Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp16 No. 6 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Onse?
  • Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake popemphera?
  • Tili Ndi Mwayi Wopemphera kwa Mulungu
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Pemphero Lingakuthandizeni Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Mulungu Angayankhe Mapemphero Anga?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kuyandikira kwa Mulungu m’Pemphero
    Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2016
wp16 No. 6 tsamba 16
Mzimayi akupemphera

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mulungu Amayankha Mapemphero Onse?

KODI MUNGAYANKHE KUTI . . .

  • Amayankha mapemphero onse

  • Amayankha mapemphero ena

  • Sayankha

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Yehova ali pafupi ndi onse . . . amene amamuitana m’choonadi.”—Salimo 145:18.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mulungu samvetsera mapemphero a anthu amene samumvera. (Yesaya 1:15) Komabe anthu oterewa akhoza kusintha zochita zawo n’kukhala “pa ubwenzi wabwino” ndi Mulungu.—Yesaya 1:18.

  • Kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kupemphera mogwirizana ndi mfundo zimene amatiuza m’Baibulo.—1 Yohane 5:14.

Kodi tiyenera kukhala mwanjira inayake popemphera?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti ayenera kupemphera atagwada, atazyolika kapena ataika manja awo pamodzi. Nanga inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Mulungu anamvetserapo mapemphero a anthu omwe ankapemphera ‘atakhala pansi,’ ‘ataimirira’, ‘atagona’ kapenanso ‘atagwada.’ (1 Mbiri 17:16; 2 Mbiri 30:27; Ezara 10:1; Machitidwe 9:40) Choncho Mulungu safuna kuti anthu azichita kukhala mwanjira inayake akamapemphera.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mulungu amamvetsera mapemphero a anthu odzichepetsa.—Salimo 138:6.

  • Mukhoza kupemphera kwa Mulungu chamumtima komanso m’chinenero chilichonse.—2 Mbiri 6:32, 33; Nehemiya 2:1-6.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 17 m’buku ili,Zimene Baibulo Limaphunzitsa? lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena