Nkhondo N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera kuti m’nthawi yathu ino kuchitika nkhondo zambiri? Mt 24:3, 4, 7, 8 Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni: Da 11:40—Mneneri Danieli analosera kuti m’masiku otsiriza mafumu awiri amphamvu adzakankhana kapena kuti kupikisana pa nkhondo Chv 6:1-4—Mtumwi Yohane anaona hatchi yofiira ngati moto yomwe ikuimira nkhondo ndipo wokwerapo wake “analoledwa kuchotsa mtendere padziko lapansi” Kodi Yehova adzachita chiyani ndi nkhondo zimene anthu akumenya padzikoli? Sl 46:8, 9; Yes 9:6, 7; Mik 4:3 N’chifukwa chiyani Akhristu samenya nawo nkhondo? Yes 2:2, 4 Onaninso “Maboma—Akhristu Salowerera Zochitika za Dziko” Kodi Yehova ndi Yesu adzamenya nkhondo yotani? Sl 45:3-5; Yer 25:31-33; Chv 19:11 Kodi Akhristu oona amamenya nkhondo yotani? Aro 13:12; 2Ak 10:3, 4; Aef 6:11-17 Kodi Akhristu mumpingo angapewe bwanji kulimbikitsa nkhondo, kukangana kapena kubwezera anthu amene awalakwira? Aro 12:17-21; Aga 5:14, 15; Tit 3:1, 2; Yak 4:1-3