Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w14 4/1 tsamba 3
  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera kwa Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera kwa Mulungu?
  • Nsanja ya Olonda—2014
  • Nkhani Yofanana
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kuti Mulungu Akhale Mnzanu
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Yesu Atiphunzitsa Ife Kupemphera
    Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2014
w14 4/1 tsamba 3
Mnyamata akupemphera

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI KUPEMPHERA N’KOTHANDIZADI?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amapemphera kwa Mulungu?

Kodi inuyo mumakonda kupemphera? Anthu ambiri amakonda kupemphera, ngakhalenso amene amati kulibe Mulungu. Koma kodi n’chifukwa chiyani anthu amapemphera? Kafukufuku amene anachitika ku France anasonyeza kuti mofanana ndi anthu ambiri a ku Ulaya, hafu ya anthu a m’dzikoli nthawi zina amapemphera kapena kusinkhasinkha koma osati n’cholinga chofuna kulambira Mulungu. Iwo amapemphera “n’cholinga chongofuna kuchepetsako nkhawa” kapena chifukwa choganiza kuti “pemphero liwathandiza kuti mtima wawo ukhale m’malo.” Koma palinso anthu ena amene amangopemphera kwa Mulungu zinthu zikawathina ndipo amayembekezera kuti Mulungu awathetsera mavuto awowo nthawi yomweyo.—Yesaya 26:16.

Kodi inuyo mumaiona bwanji nkhani ya pemphero? Kodi mumaganiza kuti pemphero limangomuthandiza munthu kuti ayambe kuona zinthu moyenera? Ngati mumakhulupirira Mulungu, kodi mumaona kuti kupemphera kumakuthandizani, kapena mumaona kuti mapemphero anu sayankhidwa? Baibulo lingakuthandizeni kudziwa kuti pemphero si njira yongochepetsera nkhawa, koma ndi njira yapadera yokuthandizani kuyandikira Mulungu.

Anthu akupemphera: Timu ya mpira itachinya chigoli, mwamuna ali ndi mkazi wake yemwe akudwala ndipo ali m’chipatala, asilikali pa nthawi ya nkhondo
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena