Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 5

      Kodi Ndi Zinthu Ziti Zomwe Mudzasangalale Nazo Pamisonkhano Yathu Yachikhristu?

      A Mboni za Yehova ali pa Nyumba ya Ufumu ku Argentina

      Argentina

      Msonkhano wa Mboni za Yehova ku Sierra Leone

      Sierra Leone

      Msonkhano wa Mboni za Yehova ku Belgium

      Belgium

      Msonkhano wa Mboni za Yehova ku Malaysia

      Malaysia

      Anthu ambiri asiya kupita kumapemphero chifukwa amaona kuti sathandizidwa kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo wawo kapena salimbikitsidwa mwauzimu. Nanga n’chifukwa chiyani muyenera kupita kumisonkhano yachikhristu ya Mboni za Yehova? Kodi kuchita zimenezi kuli ndi phindu lililonse?

      Mukasangalala kukhala pakati pa anthu achikondi. M’nthawi ya atumwi, Akhristu ankasonkhana m’mipingo yosiyanasiyana n’cholinga choti alambire Mulungu, aphunzire Malemba ndiponso alimbikitsane. (Aheberi 10:24, 25) Akhristu akasonkhana, ankaona kuti ali pakati pa mabwenzi enieni achikondi, kapena kuti abale ndi alongo awo auzimu. (2 Atesalonika 1:3; 3 Yohane 14) Masiku ano timachita misonkhano ngati mmene ankachitira Akhristu a m’nthawi ya atumwi ndipo nafenso timasangalala.

      Mudzadziwa mmene mungagwiritsire ntchito mfundo za m’Baibulo. Mofanana ndi mmene zinkachitikira m’nthawi ya Aisiraeli, masiku anonso anthu onse amasonkhana pamodzi, kaya ndi abambo, amayi kapena ana. Anthu amene ali oyenerera kuphunzitsa mumpingo, amagwiritsa ntchito Baibulo potithandiza kuona mmene tingagwiritsire ntchito mfundo zake pa moyo wathu watsiku ndi tsiku. (Deuteronomo 31:12; Nehemiya 8:8) Aliyense amakhala ndi mwayi wopereka ndemanga pa nkhani zokambirana ndiponso kuimba nawo nyimbo. Tikamachita zimenezi timakhala tikulengeza zimene Akhristufe tikuyembekezera.​—Aheberi 10:23.

      Chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chidzalimba. Mtumwi Paulo anauza anthu a mumpingo wina umene unalipo m’nthawiyo, kuti: “Ndikulakalaka kukuonani . . . kuti tidzalimbikitsane mwa chikhulupiriro, chanu ndi changa.” (Aroma 1:11, 12) Tikapita kumisonkhano yathu, timakhala pamodzi ndi Akhristu anzathu. Zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso zimatilimbikitsa kuti nthawi zonse tizichita zinthu zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo.

      Tikukulimbikitsani kuti mupite kumsonkhano wathu uliwonse kuti mukaone nokha zimenezi. Tikukutsimikizirani kuti tidzakulandirani ndi manja awiri. Komanso misonkhano yathu yonse ndi yaulere, ndipo sipayendetsedwa mbale ya zopereka.

      • Kodi misonkhano yathu ya mpingo imachitika motsatira chitsanzo chiti?

      • Kodi tingapindule bwanji tikamapezeka pamisonkhano yachikhristu?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Ngati simunapitepo kumisonkhano yathu yachikhristu, koma mukufuna kuona mmene mkati mwa Nyumba ya Ufumu ya m’dera lanu mulili, pemphani aliyense wa Mboni za Yehova kuti akakuonetseni.

  • Kodi Timapindula Bwanji Tikamasonkhana ndi Akhristu Anzathu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 6

      Kodi Timapindula Bwanji Tikamasonkhana ndi Akhristu Anzathu?

      A Mboni za Yehova akucheza

      Madagascar

      Wa Mboni za Yehova akuthandiza Mkhristu mnzake

      Norway

      Akulu achikhristu akulimbikitsana ndi Mkhristu mnzawo

      Lebanon

      A Mboni za Yehova akudyera limodzi chakudya

      Italy

      Nthawi zonse timapita kumisonkhano yachikhristu, ngakhale kuti nthawi zina nyengo imakhala yoipa kwambiri kapena tingafunike kudutsa m’nkhalango yowirira kwambiri. A Mboni za Yehova amaonetsetsa kuti akasonkhane ndi Akhristu anzawo ngakhale kuti amakumana ndi mavuto osiyanasiyana komanso nthawi zina amakhala atatopa pambuyo poweruka kuntchito. N’chifukwa chiyani iwo amachita zimenezi?

      Kusonkhana ndi anzathu kumatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino. Pa nthawi ina, Paulo ananena kuti “tiyeni tiganizirane.” Iye ananena zimenezi posonyeza zimene tiyenera kuchita ndi anthu amene timasonkhana nawo kumpingo. (Aheberi 10:24) Mawu amenewa akutanthauza kuti tiyenera kudziwana bwino ndi ena kapena kuwamvetsa bwino. Choncho mawu a mtumwi Paulo amenewa akutilimbikitsa kuti tiyenera kuganizira ena. Tikamayesetsa kudziwana bwino ndi mabanja ena achikhristu, tikhoza kudziwa zimene achita polimbana ndi mavuto ofanana ndi athu ndipo angatithandize kuti nafenso tithane ndi mavuto athuwo.

      Timalimbitsa ubwenzi wathu ndi anzathu. Sikuti anthu amene timasonkhana nawo ndi ongodziwana nawo chabe koma ndi anzathu apamtima. Nthawi zina timachitira limodzi zosangalatsa zina. Kodi zimenezi zili ndi phindu lanji? Zimenezi zimathandiza kuti tikhale ndi mtima woyamikira kwambiri Akhristu anzathu, ndipo mtima umenewu umatithandiza kuti tizikondana kwambiri. Komanso, pamene anzathu akukumana ndi mavuto, timakhala okonzeka kuwathandiza chifukwa cha ubwenzi wolimba umene ulipo. (Miyambo 17:17) Tikamasonkhana ndi mpingo komanso kuchitira pamodzi zinthu zina ndi Akhristu anzathu, timasonyeza kuti ‘tikusamalirana mofanana.’​—1 Akorinto 12:25, 26.

      Tikukulimbikitsani kuti musankhe anthu amene akuchita chifuniro cha Mulungu kuti akhale mabwenzi anu. Anthu oterewo mungawapeze pakati pa Mboni za Yehova. Musalole kuti chilichonse chikulepheretseni kusonkhana nafe.

      • Kodi timapeza madalitso otani tikamasonkhana ndi anzathu?

      • Kodi mubwera liti kumisonkhano yathu kuti mudzadziwane bwino ndi anthu a mumpingo mwathu?

  • Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 7

      Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

      Msonkhano wa Mboni za Yehova ku New Zealand

      New Zealand

      Msonkhano wa Mboni za Yehova ku Japan

      Japan

      Mnyamata wa Mboni akuwerenga Baibulo ku Uganda

      Uganda

      Anthu awiri a Mboni za Yehova akuchita chitsanzo chokambira Baibulo ku Lithuania

      Lithuania

      Pamisonkhano ya Akhristu oyambirira, ankaimba nyimbo, kupemphera, kuwerenga komanso kukambirana Malemba, ndipo sipankachitika miyambo iliyonse yamakolo. (1 Akorinto 14:26) Masiku ano, misonkhano ya Mboni za Yehova imachitikanso chimodzimodzi.

      Timalandira malangizo othandiza ochokera m’Baibulo. Pa mapeto pa mlungu, mpingo uliwonse umasonkhana kuti umvetsere nkhani ya m’Baibulo ya mphindi 30. Nkhaniyi imatithandiza kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito Malemba pa moyo wathu komanso imatithandiza kuona mmene malembawo akugwirizanira ndi zimene zikuchitika panopa. Pa nthawiyi, tonse timayenera kutsegula Baibulo lathu n’kumawerenga limodzi ndi munthu amene akukamba nkhaniyo. Nkhaniyo ikatha, timakhala ndi Phunziro la “Nsanja ya Olonda,” lomwe limachitika kwa ola limodzi. Phunziro limeneli limachitika pogwiritsira ntchito magazini yophunzirira ya Nsanja ya Olonda, ndipo aliyense mu mpingo amakhala ndi mwayi wopereka ndemanga zake. Phunziro limeneli limatithandiza kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pa moyo wathu. Mlungu uliwonse mipingo yonse ya Mboni za Yehova yoposa 110,000 padziko lonse, imaphunzira nkhani yofanana.

      Timathandizidwa kuti tikhale aphunzitsi aluso. Tsiku lina mlungu womwewo, timachita msonkhano womwe umakhala ndi mbali zitatu. Msonkhanowu, umadziwika kuti Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Nkhani zomwe zimakambidwa pa msonkhanowu zimachokera mu ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu yomwe imatuluka mwezi ndi mwezi. Mbali yoyamba ya msonkhano umenewu yomwe ili ndi mutu wakuti, Chuma Chopezeka M’Mawu a Mulungu, imatithandiza kumvetsa bwino mbali ina ya m’Baibulo imene abale ndi alongo anapemphedwa kuti awerenge mlungu umenewo. Mbali yachiwiri ili ndi mutu wakuti, Kuphunzitsa Mwaluso mu Utumiki. Abale ndi alongo amachita zitsanzo zosonyeza zimene tingachite pokambirana ndi munthu mfundo za m’Baibulo. M’bale yemwe ndi mlangizi wa mbali imeneyi amaperekanso malangizo omwe amatithandiza kuti tiziwerenga komanso kufotokoza mfundo momveka bwino. (1 Timoteyo 4:13) Mbali yachitatu, yomwe ndi yomaliza ili ndi mutu wakuti, Moyo Wathu Wachikhristu. Wokamba nkhani imeneyi amakambirana ndi abale ndi alongo mfundo zowathandiza kuti amvetse bwino Baibulo, ndipo amachita zimenezi pogwiritsa ntchito mafunso amene ali m’nkhaniyi.

      Mukadzabwera kumisonkhano yathu, sitikukayikira kuti mudzasangalala ndi maphunziro apamwamba ochokera m’Baibulo.​—Yesaya 54:13.

      • Kodi mungayembekezere kudzaphunzira zotani kumisonkhano ya Mboni za Yehova?

      • Pa misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu, kodi ndi msonkhano uti umene mungakonde kudzapezekapo?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Konzekerani zina mwa nkhani zimene tidzaphunzire pa misonkhano yathu yotsatira. Ndipo muone mfundo zimene mungaphunzire kuchokera m’Baibulo zomwe mungagwiritse ntchito pa moyo wanu wa tsiku ndi tsiku.

  • N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 8

      N’chifukwa Chiyani Timavala Bwino Tikamapita Kumisonkhano Yathu?

      Bambo ndi mwana wake avala kuti azipita kumisonkhano

      Iceland

      Mayi ndi mwana wake akukonzekera kupita kumisonkhano

      Mexico

      A Mboni za Yehova avala bwino ku Guinea-Bissau

      Guinea-Bissau

      Banja la ku Philippines likupita kumisonkhano

      Philippines

      Kodi mwaona m’zithunzi zomwe zili m’kabuku kano kuti anthu a Mboni za Yehova amavala bwino kwambiri akamapita kumisonkhano yawo yampingo? N’chifukwa chiyani timayesetsa kuvala bwino komanso kuoneka bwino pamisonkhano?

      Timachita zimenezi posonyeza ulemu kwa Mulungu wathu. N’zoona kuti Mulungu samangoona mmene tikuonekera kunja, koma amaonanso mumtima mwathu. (1 Samueli 16:7) Komabe tikasonkhana kuti timulambire, timafunitsitsa kusonyeza ulemu kwa iyeyo komanso kwa Akhristu anzathu. Mwachitsanzo, ngati tikukaonekera pamaso pa woweruza kukhoti, tingayesetse kuvala bwino komanso kuoneka bwino. Tingachite zimenezi posonyeza kulemekeza woweruzayo. Chimodzimodzinso ifeyo. Mmene tavalira popita kumisonkhano yathu zimasonyeza kuti tikulemekeza “Woweruza wa dziko lonse lapansi,” yemwe ndi Yehova Mulungu. Komanso timasonyeza kuti tikulemekeza malo amene tikumulambirirawo.—Genesis 18:25.

      Timachita zimenezi posonyeza kuti tikutsatira mfundo zimene timaphunzira. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti azivala “mwaulemu ndi mwanzeru.” (1 Timoteyo 2:9, 10) Kuvala “mwaulemu” kukutanthauza kupewa zovala zomwe zingasonyeze kuti tikudzionetsera ndiponso zosonyeza kusadzilemekeza. Komanso kuchita zinthu “mwanzeru” kumatithandiza kupewa kuvala motayirira, monga kuvala zovala zothina, zazifupi, kapenanso zazikulu kwambiri. Ngakhale kuti timatsatira mfundo za m’Baibulo zimenezi, timakhalabe ndi mwayi wosankha zovala zimene tikufuna. Mavalidwe ndi maonekedwe athu ‘angakometsere chiphunzitso cha Mpulumutsi wathu ndiponso angatamande Mulungu,’ ngakhale pamene sitinalankhule chilichonse. (Tito 2:10; 1 Petulo 2:12) Choncho, tikavala bwino popita kumisonkhano, timathandiza kuti ena aziona kulambira Yehova m’njira yoyenera.

      Musalephere kupita ku Nyumba ya Ufumu poganiza kuti zovala zanu si zabwino. Chimene chimafunika ndi zovala zochapa bwino komanso zoyenerera, osati zatsopano kapena zamtengo wapatali zokhazokha.

      • Kodi kuvala bwino polambira Mulungu n’kofunika motani?

      • Posankha zochita pa nkhani ya kavalidwe ndi kaonekedwe kathu, kodi ndi mfundo ziti zimene zingatithandize?

  • Kodi Tingatani Kuti Tizikonzekera Bwino Misonkhano?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 9

      Kodi Tingatani Kuti Tizikonzekera Bwino Misonkhano?

      Wa Mboni za Yehova akukonzekera misonkhano yampingo

      Cambodia

      Wa Mboni za Yehova akukonzekera misonkhano yampingo
      Wa Mboni za Yehova akufuna kupereka ndemanga pamisonkhano yampingo

      Ukraine

      Ngati mukuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova, muyenera kuti nthawi zonse mumayesetsa kukonzekera zimene muphunzirezo. Kuti muzipindula kwambiri ndi misonkhano ya mpingo, ndi bwino kukonzekeranso musanapite kumisonkhanoko. Zinthu zingakuyendereni bwino ngati mutakhala ndi ndandanda yabwino yokuthandizani kukonzekera.

      Sankhani nthawi ndiponso malo abwino ophunzirira. Kodi ndi nthawi iti imene mungakonzekere bwino popanda chododometsa? Kodi ndi m’mawa kwambiri musanayambe kugwira ntchito, kapena usiku ana onse atagona? Ngakhale mutamaphunzira kwa nthawi yochepa, patulani nthawi imene mukufuna kuti muziphunzirayo, ndipo musalole chilichonse kukudodometsani kapena kukulepheretsani kuphunzira. Sankhani malo opanda phokoso, ndipo muonetsetse kuti palibe chilichonse chimene chingakusokonezeni. Mungachite zimenezi pothimitsa TV, foni ndiponso wailesi. Kupemphera musanayambe kuphunzira kungakuthandizeni kuti musakhale ndi nkhawa chifukwa cha zinthu za tsikulo, ndipo zimenezi n’zofunika kuti maganizo anu onse akhale pa Mawu a Mulungu amene mukufuna kuphunzirawo.​—Afilipi 4:6, 7.

      Muzidula mzere kunsi kwa mfundo zimene mwapeza, pokonzekera kuti mukayankhe. Mukamayamba kukonzekera, muziona kaye nkhani yonse mwachidule kuti mukhale ndi chithunzi cha nkhaniyo. Mungachite zimenezi poganizira mutu wa nkhaniyo, komanso mmene timitu tamkati tikugwirizanira ndi mutu waukulu. Muzionanso zithunzi ndiponso mafunso obwereza amene akusonyeza mfundo zikuluzikulu za nkhaniyo. Mukatero, werengani ndime iliyonse ndi funso lake n’kuyesetsa kupeza yankho la funsolo. Muziwerenga m’Baibulo lanu malemba amene ali m’nkhaniyo n’kuganizira mmene akugwirizanira ndi nkhani yonseyo. (Machitidwe 17:11) Mukapeza yankho la funso la ndime imeneyo, dulani mzere kunsi kwa mfundo zofunika payankho limenelo, zimene zingakuthandizeni kuti mudzalikumbukire. Ndiyeno mukapita kumisonkhano, mungakweze dzanja kuti muyankhe mwachidule m’mawu anuanu.

      Mukamakonzekera nkhani zosiyanasiyana zimene timaphunzira mlungu uliwonse kumisonkhano, mudzawonjezera mfundo zatsopano za m’Baibulo mumtima wanu, womwe uli ngati ‘chosungiramo chuma.’​—Mateyu 13:51, 52.

      • Kodi mungatsatire ndandanda yotani pokonzekera misonkhano?

      • Kodi mungakonzekere bwanji kuti mukapereke ndemanga pamisonkhano?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Potsatira ndondomeko imene yafotokozedwa pamwambapa, konzekerani Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo. Pemphani munthu amene akukuthandizani kuphunzira Baibulo kuti akuthandizeni kukonzekera ndemanga imene mungakapereke pamisonkhano yotsatira ya mpingo.

  • Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 10

      Kodi Kulambira kwa Pabanja N’chiyani?

      Banja likuchita kulambira kwa pabanja mosangalala

      South Korea

      Mwamuna ndi mkazi wake akuphunzira Baibulo pamodzi

      Brazil

      Wa Mboni za Yehova akuphunzira Baibulo

      Australia

      Banja likukambirana nkhani za m’Baibulo

      Guinea

      Kuyambira kale, Yehova wakhala akufuna kuti mabanja azikhala ndi nthawi yochitira zinthu pamodzi n’cholinga choti alimbitse ubwenzi wawo ndi iye komanso kuti banja lawo lilimbe. (Deuteronomo 6:6, 7) N’chifukwa chake banja lililonse la Mboni za Yehova linasankha nthawi imene limachita kulambira kwa pabanja mlungu uliwonse. Pa nthawiyi, banja limakambirana momasuka zinthu zauzimu zogwirizana kwambiri ndi banja lawo. Ngati mukukhala nokha, nthawi imeneyi mungaigwiritse ntchito kuti muyandikire Mulungu. Mungachite zimenezi pophunzira Baibulo pa nkhani imene mungasankhe.

      Imakhala nthawi yoyandikira kwambiri Yehova. Baibulo limati: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” ( Yakobo 4:8) Kuphunzira Mawu a Mulungu kumatithandiza kuti timudziwe bwino Yehova. Timadziwa bwino makhalidwe ake komanso mmene iye amachitira zinthu. Njira yosavuta yoyambira kulambira kwa pabanja ndi kuyamba ndi kuwerenga limodzi Baibulo mokweza mwina pogwiritsa ntchito ndandanda yowerenga Baibulo ya mlungu umenewo ya msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu. Munthu aliyense m’banjamo angapatsidwe ndime zina m’Baibulo zoti awerenge kenako onse n’kukambirana mfundo zimene aphunzira pa zimene awerengazo.

      Imakhala nthawi yabwino yoti onse m’banjamo alimbitse ubwenzi wawo. Banja likamaphunzirira limodzi Baibulo, zimathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azikondana komanso kuti ana azikondana ndi makolo awo. Nthawi yophunzirayo iyenera kukhala nthawi yosangalatsa kwambiri imene aliyense angaiyembekezere mwachidwi mlungu uliwonse. Makolo angasankhe nkhani zimene angaphunzire, mogwirizana ndi msinkhu wa ana awo, mwina pogwiritsa ntchito nkhani za mu Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kapena pawebusaiti yathu ya jw.org. Mwina mungakambirane za vuto linalake limene ana anu akumana nalo kusukulu ndi zimene anawo angachite kuti athane nalo. Mukhozanso kuonera pulogalamu iliyonse pa TV ya JW Broadcasting (tv.jw.org/ny) n’kukambirana zimene mwaonerazo. Mungasangalalenso kukonzekera nyimbo zomwe zidzaimbidwe kumisonkhano kenako n’kudya tizakudya ndi tizakumwa pambuyo pa kulambirako.

      Nthawi yapadera imeneyi, yomwe banja lanu lizilambira Yehova limodzi mlungu uliwonse, idzathandiza kuti aliyense m’banja lanu azisangalala ndi Mawu a Mulungu, ndipo Yehova adzadalitsa kwambiri khama lanu.​—Salimo 1:1-3.

      • N’chifukwa chiyani timapatula nthawi yoti tizichita Kulambira kwa Pabanja?

      • Kodi makolo angachite chiyani kuti nthawi imeneyi izikhala yosangalatsa kwa aliyense m’banjamo?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Kuti mudziwe njira zina zochitira kulambira kwa pabanja, funsani ena mu mpingo mwanu kuti mumve zimene amachita pa kulambira kwawo kwa pabanja. Komanso fufuzani mabuku ena amene alipo ku Nyumba ya Ufumu amene mungagwiritse ntchito pophunzitsa ana anu za Yehova.

  • N’chifukwa Chiyani Timakhala ndi Misonkhano Ikuluikulu?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 11

      N’chifukwa Chiyani Timakhala ndi Misonkhano Ikuluikulu?

      Msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova ku Mexico

      Mexico

      Buku latsopano likutulutsidwa pamsonkhano wachigawo ku Germany

      Germany

      A Mboni za Yehova ali pamsonkhano wachigawo ku Botswana

      Botswana

      Mnyamata akubatizidwa ku Nicaragua

      Nicaragua

      Sewero la pamsonkhano wachigawo ku Italy

      Italy

      N’chifukwa chiyani anthu awa akuoneka achimwemwe? N’chifukwa chakuti ali pamsonkhano wina waukulu umene timakhala nawo. Mofanana ndi atumiki akale a Mulungu, amene anauzidwa kuti azichita misonkhano itatu pachaka, ifenso timachita misonkhano ikuluikulu. (Deuteronomo 16:16) Chaka chilichonse timachita misonkhano ikuluikulu itatu: Misonkhano iwiri yadera yomwe imachitika tsiku limodzilimodzi, ndiponso msonkhano wachigawo wamasiku atatu. Kodi timapindula bwanji ndi misonkhano imeneyi?

      Imathandiza kuti ubale wathu wachikhristu ukhale wolimba. Mofanana ndi Aisiraeli amene ankasangalala potamanda Yehova “pamsonkhano,” ifenso timasangalala kusonkhana pamodzi n’kumamulambira pamisonkhano ikuluikulu. (Salimo 26:12; 111:1) Misonkhano imeneyi imatipatsa mwayi wokumana komanso kucheza ndi abale ndi alongo athu a m’mipingo ina kapenanso ochokera m’mayiko ena. Masana timasangalala kudyera limodzi chakudya pamalo a msonkhano omwewo, zomwe zimatipatsa mpata wocheza ndi Akhristu anzathu. (Machitidwe 2:42) Pamisonkhano imeneyi timaona umboni wa chikondi chimene chimagwirizanitsa “gulu lonse la abale” padziko lapansi.​—1 Petulo 2:17.

      Imatithandiza kukula mwauzimu. Aisiraeli ankapindulanso chifukwa chakuti ‘ankamvetsa bwino mawu’ a m’Malemba amene ankafotokozedwa momveka bwino. (Nehemiya 8:8, 12) Ifenso timayamikira malangizo a m’Baibulo amene timalandira pamisonkhano yathu. Msonkhano uliwonse umakhala ndi mutu wochokera m’Malemba. Pamisonkhano imeneyi pamakhala nkhani zosiyanasiyana zosangalatsa komanso zitsanzo zomwe zimatithandiza kuchita zimene Mulungu amafuna pa moyo wathu. Timalimbikitsidwa kwambiri anthu ena akamafotokoza zimene achita kuti apirire mavuto amene akumana nawo pa moyo wachikhristu m’nthawi yovuta ino. Pamisonkhano yachigawo pamakhala masewero amene amatithandiza kumvetsa nkhani inayake ya m’Baibulo komanso kuona zimene tikuphunzirapo, ndipo ochita masewerowa amavala ngati mmene anthu akale ankavalira. Pamsonkhano uliwonse pamakhala ubatizo, ndipo anthu amene akufuna kusonyeza kuti anadzipereka kwa Mulungu, amabatizidwa.

      • N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amasangalala akakhala pamsonkhano waukulu?

      • Kodi mungapindule motani ngati mutapezeka pamsonkhano waukulu?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Ngati mukufuna kulidziwa bwino gulu lathu, mudzapite kumsonkhano waukulu wotsatira. Munthu amene akuphunzira nanu Baibulo angakusonyezeni pulogalamu ya msonkhano kuti muone nkhani zimene zimakambidwa pamisonkhano imeneyi. Ndiyeno pakalendala yanu lembani chizindikiro patsiku la msonkhano wotsatira ndi kumene ukachitikire, ndipo mudzayesetse kukapezekapo.

  • Kodi Ntchito Yathu Yolalikira za Ufumu Imachitika Motani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 12

      Kodi Ntchito Yathu Yolalikira za Ufumu Imachitika Motani?

      A Mboni za Yehova akulalikira kunyumba ndi nyumba

      Spain

      Wa Mboni za Yehova akulalikira kupaki[Chithunzi patsamba 15]

      Belarus

      Wa Mboni za Yehova akulalikira patelefoni[Chithunzi patsamba 15]

      Hong Kong

      A Mboni za Yehova ali mu utumiki[Chithunzi patsamba 15]

      Peru

      Yesu atatsala pang’ono kuphedwa ananena kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Koma kodi zingatheke bwanji kulalikira padziko lonse? Zingatheke potsatira chitsanzo chimene Yesu anasonyeza pamene anali padziko lapansi.​—Luka 8:1.

      Timayesetsa kuyendera anthu kunyumba zawo. Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azilalikira uthenga wabwino kunyumba ndi nyumba. (Mateyu 10:11-13; Machitidwe 5:42; 20:20) Otsatirawo anauzidwa dera loti azikalalikira. (Mateyu 10:5, 6; 2 Akorinto 10:13) Mofanana ndi zimenezi, masiku ano ntchito yathu yolalikira imachitika mwadongosolo, ndipo mpingo uliwonse umapatsidwa dera loti uzilalikira. Zimenezi zimatithandiza kutsatira lamulo la Yesu lakuti “tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira.”​—Machitidwe 10:42.

      Timayesetsa kulankhula ndi anthu kulikonse kumene angapezeke. Yesu anatipatsa chitsanzo polalikira kumalo alionse kumene kumapezeka anthu, monga m’mphepete mwa nyanja ndi pachitsime. (Maliko 4:1; Yohane 4:5-15) Ifenso timalankhula ndi anthu nkhani za m’Baibulo m’malo alionse monga mumsewu, m’malo ochitira malonda, m’malo amene anthu amakonda kupita kukacheza ndi patelefoni. Komanso tikakhala ndi mpata wabwino, timalalikira kwa anthu amene tayandikana nawo nyumba, anzathu akuntchito, akusukulu ndiponso achibale athu. Zonsezi zathandiza kuti anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse amve “uthenga wabwino wa chipulumutso.”​—Salimo 96:2.

      Kodi pali aliyense amene mukufuna kumuuza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi zimene Ufumuwo udzachite m’tsogolo? Yesetsani kuuza ena uthenga wopatsa chiyembekezowu, ndipo chitani zimenezi mwamsanga.

      • Kodi ndi “uthenga wabwino” wotani umene ukuyenera kulengezedwa?

      • Kodi a Mboni za Yehova akutsanzira bwanji Yesu polalikira?

      DZIWANI ZAMBIRI

      Pemphani munthu amene akuphunzira nanu Baibulo kuti akufotokozereni mmene mungachitire zinthu mwanzeru pouza mnzanu zimene mwaphunzira m’Baibulo.

  • Kodi Mpainiya Amachita Chiyani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 13

      Kodi Mpainiya Amachita Chiyani?

      Mpainiya ali mu utumiki

      Canada

      Apainiya akulalikira

      Kulalikira kunyumba ndi nyumba

      Apainiya akuphunzitsa munthu Baibulo

      Phunziro la Baibulo

      Mpainiya akuphunzira Baibulo

      Akuphunzira Baibulo payekha

      Mawu akuti “mpainiya” kawirikawiri amatanthauza munthu amene amayambitsa zinthu zinazake zimene ena sanachitepo ndipo amapereka chitsanzo kwa ena kuti atsanzire. Yesu anali ngati mpainiya, chifukwa chakuti anatumizidwa padziko lapansi kuti adzatumikire anthu ndi kupereka moyo wake n’cholinga choti anthuwo adzapulumuke. (Mateyu 20:28) Masiku ano, otsatira ake akumutsanzira pogwiritsa ntchito nthawi yawo yambiri pa ntchito ‘yophunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake.’ (Mateyu 28:19, 20) Pofuna kugwira ntchito imeneyi mokwanira, ena anayamba utumiki umene umadziwika ndi dzina lakuti upainiya.

      Mpainiya ndi munthu amene amagwira ntchito yolalikira nthawi zonse. Aliyense wa Mboni za Yehova amalalikira uthenga wabwino. Komabe, ena anasintha zina ndi zina pa moyo wawo kuti akhale apainiya okhazikika, ndipo amathera maola 70 mwezi uliwonse pa ntchito yolalikira. Kuti akwanitse kuchita utumiki umenewu, ambiri amayesetsa kupeza ntchito imene ingawapatse mpata. Ena amasankhidwa kuti akatumikire monga apainiya apadera, kudera limene kukufunika anthu ambiri olalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Mwezi uliwonse apainiyawa amatha maola 130 kapena kuposa akulalikira ndi kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu. Apainiya amakhala moyo wosalira zambiri chifukwa amadziwa kuti Yehova adzawapatsa zinthu zonse zofunika pa moyo wawo. (Mateyu 6:31-33; 1 Timoteyo 6:6-8) Amene sangakwanitse kuchita upainiya wokhazikika amachita upainiya wothandiza pa nthawi imene apeza mpata. Zimenezi zimawapatsa mwayi wowonjezera ntchito yawo yolalikira, ndipo amatha maola 30 kapena 50 pa mwezi akugwira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu Mawu a Mulungu.

      Mpainiya amagwira ntchito yakeyi chifukwa chokonda Mulungu ndi anthu. Mofanana ndi Yesu, ifenso timaona kuti masiku ano pali anthu ambiri amene akufunikira kuphunzitsidwa za Mulungu ndi zolinga zake. (Maliko 6:34) Choncho popeza kuti ifeyo tikudziwa zinthu zambiri zimene zingawathandize panopa, timawaphunzitsa kuti aziyembekezera zinthu zabwino m’tsogolo. Chifukwa chokonda anthu, mpainiya amagwiritsa ntchito nthawi yake komanso mphamvu zake pothandiza ena kuti amve uthenga wabwino. (Mateyu 22:39; 1 Atesalonika 2:8) Zimenezi zimachititsa kuti chikhulupiriro cha mpainiyayo chilimbe, amayandikira kwambiri Mulungu ndiponso amakhala wosangalala kwambiri.​—Machitidwe 20:35.

      • Kodi mpainiya amachita chiyani?

      • N’chifukwa chiyani ena amadzipereka kuchita upainiya nthawi zonse?

  • Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?
    Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?
    • PHUNZIRO 14

      Kodi Apainiya Ali Ndi Mwayi Wochita Maphunziro Otani?

      Apainiya akulalikira

      United States

      Ophunzira ali ku Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo
      Ophunzira akukonzekera utumiki waumishonale

      Sukulu ya Giliyadi, ku Patterson, New York

      Mwamuna ndi mkazi wake omwe ndi amishonale akulalikira ku Panama

      Panama

      Kwa nthawi yaitali, gulu la Yehova lakhala likuphunzitsa anthu pogwiritsa ntchito masukulu osiyanasiyana ophunzitsa Baibulo. Anthu amene amadzipereka kuti azilalikira za Ufumu nthawi zonse, amalowa m’sukulu yapadera yomwe imawathandiza kuti ‘akwaniritse utumiki wawo.’​—2 Timoteyo 4:5.

      Sukulu ya Utumiki Waupainiya. Mpainiya wokhazikika akakwanitsa chaka chimodzi akuchita utumiki wa nthawi zonse, amalowa m’sukulu yomwe imachitika kwa masiku 6 pa Nyumba ya Ufumu ya m’dera lawo. Cholinga cha sukuluyi ndi kuthandiza apainiya kuti azikonda kwambiri Yehova, akhale ndi luso m’mbali zonse za utumiki wawo komanso kuti apitirize kukhala okhulupirika pochita utumikiwo.

      Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu. Sukuluyi, imene imachitika kwa miyezi iwiri, inakonzedwa n’cholinga chothandiza apainiya amene achita utumikiwu kwa kanthawi komanso amene ali ndi mtima wofunitsitsa kukatumikira kumadera ofunikira ofalitsa ambiri. Anthu amene ali ndi mtima umenewu amakhala ngati akunena kuti, “Ine ndilipo! Nditumizeni” ndipo akamachita zimenezi amasonyeza kuti akutsanzira Yesu Khristu yemwe ndi Mlaliki wamkulu kuposa onse amene anagwira ntchito yolalikira padziko lapansi. (Yesaya 6:8; Yohane 7:29) Munthu akasamukira kutali ndi kwawo amafunika kuzolowera kukhala ndi moyo wosafuna zinthu zambiri. Chikhalidwe, nyengo komanso zakudya za m’dera la tsopanolo zikhoza kukhala zosiyana kwambiri ndi zimene anazizolowera. Mwina angafunikenso kuphunzira chinenero china. Sukuluyi imathandiza mabanja, abale osakwatira komanso alongo osakwatiwa, omwe ali ndi zaka za pakati pa 23 ndi 65, kuti akhale ndi makhalidwe amene angawathandize kukwanitsa utumiki wawo komanso kuti akhale ndi luso lomwe lingachititse kuti Yehova komanso gulu lake liwagwiritse ntchito.

      Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Mu Chiheberi mawu akuti “Giliyadi” amatanthauza “Mulu wa Umboni.” Kuyambira pamene sukuluyi inayamba mu 1943, anthu oposa 8,000 omwe analowa m’sukuluyi anatumizidwa monga amishonale kuti akachitire umboni “kumalekezero a dziko lapansi” ndipo zinthu zakhala zikuyenda bwino kwambiri. (Machitidwe 13:47) Mwachitsanzo, pamene amishonale anafika ku Peru, anapeza kuti m’dzikomo munalibe mpingo ngakhale umodzi. Koma panopa kuli mipingo yoposa 1,000. Amishonale atafikanso m’dziko la Japan anapeza kuti kuli Mboni zosapitirira 10. Koma panopa kuli Mboni zoposa 200,000. Sukuluyi imatenga miyezi 5 ndipo amaphunzira Mawu a Mulungu mozama kwambiri. Amishonale amene sanaloweko m’sukuluyi, apainiya apadera, amene akutumikira m’maofesi a nthambi kapena oyang’anira dera, amatha kuitanidwa kuti akalowe m’sukuluyi n’cholinga choti azitsogolera komanso kulimbikitsa ntchito yolalikira imene ikuchitika pa dziko lonse.

      • Kodi cholinga cha sukulu ya Utumiki Waupaniya n’chiyani?

      • Kodi ndani angalowe nawo mu Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena