Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ll gawo 9 tsamba 20-21
  • Kodi Paradaiso Adzabwera Liti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Paradaiso Adzabwera Liti?
  • Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
  • Nkhani Yofanana
  • Paradaiso Ali Pafupi
    Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!
  • Chigawo 9
    Mverani Mulungu
  • Kodi Tilidi ‘M’masiku Otsiriza’?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Moyo Wabwino Kwambiri—Posachedwapa!
    Nsanja ya Olonda—1995
Onani Zambiri
Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha
ll gawo 9 tsamba 20-21

CHIGAWO 9

Kodi Paradaiso Adzabwera Liti?

Mavuto amene akuchitika padzikoli akusonyeza kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira padziko lapansi. Luka 21:10, 11; 2 Timoteyo 3:1-5

Mavuto a m’masiku otsiriza—juga, nkhondo, matenda, njala, kusamvera makolo, nkhanza za m’banja

Baibulo linaneneratu zinthu zambiri zimene zikuchitika masiku ano. Linaneneratu kuti anthu adzakhala okonda ndalama, osamvera makolo, oopsa ndiponso okonda zosangalatsa.

Linanenanso kuti kudzakhala zivomezi zamphamvu, nkhondo, njala ndiponso miliri. Zinthu zimenezi zikuchitika masiku ano.

Wa Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino

Yesu ananenanso kuti uthenga wabwino wonena za Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.​—Mateyu 24:14.

Ufumu umenewu udzachotsa zinthu zonse zoipa. 2 Petulo 3:13

Anthu oipa awonongedwa pa Aramagedo ndipo Satana ndi ziwanda zake alangidwa

Posachedwapa, Yehova awononga anthu oipa.

Satana ndi ziwanda zake adzalangidwa.

Yesu wakhala pampando kumwamba ndipo anthu amitundu yosiyanasiyana akusangalala

Anthu amene amamvera Mulungu adzapulumuka n’kulowa m’dziko latsopano lolungama. M’dziko limeneli anthu adzakhala mopanda mantha ndipo azidzakhulupirirana ndi kukondana kwambiri.

  • Kodi Yesu ananena kuti chidzachitike n’chiyani m’nthawi yathu ino?​—Mateyu 24:3-14.

  • Anthu oipa adzawonongedwa.—2 Petulo 3:7.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena