Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lff phunziro 1
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • FUFUZANI MOZAMA
  • ZOMWE TAPHUNZIRA
  • ONANI ZINANSO
  • Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Yambani Kuphunzira Baibulo
  • Mungatani Kuti Kuwerenga Baibulo Kuzikuthandizani Kwambiri?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Mungatani Kuti Musasiye Kuphunzira Baibulo?
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Baibulo Limatithandiza Kuti Tikhale Ndi Chiyembekezo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff phunziro 1
Phunziro 1. Baibulo lotsegula.

PHUNZIRO 01

Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Losindikizidwa
Losindikizidwa
Losindikizidwa

Tonsefe timadzifunsa mafunso okhudza moyo, kuvutika, imfa komanso tsogolo lathu. Timafunanso titadziwa zimene tingachite kuti tithane ndi mavuto amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku, monga kusapeza ndalama zokwanira ndiponso zimene tingachite kuti tizikhala mosangalala m’banja lathu. Anthu ambiri amaona kuti Baibulo limawathandiza kupeza mayankho a mafunso ofunika komanso amapezamo malangizo odalirika. Kunena zoona, Baibulo likhoza kuthandiza munthu wina aliyense.

1. Kodi ndi mafunso ena ati amene Baibulo limayankha?

Baibulo limayankha mafunso ofunika monga akuti: Kodi moyo unayamba bwanji? Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? N’chifukwa chiyani anthu abwino nawonso amavutika? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Popeza aliyense amafuna mtendere, n’chifukwa chiyani padzikoli nthawi zambiri pamachitika nkhondo? N’chiyani chidzachitikire dzikoli kutsogoloku? Baibulo limatilimbikitsa kuti tizipeza mayankho a mafunso ngati amenewa ndipo anthu mamiliyoni ambiri apeza mayankho ogwira mtima a mafunsowa.

2. Kodi Baibulo lingatithandize bwanji kuti tizisangalala?

M’Baibulo muli malangizo abwino. Mwachitsanzo, limafotokoza zimene mabanja angachite kuti azikhaladi mosangalala. Limaperekanso malangizo othandiza kuti tisamade nkhawa kwambiri komanso kuti tizikonda ntchito yathu. Tikamakambirana zimene zili m’bukuli, muphunzira zimene Baibulo limanena pa nkhani ngati zimenezi ndi zinanso. Mudzafika pomvetsa kuti “Malemba onse [kapena kuti mawu onse amene ali m’Baibulo] . . . ndi othandiza.”​—2 Timoteyo 3:16.

Bukuli silikulowa m’malo mwa Baibulo. Koma likuthandizani kuti muzifufuza mfundo za m’Baibulo panokha. Choncho tikukulimbikitsani kuti muziwerenga malemba amene aikidwa m’phunziro lililonse, kenako muziwayerekezera ndi zimene mukuphunzira.

FUFUZANI MOZAMA

Onani mmene Baibulo lathandizira anthu ena, zimene mungachite kuti muzisangalala mukamaliwerenga ndiponso ubwino wopempha anthu ena kuti akuthandizeni kulimvetsa.

3. Baibulo lingatithandize

Baibulo lili ngati nyale yowala kwambiri. Lingatithandize kuti tizisankha zinthu mwanzeru komanso limatiuza zimene zichitike m’tsogolo.

Werengani Salimo 119:105, kenako mukambirane mafunso awa:

  • N’chiyani chikusonyeza kuti amene analemba salimoli ankaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri?

  • Nanga inuyo Baibulo mumaliona bwanji?

Munthu akuyenda m’mphepete mwa nyanja madzulo ndipo akudziunikira ndi tochi

4. Baibulo limayankha mafunso athu

Baibulo linathandiza mayi wina kupeza mayankho a mafunso amene ankamuvutitsa maganizo kwa zaka zambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

VIDIYO: Musataye Mtima! (1:48)

  • Mayi amene tamuona muvidiyoyi anali ndi mafunso ambiri. Kodi limodzi mwa mafunso amenewa ndi liti?

  • Nanga kuphunzira Baibulo kunamuthandiza bwanji?

Baibulo limatilimbikitsa kuti tizifunsa mafunso. Werengani Mateyu 7:​7, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi muli ndi mafunso ati amene mukufuna kuti Baibulo likuyankheni?

5. Kuwerenga Baibulo n’kosangalatsa

Anthu ambiri amasangalala akamawerenga Baibulo ndipo likuwathandiza kwambiri. Onerani VIDIYO, kenako mukambirane mafunso otsatirawa.

VIDIYO: Kuwerenga Baibulo (2:05)

  • Muvidiyoyi, kodi achinyamatawa ankaiona bwanji nkhani yowerenga mabuku ena?

  • Ngakhale kuti sakonda kuwerenga mabuku ena, n’chifukwa chiyani amakonda kuwerenga Baibulo?

Baibulo limatipatsa malangizo amene amatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo. Werengani Aroma 15:4, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi mungakonde kumva uthenga wa m’Baibulo womwe umatitonthoza komanso kutipatsa chiyembekezo?

6. Anthu ena akhoza kutithandiza kulimvetsa bwino Baibulo

Kuwonjezera pa kuwerenga Baibulo paokha, anthu ambiri amaona kuti kukambirana ndi ena kumawathandiza kuti azilimvetsa bwino. Werengani Machitidwe 8:26-31, kenako mukambirane funso ili:

  • Kodi tingatani kuti tizilimvetsa bwino Baibulo?​—Onani vesi 30 ndi 31.

Chithunzi: 1. Filipo akufotokozera Malemba munthu wa ku Itiyopiya. 2. Wa Mboni za Yehova akukambirana mfundo za m’Baibulo ndi mayi wina limodzi ndi ana ake awiri.

Munthu wina wa ku Itiyopiya ankafunika kuthandizidwa ndi munthu wina kuti amvetse Malemba. Masiku anonso anthu ambiri amaona kuti akamakambirana mfundo za m’Baibulo ndi munthu wina, zimawathandiza kumvetsa bwino Malemba

ANTHU ENA AMANENA KUTI: “Kuphunzira Baibulo n’kutaya nthawi.”

  • Inuyo mukuganiza bwanji? N’chifukwa chiyani mukutero?

ZOMWE TAPHUNZIRA

Baibulo limatipatsa malangizo othandiza, limayankha mafunso ofunika kwambiri komanso limatitonthoza ndi kutipatsa chiyembekezo.

Kubwereza

  • Kodi m’Baibulo mumapezeka malangizo otani?

  • Kodi Baibulo limayankha mafunso ati?

  • Kodi ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuphunzira m’Baibulo?

Zoti Muchite

ONANI ZINANSO

Onani mmene malangizo a m’Baibulo akuthandizira anthu masiku ano.

“Mfundo za M’Baibulo Sizikalamba”(Nsanja ya Olonda Na. 1 2018)

Onani mmene Baibulo linathandizira munthu wina amene anali ndi vuto lodzikayikira kuyambira ali wamng’ono

Mmene Ndinayambira Kukhala ndi Moyo Wosangalala (2:53)

Onani malangizo a m’Baibulo othandiza kuti banja liziyenda bwino.

“Mfundo 12 Zothandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino” (Galamukani! Na. 2 2018)

Onani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya amene akulamulira dzikoli ngakhale kuti anthu ambiri ali ndi maganizo olakwika pa nkhaniyi.

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?​—Vidiyo Yonse (3:14)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena