-
Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
-
-
PHUNZIRO 1
Kodi a Mboni za Yehova ndi Anthu Otani?
Denmark
Taiwan
Venezuela
India
Kodi ndi anthu angati a Mboni za Yehova amene mumawadziwa? N’kutheka kuti a Mboni ena mwayandikana nawo nyumba, mumagwira nawo ntchito kapenanso muli nawo kalasi imodzi kusukulu. Mwinanso anakambiranapo nanu nkhani za m’Baibulo. Koma kodi a Mbonife, ndife ndani kwenikweni ndipo n’chifukwa chiyani timauza ena zimene timakhulupirira?
Tili ngati anthu ena onse. Ndife anthu ochokera m’madera osiyanasiyana komanso a zikhalidwe zosiyanasiyana. Ena mwa ife poyamba anali m’zipembedzo zina, ndipo ena sankakhulupirira n’komwe Mulungu. Komabe tonsefe tisanakhale Mboni, tinayamba kaye taphunzira mosamala kwambiri zimene Baibulo limaphunzitsa. (Machitidwe 17:11) Tinavomereza kuti zimene tinkaphunzirazo n’zoonadi, ndipo aliyense anasankha yekha kuti ayambe kulambira Yehova Mulungu.
Kuphunzira Baibulo kumatithandiza. Mofanana ndi munthu wina aliyense, ifenso timalimbana ndi mavuto komanso zofooka zathu. Koma chifukwa choti tsiku ndi tsiku tikuyesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu, tikutha kuona kuti moyo wathu ukusintha ndipo zinthu zikutiyendera bwino. (Salimo 128:1, 2) Chimenechi n’chifukwa chimodzi chimene chimatichititsa kuuzako ena mfundo zabwino zimene taphunzira m’Baibulo.
Timatsatira mfundo za Mulungu pa moyo wathu. Kuphunzira mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kuti tizisangalala ndiponso kuti tizilemekeza ena. Komanso timayesetsa kukhala anthu oona mtima ndiponso achifundo. Kutsatira mfundozi kumatithandizanso kuti tikhale ndi thanzi labwinopo ndiponso kuti tikhale anthu odalirika m’dera lomwe tikukhala. Komanso mfundozi zimatithandiza kupewa makhalidwe oipa, monga chiwerewere, ndipo timakhala ndi mabanja ogwirizana. Popeza sitikayikira zoti “Mulungu alibe tsankho,” timaona kuti tili m’banja lauzimu la padziko lonse. Banjali ndi logwirizana chifukwa cha zimene timakhulupirira, ngakhale kuti tili m’mayiko osiyanasiyana komanso ndife osiyana mitundu. Gulu lathu ndi lapadera kwambiri ngakhale kuti aliyense wa ife si wosiyana ndi anthu ena onse.—Machitidwe 4:13; 10:34, 35.
Kodi anthu a Mboni za Yehova ndi ofanana bwanji ndi anthu ena onse?
Kodi kuphunzira mfundo za m’Baibulo kwathandiza bwanji anthu a Mboni?
-
-
N’chifukwa Chiyani Timatchedwa Mboni za Yehova?Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
-
-
PHUNZIRO 2
N’chifukwa Chiyani Timatchedwa Mboni za Yehova?
Nowa
Abulahamu ndi Sara
Mose
Yesu Khristu
Anthu ambiri amaganiza kuti Mboni za Yehova ndi dzina la chipembedzo chatsopano. Komabe zaka zoposa 2,700 zapitazo, Mulungu woona anatchula atumiki ake kuti “mboni zanga.” (Yesaya 43:10-12) M’mbuyomu chaka cha 1931 chisanafike, tinkadziwika ndi dzina lakuti Ophunzira Baibulo. Nanga n’chifukwa chiyani tinasintha n’kutenga dzina lakuti Mboni za Yehova?
Dzina lathu limathandiza anthu kuti adziwe Mulungu wathu. M’mipukutu yakale ya Baibulo, dzina la Mulungu lakuti Yehova linkapezekamo maulendo ambirimbiri. Koma m’Mabaibulo ambiri a masiku ano, dzinali linachotsedwamo ndipo anaikamo mayina aulemu akuti Ambuye kapena Mulungu. Komatu Mulungu woona anaulula kwa Mose dzina lake lenileni lakuti Yehova, ndipo anamuuza kuti: “Limeneli ndilo dzina langa mpaka kalekale.” (Ekisodo 3:15) Mwanjira imeneyi, iye anadzisiyanitsa ndi milungu ina yonse yonyenga. Choncho, ife timanyadira chifukwa chodziwika ndi dzina loyera la Mulungu.
Dzina lathu limasonyeza ntchito yathu yaikulu. Anthu ambirimbiri akale, kuyambira ndi munthu wolungama Abele, anachitira umboni zoti ankakhulupirira Yehova. Kwa zaka zambirimbiri, anthu enanso okhulupirika analowa m’gulu la ‘mtambo waukulu wa mboni’ umenewu. Ena mwa anthuwa anali Nowa, Abulahamu, Sara, Mose ndi Davide. (Aheberi 11:4–12:1) Mofanana ndi munthu amene amapereka umboni m’khoti wosonyeza kuti munthu winawake ndi wosalakwa, ndife otsimikiza ndi mtima wonse kuthandiza anthu kuti adziwe choonadi chokhudza Mulungu wathu.
Tikutsanzira Yesu. Baibulo limamutchula kuti “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Yesu ananena yekha kuti anathandiza anthu ‘kudziwa dzina la Mulungu’ ndipo anapitiriza ‘kuchitira umboni choonadi’ cha Mulungu. ( Yohane 17:26; 18:37) Choncho, otsatira enieni a Khristu ayenera kudziwika ndi dzina la Yehova ndi kuthandiza anthu ena kuti alidziwe. Zimenezi ndi zomwe anthu a Mboni za Yehova akuyesetsa kuchita.
N’chifukwa chiyani Ophunzira Baibulo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova?
Kodi Yehova wakhala ali ndi mboni padziko lapansili kwa nthawi yaitali bwanji?
Kodi ndani amene ali Mboni yaikulu kwambiri ya Yehova?
-
-
Kodi Chinachitika N’chiyani Kuti Choonadi cha M’Baibulo Chidziwikenso?Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
-
-
PHUNZIRO 3
Kodi Chinachitika N’chiyani Kuti Choonadi cha M’Baibulo Chidziwikenso?
Ophunzira Baibulo, m’ma 1870
Magazini yoyambirira ya Nsanja ya Olonda, mu 1879
Nsanja ya Olonda masiku ano
Baibulo linaneneratu kuti pambuyo pa imfa ya Khristu, mumpingo woyambirira wachikhristu mudzafika aphunzitsi onyenga ndipo adzapotoza choonadi cha m’Baibulo. (Machitidwe 20:29, 30) Patapita nthawi, zimenezi zinachitikadi. Aphunzitsi onyengawa anayamba kusakaniza mfundo zimene Yesu ankaphunzitsa ndi ziphunzitso za chipembedzo chachikunja. Zimenezi n’zomwe zinachititsa kuti pakhale Chikhristu chonyenga. (2 Timoteyo 4:3, 4) Kodi masiku ano tingatsimikize bwanji kuti tikumvetsa bwino mfundo zenizeni zimene Baibulo limaphunzitsa?
Nthawi yoti Yehova aulule choonadi inakwana. Iye analosera kuti ‘m’nthawi yamapeto anthu ambiri adzadziwa zinthu zambiri zoona.’ (Danieli 12:4) M’chaka cha 1870, gulu laling’ono la anthu ofufuza choonadi, linazindikira kuti mfundo zambiri zimene matchalitchi ankaphunzitsa sizinali zogwirizana ndi Malemba. Choncho anayamba kufufuza m’Baibulo kuti adziwe choonadi cha m’Malemba, ndipo Yehova anawadalitsa powathandiza kuti azimvetsa bwino malembawo.
Anthu oona mtima ankaphunzira Baibulo mwakhama. Ophunzira Baibulo akhamawo, ankagwiritsa ntchito njira yabwino kwambiri pophunzira Mawu a Mulungu, ndipo masiku ano tikugwiritsabe ntchito njira imeneyo. Iwo ankaphunzira Baibulo pokambirana mutu wa nkhani umodzi, ndipo akatha ankasankha mutu wina. Koma akapeza nkhani ya m’Baibulo yovuta kumvetsa, iwo ankafufuza mavesi ena amene angawathandize kumvetsa nkhaniyo. Ndiyeno akakambirana nkhaniyo mpaka pamapeto, n’kupeza mfundo imodzi yogwirizana ndi Malemba ena onse, ankailemba penapake. Popeza ankalola kuti Baibulo lizidzitanthauzira lokha, Ophunzira Baibulowo anadziwa choonadi chokhudza dzina la Mulungu komanso Ufumu wake. Anadziwanso chifukwa chimene Mulungu analengera anthu ndi dziko lapansili, zimene zimachitika munthu akamwalira, komanso zoti akufa adzauka. Ntchito yawo yofufuza choonadi inawathandiza kuti amasuke ku miyambo komanso zikhulupiriro zambiri zabodza.—Yohane 8:31, 32.
Pofika mu 1879, Ophunzira Baibulo anazindikira kuti nthawi yafika yoti athandize anthu enanso ambiri kuti adziwe choonadi. Choncho m’chaka chimenechi, iwo anayamba kufalitsa magazini ya Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova, imene tikufalitsabe mpaka pano. Panopa tikuphunzira choonadi cha m’Baibulo ndi anthu m’mayiko 240, m’zinenero zoposa 750. Zoonadi, mosiyana ndi nthawi ina iliyonse m’mbuyomu, panopa anthu ambiri adziwa choonadi.
Kodi anthu ena anachita chiyani ndi choonadi cha m’Baibulo pambuyo pa imfa ya Khristu?
Kodi n’chiyani chatithandiza kuti tidziwenso choonadi cha m’Mawu a Mulungu?
-
-
N’chifukwa Chiyani Tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano?Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
-
-
PHUNZIRO 4
N’chifukwa Chiyani Tinatulutsa Baibulo la Dziko Latsopano?
Congo (Kinshasa)
Rwanda
Kachidutswa ka mpukutu wotchedwa Symmachus kokhala ndi dzina la Mulungu pa Salimo 69:31, ka zaka za m’ma 200 C.E. kapena 300 C.E.
Kwa zaka zambiri, ife a Mboni za Yehova tinkagwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana komanso tinkawasindikiza ndi kuwafalitsa. Koma tinaona kuti pakufunika Baibulo lina limene lingathandize mosavuta munthu aliyense ‘kudziwa choonadi molondola,’ chifukwa ndi zimene Mulungu akufuna. (1 Timoteyo 2:3, 4) Choncho, mu 1950 tinayamba kutulutsa Baibulo la Dziko Latsopano la chinenero chamakono, ndipo tinkalitulutsa m’zigawozigawo. Baibulo limeneli linamasuliridwa molondola kwambiri ndipo likupezeka m’zinenero zoposa 130.
Pankafunika Baibulo losavuta kumvetsa. Zinenero zimasintha pakapita nthawi yaitali. Choncho m’Mabaibulo ambiri muli mawu omwe anthu anasiya kuwagwiritsa ntchito ndipo ndi ovuta kumvetsa. Komanso anthu apeza mipukutu yakale yolondola kwambiri, imene ikufanana kwambiri ndi mipukutu yoyambirira yeniyeni. Zimenezi zachititsa kuti omasulira Baibulo amvetse bwino zinenero zimene anagwiritsa ntchito polemba Baibulo, monga Chiheberi, Chiaramu, ndi Chigiriki.
Pankafunika Baibulo lomasulira mawu a Mulungu molondola. M’malo mosintha malemba ouziridwa ndi Mulungu, omasulira Baibulo ayenera kumasulira malembawo molondola kwambiri. Koma anthu amene anamasulira Mabaibulo ambiri sanagwiritse ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova, m’Malemba Opatulika.
Pankafunika Baibulo lopereka ulemu kwa Mlembi wake. (2 Samueli 23:2) Baibulo la Dziko Latsopano, linabwezeretsa dzina la Yehova m’malo 7,000 amene limapezeka m’mipukutu yakale kwambiri ya Baibulo, monga momwe chithunzi chili m’munsichi chikusonyezera. (Salimo 83:18) Zinatheka kumasulira Baibulo limeneli chifukwa chakuti, kwa zaka zambiri, anthu ena anagwira mwakhama ntchito yofufuza malemba. Kenako anamasulira Baibulo losavuta kuwerenga, lomwe limafotokoza maganizo a Mulungu momveka bwino kwambiri. Kaya muli ndi Baibulo la Dziko Latsopano m’chinenero chanu kapena ayi, tikukulimbikitsani kuti muziwerenga Mawu a Yehova tsiku lililonse.—Yoswa 1:8; Salimo 1:2, 3.
N’chifukwa chiyani tinaganiza zomasulira Baibulo latsopano?
Kodi aliyense amene akufuna kudziwa chifuniro cha Mulungu ayenera kumachita chiyani tsiku lililonse?
-