Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
    • MUTU 6

      Kodi Munthu Akamwalira Amapita Kuti?

      1-3. (a) Kodi anthu amakhala ndi mafunso otani okhudza imfa? (b) Nanga zipembedzo zosiyanasiyana zimapereka mayankho otani?

      BAIBULO limanena kuti tsiku lina “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) M’Mutu 5, tinaphunzira kuti dipo la Yesu ndi limene linachititsa kuti tikhale ndi mwayi wodzapeza moyo wosatha. Koma panopa anthu amamwalirabe. (Mlaliki 9:5) Zimenezi zimachititsa kuti tizikhala ndi funso ngati lakuti, Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

      2 Kudziwa yankho la funso limeneli n’kofunika kwambiri makamaka pamene m’bale wathu kapena mnzathu wamwalira. Tingadzifunse mafunso ngati awa: ‘Kodi wapita kuti? Kodi akutiona? Kodi angatithandize? Nanga kodi tidzamuonanso?’

      3 Zipembedzo zimapereka mayankho osiyanasiyana pa mafunso amenewa. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti ngati munthu ankachita zabwino, akamwalira amapita kumwamba koma ngati ankachita zoipa, amapita kukawotchedwa kumoto. Zina zimaphunzitsa kuti munthu akamwalira amasanduka mzimu ndipo amakakhala ndi achibale ake amene anamwalira kale. Pamene zinanso zimaphunzitsa kuti munthu akamwalira amaweruzidwa ndipo kenako amabadwanso ngati munthu wina kapena nyama.

      4. Kodi zipembedzo zambiri zimaphunzitsa mfundo yofanana iti pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira?

      4 Zipembedzo zimaphunzitsa zinthu zosiyanasiyana pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira. Koma zipembedzo zonsezi zimaphunzitsa mfundo imodzi yofanana yakuti munthu akamwalira, pali chinthu chinachake chimene chimapitirizabe kukhala ndi moyo. Kodi zimenezi ndi zoona?

      KODI MUNTHU AKAMWALIRA AMAPITA KUTI?

      5, 6. Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

      5 Yehova amadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira, ndipo iye amatiuza kuti munthu akamwalira ndiye kuti moyo wake wathera pompo. Imfa imatanthauza kusakhalanso ndi moyo. Choncho munthu akamwalira, palibe chilichonse chimene chimapitiriza kukhalabe ndi moyo kwinakwake.a Munthu womwalira sangaone, sangamve komanso sangaganize.

      6 Solomo analemba kuti: “Akufa sadziwa chilichonse.” Munthu wakufa sangakonde kapena kudana ndi wina aliyense, komanso “kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu, kapena nzeru, ku Manda.” (Werengani Mlaliki 9:5, 6, 10.) Baibulo, pa Salimo 146:4, limafotokozanso kuti munthu akamwalira, “zimene anali kuganiza” zimathera pomwepo.

      ZIMENE YESU ANANENA PA NKHANI YA IMFA

      Mwamuna ndi mkazi wake akhala pansi ndipo akuyang’ana kaduwa

      Yehova analenga anthu kuti azikhala ndi moyo padzikoli mpaka kalekale

      7. Kodi Yesu anayerekezera imfa ndi chiyani?

      7 Lazaro atamwalira, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo.” Komatu Yesu sankatanthauza kuti Lazaro anali atagona tulo teniteni, chifukwa kenako ananena kuti: “Lazaro wamwalira.” (Yohane 11:11-14) Choncho Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Iye sananene kuti Lazaro wapita kumwamba kapena wapita kumene kuli achibale ake amene anamwalira kale. Ndiponso sananene kuti Lazaro akuzunzika kumoto kapena wabadwanso ngati munthu kapena nyama. Lazaro atamwalira zinangokhala ngati wagona tulo tofa nato. Palinso malemba ena omwe amayerekezera imfa ndi tulo. Mwachitsanzo, Baibulo limanena kuti Sitefano ataphedwa, “anagona tulo ta imfa.” (Machitidwe 7:60) Mtumwi Paulo ananenanso za Akhristu ena omwe “anagona mu imfa.”—1 Akorinto 15:6.

      8. Kodi timadziwa bwanji kuti Mulungu sanalenge anthu kuti azifa?

      8 Kodi Mulungu analenga Adamu ndi Hava n’cholinga choti akhale ndi moyo kwa nthawi yochepa kenako adzafe? Ayi. Yehova anawalenga kuti azisangalala ndi moyo mpaka kalekale. Yehova analenga anthu m’njira yoti azifuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. (Mlaliki 3:11) Palibe makolo amene angasangalale kuona ana awo akukumana ndi mavuto komanso kufa, ndipo ndi mmenenso Yehova amamvera ndi anthufe. Komano ngati Mulungu anatilenga n’cholinga choti tizikhala ndi moyo mpaka kalekale, n’chifukwa chiyani timafa?

      N’CHIFUKWA CHIYANI TIMAFA?

      9. N’chifukwa chiyani tinganene kuti lamulo limene Yehova anapereka kwa Adamu ndi Hava linali losavuta kulitsatira?

      9 Adamu ali m’munda wa Edeni, Yehova anamuuza kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:9, 16, 17) Lamulo limeneli linali losavuta kulitsatira, ndipotu Yehova ndi amene anali ndi ufulu wouza Adamu ndi Hava zimene zinali zabwino kapena zoipa. Kumvera Yehova kukanasonyeza kuti ankamulemekeza. Kukanasonyezanso kuti ankayamikira zinthu zonse zomwe anawapatsa.

      10, 11. (a) Kodi Satana anatani kuti achititse Adamu ndi Hava kusamvera Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Adamu ndi Hava analibe chifukwa chomveka chowapangitsa kusamvera lamulo la Mulungu?

      10 N’zomvetsa chisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Yehova. Satana anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Hava anayankha kuti: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”—Genesis 3:1-3.

      11 Koma Satana anati: “Kufa simudzafa ayi. Mulungutu akudziwa kuti tsiku limene mudzadye chipatso cha mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:4-6) Satana ankafuna kuti Hava aziganiza zoti angathe kumasankha yekha zabwino kapena zoipa. Komanso anamunamiza pomuuza kuti sangafe ngati atadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa. Hava atamva zimenezi, anadya chipatso chimene Mulungu anawaletsa ndipo kenako anapatsanso mwamuna wake. Adamu ndi Hava ankadziwa kuti Yehova anawauza kuti asadzadye chipatsocho. Choncho kudya chipatsochi kunali kusamvera mwadala lamulo losavuta kutsatira komanso lomveka bwino limene Mulungu anawapatsa. Zimene anachitazi zinasonyezanso kuti sankalemekeza Atate wawo wakumwamba. Iwo analibe chifukwa chomveka chochitira zimenezi.

      12. N’chifukwa chiyani zinali zokhumudwitsa kwambiri pamene Adamu ndi Hava sanamvere Yehova?

      12 N’zomvetsa chisoni kuti makolo athu oyambirira sanalemekeze Mlengi wawo. Mwachitsanzo, kodi mungamve bwanji ngati ana anu atakuukirani n’kuyamba kuchita zinthu zotsutsana nanu? N’zoonekeratu kuti zingakupwetekeni kwambiri.

      Kulengedwa kwa Adamu

      Adamu analengedwa kuchokera kufumbi ndipo anabwereranso kufumbi

      13. Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamene anauza Adamu kuti “kufumbiko udzabwerera”?

      13 Pamene Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu, anataya mwayi wokhala ndi moyo mpaka kalekale. Yehova anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.” (Werengani Genesis 3:19.) Zimenezi zinkatanthauza kuti Adamu adzakhalanso fumbi ngati mmene zinalili asanalengedwe. (Genesis 2:7) Adamu atachimwa anafa ndipo anabwerera kufumbi.

      14. N’chifukwa chiyani timafa?

      14 Adamu ndi Hava akanamvera Mulungu, akanakhala alipobe mpaka pano. Koma kusamvera kwawo kunachititsa kuti achimwire Mulungu ndipo kenako anafa. Uchimo uli ngati matenda oopsa amene tinatengera kwa makolo athu oyambirira. Tonsefe timabadwa tili ochimwa ndipo n’chifukwa chake timafa. (Aroma 5:12) Koma zimenezi sizimene Mulungu ankafuna pamene ankalenga anthu. Mulungu safuna kuti anthu azimwalira ndipo Baibulo limati imfa ndi “mdani.”—1 Akorinto 15:26.

      TIMAKHALA OMASUKA CHIFUKWA CHODZIWA ZOONA

      15. Kodi kudziwa zoona zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira kumatithandiza bwanji?

      15 Kudziwa zoona pa nkhani ya imfa kumatithandiza kuti tisasocheretsedwe ndi mabodza osiyanasiyana. Baibulo limaphunzitsa kuti munthu akamwalira samva kupweteka kulikonse komanso sangathe kudana ndi wina aliyense. Sitingathe kulankhula naye ndipo iyenso sangalankhule nafe. Sitingamuthandize ndipo iyenso sangatithandize. Choncho sitiyenera kumuopa chifukwa sangativulaze. Komabe zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti munthu akafa amakhalabe ndi moyo kwinakwake ndipo tingamuthandize popereka ndalama kwa atsogoleri achipembedzo kapena anthu ena amene amaonedwa ngati oyera kuti amupempherere. Koma kudziwa zoona zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira, kumatithandiza kuti tisapusitsidwe ndi mfundo zabodza zimenezi.

      16. Kodi zipembedzo zambiri zimaphunzitsa bodza lotani lokhudza akufa?

      16 Satana amagwiritsa ntchito zipembedzo zonyenga pofuna kupusitsa anthu kuti azikhulupirira zoti munthu akafa amakakhalabe ndi moyo kwinakwake. Mwachitsanzo, atsogoleri azipembedzo ena amaphunzitsa kuti munthu akafa, mzimu wake umapitirizabe kukhala ndi moyo kwinakwake. Kodi zimenezi ndi zomwe chipembedzo chanu chimaphunzitsa, kapena chimaphunzitsa zimene Baibulo limanena? Satana amagwiritsirabe ntchito bodza pofuna kuchititsa anthu kuti asamakhulupirire Yehova.

      17. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mfundo yoti Mulungu amazunza anthu kumoto imanyozetsa Yehova?

      17 Zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa ndi zochititsa mantha kwambiri. Mwachitsanzo, zipembedzo zina zimanena kuti anthu amene amachita zoipa adzawotchedwa kumoto mpaka kalekale. Limeneli bodza ndipo kunena zimenezi kungakhale kuchitira mwano Yehova. Iye sangalole kuti anthu azizunzika mwa njira imeneyi. (Werengani 1 Yohane 4:8.) Kodi mungamve bwanji mutaona munthu wina akulanga mwana wake pomuwotcha manja pamoto? N’zodziwikiratu kuti mukhoza kumuona kuti ndi munthu wankhanza ndipo simungafune n’komwe kuti akhale mnzanu. Mmenemutu ndi mmene Satana amafuna kuti tizionera Yehova.

      18. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuopa akufa?

      18 Zipembedzo zina zimanena kuti munthu akafa, amasanduka mzimu. Zimaphunzitsanso kuti tikuyenera kulemekeza komanso kuopa mizimu imeneyi chifukwa ikhoza kukhala anzathu kapenanso adani athu oopsa kwambiri. Anthu ambiri amakhulupirira bodza limeneli. Ndipo zimenezi zimawachititsa kuopa anthu akufa n’kuyamba kuwalambira m’malo molambira Yehova. Koma musaiwale kuti anthu akufa sangamve kapena kuchita chilichonse, choncho sitiyenera kuwaopa. Yehova ndi amene anatilenga. Iye ndi Mulungu weniweni ndipo tiyenera kulambira iye yekha basi.—Chivumbulutso 4:11.

      19. Kodi kudziwa zenizeni zimene zimachitika munthu akamwalira n’kothandiza bwanji?

      19 Tikadziwa zoona zenizeni zokhudza imfa, timakhala omasuka ku zinthu zabodza zimene zipembedzo zina zimanena. Kudziwa zoona pa nkhani imeneyi kumatithandiza kumvetsa bwino zinthu zosangalatsa kwambiri zimene Yehova wakonza zokhudza moyo wathu komanso tsogolo lathu.

      20. Kodi tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?

      20 Zaka zambiri zapitazo, mtumiki wina wa Mulungu dzina lake Yobu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (Yobu 14:14) Kodi zingathekedi kuti munthu amene wamwalira akhalenso ndi moyo? Zimene Mulungu amatiuza m’Baibulo n’zosangalatsa kwambiri. Tiona zimenezi m’mutu wotsatira.

      a Anthu ena amakhulupirira kuti mzimu umapitiriza kukhalabe ndi moyo munthu akamwalira. Kuti mumve zambiri, onani Mawu Akumapeto 17 ndi 18.

      MFUNDO ZACHIDULE

      MFUNDO 1: MUNTHU AKAMWALIRA NDIYE KUTI MOYO WAKE WATHERA POMPO

      “Akufa sadziwa chilichonse.—Mlaliki 9:5

      Kodi chimachitika n’chiyani tikamwalira?

      • Salimo 146:3, 4; Mlaliki 9:6, 10

        Munthu akamwalira sangathe kuona, kumva komanso kuganiza.

      • Yohane 11:11-14

        Yesu anayerekeza imfa ndi tulo.

      MFUNDO 2: YEHOVA SANKAFUNA KUTI ANTHU AZIFA

      “Usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.”—Genesis 2:17

      N’chifukwa chiyani timamwalira?

      • Genesis 3:1-6

        Satana ananamiza Hava kuti ngati samvera lamulo la Mulungu loti asadye chipatso, sadzafa. Adamu ndi Hava anachimwa chifukwa sanamvere Yehova ndipo kenako anafa chifukwa cha zimenezi.

      • Genesis 3:19

        Adamu atamwalira sanakhalenso ndi moyo kulikonse.

      • Aroma 5:12

        Uchimo uli ngati matenda oopsa amene tinatengera kwa makolo athu oyambirira. Tonsefe timabadwa tili ochimwa ndipo n’chifukwa chake timafa.

      • 1 Akorinto 15:26

        Baibulo limanena kuti imfa ndi mdani.

      MFUNDO 3: TIMAKHALA OMASUKA CHIFUKWA CHODZIWA ZOONA

      “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo? Ndidzadikira . . . mpaka mpumulo wanga utafika.”—Yobu 14:14

      Kodi kudziwa zoona pa nkhani ya zimene zimachitika munthu akamwalira kungatithandize bwanji?

      • 1 Yohane 4:8

        Zimene zipembedzo zina zimanena zoti anthu amene amachita zoipa adzawotchedwa kumoto ndi bodza ndipo ndi kumuchitira mwano Yehova. Iye sangalole kuti anthu azizunzika mwa njira imeneyi.

      • Chivumbulutso 4:11

        Anthu ambiri amaopa anthu akufa moti amawalambira m’malo molambira Yehova. Koma Yehova ndi Mulungu woona ndipo tiyenera kulambira iye yekha basi.

  • Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
    • MUTU 7

      Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

      1-3. Kodi tonsefe ndi akapolo a chiyani, nanga Yehova adzatimasula bwanji?

      TAYEREKEZANI kuti akhoti agamula kuti mukakhale m’ndende kwa moyo wanu wonse pa mlandu womwe simunapalamule. Zimene agamulazo zikusonyeza kuti simudzatuluka mpaka kalekale. Apa mungaone kuti tsogolo lanu lawonongekeratu ndipo palibe chimene mungachite kuti mudzipulumutse. Ndiye tiyerekeze kuti mwadziwa zoti pali munthu wina amene ali ndi mphamvu zoti angakumasuleni ndipo walonjeza kuti akuthandizani. Kodi mungamve bwanji?

      2 Tonsefe ndi akapolo a imfa. Ngakhale titachita zotani, sitingathe kuithawa. Koma Yehova ali ndi mphamvu yoti angatimasule ku ukapolo umenewu. Iye analonjeza kuti “imfa . . . monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

      3 Taganizirani mmene tidzasangalalire pa nthawi imene sitidzakhalanso ndi nkhawa yoti tikhoza kumwalira. Ndipotu Yehova sikuti adzangothetsa imfa, koma adzaukitsanso anthu amene anamwalira kale. Kodi nkhani imeneyi si yosangalatsa? Yehova analonjeza kuti “anthu amene anafa” adzakhalanso ndi moyo. (Yesaya 26:19) Zimenezi ndi zomwe Baibulo limatanthauza likamanena kuti akufa adzauka.

      MMENE TIMAMVERA WACHIBALE KAPENA MNZATHU AKAMWALIRA

      4. (a) Kodi n’chiyani chingatilimbikitse pamene wachibale kapena mnzathu wamwalira? (b) Kodi ena mwa anzake apamtima a Yesu anali ndani?

      4 Wachibale wathu kapena mnzathu akamwalira, timakhala ndi chisoni chachikulu. Timathedwa nzeru chifukwa palibe chimene tingachite kuti munthuyo akhalenso ndi moyo. Koma zimene Baibulo limanena zimatitonthoza. (Werengani 2 Akorinto 1:3, 4.) Tiyeni tikambirane chitsanzo chimodzi chimene chikusonyeza kuti Yehova ndi Yesu akufunitsitsa kuukitsa achibale athu komanso anzathu amene anamwalira. Yesu ali padziko lapansi pano ankakonda kucheza ndi Lazaro komanso azichemwali ake, Marita ndi Mariya. Anthu amenewa ankagwirizana kwambiri ndi Yesu, moti Baibulo limati: “Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.” Koma patapita nthawi Lazaro anamwalira.—Yohane 11:3-5.

      5, 6. (a) Kodi Yesu anachita chiyani ataona achibale komanso anzake a Lazaro akulira? (b) N’chifukwa chiyani n’zolimbikitsa kudziwa mmene Yesu anamvera pa nkhani ya imfa?

      5 Yesu anapita kuti akalimbikitse Marita ndi Mariya. Marita atamva zoti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira. Iye anasangalala kuti Yesu wabwera, komabe ananena kuti: “Mukanakhala kuno mlongo wanga sakanamwalira.” Marita ankaona kuti Yesu wabwera mochedwa moti palibe chimene angachite. Kenako, Yesu ataona Mariya akulira, zinamukhudza kwambiri poona chisoni chimene anali nacho ndipo nayenso analira. (Yohane 11:21, 33, 35) Iye anali ndi chisoni chimene timakhala nacho wachibale kapena mnzathu akamwalira.

      6 N’zolimbikitsa kudziwa kuti Yesu amamva ngati mmene ifeyo timamvera mnzathu kapena m’bale wathu akamwalira. Ndipotu Yesu anatengera khalidwe limeneli kwa Atate ake. (Yohane 14:9) Yehova ali ndi mphamvu zothetsa imfa, ndipo aithetsa posachedwapa.

      “LAZARO, TULUKA!”

      7, 8. N’chifukwa chiyani Marita analetsa anthu kuti asachotse mwala umene anatsekera pamanda a Lazaro, koma kodi Yesu anachita chiyani?

      7 Yesu atafika pamanda amene Lazaro anaikidwa anapeza kuti khomo lake linali litatsekedwa ndi chimwala chachikulu. Yesu anauza anthu kuti: “Chotsani chimwalachi.” Koma Marita sankafuna kuti anthu achotse mwalawo chifukwa Lazaro anali atakhala m’mandamo masiku 4. (Yohane 11:39) Iye sankadziwa zimene Yesu ankafuna kuchita.

      Yesu waukitsa Lazaro ndipo achibale ake ndi anzake akusangalala kwambiri

      Taganizirani mmene achibale komanso anzake a Lazaro anasangalalira ataona kuti waukitsidwa.—Yohane 11:38-44

      8 Yesu anauza Lazaro kuti: “Tuluka!” Zimene Marita ndi Mariya anaona zinali zodabwitsa kwambiri chifukwa “amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro.” (Yohane 11:43, 44) Lazaro anakhalanso ndi moyo ndipo anapitiriza kukhala ndi achibale ake komanso anzake. Iwo ankatha kumugwira komanso kulankhula naye. Zinalitu zodabwitsa kwambiri kuona Yesu ataukitsa Lazaro.

      “KAMTSIKANA IWE, NDIKUNENA NDI IWE, ‘DZUKA!’”

      9, 10. (a) Kodi ndi ndani anam’patsa Yesu mphamvu zoukitsira akufa? (b) Kodi nkhani za m’Baibulo za anthu amene anaukitsidwa n’zofunika bwanji?

      9 Kodi Yesu ankaukitsa anthu ndi mphamvu zake? Ayi. Tikutero chifukwa asanaukitse Lazaro, iye anapemphera kwa Yehova ndipo ndi amene anam’patsa mphamvu zoukitsira Lazaro. (Werengani Yohane 11:41, 42.) Koma pali anthu enanso amene anaukitsidwa. Baibulo limanena za mtsikana wina wazaka 12 amene anadwala kwambiri. Bambo ake, a Yairo, anathedwa nzeru chifukwa mwana wawo anali yekhayu ndipo anapempha Yesu kuti amuchiritse. Yairo akulankhula ndi Yesu, anthu ena anabwera n’kumuuza kuti: “Mwana wanu uja wamwalira! Musiyeni mphunzitsiyu musamuvutitse.” Koma Yesu anauza Yairo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi, ndipo mwana wako apulumuka.” Kenako anapita limodzi ndi Yairo kunyumba kwake. Pamene ankayandikira kunyumbako, Yesu ayenera kuti ankamva komanso kuona anthu akulira. Iye anawauza kuti: “Tontholani, pakuti mwanayu sanamwalire ayi, koma akugona.” Makolo ake a mwanayu ayenera kuti anadabwa ndi zimene Yesu ananenazi. Yesu anauza aliyense kuti atuluke ndipo anatengana ndi makolo a mwanayo n’kupita kuchipinda kumene mwanayo anam’goneka. Iye anagwira dzanja la mwanayo n’kunena kuti: “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!” Taganizirani mmene makolo ake anasangalalira ataona mwana wawoyo atadzuka n’kuyamba kuyenda. Apa Yesu anali ataukitsa mwanayo. (Maliko 5:22-24, 35-42; Luka 8:49-56) Kuchokera nthawi imeneyi, makolowo ayenera kuti ankati akaona mwana wawoyo ankakumbukira zimene Yehova anawachitira pogwiritsa ntchito Yesu.a

      10 Anthu amene anaukitsidwa ndi Yesu anamwaliranso patapita nthawi. Komabe nkhani za anthu amenewa ndi zofunika kwambiri chifukwa zimatithandiza kukhulupirira kuti Yehova akufunitsitsa kuukitsa anthu ndipo palibe chimene chingamulepheretse.

      ZIMENE TINGAPHUNZIRE PA NKHANI ZA ANTHU AMENE ANAUKITSIDWA

      Anthu akuyang’ana Petulo akuukitsa Dorika

      Mtumwi Petulo anaukitsa Dorika.—Machitidwe 9:36-42

      Mkazi wamasiye akukumbatira mwana wake amene waukitsidwa ndi Eliya

      Eliya anaukitsa mwana wa mzimayi wina wamasiye.—1 Mafumu 17:17-24

      11. Malinga ndi zimene lemba la Mlaliki 9:5 limanena, kodi Lazaro atamwalira ankadziwa zimene zinkachitika?

      11 Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti “akufa sadziwa chilichonse.” Ndi mmenenso zinalili ndi Lazaro. (Mlaliki 9:5) Monga mmene Yesu ananenera, zinali ngati ali m’tulo. (Yohane 11:11) Pa nthawi imene anali m’manda, Lazaro ‘sankadziwa chilichonse.’

      12. Kodi tikudziwa bwanji kuti Lazaro anaukitsidwadi?

      12 Anthu ambiri analipo pamene Yesu ankaukitsa Lazaro. Ngakhale anthu amene ankadana ndi Yesu anadziwa kuti Yesu waukitsa Lazaro. Zinthu zimenezi zimasonyeza kuti nkhani imeneyi si yongopeka. (Yohane 11:47) Komanso anthu ambiri anapita kukaona Lazaro, zomwe zinachititsa kuti ayambe kukhulupirira zoti Yesu anatumizidwa ndi Mulungu. Anthu amene ankadana ndi Yesu sanasangalale ndi zimenezi choncho anakonza zoti aphe Yesu ndi Lazaro yemwe.—Yohane 11:53; 12:9-11.

      13. N’chifukwa chiyani sitikayikira zoti Yehova adzaukitsa anthu amene anamwalira?

      13 Yesu ananena kuti “onse ali m’manda achikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu onse amene Yehova akuwakumbukira adzakhalanso ndi moyo. Koma kuti Yehova aukitse munthu, afunika kukumbukira zinthu zonse zokhudza munthuyo. Kodi angakwanitse kuchita zimenezi? Kuti tipeze yankho, taganizirani za nyenyezi zambirimbiri zimene zili kumwamba. Baibulo limanena kuti Yehova amadziwa dzina la nyenyezi iliyonse. (Werengani Yesaya 40:26.) Ngati amatha kukumbukira mayina a nyenyezi zonse, ndiye kuti akhozanso kukumbukira mosavuta chilichonse chokhudza anthu amene akufuna kudzawaukitsa. Mfundo inanso yofunika kwambiri ndi yakuti Yehova ndi amene analenga zinthu zonse, choncho ali ndi mphamvu youkitsa anthu amene anamwalira.

      14, 15. Kodi zimene Yobu ananena zimatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya kuukitsidwa kwa akufa?

      14 Yobu, yemwe anali munthu wokhulupirika, ankakhulupirira kuti akufa adzauka. Iye anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” Kenako anauza Yehova kuti: “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” Mawu amenewa akusonyeza kuti Yobu ankadziwa kuti Yehova adzaukitsa akufa ndipo amachita kulakalaka kuti nthawi imeneyi ifike.—Yobu 14:13-15.

      15 Kodi inuyo mumamva bwanji chifukwa chodziwa kuti akufa adzauka? Mwina mungamadzifunse kuti, ‘Kodi abale anga komanso anzanga amene anamwalira nawonso adzaukitsidwa?’ Zimatilimbikitsa kudziwa kuti Yehova amafunitsitsa kuukitsa anthu amene anamwalira. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani ya anthu amene adzaukitsidwe komanso kumene adzakhale akadzaukitsidwa.

      “ADZAMVA MAWU AKE NDIPO ADZATULUKA”

      16. Kodi anthu amene adzaukitsidwe kuti akhale ndi moyo padziko lapansi adzasangalala ndi zinthu zotani?

      16 Anthu amene ankaukitsidwa m’mbuyomu, ankapitiriza kukhala ndi achibale awo komanso anzawo padziko lapansi pompano. Zimenezi ndi zomwe zidzachitikenso m’tsogolomu, kungoti nthawi imeneyo zidzakhala bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti anthu amene adzaukitsidwe n’kumakhala padziko lapansili, adzakhala ndi mwayi wosangalala ndi moyo mpaka kalekale ndipo sadzafanso. Dziko limene azidzakhala lidzakhala losiyana kwambiri ndi lomwe tikukhalali. Nthawi imeneyo sikudzakhala nkhondo, uchigawenga ndiponso matenda.

      17. Kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe?

      17 Koma kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe? Yesu ananena kuti “onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Lemba la Chivumbulutso 20:13 limanena kuti: “Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Nayonso imfa ndi Manda zinapereka akufa amene anali mmenemo.” Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ambirimbiri amene anamwalira adzaukitsidwa. Mtumwi Paulo ananenanso kuti “olungama ndi osalungama omwe” adzaukitsidwa. (Werengani Machitidwe 24:15.) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?

      M’Paradaiso, anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhala limodzi ndi abale awo komanso anzawo

      M’Paradaiso, anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhala limodzi ndi abale awo komanso anzawo

      18. Kodi anthu “olungama” amene adzaukitsidwe ndi ati?

      18 “Olungama” akuphatikizapo atumiki a Yehova okhulupirika omwe anakhala ndi moyo Yesu asanabwere padziko lapansi. Anthu monga Nowa, Abulahamu, Sara, Mose, Rute ndi Esitere adzaukitsidwa kuti adzapitirize kukhala ndi moyo padzikoli. Mungawerenge zokhudza amuna ndi akazi amenewa m’chaputala 11 cha buku la Aheberi. Nanga bwanji za atumiki okhulupirika a Yehova amene akumwalira nthawi yathu ino? Nawonso ndi “olungama,” choncho adzaukitsidwa.

      19. Kodi anthu “osalungama” ndi ati? Nanga Yehova adzawapatsa mwayi wotani?

      19 “Osalungama” akuphatikizapo anthu ambirimbiri omwe analibe mwayi wophunzira za Yehova. Ngakhale kuti anthu amenewa anamwalira, Yehova sanawaiwale. Iye adzawaukitsa n’kuwapatsa mwayi woti amudziwe komanso kumutumikira.

      20. Kodi anthu ena sadzaukitsidwa chifukwa chiyani?

      20 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti munthu aliyense amene anamwalira adzaukitsidwa? Ayi. Yesu ananena kuti anthu ena sadzaukitsidwa. (Luka 12:5) Kodi ndani adzasankhe anthu oyenera kuukitsidwa? Yehova ndi amene ali Woweruza wamkulu koma waperekanso mphamvu kwa Yesu yokhala “woweruza anthu amoyo ndi akufa.” (Machitidwe 10:42) Aliyense amene angaweruzidwe kuti ndi woipa ndipo sakufuna kusintha sadzaukitsidwa.—Onani Mawu Akumapeto 19.

      ENA AMAUKITSIDWA N’KUPITA KUMWAMBA

      21, 22. (a) Kodi anthu amene adzaukitsidwe n’kupita kumwamba adzaukitsidwa ndi thupi lotani? (b) Kodi ndi ndani anali woyamba kuukitsidwa n’kupita kumwamba?

      21 Baibulo limanenanso kuti anthu ena adzapita kukakhala kumwamba. Munthu amene wapatsidwa mwayi woti adzapite kumwamba, saukitsidwa ndi thupi lofanana ndi limene anali nalo poyamba. Anthu amene amapita kumwamba amaukitsidwa ndi thupi lauzimu.

      22 Yesu ndi amene anali munthu woyamba kuukitsidwa mwanjira imeneyi. (Yohane 3:13) Patadutsa masiku atatu kuchokera pamene Yesu anaphedwa, Yehova anamuukitsa. (Salimo 16:10; Machitidwe 13:34, 35) Yesu sanaukitsidwe ndi thupi limene anali nalo ali padziko lapansi. Mtumwi Petulo anafotokoza kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” (1 Petulo 3:18) Yesu anaukitsidwa ngati munthu wamphamvu wauzimu. (1 Akorinto 15:3-6) Koma Baibulo limafotokoza kuti palinso anthu ena amene adzaukitsidwe ndi thupi lotereli.

      23, 24. Kodi anthu amene Yesu anawatchula kuti “kagulu ka nkhosa” ndi ndani, ndipo alipo angati?

      23 Yesu asanamwalire anauza ophunzira ake okhulupirika kuti: “Ndikupita kukakukonzerani malo.” (Yohane 14:2) Zimenezi zikusonyeza kuti anthu ena okhulupirika adzaukitsidwa n’kupita kumwamba kukakhala ndi Yesu. Kodi anthu amenewa adzakhala ochuluka bwanji? Yesu ananena kuti kadzakhala “kagulu ka nkhosa,” kutanthauza kuti adzakhala ochepa. (Luka 12:32) Mtumwi Yohane anatchula chiwerengero chawo chenicheni chifukwa anaona Yesu “ataimirira [kumwamba] paphiri la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000.”—Chivumbulutso 14:1.

      24 Kodi Akhristu 144,000 amenewa adzaukitsidwa liti? Baibulo limafotokoza kuti zimenezi zidzachitika Yesu akadzayamba kulamulira kumwamba. (1 Akorinto 15:23) Panopa tikukhala mu nthawi imeneyi ndipo anthu ochuluka a m’gulu limeneli anaukitsidwa kale n’kupita kumwamba. Akhristu a m’gulu limeneli omwe adakali ndi moyo panopa ngati atamwalira amaukitsidwa nthawi yomweyo n’kupita kumwamba. Komabe anthu ambiri adzaukitsidwa m’tsogolo ndipo adzasangalala ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansi.

      25. Kodi tidzakambirana zotani m’mutu wotsatira?

      25 Posachedwapa Yehova amasula anthu ku ukapolo wa imfa ndipo imfa sidzakhalaponso mpaka kalekale. (Werengani Yesaya 25:8.) Koma kodi anthu amene adzapite kumwamba azikachita chiyani? Baibulo limanena kuti azikalamulira ndi Yesu mu Ufumu wake. Tidzakambirana zambiri zokhudza ufumu umenewu m’mutu wotsatira.

      a M’Baibulo muli nkhani zinanso za anthu amene anaukitsidwa. Anthu amenewa anali ana, akuluakulu, amuna, akazi, Aisiraeli komanso anthu amitundu ina. Mukhoza kuwerenga nkhani zimenezi pa 1 Mafumu 17:17-24; 2 Mafumu 4:32-37; 13:20, 21; Mateyu 28:5-7; Luka 7:11-17; 8:40-56; Machitidwe 9:36-42; 20:7-12.

      MFUNDO ZACHIDULE

      MFUNDO 1: YEHOVA ADZATHETSA IMFA

      “Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:26

      Kodi Baibulo limatitonthoza bwanji pamene munthu wina wamwalira?

      • 2 Akorinto 1:3, 4

        Timakhala ndi chisoni chachikulu wachibale wathu kapena mnzathu akamwalira, koma Baibulo limatitonthoza.

      • Yesaya 25:8; 26:19

        Yehova ali ndi mphamvu zothetseratu imfa. Ndipo iye adzaukitsa anthu amene anamwalira.

      MFUNDO 2: TIYENERA KUKHULUPIRIRA ZOTI ANTHU AMENE ANAMWALIRA ADZAUKITSIDWA

      “Kamtsikana iwe, ndikunena ndi iwe, Dzuka!”—Maliko 5:41

      N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti anthu amene anamwalira adzauka?

      • Yohane 11:1-44

        Yesu anaukitsa Lazaro.

      • Maliko 5:22-24, 35-42

        Yesu anaukitsa kamtsikana.

      • Yohane 11:41, 42

        Yesu ankaukitsa anthu akufa pogwiritsa ntchito mphamvu zimene Yehova anamupatsa.

      • Yohane 12:9-11

        Anthu ambiri anadzionera okha pamene Yesu ankaukitsa anthu akufa ndipo ngakhale anthu amene ankadana naye ankadziwa kuti iye ankatha kuukitsa anthu akufa.

      MFUNDO 3: YEHOVA ADZAUKITSA ANTHU MABILIYONI AMBIRI AMENE ANAMWALIRA

      “Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.”—Yobu 14:13-15

      Kodi ndi ndani amene adzaukitsidwe?

      • Yohane 5:28, 29

        Yehova adzaukitsa anthu onse amene iye akuwakumbukira.

      • Machitidwe 24:15

        Anthu olungama komanso osalungama adzuukitsidwa.

      • Yesaya 40:26

        Yehova amatha kukumbukira dzina la nyenyezi iliyonse. Choncho adzathanso kukumbukira chilichonse chokhudza anthu amene akufuna kudzawaukitsa.

      MFUNDO 4: ANTHU ENA AMAUKITSIDWA N’KUPITA KUMWAMBA

      “Ndikupita kukakukonzerani malo.”—Yohane 14:2

      Kodi ndi ndani amene amaukitsidwa n’kupita kumwamba?

      • 1 Petulo 3:18

        Yesu anali munthu woyamba amene anaukitsidwa n’kupita kumwamba.

      • Luka 12:32

        Yesu ananena kuti kagulu kochepa ka ophunzira ake ndi kamene kadzaukitsidwe n’kupita kumwamba.

      • Chivumbulutso 14:1

        Yehova wasankha anthu okwana 144,000 kuti akakhale kumwamba.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena