50 SAULO WA KU TARISO
Anasintha Kwambiri Maganizo Ake
SAULO wa ku Tariso ali wachinyamata, analipo pamene Ayuda ankapha Sitefano.a Iye ankaona kuti ndi bwino kupha Sitefano chifukwa ankakhulupirira kuti chipembedzo cha Ayuda n’chimene chinali cholondola. Baibulo limanena kuti Saulo “anapitiriza kuopseza ophunzira a Ambuye komanso ankafunitsitsa kuwapha” ku Yerusalemu. Ankagwira Akhristu ambiri n’kumakawatsekera m’ndende. Akhristu akamaimbidwa milandu, Saulo ankakhala m’gulu lovomereza kuti aphedwe. Chifukwa chakuti Akhristu ankazunzidwa koopsa, ambiri anathawa ku Yerusalemu. Saulo ankadana kwambiri ndi Akhristu moti ankawalondolanso m’madera ena. Iye anapempha makalata kwa mkulu wa ansembe omuloleza kukazunza Akhristu ku Damasiko.
Saulo atangopatsidwa makalatawo, iye ndi anzake ananyamuka kulowera chakumpoto kumzinda wa Damasiko. Iye sankadziwa kuti Yesu ali moyo ndipo ali ndi Atate wake kumwamba. Yehova ndi Yesu ankamudziwa bwino Saulo. N’zochititsa chidwi kuti iwo ankaona kuti Saulo anali ndi makhalidwe abwino ndipo akhoza kusintha n’kukhala munthu wothandiza. Pamene Saulo ndi anzake ankayandikira ku Damasiko, mwadzidzidzi anaona “kuwala kochokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa.” Zitatero, Saulo anagwa pansi ndipo anasiya kuona.
Kenako panamveka mawu akuti, “Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake nʼkumamenya zisonga zotosera.” Ndiyeno Saulo anafunsa kuti: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Iye ayenera kuti anadabwa kwambiri atayankhidwa kuti: “Ndine Yesu, amene ukumuzunza.” Kenako Yesu anamuuza kuti aimirire ndipo anamuuza za ntchito imene akuyenera kugwira. Ntchito yake inali kuchitira umboni kuti zonse zimene Yesu ankaphunzitsa ndi zoona. Saulo yemwe pa nthawiyi sankaona, ankafunika kuthandiza anthu osakhulupirira kuti adziwe za Yesu komanso Ufumu wa Mulungu.
Kodi zinatheka bwanji kuti munthu wozunza Akhristu asinthe maganizo ake n’kuyamba kulalikira za Khristu?
Masomphenyawa anamuthandiza Saulo kusintha mtima wake wodzikuza komanso wankhanza. Popeza sankaona, iye analondoleredwa njira yopita ku Damasiko komwe anakakhala, n’kumadikira Mkhristu wina. Saulo anakhala masiku atatu osadya. Umenewu unali umboni wotsimikizira kuti ankadzimvera chisoni komanso analapa mochokera pansi pa mtima. N’zosachita kufunsa kuti anapemphera kwa Yehova kwa nthawi yaitali komanso ndi mtima wonse. Pa nthawiyi Saulo anazindikira kuti ankazunza Mwana wokondedwa wa Mulungu. Kenako Yesu anatumiza kwa Saulo Mkhristu wina dzina lake Hananiya. Ngakhale kuti poyamba Hananiya ankaopa, iye anapita n’kukamugwira Saulo. Kenako “tinthu tooneka ngati mamba a nsomba tinagwa kuchokera m’maso mwa Saulo.” Zitatero, anayambiranso kuona. Saulo anasinthiratu maganizo n’kukhala wodzichepetsa komanso wanzeru “kenako anapita kukabatizidwa.”
Saulo atangokhala Mkhristu, anayamba ntchito yolalikira. M’malo mobwerera ku Yerusalemu, anachita zinthu zina zovuta kwambiri. Iye anapita kumasunagoge a ku Damasiko komwe anthu ake ankamudziwa bwino. Ayenera kuti anapempha Mulungu kuti amuthandize kukhala wolimba mtima. Anthu ayenera kuti anadabwa akuwauza kuti m’mbuyo monsemu wakhala akulakwitsa ndipo panopa ndi Mkhristu. Kuwonjezera pamenepo “Saulo anapitiriza kukhala ndi mphamvu zambiri ndipo ankathetsa nzeru Ayuda a ku Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndi Khristu.”
Pa nthawi ina Saulo adakali ku Damasiko anapita ku Arabiya komwe mwina kunali kuchipululu cha Siriya. Baibulo silinena zimene ankakachita kumeneko. Koma n’zodziwikiratu kuti pa nthawi imene anali yekhayekha m’chipululu, ankapemphera komanso kuganizira mozama za ntchito yake yomwe ankayembekezera kudzagwira. Saulo sanasiye kuphunzira Malemba ndiponso kuwaganizira mozama. Iye anasintha kwambiri maganizo ake ndipo kenako analimbikitsa Akhristu anzake a ku Roma kuti azichita zomwezo.—Aroma 12:2.
Saulo sanaiwale zinthu zoipa zomwe anachita m’mbuyo. Patapita zaka zambiri iye ananena kuti: “Ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.” (1 Tim. 1:13) Iye ankadandaulanso kuti anavomereza za kuphedwa kwa Sitefano. (Mac. 22:19-21) Koma Saulo ankadziwa kuti Yehova ndi Yesu anamukhululukira ndipo ankamudalitsa.
Saulo anakhala ku Damasiko kwa zaka zitatu, kenako anathawako Akhristu atayamba kuzunzidwa. Kuti apulumuke, ophunzira anamuika mʼdengu nʼkumutulutsira pawindo la mpanda. Kenako iye anapita ku Yerusalemu. Koma ntchito yoti agwire inali idakalipo yambiri.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Saulo wa ku Tariso anasonyeza bwanji kulimba mtima pa nthawi imeneyi ya moyo wake?
Zoti Mufufuze
1. N’chifukwa chiyani Saulo ananena kuti mzinda wa kwawo wa Tariso unali “mzinda wotchuka”? (Mac. 21:39; w99 5/15 30 ¶1-wcgr) A
Todd Bolen/BiblePlaces.com
Chithunzi A: Mabwinja a ku Tariso ndiponso misewu yake
2. N’chifukwa chiyani Paulo ankadziwa bwino chikhalidwe cha Ayuda, Agiriki ndi Aroma? (bt 62, bokosi ¶1-3)
3. Kodi Saulo ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Yesu anaonekera kwa iye “ngati khanda lobadwa masiku osakwana”? (1 Akor. 15:8; w22.09 27)
4. Kodi pali umboni wotani wotsimikizira kuti zimene Luka analemba pa nkhani ya kusintha kwa Saulo ku Damasiko ndi zoona? (Mac. 9:11, 24, 25; g03 2/8 28-31) B
Photo by ROLOC Color Slides
Chithunzi B: Geti la Bab-Sharqi la ku Damasiko pamene pankathera Msewu Wowongoka
Zomwe Tikuphunzirapo
Saulo anadzichepetsa n’kuvomera kuthandizidwa ndi Hananiya komanso Akhristu ena. (Mac. 9:17, 18; Akol. 4:10, 11) Kodi ndi pa nthawi iti pamene ifenso tingafunike kulola kuti ena atithandize?
Saulo sanalole kuti zinthu zimene anachita m’mbuyo kapena zimene analakwitsa zimusokoneze polambira Yehova. (Afil. 3:4-8; 1 Tim. 1:12-16) Kodi tingamutsanzire bwanji? C
Chithunzi C
Kodi tingatsanzire kulimba mtima kwa Saulo m’njira zinanso ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
N’chiyani chomwe mwaphunzira munkhaniyi chimene chikukuchititsani kusangalala mukaganizira kuti Saulo anasankhidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba?
Phunzirani Zambiri
Onani mmene munthu wina amene ankazunzanso anthu ngati Saulo anasinthira maganizo ake.
Chikondi Chinathandiza “Saulo wa ku Sado” Kusintha Maganizo Ake (5:50)
Kodi chitsanzo cha Saulo chingatithandize bwanji kuti tizichita khama pophunzira Mawu a Mulungu, tizikonda ena komanso tizidziona moyenera?
“Pitani Patsogolo Mwauzimu Potsanzira Paulo” (w08 5/15 21-25)
a Ngakhale kuti Saulo anadzayamba kutchulidwa kuti Paulo, munkhaniyi tizingomutchula kuti “Saulo.”