Kodi Ndakonzeka?
Kodi Ndakonzeka Kulalikira Limodzi Ndi Mpingo?
Mukhoza kukhala wofalitsa wosabatizidwa ngati . . .
Nthawi zonse mumawerenga Baibulo, mumapemphera komanso mumapita kumisonkhano yampingo.
Mumakonda komanso kukhulupirira zomwe mukuphunzira ndipo mukufuna kuyamba kuuzako anthu ena.
Mumakonda Yehova komanso mumacheza ndi anthu omwe amamukonda.
Munafufutitsa dzina lanu kuchipembedzo chilichonse chabodza ndiponso munasiyiratu kuchita zinthu zokhudza ndale.
Mumatsatira mfundo za Yehova pa moyo wanu ndiponso mukufuna kukhala wa Mboni za Yehova.
Ngati mukuona kuti mwakonzeka kuyamba kulalikira limodzi ndi mpingo, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.
Kodi Ndakonzeka Kubatizidwa?
Mukhoza kubatizidwa ngati . . .
Ndinu wofalitsa wosabatizidwa.
Mumayesetsa kulalikira nthawi zonse.
Mumamvera komanso kutsatira malangizo ochokera kwa “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
Munadzipereka kwa Yehova m’pemphero ndipo mukufuna kumutumikira mpaka kalekale.
Ngati mukuona kuti mwakonzeka kubatizidwa, amene amakuphunzitsani Baibulo angakonze zoti mukumane ndi akulu n’cholinga choti akuuzeni zoyenera kuchita.