ana a angelo oipawo anali anefili ndipo ankachita nkhanza

Dziko linadzaza ndi anthu ochita zoipa. Baibulo limati, ‘kuipa kwa anthu kunachuluka padziko lapansi, ndipo malingaliro onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.’

Nowa anamvera Mulungu ndipo anapanga chingalawa. Genesis 6:13, 14, 18, 19, 22

Nowa anamvera Mulungu

Nowa anali munthu wabwino ndipo Yehova anamuuza kuti awononga anthu oipa ndi chigumula.

Nowa ndi banja lake akupanga chingalawa

Mulungu anauzanso Nowa kuti apange chingalawa chachikulu kuti iye ndi banja lake pamodzi ndi nyama za mtundu uliwonse alowemo.

Nowa akuchenjeza anthu za Chigumula koma anthuwo akumuseka

Nowa anachenjeza anthu kuti kukubwera Chigumula, koma anthuwo sanamvere. Ena ankamuseka ndipo ena ankadana naye.

Nowa ndi banja lake akulowetsa nyama m’chingalawa

Nowa atamaliza kupanga chingalawacho, analowetsamo nyama.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena