Ndalama
N’chifukwa chiyani kukonda ndalama n’koopsa?
Onaninso “Kukonda Chuma”
Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti si kulakwa kupeza ndalama zothandizira banja?
Mla 7:12; 10:19; Aef 4:28; 2At 3:10; 1Ti 5:8, 18
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 31:38-42—Ngakhale kuti Labani ankasinthasintha zimene anapangana ndi Yakobo, mpongozi wakeyu sanasiye kugwira ntchito mwakhama ndipo Yehova anapitiriza kumudalitsa
Lu 19:12, 13, 15-23—Fanizo la Yesu likusonyeza kuti si zinali zachilendo kuti anthu azichita malonda ndi ndalama n’cholinga choti apeze phindu lochuluka
Ndi mfundo za m’Babulo ziti zimene zimatithandiza kudziwa zoyenera kuchita pa nkhani yobwereka komanso kubwereketsa ndalama?
N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kubwereka ndalama zambiri?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ne 5:2-8—M’nthawi ya Bwanamkubwa Nehemiya, Aisiraeli ena sankakomera mtima anthu omwe ankalephera kubweza ngongole
Mt 18:23-25—Fanizo la Yesu likusonyeza kuti munthu akalephera kubweza ngongole ankalandira chilango
Kodi tiyenera kuchita chiyani tisanachite mgwirizano uliwonse wa bizinesi, kaya ndi wachibale, a Mboni anzathu kapena anthu omwe si Mboni?
Nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni:
Ge 23:14-20—Pamene Abulahamu ankagula malo oti aike Sara m’manda, iye analipira ndalama zokwanira pamaso pa mboni, potsimikizira kuti wagula malowo n’cholinga choti pasadzakhale kusamvana m’tsogolo
Yer 32:9-12—Pamene mneneri Yeremiya ankagula malo kwa m’bale wawo wa bambo ake, analemba kalata ya pangano n’kuikapo chidindo, anaikopera, komanso mboni zinasainira
N’chifukwa chiyani ndi bwino kulemba bajeti ya ndalama zomwe mukufuna kugwiritsa ntchito?
N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola kuti kusamvana pa nkhani ya ndalama kusokoneze mgwirizano wathu mumpingo?
Onaninso Aro 12:18; 2Ti 2:24