Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • scl tsamba 72-73
  • Maboma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maboma
  • Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu
scl tsamba 72-73

Maboma

Kodi Akhristu amamvera komanso kugonjera boma liti?

Mt 6:9, 10, 33; 10:7; 24:14

Onaninso Da 7:13, 14

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Sl 89:18-29​—Yehova anaika Mesiya kukhala Mfumu ya dziko lonse lapansi

    • Chv 12:7-12​—Chakumayambiriro kwa masiku otsiriza, Yesu Khristu anayamba kulamulira monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo anathamangitsa Satana kumwamba

Kodi Akhristu odzozedwa omwe ali padziko lapansi amaimira bwanji Ufumu wa Mulungu?

2Ak 5:20; Afi 3:20, 21

Akhristu amalemekeza olamulira a maboma a anthu

N’chifukwa chiyani timapereka misonkho komanso kumvera malamulo a boma?

Aro 13:1-7; Tit 3:1; 1Pe 2:13, 14

Onaninso Mac 25:8

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mt 22:15-22​—Yesu anayankha mwanzeru funso lokhudza otsatira ake ngati akuyenera kupereka misonkho

N’chifukwa chiyani sitibwezera ngakhale pamene tikuzunzidwa?

Yoh 18:36; 1Pe 2:21-23

Onaninso “Chizunzo”

Akhristu salowerera zochitika zam’dziko

Ngakhale kuti timamvera olamulira a anthu, n’chifukwa chiyani timakana kuwamvera akamatiuza kuti tisamvere Yehova?

Mac 4:18-20; 5:27-29

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 3:1, 4-18​—Anyamata atatu a Chiheberi anakana kumvera lamulo la Ababulo chifukwa linali lotsutsana ndi lamulo la Mulungu

    • Da 6:6-10​—Mneneri Danieli atakalamba anakana kumvera lamulo la boma loti anthu asamapemphere kwa mulungu wina aliyense koma kwa mfumu yokha

Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti otsatira ake sayenera kulowerera ndale?

Mt 4:8-10; Yoh 6:15

Kodi malamulo a Mulungu oletsa kulambira mafano angathandize bwanji Mkhristu kuti asalowerere ndale?

Eks 20:4, 5; 1Ak 10:14; 1Yo 5:21

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Da 3:1, 4-18​—Mfumu Nebukadinezara inaimika fano lomwe mwina linkaimira mulungu wonyenga dzina lake Madaki ndipo inalamula kuti anthu onse azililambira

Ngati boma lalamula kuti Akhristu akamenye nawo nkhondo, kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zingawathandize pa nkhaniyi?

Yes 2:4; Yoh 18:36

Onaninso Sl 11:5

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • ​—Yesu anachenjeza otsatira ake kuti sayenera kumenya nawo nkhondo

    • Yoh 13:34, 35​—Ngati Mkhristu atapita kukamenya nkhondo kumayiko ena, mwinanso kukapha abale ndi alongo anzake, kodi angakhale kuti akumvera la Yesuli?

N’chifukwa chiyani Akhristu amakana kuchita nawo zionetsero zodana ndi boma?

Miy 24:21, 22; Aro 13:1-7; 1Pe 2:17

Kodi timadziwa bwanji kuti maboma akhoza kutinamizira kuti ndife oukira kapena anthu osokoneza?

Lu 23:1, 2; Yoh 15:18-21

  • Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:

    • Mac 16:19-23​—Mtumwi Paulo ndi Sila anazunzidwa chifukwa chogwira ntchito yolalikira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena