-
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 31
Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
Uthenga wofunika kwambiri m’Baibulo ndi wokhudza Ufumu wa Mulungu. Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu umenewu pokwaniritsa cholinga chimene ali nacho chokhudza dziko lapansili. Ndiye kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani? Tikudziwa bwanji kuti Ufumuwu ukulamulira panopa? Ndi zinthu ziti zimene Ufumuwu wachita kale? Nanga udzachita zotani kutsogoloku? Mafunsowa ayankhidwa m’phunziroli komanso m’maphunziro awiri otsatira.
1. Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, nanga Mfumu yake ndi ndani?
Ufumu wa Mulungu ndi boma limene linakhazikitsidwa ndi Yehova Mulungu. Mfumu yake ndi Yesu Khristu ndipo akulamulira ali kumwamba. (Mateyu 4:17; Yohane 18:36) Ponena za Yesu, Baibulo limati: “Iye adzalamulira monga Mfumu . . . kwamuyaya.” (Luka 1:32, 33) Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzalamulira anthu onse padzikoli.
2. Kodi ndi ndani amene adzalamulire ndi Yesu?
Yesu sadzalamulira yekha. Anthu ochokera “mu fuko lililonse, chilankhulo chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse . . . adzakhala mafumu olamulira dziko lapansi.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi anthu angati amene adzalamulire ndi Khristu? Kungoyambira pamene Yesu anabwera padziko lapansi, anthu ambiri akhala otsatira ake ndipo panopa alipo mamiliyoni ambiri. Koma ndi anthu okwana 144,000 okha amene adzapite kumwamba kukalamulira ndi Yesu. (Werengani Chivumbulutso 14:1-4.) Akhristu ena onse adzakhala padziko lapansi ndipo azidzalamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.—Salimo 37:29.
3. Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?
Ngakhale olamulira a dzikoli atayesetsa bwanji kuchita zinthu zabwino, iwo sangakwanitse kuchita zonse zimene akufuna. Pakapita nthawi amalowedwa m’malo ndi olamulira ena odzikonda kwambiri omwe safuna kuthandiza anthu. Mosiyana ndi olamulira amenewa, Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu sadzalowedwa m’malo ndi wina aliyense. Mulungu wakhazikitsa “ufumu umene sudzawonongedwa.” (Danieli 2:44) Yesu adzalamulira dziko lonse lapansi ndipo sazidzakondera mtundu winawake wa anthu. Yesu ndi wachikondi, wachifundo komanso wachilungamo ndipo adzaphunzitsa anthu kuti azidzasonyezana makhalidwe amenewa.—Werengani Yesaya 11:9.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake Ufumu wa Mulungu uli wabwino kwambiri kuposa maboma a anthu.
4. Ufumu wa Mulungu udzalamulira dziko lonse lapansi
Yesu Khristu ali ndi mphamvu zolamulira dzikoli kuposa olamulira onse pa dzikoli. Werengani Mateyu 28:18, kenako mukambirane funso ili:
Kodi ulamuliro wa Yesu umaposa bwanji ulamuliro wa anthu?
Maboma a anthu amasinthasintha ndipo dziko lililonse limakhala ndi wolamulira wake. Nanga bwanji Ufumu wa Mulungu? Werengani Danieli 7:14, kenako mukambirane mafunso awa:
Popeza Ufumu wa Mulungu “sudzawonongedwa,” kodi zimenezi zili ndi ubwino wotani?
Kodi mukuganiza kuti tidzapindula bwanji Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dziko lonse?
5. Maboma a anthu ayenera kuchotsedwa
N’chifukwa chiyani Ufumu wa Mulungu uyenera kulowa m’malo mwa maboma a anthu? Onerani VIDIYO, kenako mukambirane funso lotsatirali:
Kodi zotsatira za ulamuliro wa anthu ndi zotani?
Werengani Mlaliki 8:9, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuona kuti n’zoyenera kuti Ufumu wa Mulungu udzalowe m’malo mwa maboma a anthu? N’chifukwa chiyani mukutero?
6. Ufumu wa Mulungu uli ndi olamulira amene amatimvetsa
Popeza Yesu, yemwe ndi Mfumu yathu anakhalapo munthu, iye ‘amatimvera chisoni pa zofooka zathu.’ (Aheberi 4:15) Yehova anasankha amuna ndi akazi okwana 144,000 omwe adzalamulire ndi Yesu kuchokera “mu fuko lililonse, chilankhulo chilichonse, mtundu uliwonse ndi dziko lililonse.”—Chivumbulutso 5:9.
Popeza kuti Yesu komanso onse amene adzalamulire naye anakhalapo anthu, kodi mukuona kuti zimenezi n’zolimbikitsa? N’chifukwa chiyani mukutero?
Yehova wakhala akusankha amuna ndi akazi ochokera m’mitundu yosiyanasiyana kuti adzalamulire ndi Yesu
7. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri
Maboma a anthu amapanga malamulo omwe amayenera kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Nawonso Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo amene nzika zake zimayenera kuwatsatira. Werengani 1 Akorinto 6:9-11, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi mukuganiza kuti zinthu zidzakhala bwanji padzikoli aliyense akamadzatsatira malamulo a Mulungu?a
Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizitsatira malamulo ake, kodi mukuganiza kuti zimene Yehova amafunazi n’zoyenera? N’chifukwa chiyani mukutero?
Ndi mfundo iti imene ikusonyeza kuti anthu amene satsatira malamulo amenewa atha kusintha?—Onani vesi 11.
Maboma amakhazikitsa malamulo n’cholinga chofuna kuthandiza ndi kuteteza nzika zawo. Ufumu wa Mulungu uli ndi malamulo abwino kwambiri omwe amathandiza ndi kuteteza nzika zake
MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani?”
Kodi mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lili kumwamba ndipo udzalamulira dziko lonse lapansi.
Kubwereza
Kodi ndi ndani amene adzalamulire mu Ufumu wa Mulungu?
Kodi Ufumu wa Mulungu umaposa bwanji maboma a anthu?
Kodi Yehova amayembekezera kuti nzika za Ufumu wake zizichita chiyani?
ONANI ZINANSO
Onani zimene Yesu anaphunzitsa zokhudza komwe Ufumu wa Mulungu uli.
“Kodi Ufumu wa Mulungu Uli Mumtima Mwanu?” (Nkhani yapawebusaiti)
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amaona kuti kukhala okhulupirika ku Ufumu wa Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala okhulupirika ku maulamuliro a anthu?
Onani zomwe Baibulo limafotokoza zokhudza anthu 144,000 omwe Yehova amawasankha kuti adzalamulire ndi Yesu.
“Kodi Ndi Ndani Amene Amapita Kumwamba?” (Nkhani yapawebusaiti)
N’chiyani chinathandiza mayi wina yemwe anali m’ndende kukhulupirira kuti Mulungu yekha ndi amene angabweretse chilungamo padzikoli?
“Kumene Ndinadziwira Yemwe Adzathetse Kupanda Chilungamo” (Galamukani!, November 2011)
-
-
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira PanopaMungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 32
Ufumu wa Mulungu Ukulamulira Panopa
Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira kumwamba m’chaka cha 1914. Chaka chimenechi n’chimenenso masiku otsiriza a ulamuliro wa anthu anayamba. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Tiona ulosi wina wa m’Baibulo, zinthu zimene zakhala zikuchitika padzikoli ndiponso makhalidwe amene anthu akhala akusonyeza kuyambira mu 1914.
1. Kodi Baibulo linalosera chiyani?
Buku la m’Baibulo la Danieli linalosera kuti Ufumu wa Mulungu udzayamba kulamulira kumapeto kwa “nthawi zokwana 7.” (Danieli 4:16, 17) Patapita zaka zambiri Yesu anatchula nthawi imeneyi kuti ndi “nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu,” ndipo anaphunzitsa kuti nthawiyi inali isanathe. (Luka 21:24) Mogwirizana ndi zimene tione, nthawi zokwana 7 zimenezi zinatha mu 1914.
2. Kodi ndi zinthu ziti zomwe zakhala zikuchitika padzikoli kuyambira mu 1914, nanga anthu akhala akusonyeza makhalidwe otani?
Ophunzira a Yesu anafunsa kuti: “Kodi . . . chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a nthawi ino chidzakhala chiyani?” (Mateyu 24:3) Poyankha, Yesu anawafotokozera zinthu zambiri zimene zidzachitike iye akadzayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Zina mwa zinthu zimenezi ndi nkhondo, njala komanso zivomerezi. (Werengani Mateyu 24:7.) Baibulo linaloseranso kuti ‘m’masiku otsiriza’ anthu adzakhala ndi makhalidwe oipa omwe adzachititse kuti moyo ukhale wovuta kwambiri. (2 Timoteyo 3:1-5) Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika kwambiri makamaka kuyambira mu 1914.
3. N’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zoipa kwambiri kungochokera pamene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira?
Yesu atangokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anapita kukamenyana ndi Satana komanso ziwanda zake. Satana anagonja pa nkhondoyi. Baibulo limanena kuti: “Iye anaponyedwa padziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.” (Chivumbulutso 12:9, 10, 12) Satana ndi wokwiya kwambiri chifukwa akudziwa kuti awonongedwa posachedwapa. Choncho iye ndi amene akuchititsa kuti padzikoli pakhale mavuto ambiri chonchi. Zimenezi zikutithandiza kumvetsa chifukwa chake zinthu zafika poipa kwambiri padzikoli. Koma chosangalatsa n’chakuti Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto onsewa.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti muone zimene zimatithandiza kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914 komanso mmene zimenezi zimatikhudzira.
4. Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914
Mulungu anachititsa kuti Mfumu Nebukadinezara ilote maloto a zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolo. Zimene Danieli ananena pomasulira malotowo zinasonyeza kuti malotowo anali okhudza ulamuliro wa Nebukadinezara komanso Ufumu wa Mulungu.—Werengani Danieli 4:17.a
Werengani Danieli 4:20-26, kenako mugwiritse ntchito tchati kuti muyankhe mafunso otsatirawa:
(A) Kodi Nebukadinezara anaona chiyani m’maloto ake?—Onani vesi 20 ndi 21.
(B) N’chiyani chimene chinachitikira mtengo umene analota?—Onani vesi 23.
(C) N’chiyani chimene chinachitika kumapeto kwa “nthawi zokwana 7”?—Onani vesi 26.
Kugwirizana kwa Maloto a Mtengo ndi Ufumu wa Mulungu
ULOSI (Danieli 4:20-36)
Ufumu
(A) Mtengo waukulu
Ufumu unasiya kulamulira
(B) “Gwetsani mtengowo,” ndipo ‘padutse nthawi zokwana 7’
Ufumu unayambiranso kulamulira
(C) “Mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu”
Pa kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwu . . .
(D) Kodi mtengo unkaimira ndani?—Onani vesi 22.
(E) Chinachitika n’chiyani kuti asiye kaye kulamulira?—Werengani Danieli 4:29-33.
(F) N’chiyani chinachitikira Nebukadinezara “nthawi zokwana 7” zitatha?—Werengani Danieli 4:34-36.
KUKWANIRITSIDWA KOYAMBA
Ufumu
(D) Nebukadinezara, Mfumu ya Babulo
Ufumu unasiya kulamulira
(E) Pambuyo pa chaka cha 606 B.C.E., Nebukadinezara anapenga ndipo sanathe kulamulira kwa zaka 7
Ufumu unayambiranso kulamulira
(F) Nebukadinezara anachira misala yake ija ndipo anayambiranso kulamulira
Pa kukwaniritsidwa kwachiwiri kwa ulosiwu . . .
(G) Kodi mtengo unkaimira ndani?—Werengani 1 Mbiri 29:23.
(H) Chinachitika n’chiyani kuti asiye kaye kulamulira? Nanga tikudziwa bwanji kuti ufumuwo unali usanayambebe kulamulira pa nthawi imene Yesu anali padzikoli?—Werengani Luka 21:24.
(I) Kodi ufumuwu unayambiranso liti kulamulira, nanga unayamba kulamulira kuti?
KUKWANIRITSIDWA KWACHIWIRI
Ufumu
(G) Mafumu a Isiraeli amene ankaimira ulamuliro wa Mulungu
Ufumu unasiya kulamulira
(H) Yerusalemu anawonongedwa zomwe zinachititsa kuti mafumu a Isiraeli asiye kaye kulamulira kwa zaka 2,520
Ufumu unayambiranso kulamulira
(I) Yesu akuyamba kulamulira kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu
Kodi nthawi zokwana 7 zikuimira nthawi yaitali bwanji?
Mavesi ena a m’Baibulo amatithandiza kumvetsa bwino zimene mavesi ena akutanthauza. Mwachitsanzo, buku la Chivumbulutso limanena kuti nthawi zitatu ndi hafu n’zofanana ndi masiku 1,260. (Chivumbulutso 12:6, 14) Choncho nthawi zokwana 7 ndi kuwirikiza kawiri masiku 1,260 zomwe ndi masiku 2,520. Nthawi zina m’Baibulo mawu akuti tsiku amaimira chaka. (Ezekieli 4:6) Ndi mmenenso zilili ndi nthawi zokwana 7 zotchulidwa m’buku la Danieli. Nthawizi zimaimira zaka 2,520.
5. Dzikoli lasintha kwambiri kuyambira mu 1914
Yesu ananeneratu zinthu zomwe zidzachitike padzikoli akadzakhala Mfumu. Werengani Luka 21:9-11, kenako mukambirane funso ili:
Ndi zinthu ziti zimene zatchulidwa palembali, zimene inuyo munaona zikuchitika kapena kumva kuti zachitika?
Mtumwi Paulo anafotokoza makhalidwe amene anthu adzakhale nawo m’masiku otsiriza. Werengani 2 Timoteyo 3:1-5, kenako mukambirane funso ili:
Mogwirizana ndi lembali, ndi makhalidwe ati amene inuyo mukuona kuti anthu akusonyeza kwambiri masiku ano?
6. Muzisonyeza kuti mumakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira
Werengani Mateyu 24:3, 14, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi ndi ntchito yofunika kwambiri iti imene ikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira?
Mungatani kuti muyambe kugwira nawo ntchitoyi?
Ufumu wa Mulungu ukulamulira panopa ndipo posachedwapa uyamba kulamulira dziko lonse lapansi. Werengani Aheberi 10:24, 25, kenako mukambirane funso ili:
Kodi aliyense wa ife ayenera kuchita chiyani pamene ‘tikuona kuti tsikulo likuyandikira’?
Mungatani mutakhala kuti mwaphunzira mfundo inayake yomwe ikhoza kuthandiza komanso kupulumutsa anthu?
MUNTHU WINA ATAKUFUNSANI KUTI: “N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amakonda kunena kuti chaka cha 1914 ndi chapadera?”
Kodi mungamuyankhe bwanji?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ulosi wa m’Baibulo komanso zinthu zimene zikuchitika padzikoli, zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira. Tikamalalikira ndi kuchita nawo misonkhano yampingo timasonyeza kuti timakhulupirira zimenezi.
Kubwereza
Kodi chinachitika n’chiyani kumapeto kwa nthawi zokwana 7 zotchulidwa m’buku la Danieli?
N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulira mu 1914?
Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ukulamulira panopa?
ONANI ZINANSO
Onani zimene olemba mbiri ndiponso anthu ena amanena zokhudza mmene dzikoli linasinthira kuyambira mu 1914.
“Nthawi Imene Makhalidwe Analowa Pansi Kwambiri” (Galamukani!, April 2007)
Werengani kuti muone mmene ulosi wopezeka pa Mateyu 24:14 unakhudzira moyo wa munthu wina.
“Ndinkakonda Kwambiri Masewera a Baseball Kuposa Chilichonse” (Nsanja ya Olonda Na. 3 2017)
Kodi tikudziwa bwanji kuti ulosi umene umapezeka m’buku la Danieli chaputala 4 umanena za Ufumu wa Mulungu?
“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 1)” (Nsanja ya Olonda, October 1, 2014)
N’chiyani chikusonyeza kuti “nthawi zokwana 7” zimene zinatchulidwa m’buku la Danieli chaputala 4, zinatha mu 1914?
“Kodi Ufumu wa Mulungu Unayamba Liti Kulamulira? (Gawo 2)” (Nsanja ya Olonda, November 1, 2014)
a Werengani nkhani ziwiri zomalizira zomwe zili pagawo lakuti, Onani Zinanso m’phunziroli.
-
-
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
-
-
PHUNZIRO 33
Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?
Ufumu wa Mulungu unayamba kale kulamulira. Posachedwapa Ufumuwu ubweretsa madalitso ambiri padzikoli. Tiyeni tione ena mwa madalitso amene tidzasangalale nawo Ufumuwu ukadzayamba kulamulira dziko lonse lapansi.
1. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kuti ubweretse mtendere ndi chilungamo padzikoli?
Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, adzawononga anthu oipa ndi maboma onse a anthu pa nkhondo ya Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14, 16) Pa nthawi imeneyo, tidzaona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la m’Baibulo ili: “Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.” (Salimo 37:10) Yesu adzagwiritsa ntchito Ufumuwu pobweretsa mtendere komanso chilungamo padziko lonse lapansi.—Werengani Yesaya 11:4.
2. Kodi moyo udzakhala wotani zimene Mulungu amafuna zikadzachitika padziko lapansi?
Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira dzikoli, “olungama adzalandira dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.” (Salimo 37:29) Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’dziko limene aliyense ndi wolungama ndipo amakonda Yehova komanso anthu ena. Palibe aliyense amene azidzadwala ndipo anthu onse adzakhala ndi moyo mpaka kalekale.
3. Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani anthu oipa akadzawonongedwa?
Anthu oipa akadzawonongedwa, Yesu adzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000. Pa nthawiyi, Yesu ndi olamulira anzake okwana 144,000, adzathandiza anthu onse padzikoli kuti akhale angwiro. Pofika kumapeto kwa zaka 1,000, dziko lonse lidzakhala paradaiso ndipo anthu azidzakhala mosangalala chifukwa chomvera malamulo a Yehova. Kenako Yesu adzabwezera Ufumu kwa Atate wake Yehova. Pa nthawi imeneyo, dzina la Yehova ‘lidzayeretsedwa’ kwambiri kuposa kale lonse. (Mateyu 6:9, 10) Aliyense adzadziwa kuti Yehova ndi Wolamulira wabwino kwambiri yemwe amaganizira atumiki ake. Kenako Yehova adzawononga Satana, ziwanda ndi anthu onse amene adzasonyeze kuti sakufuna kumvera ulamuliro wake. (Chivumbulutso 20:7-10) Zimenezi zikadzachitika, madalitso amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse padzikoli adzakhalapo mpaka kalekale.
FUFUZANI MOZAMA
Fufuzani kuti mudziwe chifukwa chake sitikayikira kuti Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pokwaniritsa malonjezo onse amene ali m’Baibulo.
4. Ufumu wa Mulungu udzathetsa maboma onse a anthu
Baibulo limati: “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetsa zinthu zonse zopanda chilungamo zimene anthu amachitira anzawo.
Werengani Danieli 2:44 ndi 2 Atesalonika 1:6-8, kenako mukambirane mafunso awa:
Kodi Yehova komanso Mwana wake Yesu, adzachita chiyani ndi maboma a anthu komanso anthu amene amawatsatira?
Kodi zimene mwaphunzira zokhudza Yehova ndi Yesu zikukutsimikizirani bwanji kuti azidzachita zinthu mwachilungamo?
5. Yesu ndi Mfumu yabwino kwambiri
Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu adzachitira anthu zinthu zabwino kwambiri padzikoli. Onerani VIDIYO kuti muone umboni wosonyeza kuti Yesu ndi wofunitsitsa kuthandiza anthu komanso kuti Mulungu anamupatsa mphamvu zochitira zimenezo.
Zimene Yesu ankachita ali padzikoli, zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu. Pa madalitso amene ali m’munsiwa, ndi madalitso ati amene inuyo mukuwayembekezera kwambiri? Werengani malemba amene akukuthandizani kumvetsa madalitso amenewa.
ALI PADZIKOLI, YESU . . .
ALI KUMWAMBA, YESU . . .
anathetsa chimphepo chamkuntho.—Maliko 4:36-41.
adzakonza zinthu zonse zimene zawonongedwa padzikoli.—Yesaya 35:1, 2.
anadyetsa anthu ambiri modabwitsa.—Mateyu 14:17-21.
adzathetsa njala padziko lonse.—Salimo 72:16.
anachiritsa anthu ambiri.—Luka 18:35-43.
adzathetsa matenda onse.—Yesaya 33:24.
anaukitsa anthu amene anamwalira.—Luka 8:49-55.
adzathetsa imfa.—Chivumbulutso 21:3, 4.
6. Ufumu wa Mulungu udzabweretsa madalitso ambiri
Ufumu wa Mulungu udzachititsa kuti anthu azikhala moyo wabwino ngati mmene Yehova ankafunira poyamba. Anthu adzakhala ndi moyo m’paradaiso padzikoli mpaka kalekale. Onerani VIDIYO kuti muone mmene Yehova akukwaniritsira cholinga chake pogwiritsa ntchito Mwana wake Yesu.
Werengani Salimo 145:16, kenako mukambirane funso ili:
Kodi mumamva bwanji mukaganizira kuti Yehova ‘adzakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse’?
ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Ngati titamachita zinthu mogwirizana, tikhoza kuthetsa mavuto apadziko lonse.”
Kodi Ufumu wa Mulungu udzathetsa mavuto ati amene maboma a anthu alephera kuwathetsa?
ZOMWE TAPHUNZIRA
Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa cholinga chimene Mulungu anali nacho poyamba. Udzasintha dzikoli kuti likhale paradaiso, ndipo mudzakhala anthu abwino omwe azidzalambira Yehova mpaka kalekale.
Kubwereza
Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita zotani kuti dzina la Yehova liyeretsedwe?
N’chifukwa chiyani timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu udzakwaniritsa zonse zimene Baibulo linalonjeza?
Pa madalitso onse amene Ufumu wa Mulungu udzabweretse, ndi dalitso liti limene inuyo mukuliyembekezera kwambiri?
ONANI ZINANSO
Fufuzani kuti mudziwe zimene nkhondo ya Aramagedo imatanthauza.
“Kodi Nkhondo ya Aramagedo Idzakhala Yotani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zomwe zidzachitike pa nthawi imene Yesu anaitchula kuti “chisautso chachikulu.”—Mateyu 24:21.
“Kodi Chisautso Chachikulu N’chiyani?” (Nkhani yapawebusaiti)
Onani zimene zingathandize mabanja kuyerekezera kuti ali m’Paradaiso.
Munkhani yakuti, “Ndinali Ndi Mafunso Ambiri Omwe Ankandisowetsa Mtendere,” onani zimene zinathandiza munthu wina woukira boma kupeza mayankho a mafunso omwe ankamusowetsa mtendere.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, January 1, 2012)
-