Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 15

      Kodi Akulu Amathandiza Bwanji Mpingo?

      Mkulu akulankhula ndi anthu ena mumpingo

      Finland

      Mkulu akuphunzitsa mumpingo

      Kuphunzitsa

      Akulu akulimbikitsa anthu ena a mumpingo

      Kulimbikitsa nkhosa

      Mkulu akulalikira

      Kulalikira

      Gulu lathu lilibe atsogoleri amene amalipidwa. M’malomwake, mofanana ndi mmene zinalili mpingo wachikhristu utangoyamba kumene, akulu oyenerera amaikidwa kuti ‘awete mpingo wa Mulungu.’ (Machitidwe 20:28) Akulu amenewa ndi okhwima mwauzimu ndipo amatsogolera mumpingo komanso amaweta gulu la nkhosa za Mulungu “osati mokakamizika, koma mofunitsitsa. Osatinso chifukwa chofuna kupindulapo kenakake, koma ndi mtima wonse.” (1 Petulo 5:1-3) Kodi iwo amagwira ntchito zotani zothandiza mpingo ?

      Akulu amatisamalira komanso kutiteteza. Akulu amapereka malangizo a m’Malemba komanso amathandiza anthu mumpingo kuti akhalebe paubwenzi ndi Yehova. Chifukwa chakuti amadziwa kuti Mulungu wawapatsa udindo wofunika kwambiri umenewu, iwo sapondereza anthu ake koma amayesetsa kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino komanso kuti azikhala achimwemwe. (2 Akorinto 1:24) Mofanana ndi m’busa amene amagwira ntchito mwakhama posamalira nkhosa iliyonse, akulunso amayesetsa kudziwa wina aliyense mumpingo.​—Miyambo 27:23.

      Amatiphunzitsa mmene tingachitire chifuniro cha Mulungu. Mlungu uliwonse akulu amachititsa misonkhano yampingo n’cholinga chotithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Machitidwe 15:32) Amuna odzipereka amenewa amatsogoleranso pa ntchito yolalikira ndipo amagwira nafe ntchitoyi n’kumatiphunzitsa njira zosiyanasiyana zochitira utumikiwu.

      Amalimbikitsa wina aliyense payekha. Pofuna kuthandiza munthu aliyense kulimbitsa ubwenzi wake ndi Yehova, nthawi zina akulu a mumpingo angabwere kunyumba kwathu kapena angakumane nafe ku Nyumba ya Ufumu kuti atithandize ndi kutilimbikitsa pogwiritsa ntchito Malemba.​—Yakobo 5:14, 15.

      Kuwonjezera pa ntchito imene amakhala nayo kumpingo, akulu ambiri amakhalanso otanganidwa chifukwa amagwira ntchito zolembedwa komanso amasamalira mabanja awo. Choncho tiyenera kulemekeza abale amenewa, omwe amagwira ntchito mwakhama.​—1 Atesalonika 5:12, 13.

      • Kodi akulu a mumpingo ali ndi udindo wotani?

      • Kodi akulu amasonyeza bwanji kuti ali ndi chidwi ndi wina aliyense mu mpingo?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Kodi ndani amayenerera kukhala mkulu mumpingo? Kuti mudziwe yankho lake, werengani 1 Timoteyo 3:1-10, 12 komanso pa Tito 1:5-9. Malembawa ali ndi mfundo zimene munthu amafunikira kukwaniritsa kuti akhale mkulu kapena mtumiki wothandiza.

  • Kodi Atumiki Othandiza Ali Ndi Udindo Wotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 16

      Kodi Atumiki Othandiza Ali Ndi Udindo Wotani?

      Mtumiki wothandiza akuthandizira kugawa mabuku

      Myanmar

      Mtumiki wothandiza akuthandizira kugawa mabuku

      Pamisonkhano

      Mtumiki wothandiza akuthandizira kugawa mabuku

      Kagulu ka Utumiki Wakumunda

      Mtumiki wothandiza akugwira nawo ntchito yokonzanso zinthu pa Nyumba ya Ufumu

      Kukonza pa Nyumba ya Ufumu

      Baibulo limatchula magulu awiri a amuna achikhristu amene amakhala ndi maudindo mumpingo. Gulu loyamba ndi la “oyang’anira” ndipo lachiwiri ndi la “atumiki othandiza.” (Afilipi 1:1) Kawirikawiri mumpingo uliwonse mumakhala abale angapo amene ndi akulu komanso atumiki othandiza. Kodi atumiki othandiza amagwira ntchito zotani mumpingo?

      Amathandiza bungwe la akulu. Atumiki othandiza, achinyamata ndi achikulire omwe, ndi amuna omwe ali paubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo amakhala odalirika komanso amachita zinthu mosamala. Atumiki othandiza amagwira ntchito zofunika zosiyanasiyana zomwe zimayenera kuchitika nthawi zonse. Zimenezi zimathandiza akulu kuti akwaniritse udindo wawo wophunzitsa komanso kuweta nkhosa za Mulungu.

      Amagwira ntchito zosiyanasiyana pampingo. Atumiki othandiza amapatsidwa ntchito zosiyanasiyana, monga kulandira anthu amene akufika kumisonkhano, kusamalira zokuzira mawu, kusamalira mabuku. Komanso amasamalira ndalama za mpingo ndiponso amapatsa Akhristu anzawo dera loti azikalalikira. Iwo amathandizanso pa ntchito yokonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina angapemphedwe ndi akulu kuti athandize okalamba. Atumiki othandiza amakhala ofunitsitsa kugwira ntchito iliyonse imene apatsidwa, ndipo zimenezi zimachititsa kuti onse mumpingo aziwalemekeza.​—1 Timoteyo 3:13.

      Monga amuna achikhristu, iwo amapereka chitsanzo chabwino kwa ena. Atumiki othandiza amasankhidwa chifukwa cha makhalidwe awo achikhristu. Iwo amalimbitsa chikhulupiriro chathu akamakamba nkhani pamisonkhano. Komanso akamasonyeza chitsanzo chabwino pa ntchito yolalikira, amatithandiza kuti ifenso tikhale akhama. Popeza kuti iwo amamvera bungwe la akulu, zimenezi zimathandiza kuti onse azisangalala komanso kugwirizana. (Aefeso 4:16) Pakapita nthawi, iwonso angayenerere kukhala akulu.

      • Kodi atumiki othandiza ndi anthu otani?

      • Kodi atumiki amathandiza bwanji kuti mpingo uziyenda bwino?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Nthawi iliyonse mukapita ku Nyumba ya Ufumu, yesetsani kudziwana ndi mkulu kapena mtumiki wothandiza mmodzi mpaka mutadziwana ndi onse limodzi ndi mabanja awo.

  • Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 17

      Kodi Oyang’anira Dera Amatithandiza Bwanji?

      Woyang’anira woyendayenda ndi mkazi wake

      Malawi

      Woyanganira woyendayenda akuchititsa msonkhano wokonzekera utumiki

      Kagulu ka utumiki

      Woyang’anira woyendayenda akulalikira

      Utumiki wakumunda

      Woyang’anira woyendayenda akukambirana ndi akulu a mumpingo

      Msonkhano wa akulu

      Malemba Achigiriki amatchula mobwerezabwereza za Baranaba ndi mtumwi Paulo. Amuna amenewa anali oyang’anira oyendayenda ndipo ankayendera mipingo yoyambirira. N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iwo ankaganizira kwambiri za abale awo auzimu. Paulo ananena kuti ankafuna ‘kubwerera kumizinda yonse kuti akachezere abale’ ndi kuwaona kuti ali bwanji. Iye anali wokonzeka kuyenda maulendo ataliatali kuti akalimbikitse abalewo. (Machitidwe 15:36) Nawonso oyang’anira dera athu masiku ano amakhala ndi mtima umenewu.

      Amabwera kumipingo yathu kudzatilimbikitsa. Woyang’anira dera aliyense amayendera mipingo 20 kapena kuposa, ndipo mpingo uliwonse amauchezera kwa mlungu umodzi, kawiri pa chaka. Timalimbikitsidwa kwambiri ndi utumiki wa abale amenewa komanso ngati ali okwatira, timalimbikitsidwa ndi utumiki wa akazi awo. Oyang’anirawa amayesetsa kudziwana ndi aliyense, ana ndi akulu omwe, ndipo amafunitsitsa kuyenda nafe mu utumiki wa kumunda komanso kupita nafe limodzi kumaphunziro athu a Baibulo. Oyang’anira amenewa amachita maulendo aubusa limodzi ndi akulu, komanso amakamba nkhani zolimbikitsa kwambiri pamisonkhano ya pampingo ndiponso ikuluikulu.​—Machitidwe 15:35.

      Amalimbikitsa Akhristu onse. Cholinga cha oyang’anira dera n’kuthandiza mipingo kuti ikhale yolimba mwauzimu. Iwo amakumana ndi akulu komanso atumiki othandiza kuti aone mmene mpingo ukuyendera, ndiponso amawapatsa malangizo owathandiza pa maudindo awo. Oyang’anira dera amathandiza apainiya kuti utumiki wawo uziyenda bwino. Komanso amasangalala kudziwana ndi anthu amene angoyamba kumene kusonkhana nafe ndiponso kumva mmene akupitira patsogolo mwauzimu. Woyang’anira dera aliyense amadzipereka ndipo ‘amagwira nafe ntchito limodzi potithandiza.’ (2 Akorinto 8:23) Choncho tiyenera kutsanzira chikhulupiriro chawo komanso kudzipereka kwawo kwa Mulungu.​—Aheberi 13:7.

      • N’chifukwa chiyani oyang’anira dera amachezera mipingo?

      • Kodi mungatani kuti mupindule oyang’anira dera akamachezera mpingo?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Pakalendala yanu, ikani chizindikiro pa mlungu umene woyang’anira dera adzachezere mpingo kuti musadzaphonye nkhani zake ku Nyumba ya Ufumu. Ngati mukufuna kuti woyang’anira dera kapena mkazi wake adzakhalepo inuyo mukamaphunzira Baibulo mlungu umenewo kuti mudzadziwane naye bwino, dziwitsani munthu amene akukuphunzitsani Baibulo.

  • Kodi Timathandiza Bwanji Abale Athu Amene Ali M’mavuto?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 18

      Kodi Timathandiza Bwanji Abale Athu Amene Ali M’mavuto?

      JA Mboni za Yehova akupereka katundu kwa anthu amene akhudzidwa ndi masoka ku Dominican Republic

      Dominican Republic

      Anthu a Mboni za Yehova othandiza pakagwa tsoka akukonza Nyumba ya Ufumu ku Japan

      Japan

      Munthu wina wa Mboni za Yehova ku Haiti akutonthoza munthu yemwe wakhudzidwa ndi tsoka

      Haiti

      Pakachitika tsoka, nthawi yomweyo a Mboni za Yehova amayamba kukonza zoti athandize abale awo amene akhudzidwa. Zimenezi zimasonyeza kuti tili ndi chikondi chenicheni. ( Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:17, 18) Koma kodi timathandiza abale athu m’njira zotani?

      Timapereka ndalama. Ku Yudeya kutagwa njala yaikulu, Akhristu oyambirira a ku Antiokeya anatumiza ndalama zoti athandizire abale awo auzimu. (Machitidwe 11:27-30) Ifenso tikamva kuti abale athu m’mayiko ena ali pa mavuto, timapereka zopereka kudzera m’mipingo yathu n’cholinga choti zikathandizire pogula zinthu zofunikira kwa anthu amene akuvutikawo.​—2 Akorinto 8:13-15.

      Timathandiza pogwira ntchito zina zofunika. Akulu amene ali kudera kumene kwachitika tsoka, amafufuza aliyense wa mumpingo mwawo kuti atsimikizire kuti alipo komanso kuti ndi wotetezeka. Komiti yopereka chithandizo ingayang’anire ntchito yopereka chakudya, madzi abwino akumwa, zovala, pogona komanso thandizo la mankhwala. A Mboni za Yehova amene amadziwa ntchito zosiyanasiyana amadzipereka pogwiritsa ntchito ndalama zawo kuti akathandize pa ntchito yokonza nyumba za abale awo komanso Nyumba za Ufumu zomwe zawonongeka. Pakachitika tsoka, sizimavuta kupeza thandizo kapena anthu amene angadzipereke kuthandiza anthu omwe ali m’mavuto. Zili choncho chifukwa nthawi zambiri timagwirira ntchito limodzi komanso ndife gulu logwirizana. Ngakhale kuti timathandiza “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro,” timathandizanso wina aliyense mosaganizira za chipembedzo chake.​—Agalatiya 6:10.

      Timalimbikitsana pogwiritsa ntchito Malemba. Anthu amene akhudzidwa ndi tsoka amafunika kulimbikitsidwa kwambiri. Pa nthawi ngati imeneyi timalimbikitsidwa ndi Yehova yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Anthu amene akuvutika, timawauza malonjezo amene ali m’Baibulo ndipo timawalimbikitsa powauza kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa.​—Chivumbulutso 21:4.

      • N’chifukwa chiyani a Mboni amathandiza mwamsanga pakachitika tsoka?

      • Kodi anthu amene akhudzidwa ndi tsoka tingawauze uthenga wotonthoza uti wa m’Baibulo?

  • Kodi Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru Ndani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 19

      19 Kodi Kapolo Wokhulupirika Ndi Wanzeru Ndani?

      Yesu akulankhula kwa ophunzira ake
      Munthu wa Mboni za Yehova akuphunzira buku lothandiza kumvetsa Baibulo

      Tonse timapindula ndi chakudya chauzimu

      Anthu awiri a m’bungwe lolamulira la Mboni za Yehova

      Yesu atangotsala pang’ono kuphedwa, anakambirana pambali ndi ophunzira ake anayi, omwe anali Petulo, Yakobo, Yohane ndi Andireya. Pamene Yesu ankalosera zinthu zimene zidzakhale chizindikiro choti iye wayamba kulamulira, anafunsa funso lofunika kwambiri. Iye anati: “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?” (Mateyu 24:45) Pamenepa Yesu ankatsimikizira ophunzira akewo kuti iye, monga “mbuye” wawo, adzaika anthu oti nthawi zonse azidzapereka chakudya chauzimu kwa otsatira ake onse, m’nthawi ya mapeto. Kodi Yesu anaika ndani kuti akhale kapolo ameneyu?

      Ndi gulu laling’ono la Akhristu odzozedwa. “Kapolo” ameneyu amadziwikanso kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndipo akugwira mwakhama ntchito yopereka chakudya chauzimu pa nthawi yake kwa Akhristu anzawo amene akulambira nawo Yehova. Timadalira kapolo wokhulupirikayu kuti azitipatsa “chakudya chokwanira pa nthawi yake.”​—Luka 12:42.

      Kapoloyu amasamalira nyumba ya Mulungu. (1 Timoteyo 3:15) Yesu anapatsa kapoloyu udindo waukulu wotsogolera ntchito imene mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova ikuchita. Kapoloyu amatsogolera ntchito yolalikira, amatiphunzitsa kudzera m’mipingo, komanso amayang’anira katundu yense wa gulu la Yehova. Choncho pofuna kutipatsa chakudya chapanthawi yake, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amatipatsa mabuku omwe timawagwiritsa ntchito polalikira, komanso amatipatsa chakudyachi kudzera m’misonkhano yathu ya mpingo ndiponso ikuluikulu.

      Kapoloyu ndi wokhulupirika chifukwa chakuti amatsatira choonadi cha m’Baibulo ndiponso amagwira modzipereka ntchito imene anapatsidwa yolalikira uthenga wabwino. Komanso ndi wanzeru chifukwa chakuti amasamalira mwanzeru zinthu za Khristu padziko lapansi. (Machitidwe 10:42) Yehova akudalitsa ntchito imene kapoloyu akugwira. Iye akuchita zimenezi pokoka anthu ambiri kuti akhale mboni zake, komanso pothandiza kapoloyu pa ntchito yake yopereka chakudya chauzimu chochuluka.​—Yesaya 60:22; 65:13.

      • Kodi Yesu anaika ndani kuti azipereka chakudya chauzimu kwa ophunzira ake?

      • N’chifukwa chiyani tinganene kuti kapoloyu ndi wokhulupirika komanso ndi wanzeru?

  • Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 20

      20 Kodi Bungwe Lolamulira Limagwira Ntchito Bwanji Masiku Ano?

      Bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi

      Bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi

      Akhristu a m’nthawi ya atumwi akuwerenga kalata yochokera ku bungwe lolamulira

      Akuwerenga kalata yochokera ku bungwe lolamulira

      Mu nthawi ya atumwi, panali kagulu kakang’ono ka “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,” omwe anali ngati bungwe lolamulira. Bungwe limeneli linkasankha zoyenera kuchita pa nkhani zofunika kwambiri zokhudza mpingo wonse wa Akhristu odzozedwa. (Machitidwe 15:2) Iwo akamakambirana, ankagwirizana mfundo imodzi chifukwa ankagwiritsa ntchito Malemba komanso chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu unkawatsogolera. (Machitidwe 15:25) Izi n’zimenenso zimachitika masiku ano.

      Mulungu akugwiritsa ntchito Bungwe Lolamulira pokwaniritsa chifuniro chake. Abale odzozedwa amene akutumikira m’bungweli amagwira mwakhama kwambiri ntchito yophunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Popeza iwo atumikira Mulungu kwa nthawi yaitali, amadziwa bwino kutsogolera ntchito yathu komanso amadziwa bwino kuyankha mafunso okhudzana ndi nkhani zauzimu. Abalewa amakumana mlungu uliwonse kuti akambirane zinthu zokhudza mpingo wachikhristu padziko lonse. Mofanana ndi zomwe zinkachitika m’nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulira limapereka malangizo ochokera m’Baibulo kudzera m’makalata kapena potumiza oyang’anira oyendayenda komanso abale osiyanasiyana kumipingo. Zimenezi zimathandiza kuti anthu a Mulungu aziganiza ndiponso kuchita zinthu mofanana. (Machitidwe 16:4, 5) Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito yokonza chakudya chauzimu, limalimbikitsa anthu kuti aziona ntchito yolalikira za Ufumu kukhala yofunika kwambiri komanso limayang’anira ntchito yoika abale osiyanasiyana pa maudindo mumpingo.

      Limatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Bungwe Lolamulira limadalira Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, komanso Yesu yemwe ndi Mutu wampingo, kuti azilitsogolera. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23) Anthu a m’Bungwe Lolamulira sadziona ngati atsogoleri a anthu a Mulungu. Koma iwo limodzi ndi Akhristu onse odzozedwa “amatsatira Mwanawankhosa [Yesu] kulikonse kumene akupita.” (Chivumbulutso 14:4) Abale a m’bungweli amayamikira kwambiri tikamawapempherera.

      • Kodi ndani anali m’bungwe lolamulira m’nthawi ya atumwi?

      • Kodi Bungwe Lolamulira masiku ano limasonyeza bwanji kuti limafunitsitsa kutsogoleredwa ndi Mulungu?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Werengani pa Machitidwe 15:1-35, kuti mudziwe zimene bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi linakambirana ndi kugwirizana pofuna kuthetsa nkhani ina yovuta, mothandizidwa ndi mzimu woyera komanso pogwiritsa ntchito Malemba.

  • Kodi Beteli N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 21

      Kodi Beteli N’chiyani?

      Munthu wa Mboni za Yehova akugwira ntchito mudipatimenti Dipatimenti ya Zithunzi ku Beteli

      Dipatimenti ya Zithunzi, ku United States

      Munthu wa Mboni za Yehova akugwira ntchito mudipatimenti yosindikiza mabuku ku Beteli ya ku Germany

      Germany

      Munthu wa Mboni za Yehova akugwira ntchito mudipatimenti yochapa zovala ku Beteli ya ku Kenya

      Kenya

      Ogwira ntchito yoperekera zakudya akuika chakudya m’matebulo m’chipinda chodyera ku Beteli ya ku Colombia

      Colombia

      Mawu akuti Beteli anachokera ku mawu achiheberi otanthauza kuti “Nyumba ya Mulungu.” (Genesis 28:17, 19) A Mboni za Yehova ali ndi maofesi ambiri m’mayiko osiyanasiyana. Maofesiwa amatchedwa Beteli, ndipo dzinali ndi loyenereradi. Anthu omwe amagwira ntchito kumaofesi amenewa amayang’anira ndi kuthandizira ntchito yolalikira m’mayiko awo. Likulu la Mboni za Yehova lapadziko lonse lili m’dziko la United States, m’dera la New York, ndipo n’kumene kuli Bungwe Lolamulira. Bungweli limayang’anira ntchito zomwe zikuchitika m’maofesi a Mboni za Yehova amene ali m’mayiko ambirimbiri. Gulu lonse la anthu amene amatumikira pamaofesiwa limatchedwa banja la Beteli. Iwo monga banja, amachitira zinthu limodzi monga kugwira ntchito, kuphunzira Baibulo, komanso amadyera limodzi.​—Salimo 133:1.

      Beteli ndi malo apadera, ndipo anthu a m’banja la Beteli ali ndi mtima wodzipereka. Paofesi iliyonse ya Mboni za Yehova, pamakhala amuna ndi akazi achikhristu amene nthawi zonse amagwira ntchito yopititsa patsogolo zinthu za Ufumu, komanso amachita chifuniro cha Mulungu. (Mateyu 6:33) Palibe amene amalandira malipiro alionse komabe aliyense amapatsidwa chipinda chabwino chogona, chakudya komanso ndalama zochepa zoti agulire zinthu zina zofunika. Anthu a pa Beteli amagwira ntchito zosiyanasiyana, monga muofesi, kukhitchini kapena kuchipinda chodyera. Ntchito zina ndi monga kusindikiza mabuku, kukonza kuzipinda zogona, kuchapa zovala ndiponso kukonza zinthu.

      Ku Beteli kumachitika zinthu zambiri zothandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu. Cholinga chachikulu cha Beteli iliyonse n’kuthandiza anthu ambirimbiri kuti adziwe choonadi cha m’Baibulo. Kabuku kano ndi chitsanzo cha zimenezi. Bungwe Lolamulira linayang’anira ntchito yolemba kabukuka, kenako kanatumizidwa kwa omasulira osiyanasiyana padziko lonse. Omasulirawo atamaliza ntchito yawo anatumiza kwa osindikiza omwe ali m’maofesi osiyanasiyana a Mboni za Yehova. Iwo amagwiritsa ntchito makina amene amasindikiza mabuku ambiri pa nthawi yochepa, kenako amatumiza mabukuwo kumipingo yoposa 110,000. Pogwira ntchito zonsezi, mabanja a Beteli amakhala akuthandiza ntchito yofunika kwambiri yolalikira uthenga wabwino imene ikufunika kuchitika mwamsanga.​—Maliko 13:10.

      • Kodi ndi anthu otani omwe amatumikira pa Beteli, ndipo amasamaliridwa bwanji?

      • Kodi Beteli iliyonse imathandizira pa ntchito iti yofunika kwambiri, imene ikufunika kuchitika mwamsanga?

  • Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 22

      Kodi Kuofesi ya Mboni za Yehova Kumachitika Zotani?

      Kagulu ka amuna komwe kamakonza dongosolo la ntchito ya Mboni za Yehova ku Solomon Islands

      Solomon Islands

      Munthu wa Mboni za Yehova akugwira ntchito pa ofesi ya nthambi ku Canada

      Canada

      Magalimoto onyamula mabuku

      South Africa

      Abale ndi alongo a m’banja la Beteli amagwira ntchito m’madipatimenti osiyanasiyana, ndipo utumiki wawo umathandizira pa ntchito yolalikira ya m’dziko lawo kapenanso m’mayiko ena. Ena mwa abale ndi alongo amenewa amagwira ntchito yomasulira mabuku, kusindikiza magazini ndi mabuku, kutumiza mabuku kumipingo, kujambula nyimbo, masewero ndi mavidiyo, komanso ntchito zina zofunika.

      Komiti ya Nthambi imayang’anira ntchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo. Bungwe Lolamulira limapatsa Komiti ya Nthambi udindo woyang’anira ntchito zonse paofesi ya Mboni za Yehova. Komiti ya Nthambi imapangidwa ndi akulu oyenerera atatu kapena kuposa. Komiti imeneyi imadziwitsa Bungwe Lolamulira mmene ntchito ikuyendera m’dziko lawo kapena m’mayiko ena amene komitiyi ikuyang’anira komanso mavuto alionse amene angakhalepo. Malipoti amenewo amathandiza Bungwe Lolamulira kudziwa nkhani zoti lilembe m’mabuku kapena m’magazini komanso nkhani zoti zidzakambidwe pamisonkhano yampingo ndi misonkhano ikuluikulu. Abale oimira Bungwe Lolamulira amatumizidwa nthawi ndi nthawi kuti akayendere nthambi zosiyanasiyana. Iwo amapereka malangizo othandiza kwa abale omwe ali m’Makomiti a Nthambi. (Miyambo 11:14) Woimira likulu la Mboni za Yehova akabwera kudzayendera nthambi, pamachitika msonkhano wapadera. Pamsonkhanowu, iye amakamba nkhani yolimbikitsa kwambiri kwa onse okhala m’dera limene nthambiyo ikuyang’anira.

      Kuofesi ya Mboni za Yehova kumagwiridwa ntchito zothandiza mipingo ya m’dzikomo. Abale a udindo kuofesi ya Mboni za Yehova amavomereza kuti mipingo yatsopano ipangidwe. Abale akuofesiwa amayang’aniranso ntchito za apainiya, amishonale, ndiponso oyang’anira madera omwe ali m’gawo limene nthambi yawo imayang’anira. Iwo amakonza misonkhano ikuluikulu, amayang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu, komanso amaonetsetsa kuti mabuku akutumizidwa kumipingo kuti abale kumeneko azikawagwiritsa ntchito. Ntchito iliyonse imene imachitika kuofesi ya Mboni za Yehova imathandizira kuti ntchito yolalikira izichitika mwadongosolo.​—1 Akorinto 14:33, 40.

      • Kodi Makomiti a Nthambi amathandiza bwanji Bungwe Lolamulira?

      • Kodi kuofesi ya Mboni za Yehova kumachitika ntchito ziti?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Alendo amaloledwa kukaona ofesi ya Mboni za Yehova kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu, ndipo pamakhala munthu amene amawaonetsa malo osiyanasiyana. Tikukupemphani kuti inunso mupite kukaona zimene zimachitika kumeneko. Popita kuofesi ya Mboni za Yehova, mudzavale ngati mmene mumavalira mukamapita kumisonkhano ya mpingo. Mukadzapita kukacheza ku Beteli, chikhulupiriro chanu chidzalimba.

  • Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 23

      23 Kodi Ntchito Yolemba Ndiponso Kumasulira Mabuku Athu Imayenda Bwanji?

      Munthu wina akugwira ntchito mu Dipatiment Yolemba, m’dziko la United States

      Dipatimenti Yolemba, m’dziko la United States

      Kagulu ka anthu omasulira mabuku ku South Korea

      South Korea

      Bambo wina ku Armenia wagwira buku lomasuliridwa ndi a Mboni za Yehova m’manja mwake

      Armenia

      Mtsikana wina ku Burundi wagwira buku lomasuliridwa ndi a Mboni za Yehova m’manja mwake

      Burundi

      Mayi wina ku Sri Lanka akusonyeza magazini omasuliridwa ndi a Mboni za Yehova

      Sri Lanka

      Kuti ntchito yathu yolengeza “uthenga wabwino . . . kudziko lililonse, fuko lililonse, chinenero chilichonse, ndi mtundu uliwonse” iziyenda bwino, timasindikiza mabuku m’zinenero zoposa 750. (Chivumbulutso 14:6) Kodi timakwanitsa bwanji ntchito yovutayi? Ntchitoyi imatheka chifukwa imagwiridwa ndi anthu olemba nkhani ochokera m’mayiko osiyanasiyana komanso anthu omasulira omwe amagwira ntchito yawo modzipereka, ndipo onsewa ndi a Mboni za Yehova.

      Nkhani zonse zimalembedwa m’Chingelezi. Bungwe Lolamulira limayang’anira ntchito za Dipatimenti Yolemba imene ili ku likulu lathu la padziko lonse. Dipatimenti imeneyi imayang’anira ntchito ya anthu olemba nkhani amene akutumikira kulikulu lathu komanso m’maofesi ena a Mboni za Yehova. Popeza kuti amene amalemba nkhani zathu akuchokera m’mayiko osiyanasiyana, zimenezi zimathandiza kuti nkhanizo zikhale zokhudza anthu a m’mayiko ambiri komanso azikhalidwe zosiyanasiyana.

      Kenako nkhanizo zimatumizidwa kwa omasulira. Nkhani zikalembedwa zimaonedwa ndi anthu osiyanasiyana amene amatsimikizira kuti zili bwino. Kenako amazitumiza kwa omasulira padziko lonse, amene amagwira ntchito m’magulu. Omasulirawa amayesetsa kusankha “mawu olondola a choonadi” amene ali ndi tanthauzo lenileni la mawu a Chingelezi omwe akuwamasulirawo.​—Mlaliki 12:10.

      Makompyuta amathandiza kuti ntchitoyi iziyenda mwamsanga. N’zoona kuti kompyuta payokha singagwire ntchito imene olemba nkhani komanso omasulirawa amagwira. Komabe, kuti azigwira ntchitoyi mofulumira kwambiri iwo amagwiritsa ntchito madikishonale ndi mapulogalamu ena apakompyuta. A Mboni za Yehova ali ndi pulogalamu yawo ya pakompyuta [Multilanguage Electronic Publishing System (MEPS)] yomwe amagwiritsa ntchito pokonza mabuku m’zinenero zambirimbiri. Pulogalamu imeneyi imathandiza poika zithunzi ndi kukonza mmene mabuku adzaonekere akadzasindikizidwa.

      N’chifukwa chiyani timachita zonsezi, ngakhale m’zinenero zimene zimalankhulidwa ndi anthu ochepa kwambiri? N’chifukwa chakuti Yehova akufuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.”​—1 Timoteyo 2:3, 4.

      • Kodi ntchito yolemba mabuku athu imayenda bwanji?

      • N’chifukwa chiyani timamasulira mabuku athu m’zinenero zambiri?

  • Kodi Ndalama Zothandizira pa Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Zimachokera Kuti?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 24

      24 Kodi Ndalama Zothandizira pa Ntchito Yathu Yapadziko Lonse Zimachokera Kuti?

      Munthu wina akupereka ndalama
      A Mboni za Yehova akulalikira

      Nepal

      Anthu ogwira ntchito mongodzipereka akumanga Nyumba ya Ufumu ku Togo

      Togo

      Ogwira ntchito mongodzipereka pa ofesi ya Mboni za Yehova ku Britain

      Britain

      Chaka chilichonse gulu lathu limafalitsa ndi kugawira Mabaibulo ndi mabuku ena popanda mtengo uliwonse. Komanso timamanga ndi kukonza Nyumba za Ufumu ndi maofesi athu. Timathandizanso anthu ambiri omwe akutumikira pa Beteli, ndiponso amishonale, ndipo kukachitika tsoka timathandiza anthu omwe akhudzidwa. Ndiye mwina mungadabwe kuti, ‘Kodi ndalama zoyendetsera ntchito zonsezi zimachokera kuti?’

      Sitiuza anthu kuti azipereka chakhumi, komanso sitiyendetsa mbale ya zopereka. Ngakhale kuti ndalama zomwe zimafunika pothandizira pa ntchito yolalikira n’zambiri, ife sitimapemphetsa ndalama kwa anthu. Zaka zoposa 100 zapitazi, magazini ya Nsanja ya Olonda inanena zoti timakhulupirira kuti Yehova ndi amene akutithandiza. Choncho “sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi,” ndipo sitinachitepo zimenezi pa zaka zonsezi.​—Mateyu 10:8.

      Ndalama zonse zimene timagwiritsa ntchito n’zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Anthu ambiri amayamikira ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ndipo amapereka ndalama zothandizira pa ntchitoyi. Nawonso a Mboni amapereka ndalama zawo, zinthu zina zosiyanasiyana, komanso amagwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zawo pothandizira kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lonse lapansi. (1 Mbiri 29:9) Ku Nyumba ya Ufumu komanso kumisonkhano yathu ikuluikulu kumakhala mabokosi a zopereka kuti aliyense aziponyamo zopereka zake ngati angakonde kutero. M’mayiko ena, abale amapereka zopereka zawo kudzera pawebusaiti ya jw.org. Nthawi zambiri, si anthu olemera amene amaponya ndalama m’mabokosiwa. Ambiri amakhala ngati mkazi wamasiye wosauka yemwe Yesu anamuyamikira ataponya timakobidi tating’ono, moponyamo zopereka m’kachisi. (Luka 21:1-4) Choncho nthawi zonse aliyense ‘amaika kenakake pambali’ n’cholinga choti adzapereke “mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake.”​—1 Akorinto 16:2; 2 Akorinto 9:7.

      Tili ndi chikhulupiriro choti Yehova apitiriza kulimbikitsa anthu kuti ‘azimulemekeza ndi zinthu zawo zamtengo wapatali’ ndi kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu n’cholinga choti chifuniro chake chikwaniritsidwe.​—Miyambo 3:9.

      • N’chiyani chomwe chimasiyanitsa gulu lathu ndi zipembedzo zina?

      • Kodi ndalama zomwe anthu amapereka mwa kufuna kwawo zimagwiritsidwa ntchito bwanji?

  • N’chifukwa Chiyani Timamanga Nyumba za Ufumu Ndipo Timazimanga Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 25

      N’chifukwa Chiyani Timamanga Nyumba za Ufumu Ndipo Timazimanga Bwanji?

      Ogwira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ku Bolivia

      Bolivia

      Nyumba ya Ufumu yakale ku Nigeria
      Nyumba ya Ufumu yatsopano ku Nigeria

      Nigeria, nyumba yakale komanso yatsopano

      Pamalo omwe pakumangidwa Nyumba ya Ufumu ku Tahiti

      Tahiti

      Mfundo yaikulu ya m’Baibulo imene timaphunzira ku Nyumba ya Ufumu ndi yokhudzana ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipotu mfundo yaikulu pa utumiki wa Yesu inali yokhudzanso Ufumu wa Mulungu.​—Luka 8:1.

      Ndi malo amene anthu amalambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Ku Nyumba ya Ufumu n’kumene Mboni za Yehova zimakonzekera ntchito yolalikira uthenga wabwino m’deralo. (Mateyu 24:14) Kukula kwa Nyumba za Ufumu komanso kamangidwe kake kamakhala kosiyanasiyana. Komabe, zonse zimakhala zooneka bwino ndipo nyumba zambiri zimagwiritsidwa ntchito ndi mipingo ingapo. M’zaka za posachedwapa tamanga Nyumba za Ufumu zambirimbiri (tinganene kuti padziko lonse tinkamanga nyumba zisanu tsiku lililonse). Izi zachitika chifukwa chakuti mipingo ikuwonjezeka kwambiri. Kodi zatheka bwanji kuti timange nyumba zochuluka choncho?​—Mateyu 19:26.

      Nyumbazi zimamangidwa pogwiritsa ntchito ndalama zimene zimaperekedwa ku thumba lapadera. Zopereka zimenezi zimatumizidwa kuofesi ya Mboni za Yehova kuti zikaperekedwe ku mipingo imene ikufuna kumanga kapena kukonzanso Nyumba za Ufumu.

      Nyumba za Ufumu zimamangidwa ndi anthu osiyanasiyana ongodzipereka omwe salipiridwa. M’mayiko ambiri muli Magulu Omanga Nyumba za Ufumu. Abale ndi alongo amene amagwira ntchito mongodzipereka m’magulu amenewa amapita m’mipingo yosiyanasiyana m’dziko lomwelo. Iwo amakafika kumadera akumidzi kuti akathandize pa ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu komanso kuphunzitsa abale a kumeneko mmene angagwirire ntchitoyi. M’mayiko ena muli abale omwe amayang’anira ntchito yomanga ndi kukonzanso Nyumba za Ufumu m’gawo limene apatsidwa. Akulu amene amadziwa bwino ntchito ya zomangamanga amatsogolera mipingo pomanga Nyumba za Ufumu ndipo amaonetsetsa kuti zonse zimene zimafunika pa ntchitoyi zachitika. Pamakhala amisiri odziwa ntchito zosiyanasiyana, omwe amadzipereka pa ntchito imeneyi. Ngakhale kuti anthu ambiri amene amathandizira pa ntchitoyi mongodzipereka, amakhala a mumpingo momwemo. Zonsezi zikutheka chifukwa chakuti Yehova akutithandiza ndi mzimu wake komanso anthu ake akugwira ntchitoyi modzipereka.​—Salimo 127:1; Akolose 3:23.

      • N’chifukwa chiyani malo athu olambirira amatchedwa Nyumba ya Ufumu?

      • Kodi zimatheka bwanji kumanga Nyumba za Ufumu padziko lonse?

  • Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 26

      Kodi Tingathandize Bwanji Kuti Nyumba Yathu ya Ufumu Izioneka Bwino?

      A Mboni za Yehova akuyeretsa Nyumba ya Ufumu ku Estonia

      Estonia

      A Mboni za Yehova akuyeretsa Nyumba ya Ufumu ku Zimbabwe

      Zimbabwe

      Munthu wa Mboni za Yehova ku Mongolia akukonza zinthu zowonongeka pa Nyumba ya Ufumu

      Mongolia

      Munthu wa Mboni za Yehova akupenta Nyumba ya Ufumu ku Puerto Rico

      Puerto Rico

      Nyumba ya Ufumu iliyonse ya Mboni za Yehova imadziwika ndi dzina loyera la Mulungu. Choncho timaona kuti kuisamalira kuti izioneka bwino, ndiponso kukonza zinthu zomwe zawonongeka mkati ndi kunja, ndi mwayi waukulu komanso ndi mbali ya kulambira kwathu. Ndipo aliyense ali ndi mwayi wochita nawo zimenezi.

      Muzikonza nawo m’Nyumba ya Ufumu misonkhano ikatha. Pambuyo pa msonkhano uliwonse, abale ndi alongo amaonetsetsa kuti asanachoke, asesa m’Nyumba ya Ufumu. Komanso kamodzi pa mlungu, mpingo umafunika kukonza bwino Nyumba ya Ufumu. Mkulu kapena mtumiki wothandiza ndi amene amayang’anira ntchito imeneyi ndipo nthawi zambiri amakhala ndi ndandanda ya ntchito zomwe zikufunika kugwiridwa. Mogwirizana ndi zofunika kumpingo kwawo, abale ndi alongo angadzipereke kusesa, kukolopa, kupukuta mipando, kukonza kuzimbudzi, kutsuka mawindo, kutaya zinyalala kapena kusamalira zinthu zina kunja kwa Nyumba ya Ufumuyo. Ndipo nthawi zina kamodzi pachaka, mpingo umakonza zoti pakhale ntchito yaikulu yokonza zinthu. Tiyenera kutenganso ana athu kuti akagwire nawo ntchito ngati zimenezi. Tikamachita zimenezi timathandiza anawo kuti azilemekeza malo athu olambirira.​—Mlaliki 5:1.

      Muzithandiza nawo pokonza zinthu zowonongeka. Chaka chilichonse, mpingo uliwonse umafufuza zinthu zimene zikufunika kukonzedwa mkati ndi kunja kwa Nyumba ya Ufumu yawo. Zimenezi zimathandiza kuti nyumbayo izikonzedwa pafupipafupi. Zimachititsanso kuti Nyumba ya Ufumu isawonongeke kwambiri ndipo mpingo suwononga ndalama zambiri. (2 Mbiri 24:13; 34:10) Nyumba ya Ufumu ikakhala yoyera komanso yosamalidwa bwino, imakhala malo abwino olambiriramo Mulungu wathu. Choncho tikamathandiza nawo kukonza ndi kusamalira Nyumba yathu ya Ufumu, timasonyeza kuti timakonda Yehova komanso timalemekeza malo athu olambirira. (Salimo 122:1) Zimenezi zimathandizanso kuti anthu amene ayandikira Nyumba ya Ufumu yathu, aziilemekeza.​—2 Akorinto 6:3.

      • N’chifukwa chiyani sitiyenera kunyalanyaza kusamalira malo athu olambirira?

      • Kodi mpingo umakonza zotani kuti Nyumba ya Ufumu yawo izikhala yooneka bwino?

  • Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 27

      Kodi Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu Ingatithandize Bwanji?

      Munthu akuona mabuku mulaibulale ya pa Nyumba ya ufumu

      Israel

      Bambo wa Mboni za Yehova akuthandiza mnyamata kufufuza nkhani

      Czech Republic

      Kamtsikana kakulemba dzina lake m’buku lake la nyimbo

      Benin

      Akufufuza nkhani pa laibulale yapakompyuta ya Watchtower

      Cayman Islands

      Kodi mukufuna kufufuza nkhani zina kuti mulidziwe bwino Baibulo? Kodi mukufuna kuphunzira zambiri zokhudza lemba linalake, munthu, malo kapena china chilichonse chotchulidwa m’Baibulo? Kapena kodi mumadzifunsa ngati Mawu a Mulungu angakuthandizeni pa vuto linalake limene likukudetsani nkhawa? Ngati ndi choncho, kafufuzeni zimenezi mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu.

      Imakhala ndi mabuku okuthandizani kufufuza zinthu. N’kutheka kuti mulibe mabuku onse a Mboni za Yehova ofotokoza nkhani za m’Baibulo amene alipo m’chinenero chanu. Koma mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu muli mabuku ambiri atsopano. Mwina mulinso Mabaibulo osiyanasiyana, buku labwino lotanthauzira mawu ndi mabuku ena othandiza. Muli ndi ufulu wowerenga mabuku a mulaibulale, misonkhano isanayambe kapena itatha. Ngati mulaibulalemo muli kompyuta, n’kutheka kuti pakompyutapo pali Watchtower Library. Imeneyi ndi laibulale ya pakompyuta ya mabuku athu ambirimbiri ndipo ndi yosavuta kugwiritsa ntchito, moti mungathe kufufuza nkhani, mawu kapena lemba.

      Imathandiza pokonzekera nkhani za m’msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Mungagwiritse ntchito laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu pokonzekera nkhani zanu. Woyang’anira msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu ndi amene ali ndi udindo woyang’anira laibulale. Iye amaonetsetsa kuti mabuku ndi magazini atsopano aikidwa mulaibulale ndiponso kuti aikidwa madongosolo. M’baleyu kapena munthu amene amakuphunzitsani Baibulo angakusonyezeni mmene mungafufuzire nkhani iliyonse imene mukufuna. Komabe, mabuku a mulaibulale sakuyenera kutulutsidwa mu Nyumba ya Ufumu. Komanso tikuyenera kusamalira mabukuwa ndi kupewa kuwalembalemba.

      Baibulo limanena kuti ngati tikufuna ‘kumudziwadi Mulungu,’ tiyenera kukhala akhama pofufuza mawu ake ngati mmene tingafufuzire “chuma chobisika.” (Miyambo 2:1-5) Laibulale ya pa Nyumba ya Ufumu ndi malo abwino amene mungayambire kufufuza nkhani zosiyanasiyana.

      • Kodi mulaibulale ya pa Nyumba ya Ufumu mumapezeka zinthu ziti zokuthandizani kufufuza nkhani?

      • Kodi ndani amene angakuphunzitseni mmene mungagwiritsire ntchito laibulale?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Ngati mukufuna kuyamba kusunga mabuku pa laibulale yanuyanu, kaonaneni ndi m’bale woyang’anira mabuku kuti akuonetseni mabuku amene alipo. Munthu amene akukuphunzitsani Baibulo angakuuzeni mabuku ofunika amene angakhale oyambirira kuwapeza.

  • Kodi Pamalo Athu a pa Intaneti Pali Zinthu Zotani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 28

      Kodi Pawebusaiti Yathu Pali Zinthu Zotani?

      Mayi akufufuza nkhani pa Intaneti

      France

      Akugwiritsira ntchito kompyuta

      Poland

      Mayi akuonera vidiyo ya chinenero chamanja pa Intaneti

      Russia

      Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:16) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tikugwiritsa ntchito zinthu zamakono monga Intaneti. Pawebusaiti yathu ya jw.org, pamapezeka nkhani zofotokoza zimene ife a Mboni za Yehova timakhulupirira komanso zimene timachita. Kodi Pawebusaiti Yathu Pali Zinthu Zotani?

      Pamapezeka mayankho a m’Baibulo a mafunso amene anthu amakonda kufunsa. Mungapezepo mayankho a mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakonda kufunsa. Mwachitsanzo kapepala kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?, ndi kakuti Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?, timapezeka pawebusaitiyi m’zinenero zoposa 600. Mungapezeponso Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zoposa 130 komanso mabuku angapo othandiza pophunzira Baibulo monga buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndiponso mungapezepo magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mungawerenge kapena kumvetsera pa Intaneti mabuku ndi magazini amenewa. Mungathenso kuzichotsa pa Intaneti n’kuziika pa kompyuta kapena pachipangizo china kuti muzimvetsera kapena kuwerenga. Mukhozanso kusindikiza masamba ena ochepa a buku kapena magazini imene mwapeza pa Intaneti n’cholinga choti mukapatse munthu wina wachidwi m’chinenero chake. Palinso mavidiyo a m’zinenero zamanja zambiri. Mungapange dawunilodi nkhani za m’Baibulo zomwe zinajambulidwa mwasewero, mavidiyo a masewero a nkhani za m’Baibulo komanso nyimbo zosangalatsa zomwe mungamvetsere nthawi ina iliyonse.

      Pali nkhani zofotokoza bwino mmene mpingo wa Mboni za Yehova ulili. Chinanso chomwe chimapezeka pawebusaiti yathu ndi nkhani zaposachedwapa zokhudza Mboni za Yehova ndi mavidiyo osonyeza zinthu zokhudza ntchito yapadziko lonse komanso mmene timathandizirana pakagwa tsoka. Mungapezenso masiku amene misonkhano ikuluikulu idzachitike, komanso maadiresi kapena manambala a foni a maofesi osiyanasiyana a Mboni za Yehova.

      Chifukwa cha zinthu ngati zimenezi tikuonetsa kuwala kwa choonadi ngakhale kumadera akutali kwambiri. Anthu padziko lonse lapansi ngakhale kumadera akutali ngati ku Antarctica, akuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Tikupemphera kuti “mawu a Yehova apitirize kufalikira mofulumira” padziko lonse lapansi n’cholinga choti Mulungu alemekezedwe.​—2 Atesalonika 3:1.

      • Kodi webusaiti yathu ya jw.org ikuthandiza bwanji anthu kuphunzira choonadi cha m’Baibulo?

      • Kodi mungakonde kufufuza zinthu zotani pawebusaiti yathu?

      CHENJEZO:

      Anthu ena odana ndi Mboni za Yehova ali ndi malo awo pa Intaneti omwe amalembapo zinthu zabodza zokhudza gulu lathu. Cholinga chawo n’choti alepheretse anthu kutumikira Yehova. Tisamapite pamalo ngati amenewa.​—Salimo 1:1; 26:4; Aroma 16:17.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena