Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Chigawo Choyamba: Zimene Akhristu Amakhulupirira
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
    • MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA

      Chigawo Choyamba: Zimene Akhristu Amakhulupirira

      Kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kwakuthandizani kudziwa choonadi. Zimene mwaphunzira zakuthandizani kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndiponso zakupatsani chiyembekezo chodzapeza moyo wosatha m’tsogolo limodzi ndi madalitso a m’dziko lapansi la paradaiso mu Ufumu wa Mulungu. Panopo, mumakhulupirira kwambiri Mawu a Mulungu ndipo mwapeza madalitso ambiri chifukwa chosonkhana ndi abale mumpingo. Ndiponso mwadziwa mmene Yehova amachitira zinthu ndi anthu ake masiku ano.​—Zek. 8:23.

      Pamene mukukonzekera kubatizidwa, mudzapindula kwambiri pokambirana ndi akulu zimene Akhristu amakhulupirira. (Aheb. 6:1-3) Yehova apitirize kukudalitsani pamene mukuyesetsa kuphunzira Mawu ake kuti mumudziwe bwino ndiponso kuti mudzalandire mphotho imene walonjeza.​—Yoh. 17:3.

      1. N’chifukwa chiyani mukufuna kubatizidwa?

      2. Kodi Yehova ndi ndani?

      • “Yehova ndiye Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi. Palibenso wina.”​—Deut. 4:39.

      • “Inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.”​—Sal. 83:18.

      3. N’chifukwa chiyani muyenera kumagwiritsa ntchito dzina la Mulungu?

      • “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.’”​—Mat. 6:9.

      • “Aliyense amene adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.”​—Aroma 10:13.

      4. Kodi Baibulo limagwiritsanso ntchito mayina ena ati ponena za Yehova?

      • “Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, ndiye Mulungu mpaka kalekale.”​—Yes. 40:28.

      • “Atate wathu wakumwamba.”​—Mat. 6:9.

      • “Mulungu ndiye chikondi.”​—1 Yoh. 4:8.

      5. Kodi Yehova Mulungu mungamupatse chiyani?

      • “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.”​—Maliko 12:30.

      • “Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.”​—Luka 4:8.

      6. N’chifukwa chiyani mumafuna kukhala okhulupirika kwa Yehova?

      • “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.”​—Miy. 27:11.

      7. Kodi mumapemphera kwa ndani, ndipo kudzera m’dzina la ndani?

      • “Ndithudi ndikukuuzani, ngati mupempha chilichonse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani.”​—Yoh. 16:23.

      8. Kodi zinthu zina zimene tingatchule popemphera ndi ziti?

      • “Koma inu muzipemphera motere: ‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Mutikhululukire zolakwa zathu monga mmene ifenso takhululukira amene atilakwira. Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.’”​—Mat. 6:9-13.

      • “Ifetu timamudalira kuti chilichonse chimene tingamupemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yoh. 5:14.

      9. Kodi n’chiyani chingachititse kuti Yehova asamvetsere mapemphero a munthu?

      • “Adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha. . . . chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.”​—Mika 3:4.

      • “Maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzero lawo, koma nkhope ya Yehova imakwiyira anthu ochita zoipa.”​—1 Pet. 3:12.

      10. Kodi Yesu Khristu ndi ndani?

      • “Poyankha, Simoni Petulo ananena kuti: ‘Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.’”​—Mat. 16:16.

      11. N’chifukwa chiyani Yesu anabwera padziko lapansi?

      • “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira ndi kudzapereka moyo wake dipo kuwombola anthu ambiri.”​—Mat. 20:28.

      • “Iye [Yesu] anawauza kuti: ‘Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.’”​—Luka 4:43.

      12. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira nsembe ya Yesu?

      • “Iye anaferanso onse kuti amene ali moyo asakhale moyo wongodzisangalatsa okha, koma akhale moyo wosangalatsa amene anawafera n’kuukitsidwa.”​—2 Akor. 5:15.

      13. Kodi Yesu ali ndi ulamuliro wotani?

      • “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.”​—Mat. 28:18.

      • “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.”​—Afil. 2:9.

      14. Kodi mumakhulupirira kuti Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene anaikidwa ndi Yesu?

      • “Ndani kwenikweni amene ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyang’anira antchito ake apakhomo, ndi kuwapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?”​—Mat. 24:45.

      15. Kodi mzimu woyera ndi munthu?

      • “Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: ‘Mzimu woyera udzafika pa iwe, ndipo mphamvu ya Wam’mwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechinso, wodzabadwayo adzatchedwa woyera, Mwana wa Mulungu.’”​—Luka 1:35.

      • “Choncho ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.”​—Luka 11:13.

      16. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito bwanji mzimu wake woyera?

      • “Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova, ndipo makamu ake onse analengedwa ndi mpweya wa m’kamwa mwake.”​—Sal. 33:6.

      • “Koma mzimu woyera ukadzafika pa inu, mudzalandira mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezero a dziko lapansi.”​—Mac. 1:8.

      • “Ulosi wa m’Malemba suchokera m’maganizo a munthu. Chifukwa ulosi sunayambe wanenedwapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.”​—2 Pet. 1:20, 21.

      17. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?

      • “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”​—Dan. 2:44.

      18. Kodi mudzapindula bwanji ndi Ufumu wa Mulungu?

      • “Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chiv. 21:4.

      19. Kodi mukudziwa bwanji kuti madalitso a Ufumu wa Mulungu abwera posachedwapa?

      • “Atakhala pansi m’phiri la Maolivi, ophunzira anafika kwa iye mwamseri ndi kunena kuti: ‘Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?’ Poyankha Yesu ananena kuti: ‘. . . Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana. Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.’”​—Mat. 24:3, 4, 7, 14.

      • “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, osakonda achibale awo, osafuna kugwirizana ndi anzawo, onenera anzawo zoipa, osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, achiwembu, osamva za ena, odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ndiponso ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma amakana kuti mphamvu ya kudziperekako iwasinthe.”​—2 Tim. 3:1-5.

      20. Kodi mungasonyeze bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwa inuyo?

      • “Chotero pitirizani kufunafuna ufumu choyamba ndi chilungamo chake.”​—Mat. 6:33.

      • “Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo ndipo anditsatire mosalekeza.’”​—Mat. 16:24.

      21. Kodi Satana komanso ziwanda ndi ndani?

      • “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi . . . Iyeyo ndi wopha anthu chiyambire kupanduka kwake.”​—Yoh. 8:44.

      • “Chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”​—Chiv. 12:9.

      22. Kodi Satana amamunamizira chiyani Yehova komanso anthu amene amalambira Yehovayo?

      • “Pamenepo mkaziyo anayankha njokayo kuti: ‘Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, “Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.”’ Pamenepo njokayo inauza mkaziyo kuti: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.’”​—Gen. 3:2-5.

      • “Satana anamuyankha Yehova kuti: ‘Khungu kusinthanitsa ndi khungu. Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.’”​—Yobu 2:4.

      23. Kodi mungasonyeze bwanji kuti zimene Satana amanenazi ndi zabodza?

      • “Um’tumikire [Mulungu] ndi mtima wathunthu.”​—1 Mbiri 28:9.

      • “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”​—Yobu 27:5.

      24. N’chifukwa chiyani anthu amafa?

      • ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzera mwa uchimo, imfayo n’kufalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’​—Aroma 5:12.

      25. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

      • “Amoyo amadziwa kuti adzafa, koma akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlal. 9:5.

      26. Kodi pali chiyembekezo chotani chokhudza anthu amene anamwalira?

      • “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”​—Mac. 24:15.

      27. Kodi ndi angati amene amapita kumwamba kukalamulira ndi Yesu?

      • “Ndinaona Mwanawankhosa ataimirira paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000 olembedwa dzina lake ndi dzina la Atate wake pamphumi pawo.”​—Chiv. 14:1.

  • Chigawo Chachiwiri: Moyo Wachikhristu
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
    • MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA

      Chigawo Chachiwiri: Moyo Wachikhristu

      Kuphunzira Baibulo kwakuthandizani kudziwa zimene Yehova amafuna kuti muzichita ndiponso mmene mungazichitire. Zimene mwaphunzira zachititsa kuti musinthe khalidwe lanu komanso mmene mumaonera moyo. Popeza panopa mwatsimikiza mtima kuti muzitsatira mfundo zolungama za Yehova, ndinu woyenerera kukhala mtumiki wa uthenga wabwino.

      Kukambirana mafunso otsatirawa kukuthandizani kuti mumvetse bwino zimene Yehova amafuna komanso kukukumbutsani zinthu zina zimene mungachite kuti mukhale mtumiki wake wovomerezeka. Mfundo zimenezi zikuthandizani kuona kufunika kochita zinthu zonse ndi chikumbumtima chabwino komanso kulemekeza Yehova.​—2 Akor. 1:12; 1 Tim. 1:19; 1 Pet. 3:16, 21.

      Pofika pano, n’zosakayikitsa kuti mukufunitsitsa kugonjera ulamuliro wa Yehova komanso kukhala m’gulu lake. Mafunso amenewa komanso malembawo akuthandizani kudzifufuza kuti muone ngati mukumvetsa bwino nkhani yogonjera dongosolo la Yehova mumpingo, m’banja, komanso maboma a m’dzikoli. Akuthandizaninso kuona kuti dongosolo limene Yehova anakonza lophunzitsira anthu ake komanso kuwalimbikitsa mwauzimu ndi lofunika kwambiri. Zimenezi zikuphatikizapo misonkhano ya mpingo yomwenso muyenera kupezekapo kupatulapo ngati pali vuto lalikulu.

      Komanso m’chigawochi muli mfundo zokhudza kufunika kogwira nawo ntchito yolalikira za Ufumu nthawi zonse, zomwe zimathandiza ena kudziwa Yehova komanso zimene akuchitira anthu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Chigawochi chikuthandizaninso kuzindikira kuti kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa ndi nkhani yaikulu. Musamakayikire kuti Yehova amaona kuti zimene mukuchita posonyeza kuyamikira kukoma mtima kwakukulu kumene wakusonyezani, ndi zofunika kwambiri.

      1. Kodi Akhristu amauona bwanji ukwati? Kodi ndi chifukwa chimodzi chiti cha m’Malemba chomwe munthu angathetsere banja?

      • “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse. . . . Aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.”​—Mat. 19:4-6, 9.

      2. N’chifukwa chiyani anthu amene akukhala limodzi ngati mwamuna ndi mkazi ayenera kukwatirana mwalamulo? Ngati muli pa banja, kodi munakwatirana mwalamulo ndipo ukwati wanu ndi wovomerezeka ndi boma?

      • “Pitiriza kuwakumbutsa kuti azigonjera ndi kumvera maboma ndiponso olamulira.”​—Tito 3:1.

      • “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posaipitsidwa, pakuti Mulungu adzaweruza adama ndi achigololo.”​—Aheb. 13:4.

      . Kodi udindo wanu ndi wotani m’banja?

      • “Mwana wanga, tamvera malangizo a bambo ako, ndipo usasiye malamulo a mayi ako.”​—Miy. 1:8.

      • “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso mmene Khristu alili mutu wa mpingo . . . Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu monga mmene Khristu anakondera mpingo.”​—Aef. 5:23, 25.

      • “Abambo, musamapsetse mtima ana anu, koma muwalere m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake.”​—Aef. 6:4.

      • “Ananu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse, pakuti kuchita zimenezi kumakondweretsa Ambuye.”​—Akol. 3:20.

      • “Akazi, muzigonjera amuna anu.”​—1 Pet. 3:1.

      4. N’chifukwa chiyani tiyenera kulemekeza moyo?

      • “[Mulungu] amapatsa anthu onse moyo, mpweya, ndi zinthu zonse. . . . Pakuti chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.”​—Mac. 17:25, 28.

      5. N’chifukwa chiyani sitiyenera kupha munthu aliyese, kuphatikizapo mwana wosabadwa?

      • “Amuna akamamenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi wapakati, . . . ngati wina wamwalira, pamenepo uzipereka moyo kulipira moyo.”​—Eks. 21:22, 23.

      • “Maso anu anandiona pamene ndinali mluza, ndipo ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku lanu. M’bukumo munalembamo za masiku amene zinapangidwa koma panalibe ngakhale chiwalo chimodzi chimene chinali chitapangidwa.”​—Sal. 139:16.

      • ‘Yehova amadana ndi manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.’​—Miy. 6:16, 17.

      6. Kodi lamulo la Mulungu pa nkhani ya magazi ndi lotani?

      • ‘Kupitiriza kupewa magazi ndi zopotola.’​—Mac. 15:29.

      7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukonda abale ndi alongo athu?

      • “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana. Mwakutero, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukukondana.”​—Yoh. 13:34, 35.

      8. N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana sayenera (a) Kusonyeza ena chikondi powakumbatira kapena kuwapsompsona? (b) Kukhumudwa ngati ena sakumuitana kunyumba zawo? (c) N’chifukwa chiyani munthu amene akudzikayikira kuti mwina angakhale ali ndi matenda opatsirana, ayenera kukayezetsa kaye magazi asanayambe kuchita chibwenzi? (d) N’chifukwa chiyani munthu amene ali ndi matenda opatsirana ayenera kudziwitsa wogwirizanitsa ntchito za akulu asanakabatizidwe?

      • “Musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kusiyapo kukondana. . . . ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira zoipa mnzake.”​—Aroma 13:8-10.

      • “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afil. 2:4.

      9. N’chifukwa chiyani Yehova amafuna kuti tizikhululukira ena?

      • “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso teroni.”​—Akol. 3:13.

      10. Kodi mungatani ngati m’bale wakunenerani miseche kapena wakuchitirani zachinyengo?

      • “Ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo. Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu. Akapanda kuwamvera amenewanso, uuze mpingo. Ndipo akapandanso kumvera mpingowo, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.”​—Mat. 18:15-17.

      11. Kodi Yehova amaona bwanji machimo otsatirawa?

      ▪ Dama

      ▪ Kugwiritsa ntchito zifaniziro polambira

      ▪ Kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha

      ▪ Kuba

      ▪ Juga

      ▪ Kuledzera

      • “Musasocheretsedwe. Adama, opembedza mafano, achigololo, amuna amene amagonedwa ndi amuna anzawo, amuna ogona amuna anzawo, akuba, aumbombo, zidakwa, olalata, kapena olanda, onsewo sadzalowa mu ufumu wa Mulungu.”​—1 Akor. 6:9, 10.

      12. Kodi mwatsimikiza kuchita chiyani pa nkhani ya dama, lomwe limaphatikizapo mtundu uliwonse wa kugonana ndi munthu amene sunakwatirane naye?

      • “Thawani dama.”​—1 Akor. 6:18.

      13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa mankhwala osokoneza bongo?

      • “Mupereke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyera ndi yovomerezeka kwa Mulungu, ndiyo utumiki wopatulika mwa kugwiritsa ntchito luntha la kuganiza. Musamatengere nzeru za nthawi ino, koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikire chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.”​—Aroma 12:1, 2.

      14. Tchulani zinthu zina zokhudza kukhulupirira mizimu zimene Mulungu amaletsa.

      • “Pakati panu pasapezeke munthu wotentha mwana wake pamoto, wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa.”​—Deut. 18:10, 11.

      15. Ngati munthu wachita tchimo lalikulu ndipo akufuna kukhalanso pa ubwenzi ndi Yehova, kodi ayenera kuchita chiyani mwansanga?

      • “Ndinaulula tchimo langa kwa inu, ndipo sindinabise cholakwa changa. Ndinati: ‘Ndidzaulula kwa Yehova machimo anga.’”​—Sal. 32:5.

      • “Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.”​—Yak. 5:14, 15.

      16. Ngati mwadziwa kuti Mkhristu mnzanu wachita tchimo lalikulu, kodi muyenera kutani?

      • “Munthu akaona wina akuchita tchimo, kapena wamva kuti wina wachita tchimo, munthu ameneyo ndi mboni. Akamva chilengezo kuti akachitire umboni za wochimwayo koma iye osapita kukanena, ndiye kuti wachimwa. Ayenera kuyankha mlandu wa cholakwa chakecho.”​—Lev. 5:1.

      17. Ngati paperekedwa chilengezo choti wina wachotsedwa ndipo salinso wa Mboni za Yehova, kodi tiyenera kumachita naye bwanji zinthu?

      • “Muleke kuyanjana ndi aliyense wotchedwa m’bale, amene ndi wadama, kapena waumbombo, kapena wopembedza mafano, wolalata, chidakwa, kapena wolanda, ngakhale kudya naye munthu wotereyu ayi.”​—1 Akor. 5:11.

      • “Wina akabwera kwa inu ndi chiphunzitso chosiyana ndi ichi, musamulandire m’nyumba zanu kapena kumupatsa moni.”​—2 Yoh. 10.

      18. N’chifukwa chiyani anzanu apamtima ayenera kukhala anthu amene amakonda Yehova?

      • “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru, koma wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.”​—Miy. 13:20.

      • “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.”​—1 Akor. 15:33.

      19. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova salowerera ndale?

      • “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine [Yesu] sindili mbali ya dziko.”​—Yoh. 17:16.

      20. N’chifukwa chiyani muyenera kumvera boma?

      • “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu, chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola. Olamulira amene alipowa ali m’malo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.”​—Aroma 13:1.

      21. Ngati lamulo la anthu likusemphana ndi lamulo la Mulungu, kodi mungatani?

      • “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.”​—Mac. 5:29.

      22. Kodi ndi malemba ati amene angakuthandizeni kukhalabe wosiyana ndi dziko mukamasankha ntchito?

      • “Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”​—Mika 4:3.

      • “Tulukani mwa iye [Babulo Wamkulu] anthu anga, ngati simukufuna kugawana naye machimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandira nawo ina ya miliri yake.”​—Chiv. 18:4.

      23. Kodi ndi zosangalatsa ziti zimene mungasankhe, nanga ndi ziti zomwe mungapewe?

      • “Yehova . . . amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.”​—Sal. 11:5.

      • “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.”​—Aroma 12:9.

      • “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi, zilizonse zoyamikirika, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”​—Afil. 4:8.

      24. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sachita mapemphero pamodzi ndi zipembedzo zina?

      • “Sizingatheke kuti muzidya ‘patebulo la Yehova’ komanso patebulo la ziwanda.”​—1 Akor. 10:21.

      • “‘Lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa,’ ‘ndipo ndidzakulandirani.’”​—2 Akor. 6: 17.

      25. Kodi ndi mfundo ziti zimene zingakuthandizeni kudziwa ngati mukuyenera kuchita nawo chikondwerero chinachake?

      • “Anayamba kusakanikirana ndi mitundu ina, ndi kuyamba kuphunzira zochita zawo. Anayamba kutumikira mafano awo, ndipo mafanowo anakhala msampha wawo.”​—Sal. 106:35, 36.

      • “Akufa sadziwa chilichonse.”​—Mlal. 9:5.

      • “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.”​—Yoh. 17:16.

      • “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”​—1 Pet. 4:3.

      26. Kodi zitsanzo za m’Baibulo zimakuthandizani bwanji kudziwa ngati kuli koyenera kuti muzikondwerera masiku obadwa?

      • “Tsiku lachitatulo linafika, ndipo linali tsiku lokumbukira kubadwa kwa Farao. Mfumuyo inakonzera phwando antchito ake onse. Pa tsikuli, Farao anatulutsa m’ndende mkulu wa operekera chikho ndi mkulu wa ophika mkate, n’kuwaimika pamaso pa antchito ake onse. Farao anabwezeradi pa ntchito mkulu wa operekera chikho uja . . . Koma mkulu wa ophika mkate anam’pachika.”​—Gen. 40:20-22.

      • “Tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa Herode kwambiri, mwakuti analonjeza molumbira kuti adzapatsa mtsikanayo chilichonse chimene angapemphe. Tsopano mtsikanayu, mayi wake atachita kum’pangira, anapempha kuti: ‘Ndipatseni mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.’ Choncho anatuma munthu kukadula mutu wa Yohane m’ndende.”​—Mat. 14:6-8, 10.

      27. N’chifukwa chiyani mukufuna kumatsatira malangizo a akulu?

      • “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera. Iwo amayang’anira miyoyo yanu monga anthu amene adzayankhe mlandu. Muziwamvera ndi kuwagonjera kuti agwire ntchito yawo mwachimwemwe, osati modandaula, pakuti akatero zingakhale zokuvulazani”​—Aheb. 13:17.

      28. N’chifukwa chiyani n’zofunika kwambiri kuti inuyo ndi banja lanu muzikhala ndi nthawi yophunzira Baibulo nthawi zonse?

      • “Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku. Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi, umene umabala zipatso m’nyengo yake, umenenso masamba ake safota, ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​—Sal. 1:2, 3.

      29. N’chifukwa chiyani mumakonda kupezeka pamisonkhano komanso kutengapo mbali?

      • “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.”​—Sal. 22:22.

      • “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”​—Aheb. 10:24, 25.

      30. Kodi ntchito yofunika kwambiri imene Yesu anatipatsa ndi iti?

      • “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani.”​—Mat. 28:19, 20.

      31. Tikamapereka zopereka zothandiza pa ntchito ya Ufumu kapena tikamathandiza abale ndi alongo athu, kodi tiyenera kukhala ndi mtima wotani umene umasangalatsa Yehova?

      • “Uzilemekeza Yehova ndi zinthu zako zamtengo wapatali.”​—Miy. 3:9.

      • “Aliyense achite mogwirizana ndi mmene watsimikizira mumtima mwake, osati monyinyirika kapena mokakamizika, chifukwa Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.”​—2 Akor. 9:7.

      32. Kodi Akhristu amayembekezera kukumana ndi mavuto ati?

      • “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani, komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe, chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.”​—Mat. 5:10-12.

      33. N’chifukwa chiyani ndi mwayi waukulu kubatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova?

      • “Mawu anu amandikondweretsa ndi kusangalatsa mtima wanga, pakuti ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu.”​—Yer. 15:16.

  • Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa
    Gulu Lochita Chifuniro cha Mulungu
    • MAFUNSO KWA ANTHU AMENE AKUFUNA KUBATIZIDWA

      Mfundo Zomalizira Zokambirana ndi Ofuna Kubatizidwa

      Ubatizo umachitika pa misonkhano yadera ndi yachigawo ya Mboni za Yehova. Pamapeto pa nkhani ya ubatizo, wokamba nkhaniyo amapempha ofuna kubatizidwa kuti aimirire ndi kuyankha mokweza mafunso awiri otsatirawa:

      1. Kodi munalapa machimo anu, kudzipereka kwa Yehova komanso kuvomereza njira yake yopulumutsira anthu kudzera mwa Yesu?

      2. Kodi mukudziwa kuti mukabatizidwa muzidziwika kuti ndinu wa Mboni za Yehova komanso kuti muli m’gulu lake?

      Ofuna kubatizidwa akayankha kuti inde pa mafunso amenewa, amasonyeza kuti ‘akulengeza poyera’ kuti amakhulupirira dipo ndiponso anadzipereka kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Nthawi ya ubatizo isanafike, amene akufuna kubatizidwa ayenera kupemphera komanso kusinkhasinkha mafunso amenewa kuti zimene adzayankhe pa tsikuli zidzakhaledi zochokera pansi pa mtima.

      Kodi munadzipereka kwa Yehova m’pemphero n’kumulonjeza kuti muzilambira iye yekha komanso muziona kuti chofunika kwambiri pa moyo wanu ndi kuchita chifuniro chake?

      Kodi mwatsimikiza kuti mubatizidwa pamsonkhano wotsatira?

      Kodi okabatizidwa ayenera kuvala zovala zotani? (1 Tim. 2:9, 10; Yoh. 15:19; Afil. 1:10)

      Tiyenera kuvala “mwaulemu ndi mwanzeru,” posonyeza kuti ‘timalemekeza Mulungu.’ Okabatizidwa sayenera kuvala ngati akupita kukasambira kapena kuvala zovala zolemba mawu kapena zojambula zithunzi. Ayenera kuvala zaukhondo, zoyenera, zaulemu komanso zogwirizana ndi mwambowo.

      Kodi munthu ayenera kusonyeza khalidwe lotani pamene akubatizidwa? (Luka 3:21, 22)

      Zimene Yesu anachita pa nthawi ya ubatizo wake ndi chitsanzo kwa Akhristu masiku ano. Iye ankadziwa kuti ubatizo ndi chinthu chofunika kwambiri ndipo anasonyeza zimenezi mwa zochita zake. Choncho malo a ubatizo si malo ochitira nthabwala zosayenera, kusewera, kusambira kapena zina zilizonse zomwe zingapeputse mwambowo. Komanso Mkhristu amene wangobatizidwa kumeneyo sayenera kuchita zinthu ngati wapambana mpikisano winawake. Ngakhale kuti ubatizo ndi chinthu chosangalatsa, chisangalalocho chiyenera kusonyezedwa moyenera komanso mwaulemu.

      Kodi kusonkhana nthawi zonse komanso kuchita zinthu ndi mpingo kudzakuthandizani bwanji kuti muzikwaniritsa lonjezo lanu lodzipereka kwa Yehova?

      Mukabatizidwa, n’chifukwa chiyani muyenera kupitirizabe kukhala ndi ndandanda yabwino yophunzira Baibulo panokha komanso yolowa mu utumiki nthawi zonse?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena