Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yc phunziro 7 tsamba 16-17
  • Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha?
  • Phunzitsani Ana Anu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekha Ndiponso Umachita Mantha?
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Analimbikitsidwa ndi Mulungu Wake
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • Analimbikitsidwa Ndi Mulungu Wake
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mudzakhulupirika Monga Eliya?
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Phunzitsani Ana Anu
yc phunziro 7 tsamba 16-17

PHUNZIRO 7

Kodi Nthawi Zina Umaona Kuti Uli Wekhawekha?

Takaona kamnyamata komwe kali pachithunzichi. Kakuoneka kuti kali kokhakokha ndipo kakuchita mantha. Kodi zimenezi zinakuchitikirapo?— Munthu aliyense amamva choncho nthawi zina. Baibulo limafotokoza za anthu amene ankakonda Yehova omwe nthawi ina ankaona kuti atsala okha ndipo ankachita mantha. Mmodzi mwa anthu amenewa ndi Eliya. Tiye tione zimene zinamuchitikira.

Yezebeli ankafuna kupha Eliya

Eliya ankakhala ku Isiraeli kalekale Yesu asanabadwe. Pa nthawiyo Ahabu anali mfumu ya ku Isiraeli ndipo sankatumikira Mulungu woona, Yehova. Ahabu ndi mkazi wake Yezebeli ankalambira mulungu wonama, yemwe dzina lake linali Baala. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri a ku Isiraeli ayambenso kulambira Baala. Yezebeli anali munthu woipa kwambiri ndipo ankafuna kupha anthu onse amene ankalambira Yehova, kuphatikizapo Eliya. Kodi ukudziwa kuti Eliya anatani?—

Eliya anathawira kutali kwambiri. Anapita kuchipululu n’kukabisala kuphanga. Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani Eliya anachita zimenezi?— Iye ankachita mantha. Koma Eliya sankafunika kuchita mantha chifukwa ankadziwa kuti Yehova akhoza kumuthandiza. Yehova anali atamusonyeza kale Eliya kuti ndi wamphamvu. Nthawi ina, Yehova anayankha pemphero la Eliya potumiza moto wochokera kumwamba. Ndiye kuti Yehova ankanathadi kumuthandiza Eliya.

Kodi Yehova anathandiza bwanji Eliya?

Eliya atabisala kuphanga, Yehova analankhula naye n’kumufunsa kuti: ‘Kodi ukufuna chiyani kuno?’ Eliya anayankha kuti: ‘Pa atumiki anu onse ndatsala ndine ndekha. Ndatsala ndekhandekha ndipo ndikuopa kuti andipha.’ Eliya ankaganiza kuti atumiki onse a Yehova anali ataphedwa. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Ayi, zimenezo si zoona. Pali anthu ena okwana 7,000 amene akunditumikirabe. Limba mtima. Padakali ntchito yoti ugwire.’ Kodi ukuganiza kuti Eliya anasangalala atamva zimenezi?—

Kodi ukuphunzirapo chiyani pa zimene zinachitikira Eliya?— Usamaone ngati watsala wekhawekha komanso usamachite mantha. Pali anthu ambiri amene amakonda Yehova komanso amene amakukonda iweyo. Komanso Yehova ali ndi mphamvu zambiri ndipo adzakuthandiza nthawi zonse. Kodi wasangalala kudziwa kuti suli wekha?—

WERENGANI MAVESI AWA

  • 1 Mafumu 19:3-18

  • Salimo 145:18

  • 1 Petulo 5:9

MAFUNSO:

  • M’nthawi ya Eliya, kodi anthu ambiri a ku Isiraeli ankalambira ndani?

  • N’chifukwa chiyani Eliya anathawa n’kukabisala kuphanga?

  • Kodi Yehova anamuuza chiyani Eliya?

  • Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene zinamuchitikira Eliya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena