Mwana Wasukulu Apha Anthu Ambiri
Tsamba loyamba la nyuzipepala ina linali la mtundu wakuda ndipo panali mutu umodzi wokha wakuti: “N’chifukwa chiyani?” Anthu ambiri ankafunsa funso limeneli, mnyamata wina wa zaka 17 atawombera ndi kupha anthu 15 kenako n’kudziwombera yekha. Zimenezi zinachitika m’tawuni ya Winnenden yomwe ili kum’mwera m’dziko la Germany. Chifukwa cha zimenezi, boma linalamula kuti mbendera zitsitsidwe m’dziko lonselo. Posakhalitsa, nkhani yokhudza kuphedwa kwa anthuwa inafalikira padziko lonse.
Tawuni ya Winnenden ndi yotukuka ndiponso yabata. M’tawuniyi muli minda yokongola yamphesa ndiponso zipatso zina. Pa March 11, 2009, zinthu zinayamba monga mwa masiku onse pasukulu ya sekondale ya Albertville. Koma nthawi itakwana 9:30 m’mawa, mwadzidzidzi panayambika chipwirikiti.
Mnyamata wina yemwe poyamba ankaphunzira pasukuluyi, anatulukira mwadzidzidzi atatenga mfuti yomwe anaiba m’chipinda cha makolo ake. Mofulumira kwambiri, iye anawombera ndi kupha ana a sukulu 9 ndi aphunzitsi atatu omwe anali m’makalasi ndiponso panja. Komanso, anavulaza anthu ena ambiri. Posapita nthawi, apolisi anatulukira pamalowa ndipo mnyamatayo anathawira kuchipatala china chapafupi. Kumenekonso, iye anapha munthu wina wogwira ntchito pachipatalapo. Kenako analanda galimoto poopseza woyendetsa wake ndi mfuti n’kumukakamiza kuti amuyendetse. Atayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 40, woyendetsayo anapeza mpata wothawa. Atafika pamalo ena ogulitsira magalimoto, mnyamatayo anawombera ndi kupha munthu wogulitsa magalimoto ndiponso munthu wina yemwe anabwera kudzagula. Kenaka, anawombera ndi kuvulaza kwambiri apolisi awiri omwe ankafuna kumugwira. Koma apolisi ena atatsala pang’ono kumugwira, iye anadziwombera m’mutu.
Anthu amene ankamudziwa mnyamatayu ananena kuti iye anali munthu wabwinobwino ndipo ankasowa anzake ndiponso ankafuna kuti anthu ena azimukonda. Komano n’chiyani chinachititsa kuti achite zoopsa zimenezi? Zikuoneka kuti ankavutika maganizo ndiponso ankakonda mfuti zoseweretsa. Ankakondanso kuchita masewera a chiwawa a pakompyuta. Koma anthu ena amanena kuti zinam’chititsa si zimenezi chifukwa achinyamata ena amakondanso kuchita masewera amenewa. Nanga bwanji za anthu amene anawaphawo? Kodi panali anthu amene iye anawaganizira kuti awaphe kapena ankangopha mwachisawawa? Panali mphekesera zosiyanasiyana zokhuza chimene chinam’chititsa kuti aphe atsikana 8 ndi mnyamata mmodzi yekha. Koma palibe amene akudziwa chifukwa chenicheni.
Zimene Anthu Osiyanasiyana Anachita Atangomva Nkhaniyi
Mayi wina dzina lake Heike anati: “Mwana wathu ataimba foni n’kutiuza kuti mnyamata wina wapha anthu kusukulu, sindinakhulupirire. Koma nditamva kulira kwa magalimoto a polisi ndiponso ma ambulansi, ndinachita mantha kwambiri.” Zikuoneka kuti mnyamatayu akanapha anthu ambiri pasukulupo zikanakhala kuti apolisi sanafike msanga. Kenako, ana onse atawatulutsa m’makalasi n’kuwapititsa pamalo enaake abwino, panabwera anthu osiyanasiyana odzathandiza monga madokotala, anthu ena a zachipatala ndiponso atsogoleri a zipembedzo.
Atolankhani ambirimbiri anafika pasukuluyo mofulumira n’kuyamba kufunsa ana asukuluwo mafunso ngakhale kuti panthawiyi, ana ochuluka anali ali ndi mantha kwambiri. Mwana wina atawerengetsera, anapeza kuti panali magalimoto 28 a atolankhani ochokera kuwailesi zakanema 26. Atolankhaniwo ankachita kulimbirana kuti afunse mafunso ndipo zimenezi zinachititsa kuti ena alembe nkhani zopanda umboni. Tsiku lomwelo, mtolankhani wina mpaka anafika panyumba ya makolo a mmodzi wa atsikana amene anaphedwa n’kupempha kuti amupatse zithunzi za mtsikanayo. Ndipo atolankhani ena ankapereka ndalama kwa ana a sukulu kuti awajambule zithunzi. Chifukwa cha chipwirikiti chomwe chinalipo, atolankhani ena sankachita zoganizira komanso zolemekeza mabanja a anthu omwe anaphedwawo. Iwo ankachita zimenezi polimbirana kuti apeze nkhani zoti alembe.
Monga mmene zimakhalira nthawi zonse zoterezi zikachitika, anthu ankayembekezera kuti atsogoleri a zipembedzo awalimbikitsa ndiponso awafotokozera chifukwa chake zinthu ngati zimenezi zimachitika. Mnyamatayu atapha anthu, tsiku lomwelo zipembedzo zosiyanasiyana zinachita mapemphero awo pamodzi ndipo anthu ambiri anayamikira zimenezi. Komabe, anthu amene ankafuna kulimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu kapenanso amene anali ndi mafunso amene ankawavutitsa maganizo, anakhumudwa kwambiri. Mwachitsanzo, banja lina linapita kumaliro a mnzake wakusukulu wa mwana wawo. Mayi a banjalo anati: “Abishopu analalikira za mavuto a Yobu. Ndinkayembekezera kuti iwo alongosola zimene tikuphunzirapo pankhaniyo ndiponso atilimbikitsa, koma sananene chilichonse. Sanafotokoze chifukwa chake Yobu anavutika ndiponso zimene zinam’chitikira mavutowo atatha.”
Bambo winanso anakhumudwa kwambiri ndi mfundo zosalimbikitsa zimene anamva. Zaka pafupifupi 30 zapitazo, iye anaphunzirapo Baibulo ndi Mboni za Yehova koma anasiya. Tsopano, bamboyo wayambiranso kupita kumisonkhano ya Mboni za Yehova.
Mtsikana wina wa zaka 14, dzina lake Valisa, yemwe amaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anali m’kalasi pafupi ndi pamene mnyamatayo anaphera anthu. Atamva kulira kwa mfuti, anayamba kupemphera kwa Yehova. Nthawi ina atafunsidwa kuti afotokoze mmene ankamvera ndi zimene zinachitikazo, iye ananena kuti zimenezi zinangotsimikizira zimene anaphunzira m’Baibulo zokhudza masiku otsiriza ano. (2 Timoteyo 3:1-5) Zitachitika zimenezi, anthu awiri a Mboni za Yehova anayamba kulalikira uthenga wolimbikitsa m’deralo. Mayi wina wokalamba anauza anthu a Mboniwo kuti: “M’pofunika kuti anthu ambiri azichita zimene mukuchitazi.” Ngakhale kuti nkhani ya kuphedwa kwa anthuyi inali yomvetsa chisoni, inapangitsa anthu ena kuti amvetsere uthenga wolimbikitsa komanso wotonthoza wa m’Mawu a Mulungu.
Anthu Akuvutika Maganizo Akakumbukira Zimene Zinachitikazo
N’zoona kuti palibe mawu amene munthu anganene omwe angachotseretu mantha ndi chisoni chimene anthu amene anakhudzidwa ndi kuphedwa kwa anthuwa ali nacho. Palibe mawu amene angathetseretu chisoni chimene makolo amene ana awo anaphedwa ali nacho. Komanso palibe mawu amene angathetseretu chisoni chimene wapolisi wina ali nacho atathamangira kusukuluko n’kukapeza kuti mkazi wake anali m’gulu la anthu amene anaphedwa.
Ana asukulu amene anapulumukawo ndiponso mabanja awo anavutika maganizo kwambiri m’njira zosiyanasiyana. Mnyamata wina dzina lake Vassilios anadumpha kuchokera pawindo atangomva kulira kwa mfuti. Iye anafotokoza kuti: “Pomwe ndinkadumpha ndinapemphera kwa Yehova. Ndinkaganiza kuti ndifa ndipo ndinkaona kuti limeneli linali pemphero langa lomaliza.” Kwa milungu ingapo yotsatira, iye ankalota zoopsa ndipo sankafuna kulankhula ndi aliyense. Iye sanasangalale makamaka ndi zimene ofalitsa nkhani anachita polimbirana kuti apeze mfundo zoti alembe komanso pochita zinthu mosaganizira ena. Koma patapita nthawi, iye anangovomereza kuti ndi mmene zinthu zilili.
Mnyamata wina dzina lake Jonas anali kalasi imodzi ndi Vassilios ndipo anaona pomwe anzake asanu a m’kalasi ankaphedwa. Iye ananena kuti: “Zimenezi zitangochitika ndinkakonda kuuza anthu zimene zinachitikazo chifukwa zinali ngati ndikuwauza za m’filimu inayake yoopsa. Koma panopo zikumandivuta kufotokoza mmene ndikumvera. Nthawi zina sindifuna kuuza anthu zimene zinachitikazo, koma nthawi zina ndimakonda kufotokoza zimene zinachitikazo.” Iye amalotanso zoopsa ndipo amavutika kugona.
Patapita masiku angapo, ana asukuluwo anawapatsa zinthu zawo zomwe anazisiya m’kalasi. Madokotala othandiza anthu ovutika maganizo anachenjeza kuti anawo akaona zinthu zawozo angamakumbukire zoopsa zimene zinachitikazo. Poyamba, Jonas sankafuna n’komwe kugwira chikwama, jekete ndiponso chipewa chake cha njinga yamoto. Ankaopanso kwambiri akangoona munthu wooneka ngati mnyamata amene anapha anthu uja kapena munthu amene waberekera chikwama chofanana ndi cha mnyamata amene anapha anthu uja. Makolo ake akamaonera filimu ndipo mufilimumo mukamveka kulira kwa mfuti, iye ankachita mantha kwambiri. Madokotala anayesetsa kuthandiza ana amene anaona zoopsazi kuti asamavutike maganizo akakumbukira zimene zinachitikazo.
Bambo ake a Jonas omwe dzina lawo ndi a Jürgen, amagwira ntchito kuchipatala chimene mnyamata uja anaphako munthu. Bambowa anafotokoza kuti makolo ambiri ndiponso anzawo ankavutika kwambiri maganizo ndipo ankadzifunsa kuti “N’chifukwa chiyani? Nanga bwanji akanandiwombera?” Mwachitsanzo mayi wina yemwenso amagwira ntchito pachipatalacho anaima pakhonde la chipatalacho ndipo anaona munthu amene anapha anthuyo akudutsa chapafupi. Mayiyu ankachita mantha akaganiza kuti nayenso akanaphedwa. Kuti athetse mantha amenewa, mayiyu anafunika kuthandizidwa ndi madokotala othandiza anthu ovutika maganizo.
Mmene Anthu ena Anathandizidwira
Kodi anthu ena chawathandiza n’chiyani kuti apirire zoopsa zimene zinachitikazo? Jürgen ananena kuti: “Ngakhale kuti nthawi zina ndimavutika kwambiri, ndimasangalala ndikamacheza ndi ena. Ndipo n’zothandiza kwambiri ukadziwa kuti ena amakukonda komanso kukuganizira.”
Nayenso Jonas amayamikira kwambiri kuti anthu ena amamukonda, iye anati: “Anthu ambiri ananditumizira mauthenga. Ena analembamo mavesi a m’Baibulo ndipo zimenezi zinali zolimbikitsa kwambiri.” Kodi n’chiyaninso chimene chinamuthandiza? Iye anati: “Ndikadzidzimuka usiku ndipo ndikayamba kuvutika maganizo, ndimapemphera. Nthawi zina ndimamvetsera nyimbo kapena ma CD a Galamukani!”a Iye ananenanso kuti Baibulo limanena chifukwa chake zinthu zimenezi zimachitika. Chifukwa chake n’chakuti Satana ndi amene akulamulira dzikoli ndiponso tikukhala m’masiku otsiriza. Bambo ake ananena kuti mfundo zimenezi zinawathandiza kuti apirire.
Mavuto Onse Atha Posachedwapa
Patapita masiku ochepa, anthu ambiri anaika makandulo, maluwa ndiponso makalata kutsogolo kwa sukuluyo. Mtsikana wina dzina lake Kerstin anaona kuti anthu ambiri analemba funso lakuti, n’chifukwa chiyani zimenezi zinachitika ndipo n’chifukwa chiyani Mulungu analola kuti zichitike? Ataona kuti mafunso amenewa anafunika kuyankhidwa, Kerstin ndi anzake awiri a Mboni analemba kalata n’kuiika pomwe panali makalata ena aja.
Pamwambo wokumbukira anthu amene anaphedwawo, wailesi ina ya kanema inaonetsa kalatayo ndipo inaonetsa mawu oyamba a kalatayo akuti: “N’chifukwa chiyani? M’masiku otsiriza ano anthu ambiri akufunsa funso limeneli, makamaka funso lakuti: Kodi Mulungu anali kuti? Nanga n’chifukwa chiyani analola kuti zimenezi zichitike?” Koma zokhumudwitsa n’zakuti wailesi ya kanemayo inangoonetsa mawu okhawa basi.
N’chifukwa chiyani zili zokhumudwitsa? Chifukwa choti kalatayo inapitiriza kufotokoza chimene chinayambitsa kuti anthu azivutika ndipo inafotokoza kuti Mulungu “adzaonetsetsa kuti zoipa zonse zimene anthu akuchita zitheretu.” Ndiponso kalatayo inanena kuti: “M’buku la Chivumbulutso, Mulungu ananena kuti adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Yehova Mulungu adzaukitsa ngakhale akufa. Mu Ufumu wake womwe watsala pang’ono kufika, simudzachitikanso zinthu zoopsa, kuphana kapena mavuto aliwonse. Mulungu analonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.”—Chivumbulutso 21:4, 5.
[Mawu a M’munsi]
a Magazini ya Galamukani! imapezekanso pa CD ndipo imafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 12]
Jonas analandira khadi la mawu akuti: “Timakukonda”
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Focus Agency/WPN
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
© imagebroker/Alamy
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Foto: picture alliance
[Mawu a Chithunzi patsamba 11]
Foto: picture alliance