34 HEZEKIYA
“Sanamusiye Yehova”
HEZEKIYA anali mmodzi mwa mafumu abwino kwambiri a Ayuda koma bambo ake anali mmodzi mwa mafumu oipa kwambiri. Bambo ake anali Ahazi ndipo ankalimbikitsa kulambira kwabodza. Moti anafika mpaka popereka ana ake enieni nsembe kwa mafano. (2 Maf. 16:2-4; 2 Mbiri 28:1, 3) Choncho Hezekiya ayenera kuti ali mwana anaona zinthu zoopsa. Koma mulimonse mmene zinalili, iye atakula sanatsatire chitsanzo choipa cha bambo ake. Hezekiya ali ndi zaka 25, bambo ake anamwalira ndipo iye anakhala mfumu. Molimba mtima anayamba kuthetsa kulambira kwabodza.
Hezekiya anakonza ndi kutsegulanso kachisi wa Yehova ku Yerusalemu ndipo anachotsa mafano onse. Iye anauzanso ansembe kuti ayambirenso kugwira ntchito yawo. Pasanapite nthawi, anatuma anthu kuti auze Aisiraeli onse kuti apite ku Yerusalemu kuchikondwerero cha Pasika. Iye anaitananso ngakhale Aisiraeli a mu ufumu wakumpoto wa mafuko 10. Anthu ena ananyoza anthu omwe anabwera ndi uthengawo, pomwe ena anapitadi ku Yerusalemu. Chitsanzo cha Hezekiya chinachititsa kuti anthu a ku Yuda komanso a mu ufumu wakumpoto agwetse malo okwezeka omwe anthu ena ankalambirirapo mafano komanso aphwanye mafanowo. Aisiraeli anali atayamba kulambira njoka yakopa imene Yehova analamula Mose kuti apange zaka 700 m’mbuyomo. Hezekiya anaphwanyanso njokayi n’cholinga choti aliyense asamailambirenso.
Kwa zaka zambiri, Hezekiya ankaona kuti ufumu wake ukhoza kudzaukiridwa. Yehova anakhala akuuza anthu a mu ufumu wakumpoto kuti ufumu wawo udzawonongedwa. Patangopita zaka zochepa Hezekiya atayamba kulamulira, Asuri anaukira ufumu wakumpoto ndipo anatenga anthu ambiri n’kupita nawo kudziko lawo ngati akapolo. Mwina Hezekiya ankaganiza kuti kenako Asuri aukira Yuda. Nawonso anthu a ku Yuda anali osakhulupirika mwinanso kuposa Aisiraeli. Yehova anali atachenjeza anthu a ku Yuda kuti ufumu wawo udzawonongedwa ndipo nthawi zonse mawu a Yehova amakwaniritsidwa. Hezekiya anayamba kuda nkhawa chifukwa choti Asuri anali atagonjetsa mizinda yoyandikana ndi Yuda.
Pasanapite nthawi, asilikali a Asuri anafika ku Yuda ndipo ankatsogoleredwa ndi Mfumu Senakeribu yemwe anali woipa kwambiri. Senakeribu ndi asilikali ake anayamba kugonjetsa mizinda ya ku Yuda, umodzi ndi umodzi. Koma Hezekiya anakumananso ndi vuto lina. Zikuoneka kuti pa nthawi yomweyi anayamba kudwala mwakayakaya. Apa n’kuti alibe mwana ndipo akanamwalira, bwenzi palibe mbadwa ya Davide yodzakhala mfumu m’malo mwake. Choncho ndi chikhulupiriro chonse anapemphera kwa Yehova kuti amuchiritse. Yehova anayankha pemphero lake. Mwachikondi, anamuwonjezera zaka 15 zokhala ndi moyo. Koma Asuri aja anali akuopsezabe Yerusalemu.
Pofuna kukonza zinthu, Hezekiya anatumiza ndalama zambiri kwa Senakeribu n’cholinga choti asabwere kudzawononga mzinda woyera wa Yerusalemu. Senakeribu analandira ndalamazo koma anapitirizabe mapulani ake ofuna kuwononga Yerusalemu. Pa nthawiyi, Hezekiya anapitiriza kulimbitsa mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga mpanda wina komanso ngalande zobweretsa madzi mumzindawo kuti anthu asadzavutike ngati Asuri atauzungulira. Ndipo analimbikitsa anthu ake n’kuwatsimikizira kuti Yehova ndi wamphamvu kuposa gulu lililonse la asilikali.
Hezekiya analimbikitsa anthu a ku Yerusalemu pamene gulu la asilikali lamphamvu linawaopseza komanso kuwanyoza
Senakeribu anakwiya kwambiri ndipo anatumiza Rabisake kuti akanyoze ndi kufooketsa Ayuda. Iye ananyoza kwambiri Hezekiya komanso Mulungu wawo Yehova. Koma Hezekiya anapitirizabe kukhulupirira Yehova ndiponso analimbikitsa anthu ake. Kenako Senakeribu anatumizira Hezekiya makalata omuopseza. Hezekiya anatenga makalatawo n’kupita nawo m’kachisi wa Yehova ndipo anawatambasula posonyeza kuti wasiya nkhaniyo m’manja mwa Mulungu Wamphamvuyonse. Mulungu anayankha pemphero la Hezekiya ndipo anamuuza mawu olimbikitsa kudzera mwa mneneri Yesaya. Anamuuza kuti Senakeribu sadzalowa mumzinda wa Yerusalemu ndipo asilikali ake sadzaponya ngakhale muvi mumzindawo.
Usiku wa tsiku lomwelo Yehova anatumiza mngelo kumsasa wa Asuri. M’kanthawi kochepa mngelo mmodzi ameneyu anapha asilikali okwana 185,000 a Senakeribu. Yerekezerani kuti mukuona Senakeribu atadzuka m’mamawa n’kupeza mitembo yokhayokha ili mbwee. Zitatero iye anabwerera kwawo ali wamanyazi. Patapita nthawi, ana ake anamupha ali m’kachisi wa mulungu wake Nisiroki.
Choncho Yehova anathandiza Hezekiya kuti apambane. Tsopano Asuri kunalibenso komanso Hezekiya anali atachira matenda ake aja. Kenako iye anakhala ndi mwana. Koma n’zomvetsa chisoni kuti pa nthawi ina Hezekiya anachita zinthu modzikuza. Komabe Yehova atamudzudzula, iye anadzichepetsa n’kusintha. Choncho Hezekiya anali mmodzi mwa mafumu abwino a Isiraeli ndipo anasiya mbiri yakuti anachita zinthu molimba mtima pa nthawi yovuta.
Werengani nkhaniyi m’Baibulo:
Funso lokambirana:
Kodi Hezekiya anasonyeza kulimba mtima m’njira ziti?
Zoti Mufufuze
1. Kodi akatswiri ofukula zinthu zakale apeza zinthu ziti zimene zimatsimikizira kuti nkhani ya m’Baibulo ya Hezekiya inachitikadi? (w11 5/1 15 ¶1-3) A
Zev Radovan/Alamy Stock Photo
Chithunzi A: Pachidindo chadongo ichi chomwe ndi cha m’ma 800 B.C.E., panalembedwa mawu akuti: “La Hezekiya [mwana wa] Ahazi, Mfumu ya Yuda”
2. Kodi Hezekiya anakwaniritsa bwanji ulosi wa Yesaya wokhudza “njoka youluka, yaululu wamoto”? (Yes. 14:28, 29; ip-1 190-191 ¶4-6)
3. Pa zimene ofukula zinthu zakale anapeza ku Nineve, kodi Senakeribu anafotokoza zinthu ziti zomwe anakwanitsa kuchita, nanga anafotokoza zinthu ziti zomwe sanakwanitse kuchita? N’chifukwa chiyani zimenezi zili zochititsa chidwi? (g 12/10 27 ¶3-5) B
© The Trustees of the British Museum. Licensed under CC BY-NC-SA 4.0. Source
Chithunzi B: Nkhondo zomwe Senakeribu anapambana zinalembedwa pachinthu ichi chadongo
4. Mu 2003, asayansi ena anachita kafukufuku kuti adziwe ngati kunalidi Ngalande ya Hezekiya yomwe inamangidwa mu ulamuliro wake. Ndiye kodi anapeza zotani? (w09 5/1 27 ¶3-5)
Zomwe Tikuphunzirapo
Kodi chitsanzo cha Hezekiya chingalimbikitse bwanji Akhristu amene makolo awo satumikira Yehova? C
Chithunzi C
Pamene Senakeribu anaopseza kuti awononga Yerusalemu, kodi n’chiyani chimene Hezekiya ankadera nkhawa kwambiri? (2 Maf. 19:15-19) Nanga tingamutsanzire bwanji masiku ano?
Kodi mungatsanzire kulimba mtima kwa Hezekiya m’njira ziti?
Ganizirani Mfundo Yaikulu
Kodi nkhaniyi yandiphunzitsa chiyani za Yehova?
Kodi nkhaniyi ikugwirizana bwanji ndi cholinga cha Yehova?
Kodi ndingakonde kudzamufunsa chiyani Hezekiya akadzaukitsidwa?
Phunzirani Zambiri
Mukamaonera vidiyoyi, yerekezerani kuti mukuona nkhani yomwe inalembedwa pa 2 Mafumu 19:14-36 ikuchitika.
Kodi ulosi wa pa Mika 5:5 unakwaniritsidwa bwanji m’nthawi ya Hezekiya, nanga ukukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
“Kodi Abusa 7 ndi Atsogoleri 8 Akuimira Ndani Masiku Ano?” (w13 11/15 18-20 ¶9-18)