Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rr tsamba 76-77
  • Mawu Odziwika Kwambiri Opezeka M’buku la Ezekieli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mawu Odziwika Kwambiri Opezeka M’buku la Ezekieli
  • Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Mwana wa Munthu”
  • “. . . Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”
  • “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa”
  • Mmene Yehova Amatithandizira Kukwaniritsa Utumiki Wathu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • “Mapeto Akufikira”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • “Lambira Mulungu”
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
  • Kodi Kulambira N’kutani?
    Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
Onani Zambiri
Yehova Wabwezeretsa Kulambira Koyera
rr tsamba 76-77

BOKOSI 7B

Mawu Odziwika Kwambiri Opezeka M’buku La Ezekieli

“Mwana wa Munthu”

AKUPEZEKA MALO OPOSA 90

Kwa maulendo oposa 90, Ezekieli akutchulidwa kuti “mwana wa munthu.” (Ezek. 2:1) Pochita zimenezi Yehova anamukumbutsa kuti anali munthu ngakhale kuti anapatsidwa utumiki wapadera. N’zochititsa chidwi kuti mu nkhani za m’Mauthenga Abwino, Yesu akutchulidwa kuti “Mwana wa munthu” maulendo 80, kusonyeza kuti anali munthu weniweni osati mngelo amene anavala thupi la munthu.​—Mat. 8:20.

“. . . Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”

AKUPEZEKA MALO OPOSA 50

Kwa maulendo oposa 50, Ezekieli analemba zimene Mulungu ananena kuti anthu ‘adzadziwa kuti ine ndine Yehova,’ kusonyeza kuti Yehova yekha ndi amene ali woyenera kulambiridwa.​—Ezek. 6:7.

“Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa”

AKUPEZEKA MALO 217

Mawu akuti “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa” akupezeka malo 217. Zimenezi zathandiza kuti dzina la Mulungu lidziwike komanso zikutsindika mfundo yakuti chilengedwe chonse chikuyenera kugonjera Yehova.​—Ezek. 2:4.

Bwererani ku mutu 7, onani ndime 28

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena