Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wcg mutu 7 tsamba 40-tsamba 43
  • Analimba Mtima Kuti Ateteze Banja Lake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analimba Mtima Kuti Ateteze Banja Lake
  • Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zoti Mufufuze
  • Zomwe Tikuphunzirapo
  • Ganizirani Mfundo Yaikulu
  • Phunzirani Zambiri
  • Yakobo ndi Esau Akhululukirana
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Yakobo Anaona Zinthu Zauzimu Kukhala Zofunika
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Amapasa Amene Anali Osiyana
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Yakobo Analandira Madalitso
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Muziyenda Ndi Mulungu Molimba Mtima
wcg mutu 7 tsamba 40-tsamba 43

7 YAKOBO

Analimba Mtima Kuti Ateteze Banja Lake

Losindikizidwa
Losindikizidwa

ATATSALA pang’ono kufa, Yakobo anati nthawi imene anakhala ndi moyo, inali “zaka zowerengeka komanso zosautsa.” (Gen. 47:9) Iye anakumanadi ndi mavuto ambiri. Zaka zambiri m’mbuyomo Ali wachinyamata, anathawira ku Harana, mchimwene wake weniweni akufuna kumupha. Ali ku Haranako, Yakobo anakonda kwambiri Rakele ndipo ankafuna kumukwatira. Koma Labani yemwe anali bambo ake a Rakele, anamupusitsa n’kumuchititsa kuti akwatire kaye mkulu wake. Choncho Yakobo anali ndi akazi awiri omwe ankangokhalira kuyambana. Iye anagwirira ntchito Labani kwa zaka zambiri ndipo kwa zaka zonsezo, iwo ankafuna kumubera pomangosinthasintha malipiro ake. Komabe, Yakobo anali wolimba mtima, wokhulupirika komanso wopirira.

Tsiku lina Yehova anauza Yakobo kuti abwerere ku Kanani. Koma zimenezi zinali zoopsa chifukwa Labani anali wadyera ndipo ankaona kuti zinthu zonse zomwe Yakobo anali nazo zinali zake. Yakobo anakambirana ndi akazi ake zomwe Yehova anamuuza, ndipo anathawa ndi banja lake osamuuza Labani. Labani atadziwa za nkhaniyi, anasonkhanitsa amuna n’kuwatsatira. Atawapeza, Labani anakalipira Yakobo chifukwa chonyamuka mozemba. Anamuopsezanso kuti: “Ndikanatha kukuchitirani zoipa.” Koma molimba mtima Yakobo anadzudzula Labani. Anamuuza kuti wakhala akumupondereza komanso kumuchitira zachinyengo. Ngakhale zinali choncho, Yakobo anali wofunitsitsa kukhazikitsa mtendere, moti mmene ankasiyana analonjezana kuti azikhala mwamtendere.

Kodi Yakobo anakwanitsa bwanji kukhazikitsa mtendere ndi achibale ake komanso kulimbana ndi mngelo wamphamvu?

Yakobo ankayembekezeranso kukakumana ndi mchimwene wake Esau. Zaka zambiri m’mbuyomo, mayi awo anachenjeza Yakobo kuti Esau ankafuna kumupha. Esau ankaona kuti Yakobo anachita zachinyengo polandira madalitso amene ankayenera kukhala ake kuchokera kwa bambo awo. Koma pa nthawiyi Yakobo ankafuna kukhazikitsa mtendere ndi mchimwene wakeyo. Iye anamva kuti Esau akubwera limodzi ndi banja lake komanso ndi amuna 400. Yakobo anatumiza akapolo ake kuti akakumane ndi Esau n’kumupatsa mphatso zamtengo wapatali. Koma kodi zimenezi zinalidi zokwanira kukathetsa mkwiyo wa Esau? Baibulo limati: “Yakobo anachita mantha ndi kuda nkhawa kwambiri.” Koma kenako panachitika zodabwitsa.

Usiku, Yakobo ali yekhayekha, anaona munthu wachilendo. Munthuyo anali mngelo wa Yehova ndipo anayamba kulimbana naye. Iye anaganiza kuti mngeloyo akhoza kumudalitsa, choncho analimba mtima n’kuyamba kulimbana naye kwa maola angapo. Ngakhale kuti Yakobo anali ndi zaka 97 ndipo mngeloyo anali wamphamvu kwambiri, iye sanamusiye. Analimbana naye koopsa mpaka Yakobo anayamba kulira. (Hos. 12:4) Yakobo ankadziwa kuti madalitso a Yehova ndi ofunika kwambiri, choncho anatsimikiza kuchita chilichonse kuti awapeze. Kutacha, mngelo uja anagwira Yakobo polumikizana chiuno ndi fupa la ntchafu mpaka fupalo kuguluka. Mngeloyo anamuuza kuti dzina lake lidzakhala Isiraeli, kutanthauza kuti walimbana ndi Mulungu. Dzinali linali lomuyenereradi chifukwa sanagwe ulesi ndipo anagwiritsa ntchito mphamvu zake zonse kuti apeze madalitso a Yehova.

Kenako Yakobo anabwerera kwawo akutsimphina. Chapatali, anaona Esau akubwera limodzi ndi amuna 400. Yakobo anapita kuti akakumane nawo. Akuyandikira, anaweramitsa nkhope yake mpaka pansi maulendo 7. Kenako Esau anamuthamangira. Iye analibe chida chilichonse ndipo anahaga Yakobo. Kenako amuna awiriwa anayamba kulira. Kupatsa ndi kudzichepetsa kwa Yakobo, zinathandiza kuthetsa mkwiyo wa Esau. N’kutheka kuti Esau anachita chidwi ndi kulimba mtima komwe Yakobo anasonyeza. Yakobo anapeza njira yabwino kuti agwirizanenso ndi mchimwene wakeyu.

Yakobo akutsimphina pamene akupita kukakumana ndi Esau ndiponso atumiki ake.

Kungoyambira pamenepo, Yakobo ankatsimphina chifukwa cha kuvulala kuja ndipo anakumana ndi mavuto enanso ambiri. Koma sananong’onezepo bondo chifukwa chomvera Yehova kapenanso chifukwa cholimbana ndi mngelo. Patapita zaka, lonjezo losangalatsa kwambiri limene Yehova anamulonjeza linakwaniritsidwa ndipo Aisiraeli anakhala mtundu waukulu. (Gen. 28:14) Komanso nthawi zambiri, Yehova ankadziwika kuti “Mulungu wa Yakobo.” (Eks. 3:6) Yesu Khristu anagwiritsaponso ntchito mawuwa. Iye anati Yehova “ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye onsewa ndi amoyo.” (Luka 20:​37, 38) Choncho Yakobo ali ndi tsogolo labwino kwambiri, chifukwa adzakhala ndi moyo mpaka kalekale komanso wosangalala m’dziko latsopano.

Werengani nkhaniyi m’Baibulo:

  • Genesis 27:​41-45; 31:​1-29, 36-55; 32:1–33:16

Funso lokambirana:

Kodi Yakobo anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?

Zoti Mufufuze

  1. 1. N’chifukwa chiyani Yehova anaonetsetsa kuti Yakobo walandira madalitso ngati mwana woyamba kubadwa m’malo mwa Esau? (w03 10/15 29 ¶2)

  2. 2. Kodi Yehova analotetsa Yakobo maloto otani, nanga zimenezi zinamutsimikizira chiyani? (w03 10/15 28 ¶3–29 ¶1) A

    Angelo akukwera ndi kutsika pamasitepe.

    Zithunzi A

  3. 3. N’chifukwa chiyani Yakobo sanakayikire kuti akhoza kudalitsidwa ndi mngelo? (w03 10/15 31 ¶1) B

    Yakobo akukumana ndi mngelo ndipo akukonzekera kuti alimbane naye.

    Chithunzi B

  4. 4. Kodi Yakobo anachita chiyani pofuna kuteteza anthu am’banja lake kuti asatengere zochita za Akanani? (w95 9/15 21 ¶4, mawu a m’munsi-wcgr)

Zomwe Tikuphunzirapo

  • Yakobo ankaona kuti ali ndi udindo wosamalira nkhosa zonse za Labani. (Gen. 31:​38-40) Kodi abusa a Chikhristu angasonyeze bwanji kuti amadera nkhawa kwambiri abale ndi alongo awo omwe ndi nkhosa za Yehova? C

    Zithunzi: Mkulu wachinyamata akulimbikitsa m’bale wachikulire wamumpingo mwawo. Zithunzizi zabwerezedwanso m’mutuwu. Mkulu wachinyamata wakayendera m’bale wachikulire kunyumba kwawo ndipo akumumvetsera mwachidwi pamene akufotokoza mavuto ake. Kenako mkuluyo akulembera meseji m’bale wachikulire uja yakuti: “Tili pa nthawi yopuma. Ndimaganizira za inu. Mukupezako bwanji?” M’bale wachikulireyo akuyankha kuti: “Ndathokoza kwambiri. Lero bola, ndikupezako bwino ndithu.” Mkulu ndi m’bale wachikulire uja ali limodzi mu utumiki. M’bale wachikulireyo akukambirana lemba ndi munthu yemwe waima pakhomo la nyumba yake.

    Chithunzi C

  • Yakobo atachita mantha, anapemphera kwa Yehova. (Gen. 32:​6-12) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa nkhani ya mmene tingamapempherere?

  • Kodi tingatsanzire bwanji kulimba mtima kwa Yakobo?

Ganizirani Mfundo Yaikulu

  • Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?

  • Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?

  • Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Yakobo akadzaukitsidwa?

Phunzirani Zambiri

Kodi tingatsanzire bwanji Yakobo tikazindikira kuti takhumudwitsa Mkhristu mnzathu?

“Pitirizani ‘Kumumvera’” (w21.12 25-27 ¶10-18)

Gwiritsirani ntchito zithunzi zofotokoza nkhani ya m’Baibulo zotsatirazi kuti muphunzitse banja lanu zokhudza Yakobo.

“Yakobo ndi Esau” (ijwis nkhani 3)

    Mabuku a Chichewa (1974-2026)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena