Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 212
  • Kugawa Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugawa Dziko
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Malo otetezeka komanso ntchito yofunika
  • Malo ofanana
  • ‘Mugawane Dzikoli Kuti Likhale Cholowa Chanu’
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • ‘Ika Mtima Wako pa’ Kachisi wa Mulungu!
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Dzina la Mzindawo Lidzakhala Lakuti Yehova Ali Kumeneko”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • “Kachisi” ndi “Kalonga” Lerolino
    Nsanja ya Olonda—1999
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 212
Munthu wooneka ngati kopa akuonetsa Ezekieli dziko limene anthu adzalandire ngati cholowa.

BOKOSI 20A

Kugawa Dziko

Mmene anafotokozera malire oyezedwa bwino adzikolo, zinatsimikizira Ayuda amene anali ku ukapolo kuti dziko lawo lokondedwa lidzabwezeretsedwadi. Kodi masomphenyawa akutiphunzitsa chiyani masiku ano? Onani zinthu ziwiri zimene tikuzipeza m’masomphenyawa:

Mapu amene akusonyeza malire a dziko limene anthu amene adzabwerere kwawo kuchokera ku ukapolo adzalandire ngati cholowa chawo mogwirizana ndi zimene Ezekieli analemba. Gawo limene fuko lililonse linalandira linali lofanana kuyambira kumpoto mpaka kumwera kuyambira ndi fuko la Dani kenako la Aseri, Nafitali, Manase, Efuraimu, Rubeni, Yuda, Chopereka (kachigawo ka woyang’anira), Benjamini, Simiyoni, Isakala, Zebuloni, ndi Gadi.

Malo otetezeka komanso ntchito yofunika

Munthu aliyense amene adzabwerere kwawo kuchokera ku ukapolo adzakhala ndi cholowa m’Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso atumiki onse a Yehova ali ndi malo m’paradaiso wauzimu. Kaya tikuchita zambiri kapena zochepa m’gulu la Yehova, tili ndi malo otetezeka komanso ntchito yofunika kwambiri m’paradaiso wauzimu. Yehova amaona kuti atumiki ake onse ndi ofanana komanso ndi amtengo wapatali.

Malo ofanana

M’masomphenya a Ezekieli, dera lililonse m’Dziko Lolonjezedwa lobwezeretsedwa, linkathandiza anthu okhala m’dziko limenelo kupeza zinthu zabwino za m’dzikomo mofanana. Mofanana ndi zimenezi, masiku anonso Yehova wapereka mwayi wofanana kwa atumiki ake onse wopeza madalitso m’paradaiso wauzimu.

Bwererani ku mutu 20, ndime 5-11

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena