Moyo wa Anthu Akale Oimba Nyimbo Komanso Zida Zawo
“Mutamandeni [Mulungu] mwa kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa. Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe ndi zeze. Mutamandeni ndi maseche ndi gule wovina mozungulira. Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe ndi chitoliro. Mutamandeni ndi chinganga cha mawu osangalatsa. Mutamandeni ndi chinganga cha mawu amphamvu.”—SALIMO 150:3-5.
KUYAMBIRA kale, nyimbo zakhala zikugwiritsidwa ntchito kwambiri polambira Yehova Mulungu. Mwachitsanzo, Yehova atalanditsa Aisiraeli mozizwitsa pa Nyanja Yofiira, Miriamu, yemwe anali mlongo wake wa Mose, anatsogolera akazi kuimba nyimbo zotamanda Yehova. Anthu amenewa ankaimba maseche ndi kuvina. Zimene zinachitikazi zikusonyeza kuti Aisiraeli ankaona kuti kuimba n’kofunika kwambiri. Pa nthawiyi, iwo anali atangopulumutsidwa kumene m’manja mwa gulu lankhondo la Aiguputo koma akazi ambiri sanavutike kupeza zida zawo zoimbira n’kuyamba kuimba nthawi yomweyo. (Ekisodo 15:20) Patapita nthawi, Mfumu Davide inakonza zoti pakhale oimba ambiri oti aziimba pachihema pa nthawi yolambira. Dongosolo limeneli linapitiriza kuchitika pakachisi amene Solomo anamanga.—1 Mbiri 23:5.
Kodi zida zoimbira zimenezi zinkapangidwa ndi chiyani? Kodi zinkaoneka bwanji? Kodi zinkamveka bwanji akamaziimba? Nanga ankazigwiritsa ntchito pa zochitika zotani?
Mitundu Yosiyanasiyana ya Zida Zoimbira
Zida zoimbira zotchulidwa m’Baibulo zinkapangidwa ndi matabwa amtengo wapatali, zikopa za nyama, zitsulo ndiponso mafupa. Zina zinkakutidwa ndi minyanga ya njovu. Nsambo zake zinkakhala zopangidwa ndi luzi la mtengo kapena matumbo a nyama. Zida zoimbira zakalezi sizipezeka masiku ano komabe zithunzi zake zilipo.
Zida zakalezi zikhoza kugawidwa m’magulu atatu: Zoimbira za zingwe monga zeze (1) ndi choimbira changati gitala (2). Zida zoimba ndi pakamwa monga malipenga a nyanga (3), malipenga achitsulo (4) komanso zitoliro (5). Zoimba ndi manja, monga maseche (6, 7), zinganga (8), komanso mabelu (9). Oimba ankagwiritsa ntchito zida zimenezi povina, poimba nyimbo zolembedwa mwandakatulo komanso poimba nyimbo zina. (1 Samueli 18:6, 7) Njira yofunika kwambiri imene ankagwiritsira ntchito zida zimenezi ndi polambira Mulungu amene anawadalitsa ndi luso loimbali. (1 Mbiri 15:16) Tiyeni tikambirane magulu a zida zoimbira amenewa lililonse palokha.
Zoimbira za Zingwe Azeze ankakhala opepuka komanso osavuta kunyamula ndipo ankakhala ndi nsambo zimene ankazikunga pathabwa. Mfumu Sauli ikavutika maganizo, Davide ankatenga zeze n’kuiimbira nyimbo ndipo mfumuyo inkapeza bwino. (1 Samueli 16:23) Azeze anagwiritsidwanso ntchito ndi gulu lomwe linkaimba potsegulira kachisi wa Solomo, komanso ankagwiritsidwa ntchito pa zikondwerero zina.—2 Mbiri 5:12; 9:11.
Choimbira changati gitala chinkakhala ndi nsambo zochepa poyerekeza ndi zeze ndipo nsambozi ankazikunga pathabwa lomwe ankalilumikiza kun’goma ya choimbiracho. Nsambo za choimbira chimenechi zinkatulutsa nyimbo zokoma zofanana ndi za magitala amakono oimbira nyimbo za classic. Popanga nsambozi, ankapota luzi kapena matumbo a nyama.
Zida Zoimba Ndi Pakamwa Zida zimenezi zimatchulidwa kawirikawiri m’Baibulo. Pa zida zonse zoimbidwa ndi pakamwa, chida chakale kwambiri ndi lipenga la nyanga ya nkhosa limene Ayuda ankagwiritsa ntchito, lotchedwa shofar. Lipenga la nyanga limeneli lomwe linkakhala loboola konsekonse, linkamveka mokwera kwambiri. Aisiraeli ankagwiritsa ntchito lipenga limeneli akafuna kusonkhanitsa magulu ankhondo komanso akafuna kuwadziwitsa nthawi yoyamba kumenya nkhondo.—Oweruza 3:27; 7:22.
Mtundu wina wa choimbira choimba ndi pakamwa ndi lipenga lachitsulo. Zolembedwa zina zimene anazipeza limodzi ndi Mipukutu ya ku Nyanja Yakufa zimasonyeza kuti oimba ankatha kuimba chida chimenechi n’kumamveka mosiyanasiyana. Yehova anauza Mose kuti apange malipenga awiri asiliva kuti aziwagwiritsa ntchito kuchihema. (Numeri 10:2-7) Patapita nthawi, potsegulira kachisi wa Solomo, ansembe anaimba malipenga 120 ndipo zimenezi zinawonjezera chisangalalo pachikondwererocho. (2 Mbiri 5:12, 13) Anthu aluso ankapanga malipenga otalika mosiyanasiyana. Malipenga ena ankakhala otalika masentimita 91 ndipo kumapeto kwake kunkakhala kwakukulu ngati belu.
Chida choimba ndi pakamwa chimene Aisiraeli ankagwiritsa ntchito kwambiri chinali chitoliro. Tinyimbo tosangalatsa toimbidwa ndi zitoliro tinkasangalatsa anthu akasonkhana ndi mabanja awo, akakhala paphwando komanso pa ukwati. (1 Mafumu 1:40; Yesaya 30:29) Pamaliro pankaimbidwanso nyimbo zogwira mtima zoimbidwa ndi zitoliro ndipo nyimbozi zinali mbali ya mwambo wamalirowo (onani tsamba 14).—Mateyu 9:23.
Zoimba Ndi Manja Aisiraeli akakhala pazikondwerero, ankagwiritsa ntchito zida zosiyanasiyana zoimba ndi manja. Kugunda kwa zoimbirazi kunkapangitsa kuti nyimbozo zikhale zotenga mtima komanso zosangalatsa. Maseche ena ankakhala opangidwa ndi chikopa cha nyama chomwe ankachikunga pathabwa lozungulira. Masechewo ankamveka ngati kang’oma woimba kapena wovina akawamenya ndi dzanja. Komanso akamawakhutchumula, timabelu timene ankatimangirira kuthabwalo tinkalira mosangalatsa.
Maseche ena ankapangidwa ndi chitsulo chopindidwa mozungulira ndipo ankakhala ndi chigwiriro. Pachitsulopo ankazikapo timawaya mopingasa ndipo patimawayato ankamangirirapo tizitsulo tina tozungulira ngati ndalama. Woimba chidachi akamachikhutchumula chinkatulutsa phokoso lotenga mtima.
Zinganga zachitsulo zinkatulutsa phokoso lokwera kwambiri. Zingangazi ankazipanga ndi malata awiri ozungulira ngati mbale ndipo zina zinkakhala zazikulu pamene zina zinkakhala zazing’ono. Zazikuluzi ankazimenyanitsa mwamphamvu pomwe zazing’ono ankaziika pakati pa zala n’kumazimenyanitsa. Zinganga zonse ziwirizi zinkalira mofanana koma zinkangosiyana kuchuluka kwa phokoso lake.—Salimo 150:5.
Mboni za Yehova Zimatsatira Chitsanzo Cha Anthu Akale
Masiku ano, misonkhano ya Mboni za Yehova imayamba komanso kutha ndi nyimbo. Komanso pamisonkhano yawo ikuluikulu, zing’wenyeng’wenye zimene amatsatira poimba, zimakhala zoimbidwa ndi zida za zingwe, zida zoimba ndi pakamwa komanso zida zoimba ndi manja zamakono.
A Mboni akamaimba nyimbo pamisonkhano yawo amakhala akutsanzira zimene Aisiraeli akale komanso Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankachita. (Aefeso 5:19) Mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, a Mboni za Yehova masiku ano amasangalala kuimba nyimbo zotamanda Yehova.
[Zithunzi patsamba 23]
(Mmene zidazi zinkaonekera)
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)